Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 1/1 tsamba 3-4
  • Pamene Kummaŵa Kugwirizana ndi Kumadzulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pamene Kummaŵa Kugwirizana ndi Kumadzulo
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ‘Kuchokera Kummaŵa ndi Kuchokera Kumadzulo’
  • Kodi Nkhosazo ndi Mbuzizo Zili ndi Mtsogolo Motani?
    Nsanja ya Olonda—1995
  • “Khamu Lalikulu” Litamanda Boma la Dziko Likudza’lo
    Boma Lathu la Dziko Likudza’lo—Ufumu wa Mulungu
  • Khamu Lalikulu la Olambira Oona—Lachokera Kuti?
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Khristu Akadzayamba Kulamulira Adzaweruza Nkhosa ndi Mbuzi
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 1/1 tsamba 3-4

Pamene Kummaŵa Kugwirizana ndi Kumadzulo

“HA, KUMMAŴA Nkummaŵa, ndipo Kumadzulo Nkumadzulo ndithu, ndipo mbali ziŵirizo sizidzagwirizana konse.” Mawu ameneŵa a wolemba ndakatulo wa ku Britain Rudyard Kipling akutikumbutsa za kusiyana kwakukulu kwamakhalidwe kumene kumagaŵanitsa mtundu wa anthu, kumene kumachirikiza maudani aufuko, utundu, ndi adziko amene akufalikira motizinga lerolino. Ambiri amafunsa kuti, Kodi Mulungu sangachitepo kanthu pa mkhalidwewu? Inde, akhoza kutero! Ndipo ngakhale panopo iye akuchitapo kanthu! Mzera wotsatira wa ndakatulo ya Kipling unasonya zimenezi. Kodi Kummaŵa ndi Kumadzulo kukakhala kogaŵanikana kwautali wotani? Wandakatuloyo anati: “Kufikira pamene Dziko Lapansi ndi Thambo posachedwapa zidzaima pamaso pa Mpando waukulu Wachiweruzo wa Mulungu.”

Mulungu wapereka thayo la kuweruza kwa Mwana wake, Yesu Kristu. (Yohane 5:22-24, 30) Koma kodi nthaŵi ya kuweruza imeneyo ikuyamba liti? Kodi ndani amene akuweruzidwa, ndipo ndi chotulukapo chotani? Anali Yesu amene anafotokoza muulosi nkhondo zadziko ndi mavuto otsagana nazo amene anayamba kukantha mtundu wa anthu m’chaka cha 1914. Iye ananena kuti zimenezi zimasonyeza “chizindikiro” cha “kukhalapo [kwake kosaoneka] ndi cha mapeto a dongosolo la zinthu.”​—Mateyu 24:3-8, NW.

Pakaindeinde pa ulosi waukulu umenewu, Yesu akutchula nthaŵi yathu ino kukhala ya chiweruzo, akumanena za iyemwini kuti: “Pamene Mwana wa munthu adzadza muulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo iye adzakhala pa chimpando cha kuŵala kwake: ndipo adzasonkhanidwa pamaso pake anthu a mitundu yonse; ndipo iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi; nadzakhalitsa nkhosa kudzanja lake lamanja, koma mbuzi kulamanzere.” Mophiphiritsira, anthu onse a padziko lapansi asonkhanitsidwa tsopano pamaso wa Woweruzayo ndipo ayenera kuyankha kaamba ka mmene amalabadirira uthenga wake wa chipulumutso. Pamene chiweruzo chidzaperekedwa posachedwapa pa chisautso chachikulu, anthu osamvera onga mbuzi “adzachoka kumka ku chilango cha nthaŵi zonse; koma olungama [omvera onga nkhosa] ku moyo wa nthaŵi zonse.”​—Mateyu 25:31-33, 46; Chivumbulutso 16:14-16.

‘Kuchokera Kummaŵa ndi Kuchokera Kumadzulo’

Chiweruzo cha dzikoli chinayambadi mkati mwa zaka zowopsa za Nkhondo Yadziko I. Panthaŵiyo, atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu anachirikiza ndi mtima wonse magulu omenyanawo. Zimenezi zinawazindikiritsa kukhala mbali ya dziko loipali loyenerera “mkwiyo wa Mulungu.” (Yohane 3:36) Komabe bwanji nanga za Akristu okonda mtendere amene anasonyeza chikhulupiriro mwa Mulungu? Kuyambira m’chaka cha 1919, ameneŵa anayamba kusonkhanitsidwira kumbali ya Mfumuyo, Kristu Yesu.

Iwo anabwera kuchokera kumbali zonse zadziko, choyamba otsalira odzozedwa a 144,000, osankhidwa m’nyengo ya zaka mazana ambiri Yachikristu. Iwo akakhala “oloŵa anzake a Kristu” mu Ufumu wake wakumwamba. (Aroma 8:17) Kwa iwowa, mneneri wa Mulungu akuti: “Usawope; pakuti ine ndili ndi iwe; ndidzatenga mbewu zako kuchokera kummaŵa, ndi kusonkhanitsa iwe kuchokera kumadzulo. Ine ndidzati ndi kumpoto, Pereka; ndi kummwera, Usaletse; bwera nawo ana anga aamuna kuchokera kutali, ndi ana anga aakazi kuchokera ku malekezero a dziko lapansi; yense wotchedwa dzina langa, amene ndinamlenga chifukwa cha ulemerero wanga; ndinamuumba iye; inde, ndinampanga iye.”​—Yesaya 43:5-7.

Komatu sizokhazo! Makamaka kuyambira m’ma 1930, khamu lalikulu, tsopano lomafika mamiliyoni, linayamba kusonkhanitsidwa. Ameneŵa ndiwo “nkhosa” zimene Yesu anatchula pa Mateyu 25:31-46. Mofanana ndi otsalira odzozedwa amene anasonkhanitsidwa poyamba, ameneŵa amafika pakukhala ndi “chikhulupiriro” mwa Uyo amene akulengeza kuti: ‘Inu ndinu mboni zanga, ndipo ine ndine Mulungu.’ (Yesaya 43:10-12) Kusonkhanitsidwa kwa khamu lalikulu limeneli kukuchitikanso ‘kuchokera kummaŵa ndi kumadzulo, kuchokera kumpoto ndi kummwera, ndi kuchokera ku malekezero a dziko lapansi.’

Nkhosa zokonda mtendere zimenezi zikugwirizanitsidwa m’gulu limodzi la abale lamitundu yonse. Izo zimalankhula zinenero zambiri zosiyanasiyana za m’maiko 231 mmene zimakhala. Komabe zili zogwirizana mwauzimu m’kuphunzira “chinenero choyera” cha uthenga Waufumu wa Baibulo, “kuti iwo onse aitanire pa dzina la Yehova, kuti amtumikire pheŵa ndi pheŵa.” (Zefaniya 3:9, NW) Kugwirizana kwawo kwa chikhulupiriro, chifuno, ndi zochita zimapereka umboni wabwino kwambiri wakuti Kummaŵa kwagwirizanadi ndi Kumadzulo, ndipo anthu ochokera ku mbali zonse zadziko, kutumikira ndi kutamanda Mfumu Ambuye Yehova.

M’maiko ena kusonkhanitsa kumeneku kukuchitika m’mikhalidwe yodabwitsa kwambiri, monga momwe malipoti otsatirapowa adzasonyezera.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena