Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 12/15 tsamba 19-20
  • Khoti Lalikulu la Nigeria Lichirikiza Ufulu Wachipembedzo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Khoti Lalikulu la Nigeria Lichirikiza Ufulu Wachipembedzo
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Kuchokera Kukhoti kumka Kukhoti Lina
  • Ufulu Wachipembedzo Upambana
Nsanja ya Olonda—1992
w92 12/15 tsamba 19-20

Khoti Lalikulu la Nigeria Lichirikiza Ufulu Wachipembedzo

ANTHU akumidzi akufunkha zokololedwa za mwinifama. Ena akuloŵa m’nyumba ya wogwira ntchito yomanga ndi kufunkha ziwiya zake. Pamene ena akulepheretsa mkazi wina kugula ndi kugulitsa. Kodi choputira nkhanzazo nchiyani? Chiri chifukwa chakuti oukiridwawo, amene onse ali Mboni za Yehova, akukana kutenga mbali m’mayanjano a pakati pa anthu amsinkhu wofanana. ‘M’chiyani?’ inu mungafunse.

Bungwe la amisinkhu yofanana limapangidwa ndi anthu, kaŵirikaŵiri amuna, amene anabadwa pafupifupi nthaŵi yofanana ndipo m’mudzi wofananawo. Timagulu ta amisinkhu yofanana ntozoloŵereka cha kummaŵa kwa Nigeria. Iwo angachirikize ntchito ina m’chitaganya, koma iwo amaphatikizidwanso m’kulambira mafano ndi kuchita madzoma olambira mizimu kusonyeza kuti mamembala amenewo afikira msinkhu wovina chinamwali. Chifukwa chakuti Baibulo limatsutsa zizoloŵezi zotero kwa Akristu owona, Mboni za Yehova sizimagwirizana ndi timagulu totero.​—1 Akorinto 10:20, 21; 1 Yohane 5:21.

Samuel Okogbue anali kugwira ntchito yosoka mu Aba, Nigeria. Kuchiyambiyambi kwa 1978, ziŵalo za Bungwe la Umunkalu la Amisinkhu Yofanana la ku Alayi zinapempha kuti iye alipire “msonkho” wothandiza kumanga nyumba yachipatala. Monga Mkristu wowona, Samuel amachita zothekera kuthandiza anthu ena, koma mogwirizana ndi chikumbumtima chake iye anakana kuphatikizidwa m’kagulu ka amisinkhu yofanana. Pa April 22 wachaka chomwecho, ziŵalo zisanu ndi chimodzi za kaguluko zinaphwanya ndi kuloŵa m’sitolo lake ndi kufunkha makina ake osokera, amene iwo adanena kuti akawagwira chikole kufikira atalipira ndalama. Samuel anatsutsa akumati sanali wokakamizika kulipira kanthu kalikonse chifukwa chakuti iye sanali chiŵalo cha kagulu kameneko. Pamene iye analephera kutenga makina ake osokera, Samuel anapititsa nkhaniyo ku khoti.

Kuchokera Kukhoti kumka Kukhoti Lina

M’khoti la Mejasitiliti Wamkulu, akagulu ka amisinkhu yofanana kameneko ananena kuti chifukwa cha msinkhu wake, Samuel mosatofunikira kulembedwa anali mmodzi wa mamembala awo, wokhala ndi thayo lakulipira msonkho uliwonse umene unali wokakamiza pa iwo onse. Ndiponso, mwambo wafukolo unali wakuti ngati membala sanakhome msonkhowo, katundu wake akafunkhidwa kufikira akakhoma.

Khotilo silinavomerezane nazo. Pa February 28, 1980, linalamula kuti Samuel sakayenera konse kukakamizidwa kukhala membala wa akagulu kamisinkhu yofanana. Mejasitiliti Wamkuluyo anafotokoza kuti: “Mwambo umene umamana nzika ufulu wakusankha gulu ukuchita motsutsana ndi G[awo] 37 la Mpambo wa Malamulo wa Federal Lipabuliki ya Nigeria ndipo chifukwa chake sungapeze chichirikizo cha Lamulo.”

Kagulu ka amisinkhu yofanana kanachitira apilo chiweruzo chimenechi ku Khoti Lapamwamba ndipo kanapambana. Kumeneko woweruza analamulo kuti Samuel alipire msonkho, akumanena kuti inali kokha njira yothandizira chitukuko cha chitaganya cha kwawo.

Pamenepo Samuel anachitira apilo chimene adawona kuti chinali chisalungamo. Khoti la Apilo linatsutsa chiweruzo cha Khoti Lapamwamba, likumaweruza mokomera Samuel. Posafuna kulola kugonjetsedwa, kagulu ka amisinkhu yofananako kanapititsa nkhaniyo ku Khoti Lalikulu la Nigeria.

Panthaŵiyo, mamembala a kaguluko anali otanganitsidwa m’mudzi wa Samuel. Akumanena kuti Mboni zinali kutsutsana ndi ntchito zonse zachitaganya, iwo anakhutiritsa nyakwawa wa pamudzi kuletsa ntchito za Mboni za Yehova m’chigawocho. Nduna yapamudzipo inalengeza kuti munthu amene akagwirizana ndi Mboni za Yehova akalipiritsidwa faindi. Mboni za m’matawuni apafupi zinaloŵerera ndipo zinamveketsa nkhaniyo kwa madoda amudzi. Izo zinafotokoza kuti anthu a Mulungu sanatsutse konse chitukuko cha m’chitaganya. Kunena zowona, Samuel anali atatulutsa malisiti kukhoti kutsimikizira kuti anali atathandizira ntchito zachitaganya zimene sizinachirikizidwe ndi kagulu ka amisinkhu yofanana. Pamenepo madoda apamudziwo anasintha chosankha chawo choletsa Mboni.

Ufulu Wachipembedzo Upambana

Pa October 21, 1991, oweruza asanu a Khoti Lalikulu la Nigeria analamula moyanja Samuel. Akumafotokoza mwatsatanetsatane zimene zinatsogolera ku chiweruzo choperekedwa ndi Woweruza Paul Nwokedi, Woweruza Abubakar Wali anati: “Siliri thangata [msonkho wokakamiza] limene woimbidwa mlanduyo [Samuel] akukana kulipira koma kukhala chiŵalo cha gulu lirilonse, kalabu kapena kagulu ka amisinkhu yofanana, popeza kuti kutero kuli kotsutsana ndi chiphunzitso cha chipembedzo chake, popeza iye ali membala wa Mboni [za] ya Yehova.”

Woweruzayo anapitiriza kuti: “Mpambo wa Malamulo wa 1963, chigawo 24(1) unatsimikizira nzika zonse za Nigeria ufulu wachikumbumtima, lingaliro, ndi chipembedzo. Wonenezedwayo ali ndikuyenera kwakuumirira kuchiphunzitso cha chipembedzo chake, lingaliro ndi chikumbumtima chimene chimamuletsa kugwirizana ndi a Misinkhu yofanana. Mwambo uliwonse umene ukakamiza mosiyana ndi izi ukutsutsana ndi Mpambo wa Malamulo ndipo chifukwa chake kumlingo umenewo uli wopanda ntchito.”

Mwachidule, khoti linalamula kuti palibe munthu amene angakakamizidwe mwalamulo kugwirizana ndi kagulu ka amisinkhu yofanana ngakhale ngati kukhala membala wake kungakhale mwambo wachitaganya. Linalamulanso kuti palibe munthu amene angakakamizidwe mwa lamulo kulipira thangata kupyolera mwa gulu limene iye sali membala wake, ngakhale pamene thangatalo liri lachitukuko chachitaganya. Chotero m’mawu owonekera kukhala achidule amenewa, ufulu wachipembedzo ku nzika zonse za Nigeria unachirikizidwa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena