Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 10/1 tsamba 24-25
  • Kuŵala Monga Zounikira m’Dziko

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuŵala Monga Zounikira m’Dziko
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Sukulu Yaupainiya m’Central African Republic
Nsanja ya Olonda—1992
w92 10/1 tsamba 24-25

Kuŵala Monga Zounikira m’Dziko

M’DZIKO lino loipitsidwa ndi makhalidwe okhota ndi kululuzika, Akristu owona padziko lonse ayenera kukhala magwero a kuunika. Iwo ayenera kukhala miyuni m’dziko la mdima. (Afilipi 2:15) Zikwi zambiri ziri zofunitsitsa kuchita zimenezi monga apainiya, kapena alaliki anthaŵi yonse. Ochuluka a iwo athera zaka zambiri muutumiki umenewu ndipo afupidwa mwa kuwona anthu a mitundu yonse akumasintha miyoyo yawo kukhala ophunzira owona a Yesu Kristu.​—Mateyu 28:19.

Kuti zilimbikitse apainiya ameneŵa kupitiriza muutumiki wopatulika umenewu ndi kuwongolera maluso awo akuphunzitsa, Mboni za Yehova zalinganiza Sukulu ya Utumiki Waupainiya. Ndiyo kosi ya Baibulo ya masiku khumi yolinganizidwira kuthandiza apainiya m’mbali zitatu: kuyenda ndi Yehova monga otsatira Yesu Kristu; kuchuluka m’chikondi cha gulu lonse la abale; kuŵala monga zounikira m’dziko.

Sukulu Yaupainiya m’Central African Republic

Mu Bangui, likulu la Central African Republic, ophunzira 48 ndi alangizi aŵiri anasonkhana mu August wa 1991. Ophunzirawo anali kudzapatsidwa malangizo ndi malingaliro othandiza a ntchito yawo. Kodi nchiyani chimene chinali chokondweretsa kwambiri ponena za kalasilo ku Bangui?

Choyamba, ophunzira 21 anali akali pasukulu yakudziko. Pamene anali kusukulu, anali okhoza kupanga makonzedwe a kuchita utumiki wa upainiya wokhazikika. Anagwiritsira ntchito miyezi ya matchuthi awo, kutha kwa mlungu, ndi masana kulalikira ndi kuphunzitsa.

Achichepere ameneŵa awona kufunika kwa kutumikira Mlengi wawo tsopano lino. (Mlaliki 12:1; yerekezerani ndi 1 Akorinto 7:29.) Chinthu chapadera chinali chakuti 12 a iwowa anali ndi makolo osakhulupirira. Anali iwo okha m’chowanadi kwawo. Anyamata ena aŵiri achichepere, pachibale, anathamangitsidwa panyumba ndi atate wawo chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Banja lina lachichepere linapereka malo okhala kwa anyamata aŵiri ameneŵa.

Nkhaniyo inali yosiyana ndi ya Michée ndi Sulamithe Kaleb. Onsewo ndiapainiya ndiponso amapita kusukulu, koma makolo awo ndi Mboni za Yehova. Kwenikweni, atate wawo anali wophunzira m’kalasi limodzimodzilo!

Mipingo ya m’Bangui inakhalanso ndi phande m’sukuluyi, koma m’njira yosiyana. Iyo inasamalira zofunika zakuthupi, monga ngati chakudya. Ndalama, ndiponso nkhuku, suga, mpunga, ndi nsima ya chinangwa zinaperekedwa kudyetsa kalasilo.

Timagulu ta ophika tinalinganizidwa ndi mipingo yapafupipo kuti tikonze chakudya chokoma chosavuta kuphika. Central African Republic ngwodziŵika ndi ngunza, chakudya chimene chimakondedwa ndi aliyense. Zofunikira zake? Masamba achinangwa, mafuta a ngole, anyenzi, garlic (adyo) wambiri, chiponde chambiri, ndi kuyembekezera nthaŵi yaitali kuti zipse mokwanira. Kagulu kalikonse kanali ndi njira yakeyake yapadera yophikira chakudyacho. Chinali chabwino koposa; palibe aliyense akanaleka kuchidya.

Kunja kwa Bangui makalasi ena aŵiri anachitidwa, limodzi ku Bouar ndipo lina ku Bambari, akumafikitsa chiwonkhetso cha ophunzira pa 68. Mkati mwa zaka ziŵiri zapitazo, Central African Republic wakhala ndi kuwonjezereka kwa apainiya. Mu January wa 1992 munali apainiya okhazikika 149 ndipo apainiya apadera 17 limodzi ndi apainiya othandiza 78. Zimenezi zachititsa chiwonjezeko cha ntchito m’dziko lonselo chokhala ndi ziŵerengero zapamwamba zatsopano za ofalitsa, maola, maulendo obwereza, ndi maphunziro a Baibulo. Pamene pali antchito ambiri, kututa kumawonjezereka.​—Yesaya 60:21, 22; Mateyu 9:37, 38.

Zithokozo zathu zimke kwa Yehova Mulungu kaamba ka makonzedwe amenewa ndi kugulu lake lapadziko lapansi kaamba ka kulinganiza makalasi ameneŵa. Amathandiza ophunzira ndi alangizi mofanana kuŵala monga zounikira m’dziko lino lamdima.

[Chithunzi patsamba 24]

Ophunzira makumi aŵiri ndi mmodzi a sukulu yaupainiya amene akali kusekondale

[Chithunzi patsamba 25]

Anyamata aŵiri ameneŵa anathamangitsidwa panyumba chifukwa cha chowonadi

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena