Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 6/1 tsamba 27-30
  • Ndinapeza Chowonadi Pambuyo Potuluka m’Ndende ya Buchenwald

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndinapeza Chowonadi Pambuyo Potuluka m’Ndende ya Buchenwald
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kugwidwa Kwanga
  • Ulendo Wopita ku Jeremani
  • Moyo wa Tsiku ndi Tsiku
  • Gulu Losiyana
  • Sitima ya Imfa
  • Njira Yatsopano
  • Yehova Anatipulumutsa ku Ulamuliro Wankhanza
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Kumapeza Chomchitira Yehova Nthaŵi Zonse
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Kulibe Chinthu Chabwino Choposa Choonadi
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Kudalira Mulungu Kunandilimbitsa
    Galamukani!—2002
Nsanja ya Olonda—1992
w92 6/1 tsamba 27-30

Ndinapeza Chowonadi Pambuyo Potuluka m’Ndende ya Buchenwald

NDINAKULIRA ku Grenoble, Falansa, m’ma 1930. Mphunzitsi wanga wa Chijeremani, Mfalansa, anali Mnazi wonkitsa. Kusukulu, iye nthaŵi zonse ankaumirira kuti tsiku lina chinenero cha Chijeremani “chidzakhala chothandiza” kwambiri. Komabe aphunzitsi athu ochuluka, omwe anali asirikali m’Nkhondo Yadziko ya I, anada nkhaŵa ponena za kubuka kwa Chinazi m’Jeremani. Nanenso ndinada nkhaŵa kwambiri pamene kunakhala kowonekeratu kuti nkhondo inali pafupi.

Mu 1940, kuchiyambi kwa Nkhondo Yadziko ya II, ndinataya amalume okondedwa m’kuwomberana mfuti kowopsa kumtsinje wa Somme. Ndinakwiya ndithu koma ndinali wamng’ono kwambiri wosakhoza kuloŵa m’Gulu Lankhondo la Falansa. Komabe, pambuyo pa zaka zitatu, pamene asirikali a Jeremani analoŵerera Falansa, ndinapeza mwaŵi wakugwiritsira ntchito luso langa la kujambulira mapulani Gulu Lachizembera la Falansa. Ndinapambana kujambula masaini ndiponso ndinagwira ntchito yakupanga zokhomera zachinyengo za Jeremani. Ndinakhutira kwambiri ndi kulimbana mwanjirayi ndi magulu a asirikali audani oloŵerera m’dziko lathu kotero kuti malingaliro achikomyunizimu a oyanjana nawo anali osafunika kwenikweni kwa ine panthaŵiyo.

Kugwidwa Kwanga

Pa November 11, 1943, Gulu Lachizembera lakwathu linaitanitsa chisonyezero chokumbukira pangano lothetsera Nkhondo Yadziko ya I. Koma alonda Achifalansa oyenda ndi magalimoto anali atatseka njira yopita kuulalo womkira kuchikumbutso, ndipo anatilimbikitsa kubwerera kunyumba. Mmalomwake gulu lathu linasankha kuguba kupita kuchikumbutso china cha nkhondo mkati mwa tauniyo. Koma tinaiŵala chinthu chimodzi. Chikumbutsocho chinali pafupi kweikweni ndi maofesi a Gestapo.

Gulu lathu linazingidwa mwamsanga ndi asirikali onyamula zida, omwe anatindandalika kukhoma. Pamene asirikaliwo anatichotsako, anapeza timfuti tamthumba tingapo pansi. Popeza kuti palibe anaulula kukhala mwini wake, asirikaliwo anangomasula kokha akazi ndi achichepere azaka 16 zakubadwa ndi ocheperapo. Motero, pausinkhu wa zaka 18, ndinamangidwa, pamodzi ndi akaidi ena okwanira 450. Pambuyo pa masiku angapo, anatisamutsira kundende yogonera pafupi ndi Compiègne, kumpoto kwa Falansa.

Ulendo Wopita ku Jeremani

Pa January 17, 1944, ndinakumana kwa nthaŵi yoyamba​—koma mwatsoka osati kwa nthaŵi yomalizira​—ndi asirikali a Jeremani ovala zisoti zolembedwa mtanda wa swastika kumanzere ndi zilembo zachidule za SS (Schutzstaffel) kulamanja. Anasonkhanitsa akaidi mazanamazana, ndipo tinayenda ndi miyendo kupita kusiteshoni ya Compiègne. Anatiponda chidyali poloŵa m’ngolo za sitima. M’ngolo yomwe ndinali, tinalimo akaidi 125. Kwa masiku atatu ndi mausiku aŵiri, sitinadye kapena kumwa kalikonse. M’maola ochepa okha, ofooka anagwa namapondedwa. Pambuyo pa masiku aŵiri tinafika ku Buchenwald, pafupi ndi Weimar, mkati mwenimweni mwa Jeremani.

Pambuyo powazidwa mankhwala opha tizilombo ndi kumeta tsitsi, ndinapatsidwa nambala 41,101 yondidziŵira monga wa gulu la “Zigaŵenga Zachikomyunizimu.” M’nyengo yakubindikiritsidwa, ndinakumana ndi Michel Riquet, wansembe wa gulu la Dominic, yemwe anakhala wotchuka pambuyo pa nkhondo ndi maulaliki ake mu Notre Dame Cathedral, ku Paris. Pamodzi ndi achichepere ena ausinkhu wanga, tinamfunsa chifukwa chimene Mulungu analolera kuipa koteroko. Iye anayankha kuti: “Muyenera kuvutika kwambiri kuti mukapite kumwamba.”

Moyo wa Tsiku ndi Tsiku

Tonsefe okhala m’misasa 61 tinkauka pafupifupi 4:30 m’maŵa. Tinkatulukira kunja osavala malaya ndipo kaŵirikaŵiri kunali kuzizira kwambiri moti tinkaswa madzi oundana kuti tipeze madzi osamba. Akhale wathanzi kapena wodwala, munthu aliyense anayenera kugonjera. Ndiyeno tinkagaŵiridwa mkate wosuluka​—wolemera magramu okwanira 200 mpaka 300 patsiku, ndi bata yopakako ndi zina zowoneka ngati jamu. Pa 5:30 a.m., aliyense anaitanidwa kuwona ngati alipo. Chinali chochitika chomvetsa chisoni chotani nanga kubereka amene anafa usiku! Fungo lonyansa la utsi wa mitembo yomawotchedwa linatikumbutsa anzathuwo. Tinaipidwa, kutaya mtima, ndi kukulitsa udani, chifukwa tinadziŵa kuti nafenso tikafa mwanjira imeneyo.

Ntchito yanga m’gulu lomanga la BAU II Kommando inaphatikizapo kukumba michera yopanda ntchito. Titangomaliza kukumba mchera wamamita asanu ndi aŵiri tinkaufocheranso kuulinganiza bwinobwino. Tinkayamba kugwira ntchito pa 6:00 a.m., ndi kupuma kwa theka la ola masana, ndi kupitiriza ntchitoyo mpaka 7:00 p.m. Kuitana maina kwamadzulo kunawoneka kukhala kosatha. Nthaŵi iriyonse imene asirikali a Jeremani anaphedwa kwambiri kumalire ogaŵana ndi Russia, kuitanako kunkapitiriza mpaka pakati pa usiku.

Gulu Losiyana

Aliyense yemwe anayesa kuthaŵa mundendemo anadziŵika mosavuta chifukwa tonsefe tinali ndi tsitsi lometedwa mosiyanasiyana. Tsitsi lathu linkametedwa ndi mzera pakati kapena kufupikitsidwa kwambiri pakati pa mutu kapena m’mbali mwake. Ngakhale nditero, akaidi ena anali kumetedwa bwino. Kodi anali ayani? Kapitawo wa msasa wathu anatiyankha mokhutiritsa. Iye anati: “Iwo ndi a Bibelforscher (Ophunzira Baibulo).” Koma ine ndinazizwa kuti: “Kodi Ophunzira Baibulo anali kuchitanji m’ndende yachibalo?” Ndinauzidwa kuti: “Ali muno chifukwa chakuti amalambira Yehova.” Yehova! Imeneyo inali nthaŵi yanga yoyamba kumva dzina la Mulungu.

Mkupita kwa nthaŵi ndinafikira pakudziŵako zochepa ponena za Ophunzira Baibulo. Ambiri anali Ajeremani. Ena mwa iwo anali m’ndende zachibalo kuyambira chapakati pa ma 1930 chifukwa chokana kumvera Hitler. Iwo akanamasulidwa, koma anakana kugonja. Nduna za SS zinawagwiritsira ntchito monga ometa aumwini, ndipo anapatsidwa ntchito zapadera zofuna antchito odalirika, monga maudindo auyang’aniro. Zomwe zinatikopa kwambiri zinali kudekha kwawo, kupanda kwawo udani uliwonse kapena mzimu wakutsutsa ndi kubwezera chilango. Sindinamvetsetse. Mwatsoka, sindinachidziŵe kwambiri Chijeremani kuti ndidzilankhula nawo panthaŵiyo.

Sitima ya Imfa

Pamene magulu ankhondo ogwirizana anayandikirayandikira, akaidi anatumizidwa kundende za mkati mwa dziko, koma zimenezo zinakhala zikumadzala kwadzawoneni. M’maŵa wa pa April 6, 1945, a SS anatitenga ifeyo okwanira 5,000, natikakamiza kuyenda ndi miyendo kupita ku Weimar pamtunda wamakilomita asanu ndi anayi. Amene sanakhoze kuyenda anawomberedwa mfuti pakhosi. Pamene pomalizira tinafika pasiteshoni ya Weimar, tinakwera m’ngolo za sitima zotseguka pamwamba, ndipo sitimayo inanyamuka. Kwa masiku 20, inapitirizabe kuyenda kupyola masiteshoni onse m’Jeremani mpaka kukaloŵa mu Chekosolovakiya.

Tsiku lina m’maŵa, mbali ina ya sitima yathu inagululidwa nuimikidwa pamajiga. Asirikali anatetekera mfuti zawo zachiwaya, kutsegula zitseko za ngolo, ndi kupululutsa akaidi Achirussia omwe anali mkati. Chifukwa? Akaidi khumi ndi aŵiri adapha alonda awo usiku nathaŵa. Ngakhale lerolino ndimachiwonabe m’maganizo chithunzi cha mwaziwo ukudonthera m’njanje kuchokera m’ngolo.

Potsirizira, sitimayo inafika ku Dachau, kumene tinamasulidwa ndi Asirikali Achimereka pambuyo pa masiku aŵiri. Paulendo wonse wamasiku 20, chakudya chokha chomwe tinadya chinali mbatata zingapo zaziŵisi ndi madzi ochepa. Pamene ulendowo unayamba, tinali okwanira 5,000, koma kokha 800 ndife tinapulumuka. Ena ambiri anafa m’masiku otsatira. Ndipo ineyo, ndinakhala pamtembo kwa mtunda wautali wa ulendowo.

Njira Yatsopano

Nditamasulidwa palibe chinawonekera kukhala chanzeru kwa ine koposa kuchirikiza mwachangu chipani cha French Communist Party, popeza kuti ndinayanjana kwambiri ndi ziŵalo zake zambiri​—kuphatikizapo zotchuka​—m’Buchenwald. Ndinakhala mlembi wachiŵiri wa kachigawo kachipani ku Grenoble ndipo ndinalimbikitsidwa kuchita kosi yophunzira zauyang’aniro ku Paris.

Komabe, posapita nthaŵi ndinagwiritsidwa mwala. Pa November 11, 1945, tinaitanidwa kukatenga mbali m’perete ku Paris. Camarade (mnzathu) wotsogoza kagulu kathu analandira ndalama zakutizakuti zopezera malo athu ogona, komabe anawoneka kukhala wosafuna kuzigwiritsira ntchito mmalo mwathu. Tinakakamizika kumukumbutsa za malamulo amakhalidwe abwino a kuwona mtima ndi ubwenzi omwe anayenera kutigwirizanitsa pamodzi. Ndinazindikiranso kuti amuna onse otchuka amene ndinadziŵa analibiretu mankhwala a mavuto a dziko. Ndiponso, kwakukulukulu, anali okana kukhalako kwa Mulungu, koma ine ndinakhulupirira Mulungu.

Pambuyo pake ndinasamukira ku Lyons, kumene ndinapitirizabe kugwira ntchito yolemba mapulani. Mu 1954, Mboni za Yehova ziŵiri zinandichezera, ndipo ndinalembetsa magazini a Galamukani! Pambuyo pa masiku aŵiri, mwamuna wina anadza ndi mmodzi wa akazi omwe anandichezera poyamba. Mwadzidzidzi mkazi wanga ndi ine tinazindikira kuti tonsefe tinali kukonda zinthu zauzimu.

Mkati mwa kukambitsirana komwe kunatsatira, ndinakumbukira a Bibelforscher m’ndende ya Buchenwald omwe anali omamatira zolimba ku chikhulupiriro chawo. Panali panthaŵiyo pamene ndinazindikira kuti a Bibelforscher ndi Mboni za Yehova anali anthu amodzimodzi. Mothandizidwa ndi phunziro Labaibulo, mkazi wanga ndi ine tinatenga kaimidwe kathu kumbali ya Yehova ndipo tinabatizidwa mu April 1955.

Ndimazikumbukira bwino zonse monga ngati zinachitika dzulo. Sindimachita chisoni ndi kuvutika kwanga kwakaleko. Kwandilimbikitsa ndi kundithandiza kuwona kuti maboma a dzikoli alibe zambiri zopereka. Ngakhale kuti chokumana nacho cha munthu chingawathandizeko ena, ndingakhale wokondwa ngati chokumana nacho changa chingathandize achichepere lerolino kuwona chinyengo cha dzikoli ndiyeno kufuna ubwino, ndi makhalidwe olungama m’Chikristu chowona, zomwe Yesu anaphunzitsa.

Lerolino, kuvutika ndi chisalungamo ziri mbali ya moyo wa tsiku ndi tsiku. Mofanana ndi a Bibelforscher m’ndende zachibalo, nanenso ndikuyembekezera dziko labwinopo lirinkudza, m’mene chikondi cha abale ndi chiweruzo cholungama zidzafunga mmalo mwa chiwawa ndi nthanthi zotengetsa maganizo. Pakali pano, ndikutumikira Mulungu ndi Kristu bwino koposa monga mkulu mumpingo Wachikristu malinga ndi mphamvu zanga, pamodzi ndi mkazi wanga, ana, ndi adzukulu. (Salmo 112:7, 8)​—Monga momwe yasimbidwira ndi René Séglat.

[Zithunzi patsamba 28]

Pamwamba: Kuitana maina m’ndende

Kumanzere: Chipata choloŵera m’Buchenwald. Chikwangwanicho chimati: “Aliyense alandire chilango chomuyenerera”

[Zithunzi patsamba 29]

Pamwamba: Kowotchera mitembo m’Buchenwald

Kumanzere: Akaidi khumi mphambu asanu ndi mmodzi pamzera uliwonse wa makama

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena