Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 5/15 tsamba 31
  • Mbiri Yabwino Yochokera ku Malaŵi!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mbiri Yabwino Yochokera ku Malaŵi!
  • Nsanja ya Olonda—1994
Nsanja ya Olonda—1994
w94 5/15 tsamba 31

Mbiri Yabwino Yochokera ku Malaŵi!

PA NOVEMBER 15, 1993, Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania inalembetsedwa mwalamulo m’dziko la kummwera koma cha kummaŵa kwa Afirika la Malaŵi. Zimenezi zikazindikiritsa Mboni za Yehova mwalamulo ndi kuzipatsa ufulu wa kulalikira choonadi cha Baibulo kwa anthu a m’Malaŵi.

Kalelo mu 1948, ofesi yanthambi ya Watch Tower Society inakhazikitsidwa m’Malaŵi kugwirizanitsa ntchito ya Mboni za Yehova m’dziko limenelo. Pa January 8, 1957, Watch Tower Society inalembetsedwa kumeneko kwa nthaŵi yoyamba. Kwa zaka zingapo Mboni za Yehova zinakondwera ndi chiŵerengero chomakula mofulumira. Koma chizunzo chachiwawa chinaulika mu 1964. Chifukwa ninji?

Chifukwa cha kumvera Mulungu, Mboni za Yehova zinasunga uchete wamphamvu m’ndale. (Yohane 17:16) Mwachionekere, ena sanamvetsetse bwino kaimidwe ka Malemba kameneka ndi kuziona molakwa Mboni kukhala chipembedzo chofuna kusintha zinthu ndiponso monga oletsedwa ndi lamulo. Chifukwa chake, ena analingalira kukhala olungama pozunza Akristu okonda mtendere ameneŵa. Mboni zambiri zinachotsedwa ntchito, kumenyedwa, ndi kunyazitsidwa mwa njira zina. Ena anapirira kupweteka kwa kupatulidwa mokakamizidwa ndi ana awo.

Mu 1972 Mboni zoposa 30,000 ndi ena amene anali kuphunzira nazo Baibulo anafunikira kuchoka m’dzikomo kuwopera kutaya miyoyo yawo. Zikwi zambiri zinakhala m’misasa ya othaŵa kwawo mu Mozambique wapafupi. Koma mu 1975 othaŵa kwawo ameneŵa anabwezeretsedwa ku Malaŵi, kumene anayang’anizana ndi chizunzo chowonjezereka. Ambiri anaikidwa m’misasa yachibalo. Mkati mwa zovuta zimenezi, Watch Tower Society inafutidwa pa ndandanda ya magulu ovomerezedwa mwa lamulo m’Malaŵi. Kuyambira panthaŵiyo Mboni za Yehova ndi magulu awo ovomerezedwa mwalamulo anali oletsedwa m’dzikolo.

Mosasamala kanthu za zochitika zimenezi, Mbonizo sizinabwezere. Izo sizinapange konse magulu achiwawa kapena kusakaza katundu wa ena kusonyeza kusakondwa ndi boma. Mmalo mwake, mwa pemphero izo zinasunga thayo lawo Lachikristu la kusonyeza ulemu woyenerera kwa “maulamuliro aakulu” aboma. (Aroma 13:1-7; 1 Timoteo 2:1, 2) Mbonizo zinachirikizanso miyezo yapamwamba ya chikhalidwe cha Chikristu yoperekedwa m’Baibulo ndipo motero zapitiriza kupereka chitsanzo chabwino koposa cha chikhalidwe.

Pokhala ndi ufulu wawo wopezedwa chatsopano, Mboni za Yehova m’Malaŵi zili zotsimikiza kupitiriza kulalikira choonadi cha Baibulo, “pa nthaŵi yake.”​—2 Timoteo 4:2.

[Chithunzi patsamba 31]

M. G. Henschel ndi banja la Beteli la Malaŵi m’ma 1960

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena