Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 11/15 tsamba 23-27
  • Kulalikira Kumudzi ndi Mudzi mu Spain

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulalikira Kumudzi ndi Mudzi mu Spain
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Chilolezo Chalamulo Chisonkhezera Umboni wa m’Midzi
  • ‘Funitsani Oyenera’
  • Oŵerenga Baibulo Akuvomereza Mosavuta
  • Kulaka Kulingaliridwa Molakwa
  • Kufunafuna Chowonadi m’Baibulo
  • Kututa Kwabwino
Nsanja ya Olonda—1993
w93 11/15 tsamba 23-27

Kulalikira Kumudzi ndi Mudzi mu Spain

YESU KRISTU anayendayenda “pakati pa mizinda ndi midzi, naphunzitsa, nayenda ulendo kumkabe ku Yerusalemu.” (Luka 13:22) Kuti akwaniritse utumikiwo, Yesu ndi ophunzira ake sanalalikire ‘kumzinda ndi mzinda’ kokha komanso ‘kumudzi ndi mudzi.’ Ngakhale kuti kukanakhala kosavutirapo kulalikira m’mizinda mokha, iwo sanapitirire midzi yambiri yokhala m’mbali mwa mizinda.a

Mboni za Yehova mu Spain zinayang’anizana ndi chitokoso chofanana ndi cha Yesu. Osati kale kwambiri mu 1970, panali madera aakulu akumidzi osafoledwapo chikhalire oyembekezera kututidwa. (Mateyu 9:37, 38) Mazana ambiri a midzi ya m’mapiri amvula kumpoto, m’zidikha zouma m’chigawo chapakati, ndi m’mphepete mwa gombe inali isanafikiridwepo ndi uthenga wa Ufumu.

Mboni za Yehova za ku Spain zinali zofunitsitsa kuyesayesa mwamphamvu kotero kuti zipereke mbiri yabwino kuzigawo zimenezi. Koma kodi nchifukwa ninji anthu a m’madera ameneŵa anali asanamve uthenga wa Ufumu kwanthaŵi yaitali yonseyo? Ndipo kodi anaulandira motani?

Chilolezo Chalamulo Chisonkhezera Umboni wa m’Midzi

Ntchito ya Mboni za Yehova mu Spain inali yoletsedwa chiyambire pamene nkhondo yachiweniweni inatha mu 1939. Mkati mwa ma 1950 ndi ma 1960, Mboni zachangu zinalalikira mochenjera m’mizinda, mmene sizinadziŵike kwambiri. Pamene ntchito yawo inaloledwa potsirizira pake mu 1970, mu Spain munali ofalitsa Ufumu pafupifupi 10,000. Pafupifupi onsewo anali kukhala m’mizinda ndi m’matauni aakulu, koma midzi ya mu Spain inafunikiranso kumva uthenga wa Ufumu. Kodi ndani akayang’anizana ndi chitokosocho?

M’ma 1970 mkupiti unalinganizidwa wofikira madera onse a chisumbucho ndi mbiri yabwino. Pafupifupi mwezi uliwonse kuyambira mu 1973 mpaka mu 1979, zilengezo zapadera zofotokoza kusoŵa m’zigawo zosiyanasiyana za dzikolo zinaperekedwa mu Utumiki Wathu Waufumu, chofalitsidwa chautumiki cha mwezi ndi mwezi cha mipingo ya Mboni za Yehova. Mabanja ambiri ofunitsitsa anayankha pempholo ndipo anadzipereka kukatumikira kumene kunali kusoŵa kokulira.

Chitsanzo chapadera ndicho cha Rosendo ndi mkazi wake, Luci. Iwo anatumizidwa monga apainiya apadera (alaliki anthaŵi yonse a Ufumu) kumudzi wa asodzi kumpoto chakummwera kwa Spain ndiyeno anasankha kukhaliratu kumaloko pamene anakhala makolo. “Ndiyenera kuvomereza kuti tinakumana ndi nthaŵi zovuta kwambiri,” akutero Rosendo. “Ntchito yakuthupi inali yovuta kupeza, koma tinadalira chithandizo cha Yehova ndipo sitinasoŵepo chakudya kapena kusoŵa pogona. Kuvutikako kunalidi koyenerera.” Kwazaka zambiri, iwo akhoza kuthandiza kupangidwa kwa mipingo inayi m’chigawo chimenechi cha Spain.

‘Funitsani Oyenera’

Yesu anauza ophunzira ake ‘kufunitsa’ oyenera mumzinda uliwonse kapena mudzi. (Mateyu 10:11) M’madera akumidzi a Spain, kufunafuna kotero kumafuna khama ndi nzeru, monga momwe anaonera Ángel, mbale wa ku Alcoy (Alicante). Iye anali atangotsiriza kumene kufikira nyumba zina m’mudzi wa Masías pamene anamva kulira kwa tambala. Anaganiza kuti, “Ngati pali tambala, payenera kukhala nyumba chapafupi​—nyumba imene sitinaione.” Atafunafuna, Ángel anapeza kanjira kamene kanamtsogolera cha kumtunda mphepete mwa phiri nikamfikitsa panyumba yokhala payokha kuseri kwake.

Pamalo pamenepa panali kukhala José ndi Dolores, mbale ndi mlongo wake azaka zoposa 60. Iwo anamvetsera mwatcheru ndipo mwamsanga anavomereza phunziro la Baibulo. Komabe, kunali kovuta kuphunzira ndi anthu odzichepetsa ameneŵa, popeza kuti sanali okhoza kuŵerenga kapena kulemba, ndipo chilichonse chinafunikira kumasuliridwa kuchotsa m’Chispanish kuika m’chinenero cha ku Valencia, chinenero chokha chimene anamva. Ndiponso, iwo anayang’anizana ndi chitsutso chachikulu chochokera kwa anansi awo. Mosasamala kanthu za zopinga zimenezi, onse aŵiri José ndi Dolores anapita patsogolo m’chowonadi, ngakhale kuti kupezeka pamisonkhano kunafuna kuyenda ulendo wautali m’mapiri. Potsirizira pake, iwo anayenerera ubatizo, ndipo onse aŵiriwo akupitirizabe kutumikira Yehova mokhulupirika.

Rosendo ndi Luci, otchulidwa poyambawo, akukumbukira mmene munthu wopuwala m’nyumba yokhala payokha pafupi ndi Moaña, kumpoto chakumadzulo kwa Spain, analandilira chowonadi. Dzina lake linali María. Pamene analankhula ndi Mboni kwa nthaŵi yoyamba, sanali wokhoza kuŵerenga kapena kulemba ndipo anali chigonere pakama kwa zaka zambiri chifukwa cha kudwala poliyo pamene anali mwana. Nyumba yake inali pafupifupi makilomita aŵiri kuchokera pamsewu wapafupi. Komabe, iye anali wofunitsitsa kuphunzira Baibulo, ndipo kutsimikiza mtima kwake kutumikira Yehova kunaonekera posapita nthaŵi. María anaphunzira kuŵerenga ndi kulemba ndipo anayamba kupezeka pamisonkhano, chifukwa cha zoyesayesa za mpingo wodziperekawo. Abale ankamunyamula pamtunda wa mamita mazana aŵiri kuchokera panyumba pake mpaka pamene msewu uli wosalala ndiyeno kumuloŵetsa m’galimoto mosamala kwambiri. Mosasamala kanthu za chitsutso cha poyamba cha banja lake, iye anapita patsogolo mpaka paubatizo. Chifukwa cha chidaliro chimene anachipeza m’kupita kwake patsogolo kwauzimu, tsopano waphunzira kuyendetsa galimoto lapadera lolinganizidwira iye ndipo anamaliza maphunziro akusukulu oyambirira. “Kukhala wokhoza kuthandiza anthu onga María kumapangitsa kudzimana kulikonse kukhala koyenerera,” akufotokoza motero Rosendo.

Oŵerenga Baibulo Akuvomereza Mosavuta

M’ma 1970, Baibulo linakhala lopezeka kwa anthu onse mu Spain kwanthaŵi yoyamba. Anthu a ku Spain ambiri anagula makope awo, ndipo ena anayamba kuŵerengera Malemba. Pilar, wa ku Medina del Campo (Valladolid), anali atayamba kale kuŵerenga Baibulo pamene Mboni za Yehova zinafika kwa nthaŵi yoyamba m’tauni yakwawo mu 1973. Pokhala Mkatolika, anali kuwopa kulandira mabuku kwa Mboni, koma anafuna kwambiri kumvetsetsa Baibulo. M’kupita kwa nthaŵi, anavomera kukhala ndi makambitsirano a mlungu ndi mlungu oyankha mafunso ake a Baibulo.

Pogwiritsira ntchito bwino mabuku ofalitsidwa ndi Watch Tower Society, mlongo yemwe ndimpainiya amene anafikira Pilar anakhoza kuyankha mafunso ake ambiri. Atasangalatsidwa ndi zimene anali kuphunzira, Pilar anavomera pambuyo pa milungu ingapo kuphunzira Baibulo mwakugwiritsira ntchito buku la Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya. Asanamalize phunziro lake la buku la Coonadi, iye anali atamaliza kuŵerenga Baibulo lonse ndipo anali wokhutiritsidwa kuti anali atapeza chowonadi. Anakhala Mboni yoyamba mu Medina del Campo, kumene tsopano kuli Nyumba Yaufumu yabwino kwambiri ndi mpingo wa ofalitsa 63.

Mboni za ku Spain zikupezabe anthu “ozindikira kusoŵa kwawo kwauzimu” ndi amene amaŵerenga Baibulo nthaŵi zonse kuyesayesa kumvetsetsa chifuniro cha Mulungu. (Mateyu 5:3, NW) Pepi, amene kale anali Mkatolika yemwe panthaŵi ina anali mphunzitsi wa katekizimu wa dera la Zumaia (kumpoto kwa Spain), anali kulalikira m’mudzi wapafupi pamene anakumana ndi wansembe woyang’anira deralo.

Wansembeyo anamuuza kuti: “Pepi, ukungotaya nthaŵi yako. M’mudzi uno wa Itziar, muli anthu aŵiri okha​—okwatirana​—amene amakonda zinthu zauzimu. Ena onse amangopita kutchalitchi monga chizoloŵezi chabe.”

Pepi anayankha kuti: “Chabwino, ngati muli anthu aŵiri okha okonda zinthu zauzimu, amenewo adzakhala Mboni za Yehova.”

Pepi anapitiriza ndi ntchito yake yolalikira kunyumba ndi nyumba limodzi ndi Mboni zina kufikira atamaliza mudzi wonsewo. Ndipo zowonadi, abalewo anapeza m’nyumba yapayokha okwatirana aja amene wansembeyo anawatchula. Iwo anali kuŵerenga Baibulo koma sanalimvetsetse. Anavomereza mofunitsitsa phunziro la Baibulo, anapita patsogolo mofulumira, ndipo anabatizidwa mu April 1991.

Anthu ena owona mtima aphunzira chowonadi mwa kungoŵerenga paokha mabuku ozikidwa pa Baibulo ofalitsidwa ndi Watch Tower Society. Mwachitsanzo, Mboni za ku Almadén (Ciudad Real) zinali kulalikira m’tauni yaing’ono ya Ciruelas (Badajoz) pamene zinapeza mkazi amene anamvetsera mosamalitsa uthenga wawo. Poona chikondwerero chake choonekeracho, iwo anapereka kwa iye mwaŵi wa phunziro la Baibulo la panyumba. Komabe, iye anakana akumanena kuti analipo mwamuna wina wokalamba amene anali kuphunzira naye Baibulo. Anthu angapo m’deralo ananenanso zofananazo. Atachita chidwi kwambiri, abalewo anafunsafunsa za mwamuna wokalambayo. Iwo anauzidwa kumene anali kukhala ndipo anakamchezera.

Zinawadabwitsa kupeza kuti mu Madrid mwamuna ameneyu, wotchedwa Felipe, anali ndi buku la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. Ataliŵerenga lonselo, iye anaona kuti linali thayo lake kulalikira mbiri yabwino kwa anansi ake. Chifukwa chake, iye anali kugwiritsira ntchito bukulo kuwapatsa maphunziro a Baibulo. Abalewo anapanga makonzedwe a kuphunzira naye. Mkazi amene anaphunzira naye Baibulo nayenso anavomereza phunziro. Ngakhale kuti ali ndi zaka 80 ndi wodwaladwala, Felipe akupita patsogolo bwino lomwe m’chowonadi.

Kulaka Kulingaliridwa Molakwa

Magawo akumidzi amapereka mavuto apadera. Miyambo yachipembedzo ndi kukhulupirira malaulo kaŵirikaŵiri nzozama m’madera oterowo, ndipo anthu ambiri okhala m’madera akumidzi ali ndi chikayikiro chachikulu ponena za “chipembedzo chatsopano.” Anthu akumidzi ena amada nkhaŵa kwambiri ponena za zimene anansi awo ndi achibale adzalingalira ngati iwo asintha chipembedzo chawo. Koma mphamvu ya Mawu a Mulungu ikhoza kulaka mavuto oterowo ndi kusintha moyo wa munthu. Zimenezo ndizo zinachitika m’mudzi wa asodzi wa Cangas de Morrazo kumadzulo chakumpoto kwa Spain.

Roberto, nzika ya mudzi umenewu, anakagwira ntchito ya m’madzi pausinkhu wa zaka 14 chifukwa chakuti analakalaka kudzikhalira yekha. Moyo wake monga mmalinyero wamalonda unamloŵetsa m’gulu la amalinyero ena achichepere amene anali kuledzera kwambiri ndi kugwiritsira ntchito anamgoneka kupeŵa kusukidwa kwa maola ambiri kunyanjako. Posapita nthaŵi, Roberto nayenso anakhala wakumwa kwambiri ndi womwerekera ndi anamgoneka.

M’kupita kwanthaŵi, Roberto anabwerera kwawo koma anali wosakhoza ndi wosafunitsitsa kuleka zizoloŵezi zake zoipazo. Kuti apeze ndalama zogulira anamgoneka, anakhala mbala ndipo anaikidwa m’ndende kasanu ndi kamodzi panthaŵi zosiyanasiyana. Pamene anali ndi zaka 18, anamwa msanganizo wa vinyo ndi mankhwala opha ululu amene anatsala pang’ono kumupha. Madokotala ndiwo anapulumutsa moyo wake, koma anapuwala mikono yake ndi miyendo. Anatuluka m’chipatala ali wopuwala mikono ndi miyendo. Ngakhale kubindikiritsidwa pampando wamagudumu sikunamchititse kuthetsa chizoloŵezi chake cha kugwiritsira ntchito anamgoneka. Iye anagwiritsidwa mwala ndi chipembedzo, ndipo anamgoneka anaonekera kukhala njira yokha yochititsira moyo wake kukhala watanthauzo​—mpaka zaka zitatu pambuyo pake pamene anafikiridwa ndi Mboni za Yehova.

Kuphunzira ponena za kukwaniritsidwa kwa maulosi a Baibulo kunathandiza Roberto kulaka zikayikiro zake. Kulandiridwa kwake kwachikondi ku Nyumba Yaufumu kunamkhutiritsa maganizo kuti chipembedzo chowona chimalemeretsa miyoyo ya anthu. M’miyezi isanu ndi inayi, Roberto anagonjetsa kumwerekera kwake ndi anamgoneka ndipo anabatizidwa. Mosasamala kanthu za kupunduka kwake kwakukuluko, iye wakhala akutumikira monga mpainiya kwa zaka zisanu ndi zitatu. Wakhalanso mkulu mumpingo kwa zaka ziŵiri zapitazo. Francisco, mmodzi wa mabwenzi ake akale, anachita chidwi kwambiri ndi masinthidwe a moyo wa Roberto kotero kuti nayenso anakhala Mboni ndipo tsopano ndimtumiki wotumikira. Kusintha kwakukuluko kwa munthu ameneyu amene analingaliridwa kukhala womwerekera wosachiritsika kunathandiza anthu m’malowo kumvetsetsa bwinopo mtundu wa ntchito yathu. Mkazi wina anabweretsadi mwana wake wamwamuna womwerekera ndi anamgoneka ku Nyumba Yaufumu kuti mwina Mboni zingamchiritse.

Kufunafuna Chowonadi m’Baibulo

Kwakukulukulu, anthu akumidzi amakhala ndi chiyamikiro chachikulu cha chowonadi kotero kuti kaŵirikaŵiri amachititsa manyazi anzeru adziko. (1 Akorinto 1:26, 27) Adelina, mkazi wamanyazi wa usinkhu wapakati, ali mmodzi wa anthu oyamikira ameneŵa. Iye anali kuona mwamphamvu kwambiri chikhulupiriro chake Chachikatolika. M’maŵa uliwonse mosalephera anali kugwada ndi kupemphera, akumabwerezabwereza pemphero la Atate Wathu ndi la Atamandike Mariya. Iye anali kulunjikitsa mapemphero ake kwa “woyera mtima” wina tsiku lililonse la mlungu​—kungotsimikizira kuti ena a mapemphero ake akuyankhidwa.

Pamene Adelina anayamba kuphunzira Baibulo, anatembenuzira changu chake cha kupembedza ku chikhulupiriro chake chopezedwa chatsopano. Ngakhale manyazi ake sanamletse, ngakhale kuti nthaŵi yoyamba pamene iye ndi mwamuna wake anapita ku Nyumba Yaufumu, zinawatengera mphindi khumi kuti alimbike mtima ndi kuloŵa. Komabe, pamene anali mkati, iye anamvetsera mosamalitsa. Panthaŵi ina, anaphunzira ponena za Ulamuliro wa Zaka Chikwi wa Kristu. Nkhaniyi inamchititsa chidwi, ndipo atabwerera kunyumba, anafuna kuŵerenga zowonjezereka ponena za nkhaniyo m’Baibulo lake. Koma iye kapena mwamuna wake sanadziŵe pamene akapeza nkhaniyo, ngakhale kuti analingalira kuti inali itatchulidwa penapake m’buku la Chivumbulutso. Motero Adelina anayamba kuŵerenga Chivumbulutso usikuwo ndipo anapitirizabe kuŵerenga kufikira anafika pa chaputala 20 m’maola a m’maŵa.

Panthaŵi ina, Adelina anaphunzira kuti kunali koyenera kwa mwamuna kuimira mkazi wake m’pemphero. Ngakhale kuti mwamuna wake anali wofunitsitsa kupemphera, sanadziŵe chonena m’pemphero. Usiku womwewo, Adelina anaganiza za kufunafuna malangizo m’Baibulo. Pa 2 koloko m’maŵa, anadzutsa mwamuna wake kuti amuuze kuti anapeza pa Mateyu chaputala 6, pamene pamafokotoza nkhani ya pemphero mwatsatanetsatane. Ataŵerenga malangizo a Yesu, mwamuna wakeyo potsirizira pake anapereka pemphero la onse aŵiri. Tsopano onse aŵiri Adelina ndi mwamuna wake ali Mboni za Yehova.

Kututa Kwabwino

Pambuyo pazaka pafupifupi 25 za kuchitira umboni kumidzi kwa atumiki achangu a Yehova, mbali iliyonse ya Spain yamva mbiri yabwino. Monga momwe zinaliri mu Asia Minor m’zaka za zana loyamba, ‘mawu a Ambuye akubukitsidwa m’dziko lonse.’ (Machitidwe 13:49) Chotsatirapo, zikwi za anthu akumidzi alabadira.

Mu Spain ndi kwina kulikonse, kulalikira bwino lomwe m’madera akumidzi kumafuna kuleza mtima ndi kudzimana. Koma popeza kuti chifuniro cha Mulungu nchakuti ‘anthu onse apulumuke,’ Mboni za Yehova zili zokondwa kufunafuna anthu oyamikira. (1 Timoteo 2:4) Ndipo monga momwe zokumana nazo zapitazo zasonyezera, Yehova wadalitsa kwambiri zoyesayesa za kulalikira kumudzi ndi mudzi mu Spain.

[Mawu a M’munsi]

a Josephus anaŵerengera kuti panali “mizinda ndi midzi” yokwanira 204 m’Galileya, ndipo anatcha chigawocho kukhala cha “midzi yochuluka kwambiri.”

[Mapu patsamba 23]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

FRANCE

PORTUGAL

SPAIN

BALEARIC ISLANDS

CANARY ISLANDS

[Mawu a Chithunzi patsamba 24]

Vilac, Lérida

[Mawu a Chithunzi patsamba 24]

Puebla de Sanabria, Zamora

[Mawu a Chithunzi patsamba 25]

Casarabonela, Málaga

[Mawu a Chithunzi patsamba 25]

Sinués, Huesca

[Mawu a Chithunzi patsamba 26]

Lekeitio, Vizcaya

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena