Katundu Wachithandizo Asonyeza Chikondi Chachikristu
“KONDANI gulu lonse la abale,” analimbikitsa chotero mtumwi Petro Akristu anzake. (1 Petro 2:17) Chikondi chotero chinali kudzalumpha malire aufuko, anthu, ndi mtundu, kusonkhanitsa anthu pamodzi mu ubale wowona. Pamene kusoŵa zinthu zakuthupi kunabuka pakati pa Akristu oyambirira, chikondi chinasonkhezera ambiri kupereka zopereka kwa atumwi kuti zikagaŵiridwe kwa osoŵa amenewo. Cholembedwacho chimati “nakhala nazo zonse zodyerana”—Machitidwe 2:41-45; 4:32.
Chikondi chotero chinawoneka pamene Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, linapempha nthambi zingapo za Watch Tower Society zakumadzulo kwa Yuropu kumapeto kwa 1991, kugaŵira chakudya ndi zovala kwa abale awo osoŵa Kummaŵa kwa Yuropu, kuphatikizapo zigawo za imene kale inali Soviet Union. Panopa tikupereka mpambo wamalipoti ochokera kunthambi zina zophatikizidwa.
Sweden
Pa December 5, 1991, kalata yofotokoza kusoŵa inatumizidwa kumipingo yonse 348 m’Sweden. Kulabadira kunali kwamwamsanga. Mkati mwa masiku oŵerengeka, tirela loyamba lodzala linali paulendo wopita ku St. Petersburg Russia, lopachiridwa matani 15 aufa watirigu, mafuta ophikira, nyama yam’zitini, mkaka waufa, ndi zina zotero. Mboni za Yehova zamomwemo zinatsitsa katundu pagalimoto ndipo mwamsanga zinagaŵira maphukusi 750 kwa osoŵa. Pambuyo pake, matirela owonjezereka aŵiri anapititsa chakudya ku Russia. Onse pamodzi, oposa matani 51.5 anatumizidwa kuchokera ku Sweden.
Kufunitsitsa kupereka chithandizo cha zovala ndi nsapato kunapitirira kwambiri zoyembekezeredwa. Miyulu yambirimbiri yamaphukusi azovala inakula mofulumira m’Nyumba Zaufumu. Akristu ambiri anapereka chithandizo cha zovala kuchokera pazovala zawo. Ena anagula zatsopano. Mbale wina anagula masuti asanu. Pamene mwini sitolo wodabwa anamva chifuno chake, anapanga chopereka cha masuti ena asanu. Mbale wina anagula bokosi la masokisi, maglovisi, ndi masikafu. Pamene anafotokoza chifuno chake, mwini sitolo anamtchipisira masuti atsopano 30 pamtengo wa aŵiri. Mwini sitolo wogulitsa zovala zamaseŵera anapanga chopereka cha mapeya 100 ansapato zatsopano.
Pamenepo zinthu zonsezi zinabweretsedwa kunthambi kudzasankhidwa, kuikidwa m’zotengera, ndi kupachiridwa. Zovala—zokwanira kunyamulidwa ndi matirela 40—zinadzaza malo aakulu panthambi! Abale ndi alongo anagwira ntchito masabata angapo kuika zinthuzo m’miulu ya za amuna, akazi, ndi za ana ndi kuzipachira m’makatoni. Matirela osiyanasiyana khumi ndi asanu anagwiritsiridwa ntchito kunyamulira zovala mosungika kumka nazo ku Russia, Ukraine, ndi Estonia.
Mbale amene anayendetsa imodzi yamagalimoto a Sosaite nthaŵi zisanu ndi zitatu kumka ku imene kale inali Soviet Union anati: “Kuchingamiridwa ndi abale athu komwe tinapita kunali mphotho yaikulu. Iwo anatikupatira ndi kutipsopsona, ndipo mosasamala kanthu za kusauka kwawo, iwo anatipatsa ife phunziro labwino kwambiri m’kuoloŵa manja Kwachikristu.
Finland
Mosasamala kanthu za kukanthidwa moipa kwachuma kwa Finland, kuwanda kwa ulova, ndi mavuto azachuma, kufunitsitsa pakati pa abale pafupifupi 18,000 aku Finland kuthandiza abale awo m’maiko amene kale anali Soviet Union kwakhala kwakukulu. Iwo anatumiza oposa matani 58 achakudya m’makatoni 4,850 ku St. Petersburg, Estonia, Latvia, Lithuania, ndi Kaliningrad. Iwo anadzazanso malo opanda kanthu m’magalimoto ndi mulu wa zovala wa makyubiki mita 12. Magalimoto okwanira 25 ogwiritsiridwapo ntchito ndi mabokosibode nawonso anaperekedwa monga mphatso kuti akagwiritsidwe m’ntchito ya Ufumu.
Chakudya china m’mabokosi chinafika kumpingo wa ofalitsa 14 ku Slanti m’chigawo cha St. Petersburg. Iwo anathokoza kwambiri m’kalata. “Tiri ndi alongo okalamba khumi mu mpingo wathu. Unyinji wa ife tikudwala kwa kayakaya ndipo sitingathe kuimirira m’mizera kwamaola ochuluka kukapeza chakudya. Komabe, Atate wathu wakumwamba sanatilole kukhwetemuka maganizo m’nthaŵi zovuta zino koma akudzaza mitima yathu ndi chimwemwe. Tikuchititsa maphunziro a Baibulo apanyumba 43.” Pamene mlongo wina mu St. Petersburg analandira phukusi lake lachithandizo, anakhudzidwa mtima kwambiri kotero kuti analira kwamaola aŵiri asanalitsegule.
Denmark
M’dziko laling’ono limeneli pachipata choloŵera ku Nyanja ya Baltic, Mboni za Yehova pafupifupi 16,000 zinasonkhana ndi kutumiza ku Ukraine malole 19 okhala ndi chakudya chokwanira matani 64 m’mabokosi 4,200; mabokosi 4,600 azovala zokwera mtengo; ndipo mapeya 2,269 a nsapato zatsopano. Mbale wina m’Jeremani analola nthambi kugwiritsira ntchito malole ake asanu amene pambuyo pake anati akhale zopereka kwa abale mu Ukraine. Pobwerera kwawo, mmodzi wa oyendetsa magalimoto anati: “Tinapeza kuti tinabweretsa zochulukirapo kuposa zimene tinapititsa. Chikondi ndi mzimu wodzimana wosonyezedwa ndi abale athu a ku Ukraine zinalimbikitsa chikhulupiriro chathu kwambirimbiri.”
Oyendetsa magalimoto ena anafunikira kuchenjera ndi achifwamba pa misewu ya kumene kale kunali ku Soviet Union. Masiku ochepekera galimoto lina laku Denmark lisanadutse, panali uchifwamba umene unachitika pamsewu umenewo. Magalimoto asanu oyendera pamodzi onyamula chakudya a gulu lina lopereka chithandizo anaimikidwa ndi achifwamba ogwiritsira ntchito mahelikoputala ndi mfuti za akasinja. Iwo anatenga malole onse asanu, akumasiya oyendetsa malolewo pambali pamsewu. Mosasamala kanthu za upandu wotero, mitokoma yonse yochokera kunthambi ya Denmark inafika kwa abale mosungika. Ndiponso, iwo anapatsira woyendetsa loleyo kalata yotsatirayi kubwerera nayo kumudzi, yolembedwa movutikira kwambiri m’Chingelezi: “Abale okondedwa ndi alongo aku Denmark: Talandira chithandizo chanu. Yehova adzakufupani.”
Netherlands
Nthambi ya Netherlands inatumiza matani 52 achakudya m’maphukusi 2,600. Anatumizidwa ku Ukraine pamilongo iŵiri ya malole. Panthaŵi iriyonse, malolewo anasiidwa, pakuti anaperekedwa monga mphatso ndi abale ku Jeremani kuthandiza ntchito ya Ufumu Kummaŵa. Abale a ku Ukraine anatumiza chakudya chambirimbiri ku Moscow, Siberia, ndi malo ena kumene kusoŵa kunali kwakukulu. Ndiponso, mulu wa zovala wa makyubiki mita 736 ndi nsapato zinaperekedwa ndi abale Achidatchi monga mphatso. Zinatumizidwa ku Lviv mu Ukraine, pamulongo wa malole 11 operekezedwa ndi galimoto laling’ono.
Pambuyo paulendo wautali kudutsa Jeremani ndi Poland, magalimoto oyendera pamodziwo anadutsa bwino lomwe pa kasitomu ya Ukraine, ndipo anafika kumilaga ya Lviv pa 3 koloko mbandakucha. Oyendetsawo akusimba kuti: “M’nthaŵi yaifupi, gulu la abale 140 linali chire kutsitsa katundu pamagalimoto. Asanayambe ntchitoyo, abale odzichepetsa amenewa anasonyeza kudalira kwawo Yehova, mwakupereka pemphero pamodzi. Pamene ntchitoyo inamalizidwa, anatisonkhanitsa kuti apereke pemphero lothokoza kwa Yehova. Pambuyo pakusangalala ndi kuchereza kwa abale athu amomwemo, amene anapereka mooloŵa manja zochepekera zimene anali nazo, tinaperekezedwa kumsewu waukulu, kumene anapereka pemphero pambali pamsewu tisanachoke.
“Mkati mwaulendo wautali wobwerera kwathu, panali zambiri zakuzilingalira mosinkhasinkha—kuchereza kwa abale m’Jeremani ndi Poland, ndi kwa abale athu mu Lviv; chikhulupiriro chawo cholimba ndi mkhalidwe wawo wopemphera; kuoloŵa manja kwawo m’kutigaŵira malo ogona ndi chakudya pamene iwo eni ali m’mikhalidwe yakusoŵa; kusonyezana kwawo chigwirizano ndi umodzi; ndi kuyamikira kwawo. Tinalingaliranso za abale athu ndi alongo kwathu, amene anapereka mooloŵa manja chotero.”
Switzerland
Nthambi ya Switzerland ikuyamba lipoti lake mwakugwira mawu Yakobo 2:15, 16: ‘Mbale kapena mlongo akakhala wausiŵa, nichikamsoŵa chakudya cha tsiku lake, ndipo wina wa inu akanena nawo, Mukani ndi mtendere, mukafunde ndi kukhuta; osawapatsa iwo zosoŵa za pathupi; kupindula kwake nchiyani?’ Kenako lipotilo likupitiriza kuti: “Tinakumbukira Lembali pamene Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova linatipempha kupereka chithandizo cha zinthu zakuthupi kwa abale athu osoŵa.
“Mwamsanga pompo aliyense anali wotanganitsidwa! M’masiku aŵiri okha, chakudya chokwanira matani 12 m’maphukusi 600 chinatumizidwa ku Ukraine ndi malole atatu ochokera ku Jeremani, amene anali kudzakhala chopereka kuntchito kumeneko. Mbiri yakuti onse anafika mosungika inachititsa chikondwerero chachikulu pakati pa abale kunoku. Panthaŵiyo, mipingo inasonkhanitsa zovala, ndipo mwamsanga nthambi yathu inadzala thothotho ndi makatoni, masutikesi, ndi matumba! Zokhala ndi zovala za ana zinaphatikizapo zoseŵeretsa kuchokera kwa ana Achiswiss kumka kwa mabwenzi awo osadziŵika kutaliko Kumpoto. Machokoleti ambiri anali kuikidwanso pakati pamiyalo yazovala.”
Kodi zonsezi zinali kudzatumizidwa motani? Lipotilo likuti: “Nthambi ya Falansa inatithandiza mwakutipatsa matirela aŵiri ndi oyendetsa magalimoto anayi oti tigwiritsire ntchito. Kuwonjezera, lole imodzi yochokera panthambi yathu ndi ena anayi a abale akuno anafunika kupititsa matani 72 ku Ukraine.” Magalimoto oyendera limodzi, pa mzera wotalika mamita 150, anafika mosungika bwino padepo mu Lviv, kumene pafupifupi abale amomwemo zana limodzi anayembekezera kutsitsa katundu pamagalimoto. Oyendetsawo anasimba kuti chopinga cha chinenero sichinali chidodometso chifukwa chakuti nkhope zawo zinasonyeza chiyamikiro chachikulu.
Austria
Abale aku Austria anatumiza matani 48.5 achakudya, makatoni 5,114 azovala, ndi mapeya 6,700 a nsapato ku Lviv ndi Uzhgorod mu Ukraine. Iwo anatumizanso matani 7 achakudya, mabokosi 1,418 azovala, ndi mapeya 465 a nsapato ku Belgrade, Mostar, Osijek, Sarajevo, ndi Zagreb mu imene kale inali Yugoslavia. Lipoti lanthambi likuti: “Tinali ndi matirela 12 opachiridwa amene anayenda ulendo wamakilomita 34,000. Mbali yaikulu ya ntchito yoyendetsa katundu inachitidwa ndi mbale wina ndi mwana wake wamwamuna amene ali ndi bizinesi yonyamula zinthu ndi malole.”
Ponena za zopereka za zovala, lipotilo likupitiriza kuti: “Tinagwiritsira ntchito Nyumba Yamsonkhano monga malo apakati osungira katundu. Malole odzala katundu anapitirizabe kumafika, kufikira panalibenso malo. Mofanana ndi masiku a Mose, anthu anafunikira kuletsedwa kusabweretsanso zowonjezereka. (Eksodo 36:6) Ngakhale anthu ena amene sali Mboni za Yehova anapereka mphatso za ndalama, ‘chifukwa chakuti,’ monga momwe iwo eni adanenera, ‘mwanjirayi tikudziŵa kuti anthu osowa adzachilandira.’ Tinapezanso makatoni ochuluka kwambiri opanda kanthu ofunikawo kuchokera ku makampani akudziko kwaulere.” Abale ndi alongo amene anali kupatula ndi kupachira zinthu zonse anayambira pa zaka 9 zakubadwa kufikira pa zaka 80. Iwo anayesa ngakhale kusankha shati yoyenerana ndi suti iriyonse.
Lipotilo likuti: “Akuluakulu aboma mu Austria ndi kumalire akhala othandiza kwambiri m’kupangitsa maulendo amagalimoto onyamula chithandizo osiyanasiyana kukhala otheka ndi m’kupereka zikalata zofunika kuti maulendo onse apangidwe popanda vuto lokulira.”
Italiya
Kuchokera ku Roma kunadza matani 188 achakudya otumizidwa m’malole aŵiri oyendera pamodzi kudutsa Austria, Czechoslovakia, ndi Poland kumka ku imene kale inali Soviet Union. Magalimoto aliwonse oyendera limodzi anaphatikizapo oyendetsa magalimoto asanu ndi mmodzi, makanika, makanika wamagetsi agalimoto, womasulira, woimira wotumizawo, wophika, dokotala, mtsogoleri wamagalimoto oyendera pamodzi m’jipi, ndi mbale wonyamula mahema.
Chakudyacho chinagulidwa kumakampani ogulitsa chakudya ndi ziŵiya asanu ndi aŵiri. Nthambiyo ikusimba kuti: “Ndipo otigulitsirawo anamva chifukwa chimene tinali kugulira, ena a iwo anafuna kutenga mbali. Mazana angapo a makilogramu asipageti ndi mpunga, kuphatikizapo mabokosi ophachiramo, anaperekedwa monga mphatso ndi makampani adziko. Pamene ena anapereka matayala oyenda pachipale chofeŵa amalole kapena analonjeza kupereka mphatso zandalama.
“Abale mu Italiya anayamikira mwaŵi umenewu wakuthandiza. Ana nawonso anafuna kuthandiza m’zopereka. Mnyamata wina wa zaka zisanu zakubadwa anatumiza chopereka chake chimene anayembekezera kuti chikagula ‘chitini chachikulu cha nsomba za tuna cha abale a ku Russia.’ Msungwana wina wachichepere analandira ndalama kuchokera kwa agogo ake chifukwa chakupeza kwake magiredi abwino kusukulu kuti akagulire mphatso makolo ake. ‘Koma,’ monga momwe analembera, ‘pamene ndinazindikira kuti abale anga ambiri alibe konse zinthu zabwino zakudya zomwe ine ndili nazo, ndinaganiza kuti mphatso yabwino koposa imene ndikakhoza kugulira makolo anga inali yakuthandiza abale amenewo.’ Iye anaika ndalama zochulukirapo m’bokosi lazopereka. ‘Ndifuna kupitirizabe kupeza magiredi abwino, kotero kuti ndidzakhoza kutumiza ndalama zowonjezereka,’ iye anatero.” Lipoti lanthambi likumaliza mwakunena kuti makalata osonyeza chiyamikiro chachikulu kuchokera kwa abale ku Ukraine, mawu ambiri osonyeza chiyamikiro kuchokera kwa abale a ku Italiya, ndi zokumana nazo zabwino kwambirizo m’kukonzekera ndi kutumiza katunduyo zinali zosonkhezera, zolimbikitsa, ndi zomangirira.
Chakudya cha Nthumwi Zikwi Zambiri
Msonkhano woyamba wamitundu yonse wa Mboni za Yehova mu imene kale inali Soviet Union unachitidwira mu Kirov Stadium ku St. Petersburg m’Russia, June 26-28, 1992. Msonkhano wopanga mbiri umenewu, wamutu wakuti “Onyamula Kuunika,” unali ndi nthumwi zoposa 46,200 zofikapo kuchokera kumaiko 28. Unapereka mpata wina wakusonyeza chikondi Chachikristu ku “gulu lonse la abale.”—1 Petro 2:17.
Matani ambirimbiri achakudya chochokera ku Denmark, Finland, Sweden, ndi maiko ena a Kumadzulo kwa Yuropu anagaŵiridwa kwaulere kwa nthumwi za msonkhano zikwi zambiri zochokera ku imene kale inali U.S.S.R., kuti chidyedwe m’nthaŵi yamsonkhano. Pamene iwo anachoka pamsonkhano pambuyo pa programu yomaliza, anapatsidwanso maphukusi achakudya ndi kamba waulendo wawo wobwerera kumudzi.
Malipoti otchulidwa pano amasonyeza kuti kupatsa sikunakhale kopita malo amodzi—chakummaŵa—kokha. Pakhalapo kupatsana. Inde, chakudya ndi zovala zinapita kummaŵa, koma kumadzulo kunapita mawu osaŵerengeka othutsa mtima achikondi ndi zokumana nazo zosonkhezera chikhulupiriro zosonyeza kupirira ndi kukhulupirika za olambira Yehova zikwi zambiri mkati mwa zaka zambiri zachitsenderezo ndi chivuto. Chotero, mbali zonse ziŵiri zatsimikizira chowonadi cha mawu a Yesu akutiwo: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.”—Machitidwe 20:35.
[Chithunzi patsamba 21]
1. Kuchokera ku Finland: St. Petersburg, Russia; Tallinn ndi Tartu, Estonia; Riga, Latvia; Vilnius ndi Kaunas, Lithuania; Kaliningrad, Russia; Petrozavodsk, Karelia
2. Kuchokera ku Netherlands: Lviv, Ukraine
3. Kuchokera ku Sweden: St. Petersburg, Russia; Lviv, Ukraine; Nevinnomyssk, Russia
4. Kuchokera ku Denmark: St. Petersburg, Russia; Lviv, Ukraine
5. Kuchokera ku Austria: Lviv, Ukraine; Belgrade, Mostar, Osijek, Sarajevo, Zagreb (mu imene kale inali Yugoslavia)
6. Kuchokera ku Switzerland: Lviv, Ukraine
7. Kuchokera ku Italiya: Lviv, Ukraine
[Zithunzi patsamba 23]
Makatoni azovala mu nthambi ya Sweden
Kupachira katundu wachithandizo
Zakudya m’phukusi limodzi
Nyama yankhumba ya ku Denmark
Mulongo wa malole 11 ndi galimoto 1
Maphukusi ndi masutikesi panthambi ya Austria
Kutsitsa katundu palole ku Lviv, Ukraine