“Olengeza Ufumu” amaloŵa pamadzi a Guyana
GUYANA.a Liwu la chi Amerindian limeneli limatanthauza “dziko la madzi.” Dzinali limafotokoza moyenerera chotani nanga mawonekedwe a dziko lokha lolankhula Chingelezi limeneli mu South America. Dzikolo lili ndi mitsinje yambiri yoloŵanaloŵana imene ili ndi mitsinje ina imene imatsira mwa iyo, imene imayenda mokhotakhota kuchokera ku Guiana Highlands kudutsa nkhalango ya malo otentha mpaka ku Atlantic Ocean. Mitsinje imeneyi njofunika kwambiri pakuchirikiza midzi ndi mafamu a m’mphepete mwake.
Mboni za Yehova mu Guyana zimazindikira kuti pamene Yesu ananeneratu kuti “mbiri yabwino imeneyi yaufumu [ika]lalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni ku mitundu yonse,” zimenezo zikaphatikizapo kulalikira mbiri yabwino kwa anthu okhala m’magawo amphepete mwa mitsinje ameneŵa. (Mateyu 24:14, NW) Chotero, kwa zaka zambiri, magulu a Mboni, ambiri a iwo apainiya, agwiritsira ntchito mabwato, aakulu ndi aang’ono, kuloŵa pamadzi a Guyana kupereka mbiri yabwino kwa anthu.
Kuti ithandizire ntchitoyi, Watch Tower Society mu Guyana yagwiritsira ntchito, kufikira leroli, mabwato amatabwa asanu otchedwa Kingdom Proclaimer I (Wolengeza Ufumu) mpaka Kingdom Proclaimer V. Iwo ndimabwato amatabwa otchedwa balahoo, otalika mamita 7, otseguka pamwamba, ampangidwe wa V pansi pake, opangidwa ndi banja la Mboni limenenso limawasamalira. Ngakhale kuti Mboni zakumaloko mwachikondi zinawatcha onse kuti Proclaimers, mabwato aŵiri oyambirira anachotsedwa pantchito pambuyo pakutumikira kwa zaka makumi ambiri. Komabe, nambala III, IV, ndi V, akugwirabe ntchito zolimba m’mitsinje ya Pomeroon, Mahaica ndi Demerara.
Ku Demerara
Ku Briteni ndi mbali zina za Ulaya, liwu lakuti “demerara” lingakumbutse suga wamawonekedwe a golidi wodera, mwachiwonekere wotengedwa ku nzimbe wa ku minda ya m’mphepete mwa mtsinje wamatope ndi nsenga. Kugombe lakumadzulo, msewu wochokera kudoko umathera pamapeto a minda ya nzimbe. Kupitirira pamenepo, Mboni zimadalira mabwato a Kingdom Proclaimer kuti zipereke uthenga wotsekemera wa Ufumu wa Yehova kwa nzika za m’mphepete mwa mtsinje—Ahindu, Asilamu, ndi Akristu mwa dzina lokha.
Mikupiti yakulalikira mu Demerara ingakhale maulendo a tsiku limodzi kapena ingathe milungu ingapo, kumka ku doko ndi doko, kuyambira mbanda kucha mpaka kuloŵa kwa dzuŵa. Pamaulendo a usiku onse, apainiya samangophika ndi kudyera m’bwato komanso amagona m’menemo. Kutada, Proclaimer amamangiriridwa kumtengo wa mangrove kapena kukochezedwa padoko ngati liripo. Mizati iŵiri yotalika mamita 2.5 imaimikidwa kutsogolo ndi kumbuyo kwa chombocho. Chingwe chimamangidwa zolimba pamwamba pa nsanamira zimenezi, ndipo chilona chachikulu chimayalidwa pamwamba pake kupanga tsindwi, kapena denga. Matabwa amakhala makama, ndipo mabulangeti ndi mabedishiti amakhala matiresi. Mosasamala kanthu za zimenezo, kugona sikuvuta pambuyo pa tsiku lotanganitsa limenelo.
Apainiya amafunsidwa kuti, “Kodi mumasamba madzi amatopewo?”
“Osati pamene tikhoza kupeŵa zimenezo!” amayankha motero. “Nthaŵi iliyonse imene tifika pakamfuleni kamadzi abwino, timadzaza zotengera zathu ndi madzi ophikira, akumwa, ndi osamba.”
Chipiriro chawo chimafupidwa ndi zokumana nazo zambiri zokondweretsa. Panthaŵi ina, mwamuna wina anafika padoko, naimirira chiliri, atagwira manja m’chuuno, natipenya mochita chidwi kwambiri. “Kingdom Proclaimer V!” iye anaŵerenga dzinalo mofuula kutsogolo kwa bwato. “Muyenera kukhala Mboni za Yehova. Ndinu nokha amene mumagwiritsira ntchito liwu lakuti ‘ufumu’ mwanjirayi. Muli ndi Nyumba yanu Yaufumu ndipo tsopano muli ndi Kingdom Proclaimer.”
Kuchokera ku Gileadi Kupita ku Pomeroon
Ntchito ya m’mphepete mwa mtsinje wa Pomeroon ili yosiyana pang’ono, monga momwe Frederick McAlman akukumbukirira. Patapita chaka chimodzi pambuyo pa kumaliza maphunziro ake ku Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower mu 1970, iye anapita ku Charity, mudzi wa ku mtsinje wokhala pamtunda wa makilomita 34 kugombe lakummaŵa la Pomeroon, kumene kunali kagulu ka ofalitsa a Ufumu asanu.
“Kwa zaka zotopetsa zisanu, tinali ndi ‘mwaŵi’ wakupalasa Proclaimer II cha uku ndi cha uko mu Pomeroon tisanagule injini yogwiritsidwapo ntchito yamphamvu zokwanira six-horsepower,” akukumbukira motero Mbale McAlman. “Popalasa m’mafunde, tinali kulalikira kugombe lakummaŵa kufikira titafika ku Hackney, [makilomita 11] kuchokera ku matsiriro. Kumeneko, tinali kugona bwino m’nyumba ya Mlongo DeCambra, namwino amene anagwira ntchito m’chigawocho panthaŵiyo. Tsiku lotsatira m’mamaŵa, tinkapitirizabe mpaka kumatsiriro a mtsinje tisanawolokere kugombe lakumadzulo. Ndiyeno pobwerera tinali kulalikira mtunda [wamakilomita 34] kumka ku Charity.”
Injini ya six-horsepower inawatumikira bwino lomwe kwa zaka khumi. Ndiyeno, mu 1986, inasinthidwa nkuikako yatsopano yamtundu wa 15-horsepower. Pambuyo potumikira mokhulupirika kwa zaka zoposa 21 ku Pomeroon, Mbale McAlman amayang’ana mokhutira Nyumba Yaufumu yomangidwa chatsopano mu Charity, imene tsopano ikugwiritsidwa ntchito ndi mpingo wa ofalitsa 43, amene amachokera kumtunda ndi kumunsi kwa mtsinjewo. Avareji ya opezeka pamsonkhano imapitirira 60, ndipo pa Chikumbutso cha imfa ya Yesu Kristu cha 1992, panali khamu la anthu okwanira 190!
Kufunafuna “Mwamuna wa Nsanja ya Olonda”
Lolemba nditsiku lamsika ku Charity. Chotero ili nthaŵi yabwino kulalikira mbiri yabwino, ndipo Mboni zimakhala kumeneko ndi magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Tsiku lina kuchiyambi kwa ma 1970, Monica Fitzallen wa ku Warimuri ku Moruka anadza kumsika ndipo analandira magazini aŵiri kwa Mbale McAlman. Koma pamene anafika kunyumba, anangoika magaziniwo mudrowa yapansi ya zovala zake.
“Iwo anakhala mmenemo kwa zaka ziŵiri popanda kuwaŵerenga,” akukumbukira motero Monica. “Ndiyeno ndinadwala ndipo ndinali chigonere kwa nthaŵi yakutiyakuti. Pamene ndinali kuchira, ndinayamba kufunafuna nkhani iliyonse yoti ndiŵerenge panyumba kuti ndisasungulumwe. Potsirizira pake, ndinakumbukira magazini aŵiri mudrowa yazovala ndipo ndinayamba kuwapenda.” Iye anazindikira nthaŵi yomweyo kuti iwo ndichowonadi.
Pamene Monica anachira, anafunsa mwamuna wake, Eugene, kuti akafune ntchito m’mphepete mwa Pomeroon kuti akapeze mwamuna amene anampatsa magaziniwo. Eugene anavomereza koma anangopeza ntchito ya mlungu umodzi pa famu ya m’mphepete mwa Pomeroon, kuyambira pa Lolemba kufikira pa Loŵeruka masana.
Podzafika Loŵeruka, Monica anali asanapezebe mwamuna amene anampatsa magazini. Chakumasana, iye anafunsa mwamuna wake ngati mafunde akanawalola kupalasa bwato kumka ku Charity kukafuna “Mwamuna wa Nsanja ya Olonda.” Atangotha kulankhula, iwo anamva mapazi m’likole ndipo anawona nkhope yachimwemwe ya mlongo amene anali kudzamugaŵira makope atsopano a magazini. “Kodi ndinu mmodzi wa anthu a Nsanja ya Olonda?” Monica anafunsa motero. Chotero panakhala mafunso ambiri kotero kuti mlongoyo anafunikira kubwerera kubwato kukapempha chithandizo. Kodi wodzathandizayo anali yani? Osati wina aliyense koma Mbale McAlman!
Phunziro Labaibulo mwa kulemberana makalata linalinganizidwa. Pambuyo pa nthaŵi yaifupi, Monica anatumiza kalata yochoka m’Tchalitchi cha Anglican. Monga yankho, iye analandira kakalata kochokera kwa wansembe kakuti: “Usamvere a JW [Mboni za Yehova]. Iwo alibe chidziŵitso chozama cha Baibulo. Ndidzafika kudzakambitsirana nawe nkhaniyo.” Kufikira tsopano, wansembeyo sanafikebe. Komabe, Monica anabatizidwa mu 1975. Pambuyo pa chaka chimodzi, mwamuna wake, amene tsopano mwachikondi amatchedwa Bambo Eugene ndi abale, nayenso anabatizidwa pambuyo pakupenda mosamalitsa Malemba. (Machitidwe 17:10, 11) Ngakhale kuti iwo akukhala pamtunda womwe umatenga ulendo wa maola 12 ndi bwato kuchokera pa mpingo wapafupi kwambiri mu Charity, iwo apitirizabe kukhala ofalitsa okangalika a Ufumu kufikira lero.
Maulendo Aumishonale m’Zigawo za Mkati
M’zaka zaposachedwapa Watch Tower Society yakhala ikulingaliza maulendo anthaŵi zonse aumishonale a kuzigawo zamkati. Ndi mabwato a mainjini akunja, antchito odzifunira ofunitsa alaŵa chikondwerero chakutengera mbiri yabwino anthu okhala m’malo otetezereka a Amerindian ndi malo kumene amadula mitengo ndi mafamu a m’mphepete mwa mitsinje m’madera akutali. Pokhala apainiya enieni malinga ndi tanthauzo la liwulo, iwo ali ndi mwaŵi wakupereka “dzina la [Yehova, NW]” lopulumutsa moyo kwa nzika zimenezi za kumadera akutali kwa nthaŵi yoyamba. (Aroma 10:13-15) Abale amapirira mavuto ambiri, nthaŵi zina amayenda ndi bwato m’mitsinje imeneyi kwa masiku atatu kuti afikire ena a malo ameneŵa. Koma mphotho zake nzoyenera.
Mnyamata wina wa Pentekoste wokhala pafupi ndi Kwebanna, malo kumene amadula mitengo ku mtsinje wa Waini, anachezeredwa paulendo waumishonale woyamba ku chigawocho m’July 1991. Paulendo wotsatira mu October, phunziro Labaibulo linayambidwa. Kwanthaŵi yoyamba, iye anawona mu Baibulo lakelake kuti dzina la Mulungu ndilo Yehova, kuti Yesu saali Wamphamvuyonse, ndi kuti chiphunzitso cha Utatu sichiri cha m’Malemba. (Salmo 83:18; 1 Akorinto 11:3) Iye anali wotenthedwa maganizo kwambiri kotero kuti, abalewo atachoka, anasonkhanitsa Apentekoste anzake pamodzi nayamba kuwasonyeza m’Mabaibulo awo chowonadi chonena za Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu. Pamene ambiri anakana chowonadicho, iye anawona kuti inali nthaŵi yakusiya ndi kutuluka mu “Babulo Wamkulu.” (Chivumbulutso 18:2, 4) Pamene abalewo anabwera kudzamuwonanso mu February 1992, iye anawauza zimene zinachitika nawonjezera kuti: “Ndifuna kugwirizana nanu. Ndifuna kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova. Ndifuna kuphunzitsa anthu chowonadi!”
Zokumana nazo zonga chimenechi zimathandizira abale kupitiriza ntchito yovuta imeneyi. Awo amene amapita pa maulendo aumishonale ayenera kudzimana maubwino a nyumba, ndi kudziika paupandu wamatenda onga malungo, ndi kupirira maupandu a moyo wamtchire. Komanso awo amene samapita amadzimana. Mabanja amalakalaka okondedwa awo, nthaŵi zina kwa milungu ingapo. Mipingo imakhala yopanda akulu ndi amuna ena achichepere popeza kuti, nthaŵi zina, pamatsala mbale mmodzi yekha wosamalira zosoŵa za mpingo. Komabe, nchisangalalo ndi chilimbikitso chotani nanga chimene chimakhalapo pamene mpingo umva zokumana nazo zawo zochititsa nthumanzi ngati iwo abwerako! Mavutowo samakhalanso kanthu.
Olengeza Ufumu amene amaloŵa pamadzi a Guyana ndi mbiri yabwino amakhaladi ndi zokumana nazo zapadera. Limodzi ndi antchito anzawo kuzungulira dziko lapansi, iwo molimba mtima ndipo mofunitsa ‘amapereka chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.’—Ahebri 13:15.
[Mawu a M’munsi]
a Kale linali kutchedwa British Guiana, dzinalo linasinthidwa kukhala Guyana pambuyo pakupeza ufulu wakudzilamulira kuchokera ku Britain mu 1966.
[Mapu patsamba 24]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
HONDURAS
NICARAGUA
COSTA RICA
PANAMA
VENEZUELA
COLOMBIA
GUYANA
SURINAME
FRENCH GUIANA
BRAZIL
BOLIVIA
ATLANTIC OCEAN
[Zithunzi pamasamba 26, 27]
Kulamanzere: Kuchitira umboni pa tsiku lamsika
Pamwamba: Kukambitsirana mbiri yabwino ku mtsinje wa Demerara
Pamwamba kulamanja: Kagulu ka amishonale kakupalasa kubwerera ku msasa