“Mboni za Yehova Zandichinjiriza!”
MKATI mwa masiku ano otsiriza, ambiri akhaladi “aukali, osakonda abwino.” (2 Timoteo 3:1, 3) Isaac, mtumiki wodzipereka modzifunira pa ofesi yanthambi ya Watch Tower Society mu West Africa, anatsimikizira zimenezi kukhala zoona. Iye akusimba kuti:
“Mu January 1992, ndinali kuyenda pa msewu wautali wopanda anthu mu takisi ya onse ndi apaulendo ena asanu. Ndinayamba kukambitsirana ndi mkazi amene anakhala pafupi nane, ndipo mwachimwemwe analandira brosha lonena za Baibulo.
“Mwadzidzidzi, pafupifupi 4 koloko masana, galimoto latsopano lopanda nambala linatidulira kutsogolo, ndipo galimoto lathu linalira kuti kwichi pamene linaima mwadzidzidzi. Amuna atatu okulupala, aliyense atanyamula mfuti, anatuluka m’galimoto linalo ndi kutsegula zitseko zathu. ‘Tulukani nonsenu,’ anatuluma motero mmodzi wa iwo.
“Mwamuna wina anatsomphola chola changa chamabuku. Pamene anaona kuti chinali ndi mabuku a Baibulo okha, anachitaya kumbali. ‘Kodi nchiyani china chimene uli nacho?’ anafunsa choncho atandiloza mfuti yake. Mwamsanga ndinampatsa ndalama zimene zinali m’kachikwama kanga. ‘Kodi nzomwezi?’ iye anafunsa motero. Ndinamuuza kuti ndinali mmodzi wa Mboni za Yehova ndi kuti Mboni sizimanama. Ananditsomphola kachikwamako, naona khadi langa lodziŵikitsa la Watch Tower ndiyeno anati, ‘Oo, Wachitawala. Dikira apa.’
“Kenako, anatembenukira kwa mkazi amene ndinalankhula naye m’takisimo. Iye anachotsa mwamsanga unyolo wake wa m’khosi nampatsa ndalama zimene zinali m’chikwama chake. Pamene wakubayo anaona brosha m’dzanja lake lonjenjemera, anaganiza kuti tinali pamodzi, ndipo anamuuza kukhala nane.
“Panthaŵiyo, mbala zina za mfutizo zinaukira mwaukali apaulendo anzathu. Zinamenya ndi kubera dalaivala ndi mwamuna wina amene tinali naye paulendowo. Wakuba wina anagwira unyolo wa m’khosi wa mkazi wina. Pamene analimbalimba, anamkang’antha ndi thendere la mfuti pa mutu ndi pachifuwa kufikira anafa. Mkazi wina wachitatu anamkokera kunja kwa galimotolo ndi kumuwombera pachifuwa. Mwachisoni, nayenso anafa. Ine ndekha ndi mkazi wachichepereyo tinasiyidwa osavulazidwa.
“Pambuyo pake pamene tinanyamulidwa ndi galimoto lodutsa, mkazi wamanthayo anapitiriza kubwereza mawu akuti, ‘Mboni za Yehova zandichinjiriza!’”