Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 9/15 tsamba 24-28
  • Kulalikira ndi Chipiriro m’Dziko la Madzi Oundana ndi la Moto

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulalikira ndi Chipiriro m’Dziko la Madzi Oundana ndi la Moto
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Mbiri Yabwino Ifika ku Iceland
  • Antchito ya Kututa Owonjezereka
  • Kuzungulira Mkati mwa Likulu
  • Kumalire a Kummaŵa
  • Tipita ndi Msewu wa Kumpoto
  • Ziyembekezo Zabwino za Chiwonjezeko
Nsanja ya Olonda—1993
w93 9/15 tsamba 24-28

Kulalikira ndi Chipiriro m’Dziko la Madzi Oundana ndi la Moto

DZIKO la Iceland lili m’nyanja ya North Atlantic chapakati pa North America ndi Ulaya. Ngakhale kuti lili kumunsi kwa malo ozizira a Arctic Circle, mphepo yake siyozizira kwambiri monga momwe mungaganizire, chifukwa cha kufunda kwa madzi ochokera ku Gulf of Mexico. Iceland watchedwa dziko la madzi oundana ndi la moto chifukwa chakuti lili ndi mulu waukulu koposa wa madzi oundana mu Ulaya ndipo alinso amodzi a malo a dziko kumene mapiri amoto amaphulika kwambiri. Otchuka kwambiri ndiwo akasupe ake ambiri otulutsa madzi otentha ndi malo otulutsa mpweya wotentha ndi wa sulufure.

Anthu okwanira 260,000 a pa chilumba chimenechi chachiŵiri muukulu wake mu Ulaya yense ali mbadwa za a Viking, amene anadzakhala m’malo ameneŵa zoposa zaka 1,100 zapitazo. Chinenero cha Icelandic kwenikweni chimafanana ndi cha Old Norse, chinenero cha ku Scandinavia cha m’nyengo ya a Viking. Icho chakhalabe chosasintha chifukwa chakuti nzika za Iceland zinali kukonda kuŵerenga ndakatulo zakale, zimene zinalembedwa makamaka m’zaka za zana la 13.

Pofika m’zaka za zana la 16, Baibulo linayamba kutembenuzidwa m’chinenero cha Icelandic. “Chipangano Chatsopano” chinaonekera mu 1540 ndipo Baibulo lathunthu mu 1584. Oposa pa 90 peresenti ya anthuwo amaloŵa chipembedzo cha Boma cha Evangelical Lutheran Church. Ngakhale kuti Baibulo limapezeka pafupifupi m’nyumba iliyonse, oŵerengeka okha ndiwo amakhulupirira kuti lili Mawu a Mulungu. Anthu ambiri a ku Iceland ali ndi malingaliro osiyanasiyana ponena za chipembedzo, unyinji wa iwo ngamalingaliro odzigangira.

Mbiri Yabwino Ifika ku Iceland

Nzika za ku Iceland zimene zinayamba kumva mbiri yabwino ya Ufumu panthaŵiyo zinali kukhala m’Canada. Mmodzi wa iwo anali Georg Fjölnir Lindal. Makolo ake anachokera ku Iceland, ndipo iye anali kulankhula chi Icelandic. Mwamsanga atapatulira moyo wake kwa Yehova Mulungu, anakhala mlaliki wanthaŵi yonse wa mbiri yabwino. Mu 1929, pamene anali ndi zaka 40, anapereka mbiri yabwino kwa anthu a m’dziko la madzi oundana ndi la motolo.

Inali ntchito yaikulu chotani nanga kwa munthu mmodzi! Iceland ali ndi makilomita pafupifupi 320 kuchokera kumpoto kufika kummwera ndi makilomita pafupifupi 500 kuchokera kummaŵa kufika kumadzulo. Malire ake a m’gombe, kuphatikizapo madoko ndi matsiriro, ali ndi utali wa makilomita pafupifupi 6,400. Panthaŵi imeneyo, kunalibe misewu yeniyeni ndiponso kunalibe magalimoto kapena zoyendera zilizonse zamakono. Komabe, Mbale Lindal anafola chilumba chonsecho m’zaka khumi zokha ndipo anagaŵira zikwi za mabuku. Iye anayenda m’mphepete mwa nyanja ndi bwato, ndipo pochezera mafamu a kumtunda, anagwiritsira ntchito akavalo aŵiri, mmodzi wokwerapo iye ndi winayo wonyamulira mabuku ake ndi katundu.

Kwa pafupifupi zaka 18, Mbale Lindal anali Mboni yokha mu Iceland yense. Ngakhale kuti iye anagwira ntchito zolimba, sipanakhale munthu aliyense amene anaima kumbali ya Ufumu mkati mwa nthaŵiyo. Kukhala yekha kwa nthaŵi yaitali ndi kosungulumwitsa kunatha pa March 25, 1947, pamene omaliza maphunziro a Sukulu ya Baibulo ya Gileadi ya Watchtower oyamba anafika. Mungayerekezere chisangalalo chake pamene potsirizira pake Yehova anayankha mapemphero ake opempha antchito ya kututa owonjezereka. (Mateyu 9:37, 38) Mbale Lindal anapitiriza utumiki wake mu Iceland kufikira pamene anabwerera ku Canada mu 1953.

Antchito ya Kututa Owonjezereka

Amishonale amene anabwera mu 1947 anali abale aŵiri a ku Denmark. Amishonale owonjezereka anafika pambuyo pa zaka ziŵiri. Pamene anapitiriza ntchito yolalikira pamodzi ndi mabwenzi oŵerengeka amene anasamukira ku Iceland, zofalitsidwa zikwizikwi zinagaŵiridwa. Anthu ambiri a ku Iceland amakonda kuŵerenga kwambiri, koma siambiri amene analabadira mbiri yabwino. Pambuyo pa zaka 27 za kuoka ndi kuthirira, abale oleza mtimawo anayamba kuona zipatso za ntchito yawo. Mu 1956 atsopano asanu ndi aŵiri anaima kumbali ya Ufumu napatulira miyoyo yawo kwa Yehova.

Mkati mwa zaka khumi zapitazo, chiŵerengero cha ofalitsa Ufumu chaŵirikiza kuposa kaŵiri. Tsopano, pali mipingo isanu ndi iŵiri ndi gulu lakutali limodzi, kupanga chiwonkhetso cha olengeza mbiri yabwino okwanira 280. Tiyeni titenge ulendo wozungulira pachilumbacho ndi kuchezera mipingo imeneyi.

Kuzungulira Mkati mwa Likulu

Abale ndi alongo amene anapirira kwa zaka zonsezi adalitsidwa kwambiri. Tsopano pali mipingo iŵiri yopita patsogolo mu Reykjavík, likulu lake. Iwo amasonkhana m’Nyumba Yaufumu yokongola yokhala pa ofesi yanthambi, imene inapatuliridwa mu 1975.

Friðrik ndi Ada anali pakati pa asanu ndi aŵiri amene anabatizidwa kalero mu 1956. “Ndikukumbukira kuti tinali kusonkhana m’chipinda chaching’ono chapamwamba m’nyumba yokhalamo amishonale,” akutero Friðrik. “Munali malo okwanira mipando 12, koma nthaŵi zina, pamene kunafika anthu ochulukirapo, tinatsegula khomo loloŵera ku chipinda china chaching’ono. Nzosiyana chotani nanga lerolino pamene mipingo iŵiri imadzaza Nyumba Yaufumu!”

Friðrik ndiye anali kuyang’anira Dipatimenti ya Utumiki wa Chakudya pamene anakhala ndi misonkhano yaikulu yoyamba. “Ntchito yambiri ndinachita ndekha, ndipo panthaŵi imodzimodziyo, sikunali kwachilendo kwa ine kukhala ndi mbali zitatu kapena zinayi paprogramu tsiku lililonse. Pogwira ntchito m’kitchini, ndinali kuvala apuloni. Nthaŵi yokakamba nkhani ikakwana, ndinali kuvala jekete ndi kuthamangira m’holo. Kaŵirikaŵiri abale anali kundikumbutsa kuvula apuloni. Tsopano timakhala ndi anthu 400 kufika 500 ofika pamisonkhano yaikulu, kuphatikizapo akulu abwino amene amakhala ndi phande m’programu. Pamakhalanso ambiri odzipereka kuntchito yodzifunira m’Dipatimenti ya Utumiki wa Chakudya.”

Mpingo wapafupi kwambiri ndi Reykjavík ndiwo Keflavík, wokhala pamtunda wa makilomita pafupifupi 50 kumadzulo. Tili paulendo wa galimoto tikudzera m’malo a matope ouma ochokera m’phiri lamoto limene linaphulika. Chigawo cha dziko la Iceland chokwanira maperesenti khumi nchokutidwa ndi matope ouma ochokera m’phiri lamoto lophulika. Zomera zoyamba kuonekera m’malo ameneŵa zimakhala za mitundu ya ndere, koma m’minda yakale ya matope ouma ochokera m’phiri lamoto lophulika, mukhoza kupeza mtundu wa nkandankhuku ndi zitsamba zazifupi.

Mpingo wa Keflavík uli ndi ofalitsa 19 ndipo unapangidwa mu 1965. Chapafupipo pali bwalo lalikulu la ndege, ndipo msasa wa asilikali a ku United States ulinso kunoko. Ngakhale kuti Mboni sizinachitepo ntchito ya kunyumba ndi nyumba pamsasa umenewu, maphunziro a Baibulo ambiri akhala akuchititsidwa kumeneko, ndipo anthu angapo aphunzira chowonadi.

Mpingo wina uli mu Selfoss, pamtunda wa makilomita 55 kummaŵa kwa Reykjavík. Kunoko tikuona dziko lobiriŵira ndi mafamu okhala ndi ng’ombe ndi nkhosa, kuphatikizapo famu ya mkaka yaikulu koposa mu Iceland. Panjira, tikudutsa Hveragerði, tauni yaing’ono yokhala m’chigwa chamaonekedwe okongola. Chapatalipo, tikuona mitambo ya nthunzi yotuluka mu akasupe amadzi otentha m’chigwa chonsecho. Awa ndiwo amodzi amalo achitungu kwambiri m’dzikoli, ndipo nyumba zachitungu zambiri zamangidwa kugwiritsira ntchito zinthu zachilengedwe zimenezi ndi kutulutsa matimati olimidwa m’nyumba zachitungu, minkhaka, ndi maluŵa a mitundumitundu.

M’malo ameneŵa muli mpingo waung’ono koma wokangalika wa ofalitsa Ufumu okwanira 19. Sigurður ndi Guðrún Svava anasamuka kuchokera ku Reykjavík kudzachilikiza mpingo waung’ono umenewu pafupifupi nthaŵi imene mpingowo unapangidwa mu 1988. Sigurður ndiye mkulu yekha kunoko. Asanakhale mmodzi wa Mboni za Yehova pafupifupi zaka khumi zapitazo, anali woimba nyimbo wotchuka kwambiri, akumaimba ng’oma m’magulu oimba osiyanasiyana. Lerolino, iye akudzichilikiza mwa ntchito ya kuyeretsa mazenera, ndipo amaphunzitsanso nyimbo. Njira yake ya moyo monga wosangalatsa anthu inamgwetsera m’mavuto ambiri, monga ngati kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala oledzeretsa, uchidakwa, kusweka kwa ukwati. Ali wokhutiritsidwa chotani nanga tsopano, pokhala ndi chifuno cha moyo ndi kutumikira Yehova!

Kumalire a Kummaŵa

Titachoka mu Selfoss, tikutenga ulendo wa pa galimoto wa makilomita 680, tikuyenda mtunda wautali pamisewu yaing’ono yafumbi ndi yamajidumajidu. Tikupita ku mpingo wotsatira, m’tauni ya Reyðarfjörður, kugombe la kummaŵa. Pambuyo pa theka la ola chabe, tikuona Hekla, phiri lamoto lophulika lotchuka kwambiri la Iceland. Ilo laphulika kanayi konse m’zaka za zana lino.

Mu 1973 phiri lamoto linaphulika mwadzidzidzi ku Vestmannaeyjar (Westmann Islands). Anthu onse okwanira pafupifupi 5,300 anasamutsidwira kumtunda motetezereka m’maola oŵerengeka chabe. Atakonzanso tauniyo, nzika zake zambiri zinabwerera m’kupita kwa nthaŵi. Mboni ziŵiri tsopano zikukhala kumeneko ndipo zikulalikira mbiri yabwino kwa anthu a chitaganya chaching’ono chimenechi. Titayenda ndi galimoto kwa maola ena aŵiri, tikuonanso maonekedwe okongola a Vatnajökull, mulu waukulu koposa wa madzi oundana wa Iceland, wokhala ndi ukulu wa makilomita 8,300 mbali zonse zinayi. Tili m’njira, tikuonanso mathithi ambiri okongola ndi mitsinje.

Titathera pafupifupi maola khumi paulendo, tikufika kumene tikupitako. Mu Reyðarfjörður tikuonana ndi ofalitsa 12 a mpingo watsopano kwambiri m’Iceland. Palibe Mboni iliyonse imene inakhala m’maloŵa kufikira pamene nyumba ya amishonale inakhazikitsidwa cha kumapeto kwa 1988. Kjell ndi Iiris, amishonale okwatirana a ku Sweden amene atumikira mu Iceland chiyambire 1963, anagaŵiridwa kugwira ntchito pakati pa anthu 15,000 m’malo akumidzi ameneŵa. Ambiri amakhala m’midzi yaing’ono ya asodzi pagombe lalitali la makilomita pafupifupi 500.

Kjell akusimba kuti: “Sikokayikiritsa kuti Yehova wadalitsa kwambiri ntchito ya Ufumu m’mbali ino ya Iceland. Pa January 1, 1993, mpingo unapangidwa, ndipo tikuchititsa maphunziro a Baibulo ambiri abwino kwa anthu amene akupita patsogolo. Ngakhale kuti zoyendera zasintha chiyambire pamene Mbale Lindal anayendera pa kavalo, kuli kovutabe kuyendetsa galimoto m’njira zokhala ndi madzi oundana zodzera m’mapiri m’miyezi ya mdima ya m’chisanu, ngakhale ndi galimoto lamphamvu la jipi. Tsiku lina, linaterereka pamsewu wa madzi oundana ndi kugubuduka kaŵiri kapena katatu kumaterezi. Tinali achimwemwe chotani nanga pamene tinapulumuka osavulala!”

Atakhala zaka 30 mu Iceland, Iiris akunena kuti: “Mkati mwa zaka zambiri anthu ambiri abwera kuchokera kumaiko ena kudzathandiza. Ngakhale kuti ochuluka anafunikira kupita kaamba ka zifukwa zosiyanasiyana, iwo analidi ndi phande lalikulu m’ntchito ya kuoka ndi kuthirira. Tili okondwa kuti tili okhoza kukhalabe, popeza kuti tsopano tili ndi mwaŵi wakuona zotuta zikubwera. Yehova akufulumizitsa ntchito yake kunonso.”

Pakhala kuwonjezereka kwakukulu chifukwa chakuti atsopano nawonso amalalikira kwa antchito anzawo. Atli anaphunzira chowonadi kwa amishonale ndipo anayamba kulankhula kwa ena apakampani yomanga nyumba imene anagwirapo ntchito. Antchito anzake aŵiri tsopano akukhala ndi phande m’ntchito yolalikira, mmodzi wa iwo anabatizidwa pamodzi ndi mkazi wake mu November 1992. Wantchito mnzake wachitatu wakhala akuphunzira Baibulo ndi Mboni.

Tipita ndi Msewu wa Kumpoto

Titachoka mu Reyðarfjörður, tikumka kumadzulo. Mpingo wotsatira uli pamtunda wa makilomita 300, m’tauni ya Akureyri. Alaliki apadera anthaŵi yonse anagaŵiridwa kugwira ntchito kunoko kuchiyambi cha ma 1950. Kuyambira pachiyambi penipeni, ntchitoyo inayang’anizana ndi chitsutso champhamvu cha atsogoleri achipembedzo. Nkhani zinafalitsidwa m’manyuzipepala zochenjeza anthu ponena za Mboni za Yehova. Anthu ambiri a m’tauni analinso okhulupirira kwambiri mizimu. Koma chifukwa cha chipiriro ndi kuleza mtima kwa apainiya ndi amishonale osiyanasiyana, lerolino muli mpingo wokangalika ndi wachikondi wa ofalitsa Ufumu okwanira 35.

Friðrik, mmodzi wa akulu kunoko, anali msodzi. Atapezeka pamsonkhano wachigawo mu 1982, anakhutiritsidwa kuti zimene anali kuphunzira zinali chowonadi. Anabwerera ku Akureyri ali wotsimikiza mtima kukalalikira kwa banja lake, mabwenzi, ndi anzake akuntchito. Friðrik anapanga makonzedwe akuleka ntchito yake yausodzi kotero kuti akhale ndi nthaŵi yowonjezereka ndi mpingo. Anauza tsamwali wake wamkazi, Helga, kuti sangakhalenso pamodzi kufikira atakwatirana, chifukwa chakuti anafuna kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova. Friðrik anafunanso kuti mkaziyo aphunzire Baibulo chifukwa sanafune kukwatira ‘wosakhulupirira.’ (1 Akorinto 7:39) Iye anadabwa kuona kuti Helga anayamba kuphunzira. Iwo anakwatirana m’February 1983 ndipo anabatizidwa posapita nthaŵi. M’kupita kwa nthaŵi amayi ake a Friðrik ndi mchemwali wake nawonso analandira chowonadi.

Ulendo wathu womalizira ndi wa ku Akranes, makilomita 350 kuchokera ku Akureyri, pamwamba pa mitandadza itatu ya mapiri ndi kudzera m’zigwa zokongola zambiri. Kunoko msewu ngwokonzedwa bwino, kuchititsa ulendo wa pa galimotowu kukhala wosangalatsa kusiyana ndi misewu ija ya fumbi ndi majidumajidu imene tayendamo kwa mtunda wautali. Mu Akranes tikupeza mpingo waung’ono koposa mu Iceland​—wokhala ndi ofalitsa asanu, aŵiri a iwo otumikira monga akulu. Uwo ngwa mabanja aŵiri amene anavomereza chiitano cha ku Makedoniya, anachoka ku umodzi wa mipingo yaikulu mu Reykjavík, ndi kudzakhazikika m’tauni yaing’ono ino kudzatumikira kumene kusoŵa kunali kokulirapo. (Machitidwe 16:9, 10) Kwa zaka zoposa ziŵiri tsopano, iwo alalikira moleza mtima mbiri yabwino m’gawoli, ali ndi chidaliro chakuti Yehova adzakulitsa zinthu.​—1 Akorinto 3:6.

Ziyembekezo Zabwino za Chiwonjezeko

Pokhala ndi nyumba zachitungu zotenthetsedwa ndi chitungu chochokera m’nthaka ndi kuunikiridwa ndi magetsi, alimi a m’Iceland akhala okhoza kulima mitundu yosiyanasiyana ya zipatso, ndiwo zamasamba, ndi zinthu zina. Mofananamo, Mboni nazonso, pokhala zokonzekeretsedwa ndi chowonadi chauzimu, kufunda kwa mawu awo olimbikitsa, ndi dalitso la mzimu woyera wa Yehova, zakhala ndi zotulukapo zabwino koposa m’munda wa Iceland.

Chaka chino anthu 542 anafika pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu, ndipo maphunziro a Baibulo apanyumba pafupifupi 200 akuchititsidwa tsopano. Kuwonjezerapo, kuchitapo kanthu kwabwino pa chilimbikitso cha kukatumikira kumagawo osagaŵiridwa kukutipatsa chidaliro chakuti anthu onse onga nkhosa m’chilumba chachikulu chino adzamva liwu la Mbusa Wabwino, Yesu Kristu. (Yohane 10:14-16) Nchotulukapo chosangalatsa chotani nanga kwa olengeza Ufumu okhulupirika amenewo amene asonyeza kuleza mtima kwakukulu ndi chipiriro m’kulalikira mbiri yabwino m’dziko la madzi oundana ndi la moto m’zaka 64 zapitazo!

[Mapu patsamba 24]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Akureyri

Akranes

Keflavík

Selfoss

Vestmannaeyjar

Reyðarfjörður

Hekla

Geysir

VATNAJÖKULL

REYKJAVÍK

[Mawu a Chithunzi]

Chozikidwa pa mapu a Jean-Pierre Biard

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena