Tawonani Zimene Yehova Watichitira!
“TINKAPEMPHERERA chochitika chonga ichi,” anatero mwamuna wina. Wina ankadzuka mamaŵa alionse paola lachinayi kupemphera. Kaamba ka chiyani? “Kupempherera kuti tsiku lina tidzakhale ndi ufulu wa kulambira Yehova poyera,” iye anatero. M’January 1992, pamene Mboni za Yehova mu Ethiopia zinakumana mu Addis Ababa kaamba ka Msonkhano wawo Wachigawo wakuti “Okonda Ufulu,” kunali kwachiwonekere kuti mapemphero odzichepetsa, owona mtima ameneŵa anayankhidwa.
Msonkhano wa ku Ethiopia umenewo unali chisonyezero cha mmene zinthu zinali kusinthira m’Afirika. M’zaka zaposachedwapa anthu a Yehova m’maiko 13 kumeneko asangalala kuvomerezedwa mwalamulo kumene poyamba analetsedwa kapena kuikiridwa malire. Mu Ethiopia, zaka 34 za chiletso chalamulo zinatha pa November 11, 1991, pamene akuluakulu aboma anapereka chivomerezo ndipo kulembedwanso m’kaundula waboma kunachitika. Mwamsanga, Mbonizo zinalinganiza kudzachita msonkhano wa mitundu yonse. Komabe, kuwona khamu la osonkhana 7,573 m’Bwalo Lamasewera la Mzinda wa Addis Ababa kunali chochitika chosangalatsa kwambiri kwa aliyense. Kwa ambiri a amene anali mwa omvetsera, kunali monga ngati kuti anali kulota. Iwo mobwerezabwereza anali kulankhulirana wina ndi mnzake kuti: “Mbale, tawonani zimene Yehova Mulungu wathu watichitira!”—Yerekezerani ndi Salmo 66:1-5; 126:1.
Kukhala kwawo oletsedwa kwazaka 34 kunapangitsa mavuto ena osayembekezereka. Ambiri anali osazoloŵerana ndi nyimbo zokongola Zaufumu. Kodi iwo akaphunzira motani kuziimba msonkhano usanachitike? Nyimbo makumi anayi, kuphatikizapo 17 zogwiritsiridwa ntchito paprogramu yamsonkhanowo, zinatembenuzidwira m’chinenero cha Amharic. Kenako, gulu lapadera la oyimba linalinganizidwa kujambula nyimbozo pakaseti. Mpingo uliwonse mumzinda unalandira kope la tepiyo, ndipo mpingo wathunthu unkatenga mphindi 30 misonkhano isanayambe ndi pambuyo pake kuyeseza nyimbozo. Kodi chotulukapo chinali chotani? Bwalo lamaseweralo linadzazidwa ndi kuimba kwamtima wonse ndi kwachisangalalo mkati mwa msonkhanowo.
Chifukwa cha zododometsa kumbali za kummaŵa kwadzikolo, msewu wopita kumalikulu kuchokera ku Diredawa ndi Harar inatsekerezedwa. Njira yokha yoyendera kuchokera kumeneko inali pandege. Posakhoza kulipilira ndege, koma ali otsimikiza kufika pamsonkhano, abale asanu ndi atatu m’Harar anapita kumalikulu a asilikali ankhondo napempha kunyamulidwa ndi ndege zankhondo. Mowadabwitsa pempholo linavomerezedwa. Iwo anayendetsedwa mosalipilitsidwa kumsonkhano wachigawoko!
Kuwona mapemphero awo akuyankhidwa kunabweretsa misozi yachisangalalo kwa abale aku Ethiopia ameneŵa, amene kwazaka makumi atatu zapitazo anapirira mavuto ndi zizunzo ndipo anawona ngakhale mabwenzi awo akuphedwera chikhulupiriro chawo. Nthumwi ina inati: “Ndinakhala ndikulira kuyambira pachiyambi cha msonkhano.” Ina inati: “Ngati munali wokhoza kuwerenga mitima, mukanawona mmene ndiliri wachimwemwe.” Inde, ndichinthu chodabwitsa chotani nanga chimene Yehova anachitira Mboni zokhulupirika zimenezi!—Salmo 66:16, 19.
Ufulu Wokulirapo Kumadzulo ndi Pakati pa Afirika
Benin ndidziko lina kumene ntchito ya anthu a Yehova posachedwapa yaloledwa mwalamulo. Kodi Mbonizo zimalingalira motani za zimenezi? Wolankhula wina pamsonkhano Wachikristu kumeneko anati: “Ufulu wa kulambira m’dziko lino ulidi mphatso yochokera kwa Yehova.” Inde, atumiki a Yehova kumeneko ali oyamikira kwambiri kuti tsopano angasangalale ndi ufulu wosadodometsedwa wa kusonkhana pamodzi m’kulambira ndi kulankhula ndi anansi awo za Ufumu wa Yehova—maufulu amene ambiri a ife timatenga mopepuka.
Kodi adzasonyeza motani chisangalalo chawo? Wolankhula wogwidwa mawu pamwambapa anatchula njira imodzi pamene anati: “Kukhala kwathu ndi phande m’ntchito yolalikira—makamaka kumka kunyumba ndi nyumba ndi mbiri yabwino—kumasonyeza chiyamikiro chathu ufulu umenewu.” M’Benin zimenezi zakhaladi choncho. Monga umboni, tangowonani ziŵerengero za apainiya. M’January 1990, mwezi umene chiletso cha zaka 14 chinachotsedwa, ofalitsa 77 anaphatikizidwa muutumiki wanthaŵi yonse. Zaka ziŵiri pambuyo pake chiŵerengerocho chinaŵirikiza koposa katatu kufikira ku 244!
Kutero sindiko kunena kuti Mbonizo m’Benin zinali zosagwira ntchito chiletsocho chisanachotsedwe. Ndithudi, chipiriro chawo chinali ndi chiyambukiro chachikulu pa mkulu wa ankhondo wina amene anagaŵiridwa kumsasa kumene iwo anabweretsedwa pamene anamangidwa. Popeza kuti kutsimikiza kwawo kutumikira Yehova kunatsogolera kukumangidwa kwakaŵirikaŵiri, iye anadzipeza kukhala akumawonana nawo mosalekeza. Komatu zimenezi zinangotumikira kokha kumkumbutsa za makambitsirano Abaibulo osangalatsa amene anali atakhala nawo m’masiku oyambirirawo pamene iwo anali ndi ufulu walamulo.
Potsirizira, chikhulupiriro chawo champhamvu chinadzutsa lingaliro la kumva njala yauzimu mwa iye. Iye anamka kumatchalitchi osiyanasiyana ndi timagulu tampatuko koma sanathetse njalayo. Kunali kokha pambuyo pa kuchotsedwa kwa chiletsocho mu January 1990 kuti iye anali wokhoza kukambitsirana Baibulo momasuka ndi Mboni napeza yankho la chosowa chake chauzimu. Iye tsopano ngwobatizidwa ndipo akutumikira monga mpainiya. Mwapang’ono, kusintha kwake kumakumbutsa abalewo m’Benin za zimene zinachitikira Saulo wa ku Tariso: “Iye wakutilondalonda ife kale, tsopano alalikira chikhulupirirocho.”—Agalatiya 1:23.
M’December 1991, Mboni za Yehova m’dziko lina la Kumadzulo kwa Afirika, Niger, zinalembetsedwa m’kaundula monga gulu lololedwa mwalamulo, ndipo ziletso pantchito yawo zinatha. Kunonso kunali kulabadira kwachimwemwe. Nthambi ya Nigeria, imene imasamalira Niger, ikusimba chilabadiro pamsonkhano wachigawo: “Pambuyo pa nkhani yapadera ya msonkhano ku Maradi pa Lachisanu, kunalengezedwa kwa abale kuti tsopano tinazindikiridwa mwalamulo mu Niger. Anakondwera kwambiri ndipo anawomba m’manja kwamphindi zingapo. Pamapeto a programuyo, abale anali kulankhula mokondwera kwambiri, kukupatirana ndi kusangalala ndi mbiri yabwinoyo.” Tingayerekezere chochitikacho, ndipo tikusangalala limodzi nawo.
Kodi abalewo kumeneko adzagwiritsira ntchito motani ufulu wawo wopezedwa chatsopano? Mlongo wina mpainiya m’Niger alibe chikaikiro ponena za yankho la funsolo. Iye akulemba kuti: “Zenizeni zikusonyeza kuti m’gawo lathu m’Niger, awo amene adzatuluka m’Babulo Wamkulu mapeto asanafike ali ochuluka. Monga chitsimikizo cha zimenezi, ndakhala wokhoza kuperekera lipoti maulendo obwereza oyambira pa 80 kufikira 85 mwezi uliwonse ndi kuchititsa maphunziro Abaibulo 13 kapena 14, mosasamala kanthu za chenicheni chakuti ndapereka ambiri a anthu okondwerera kwa ofalitsa ena.” Mlongo wokhulupirika ameneyu akuwonjezera kuti: “Chifukwa cha mavuto anga athanzi, sindingachite zambiri monga momwe ndikanafunira muutumiki wakumunda, koma aliyense amachita zimene angathe.”
M’Rwanda cha Pakati pa Afirika, mkhalidwe wa Mboni za Yehova nawonso wasintha mwadzidzidzi. Mu April 1992 chikalata chinatulutsidwa chonena kuti potsirizira pake zinali gulu lololedwa mwalamulo. Chikalatacho chinalandiridwa mumlungu umodzimodzi wa Chikumbutso, ndipo ofalitsa 1,526 m’Rwanda anachita chidwi kuwona okwanira 6,228 akumafika pachochitikacho. Kodi abale okhulupirika ameneŵa adzasonyeza chisangalalo chawo ndi chiyamikiro mwa ntchito yowonjezereka m’kulengeza mbiri yabwino? Mwachiwonekere! M’mwezi umodzimudziwo wa April, ofalitsa ampingo anachita maola 27.7 paavereji m’ntchito yofalitsa ndi maulendo obwereza 17, akumachititsa maphunziro Abaibulo 2.4 paavareji. Ndipo pafupifupi 40 peresenti ya iwo anali mumtundu wakutiwakuti wa utumiki wanthaŵi yonse.
Kuvomerezedwa Mwalamulo Kumwera kwa Afirika
Cha Kummwera kwa Afirika, ufulu watsopano unapezedwa m’maiko okongola aŵiri, Mozambique ndi Angola. M’Mozambique kuvomerezedwa mwalamulo kunaperekedwa m’February 1991. Pamene mkhalidwe unazilara kumeneko, Watch Tower Bible and Tract Society inatumiza amishonale m’dzikolo, limene lasakazidwa kwambiri ndi nkhondo yachiweniweni. Amishonalewo anapeza nthaka yachonde. Mabukhu ofotokoza Baibulo—makamaka bukhulo Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza—akufunidwa kwambiri. Mmishonale wina akusimba kukhala akugaŵira mabukhu 50 m’maola osafikira aŵiri ndi theka.
Anthu okondwerera amalabadira mofulumira. Mmishonale wina anapita kukeyala imene inaperekedwa ku Sosaite, ndipo kunachitika kuti mwamunayo anali msilikali. Makambitsirano abwino anakhalapo ndi mwamunayo ndi aŵiri a achibale ake. Paulendo wobwereza, makambitsirano ena opindulitsa anachitika ndi mwamunayo limodzi ndi ena asanu. Pamenepo iwo anavomereza chiitano cha kukafika pankhani yapoyera ndi Phunziro la Nsanja ya Olonda—zonsezo zinachitika m’masiku anayi.
Mu Angola Mbonizo zasangalala ndi ufulu womakulakula umene unathera m’kuzindikiridwa mwalamulo kwa ntchito yawo mu April 1992. Kodi iwo akugwiritsira ntchito motani ufulu wawo wowonjezerekawo? Iwo akukhala ndi phande muutumiki wakumunda! Muli pafupifupi ofalitsa 17,000 mu Angola, ndipo ofalitsa amenewo akuchititsa maphunziro Abaibulo pafupifupi 60,000. Nchiyembekezo chotani nanga cha chiwonjezeko chamtsogolo!
Achichepere Akhala ndi Phande m’Kuchitira Umboni
M’maiko ameneŵa kumene ntchito yolalikira inavomerezedwa mwalamulo posachedwapa, ngakhale achichepere ndi amene sanabatizidwebe akusonyeza chiyamikiro chawo mwantchito yauminisitala. M’Cape Verde Republic, kumene Mboni za Yehova zinavomerezedwa mwalamulo mu November 1990, pamsonkhano wina wachigawo msungwana wina wazaka 17 zakubadwa anaimirira ndi kulankhula poyera za chikhulupiriro chake. Pambuyo pa ubatizo, mlendo wina anawona khamu litakweteza msungwanayo. Mlendoyo anapita kukayamikira msungwanayo namfunsa kuti khamulo linali ayani. “Eya,” anayankha motero msungwanayo, “ameneŵa ndiwo ophunzira Baibulo anga.” Iye anali kuchititsa maphunziro asanu ndi aŵiri, ndipo analipo kumuyamikira pa kubatizidwa kwake. Anali atapereka kale chofunsirira kudzatumikira monga mpainiya wothandiza nayang’ana mtsogolo kuti potsirizira pake adzayeneretsedwe monga mpainiya wokhazikika.
Msungwana wina wazaka khumi zakubadwa mu Angola anafunsidwa ngati anali wofalitsa. Iye anayankha kuti: “Inde.” Kodi anachititsa maphunziro Abaibulo alionse? “Ndithudi.” Angati? “Asanu ndi aŵiri,” ndimo mmene anayankhira wazaka khumi zakubadwa ameneyu.
Timaŵerenga m’bukhu la Machitidwe kuti panthaŵi ina m’zaka za zana loyamba, “mpingo wa m’Yudeya lonse ndi Galileya ndi Samariya unali nawo mtendere, nukhazikika; ndipo unayenda m’kuwopa kwa [Yehova, NW] ndi m’chitonthozo cha mzimu woyera, nuchuluka.” (Machitidwe 9:31) Tikupempherera abale athu mu Afirika, kuti imeneyinso idzakhale nyengo ya mtendere. Tikusangalala nawo pamene akumangiliridwa ndipo tikupempherera mzimu wa Yehova kuti ukhale pa iwo pamene agwiritsira ntchito ufulu wawo kufalitsa mbiri yabwino ndi kuwonjezerekabe.
[Mapu patsamba 24]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Maiko Kumene Mboni za Yehova Zinavomerezedwa Mwalamulo Kapena Kumene Ziletso Zinachotsedwa pa Iwo
1. The Gambia, December 1989
2. Benin, January 1990
3. Cape Verde Republic, November 1990
4. Mozambique, February 1991
5. Ghana, November 1991
6. Ethiopia, November 1991
7. Congo, November 1991
8. Niger, December 1991
9. Togo, December 1991
10. Chad, January 1992
11. Kenya, March 1992
12. Angola, April 1992
13. Rwanda, April 1992
[Chithunzi patsamba 23]
M’Benin wofalitsa Waufumu akuwomba ng’oma yake kuti amveketse mawu a pa Mateyu 24:14
[Chithunzi patsamba 25]
M’maiko ambiri a mu Afirika, Akristu owona akugwiritsira ntchito bwino ufulu wawo wopezedwa chatsopano
[Chithunzi patsamba 26]
Mboni zatsopano zikuchitira chisonyezero kudzipereka kwawo kwa Yehova mwa ubatizo wa m’madzi