Zisumbu za mu Indian Ocean Zimva Mbiri Yabwino
ZONDANDAMA mozungulira pang’ono pafupi ndi Madagascar ndipo zotenga malo okwanira makilomita 3.9 miliyoni mbali zonse zinayi mu Indian Ocean yakumadzulo ndizisumbu za Rodrigues, Mauritius, Réunion, Seychelles, Mayotte, ndi Comoros. Ngakhale kuti zisumbu zimenezi zimakuta malo aakulu motero, ukulu wawo wa nthaka uli kokha wamakilomita 7,300 mbali zonse zinayi. Pokhala ndi anthu okwanira 2.3 miliyoni, zili pakati pa zisumbu zokhala ndi anthu ochulukitsitsa padziko lonse.
Chiŵerengero cha anthu chimenechi chimaphatikizapo Mboni za Yehova zokwanira 2,900, zimene zimagwira ntchito mwakhama kulengeza mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu kwa nzika za zisumbuzo. Popeza zimakhala kutali, Mboni zimenezi zimayamikira kwambiri kuchezetsa kwa oyang’anira oyendayenda ndi misonkhano yapachaka yolinganizidwa ndi ofesi yanthambi ya Watch Tower Society ku Vacoas, Mauritius. Pazochitika zimenezi mpamene zimamvetsetsa tanthauzo la mawu a Yesaya 42:10 akuti: ‘Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, ndi matamando ake kuchokera ku malekezero a dziko lapansi; inu amene mutsikira kunyanja, ndi zonse ziri m’menemo, zisumbu ndi okhala mommo.’
Posachedwapa, oimira ofesi yanthambi anapita kuzisumbuzo kukayendera mipingo ndi kuchititsa mpambo wapachaka wa tsiku la msonkhano wapadera, umene unali ndi mutu wakuti “Khalani Oyera m’Makhalidwe Anu Onse,” wozikidwa pa 1 Petro 1:15. Kuti akwaniritse malo aakuluwo apanyanja, maulendowo anali kwakukulukulu apandege—nthaŵi zina anayenda ndi ndege zazikulu zamakono koma kaŵirikaŵiri anayenda ndi ndege zapolopela zocheperapo. Ndiponso zombo ndi mabwato zinagwiritsiridwa ntchito. Tatitsatirani, kuti mukawone mmene zisumbuzo za mu Indian Ocean kutaliko zikumverera mbiri yabwino!
Sitesheni Yoyamba—Rodrigues
Pambuyo pa kuyenda pandege kwa ola limodzi ndi theka kuchokera ku Mauritius, tiwona mtandadza wa mathanthwe a korali. Umachinga thamanda lalikulu lamadzi osaya ozungulira kachisumbu kakang’ono mu Indian Ocean. Pamenepo ndipo pasitesheni yathu yoyamba, chisumbu cha Rodrigues.
Bwalo la ndege nlomangidwa padoko lathanthwe lakorali, lotchedwa Point Coraille. M’dera limeneli thanthwe lakoralilo nlochindikala kwambiri kwakuti akhoza kuchekako njerwa zomangira nyumba. Tikwera basi yaing’ono ndi kudzera mumsewu waung’ono wokhotakhota, wochokera kubwalo la ndege kumka kutauni lalikulu la Port Mathurin. Pamalo ena, tiwona chapatali kutsogolo kwa chisumbuchi mitandadza ya mathanthwe akorali, thamanda lobiriŵira, ndi gombe lamiyala. Popeza kuti nyengo ya mvula inatha posachedwa, mapiri ngokutidwa ndi udzu wobiriŵira, wofeŵa, ndi ng’ombe, nkhosa, ndi mbuzi zikubudula udzuwo.
Tikachitira msonkhano wathu watsiku lapadera pa Nyumba Yaufumu yaing’ono yaudongo yokhala pakati pa Port Mathurin. Ntchito yolalikira mu Rodrigues inayamba mu 1964. Tsopano, pa anthu okwanira 37,000, pali ofalitsa mbiri yabwino okwanira 36. Nkosangalatsa chotani nanga kuwona anthu 53 opezekapo ndi mnyamata wazaka 18 akubatizidwa. Amayi ŵake analandira chowonadi mu 1969, ngakhale kuti iwo sanadziŵe kuŵerenga kapena kulemba, ndipo apitirizabe kutumikira Yehova mosasamala kanthu ndi chitsutso chabanja. Tsopano ana aŵiri a amayiwo ngodzipereka kwa Yehova.
Pambuyo pa msonkhanowo, tikutha mlungu umodzi tikulalikira pachisumbuchi. Tilankhula Chicreole cha kwathu ku Mauritius, pakuti chinenerochi chilankhulidwanso kunoko ku Rodrigues. Tikwera basi, ndiyeno kuyenda pansi kupita kugawo lathu—chigwa chobiriŵira ndi zomera chochokera kumsewu wakumtunda kutsikira kunyanja. Ndimalo ochititsa chidwi chotani nanga owonekera chapatali kutsogoloko—thamanda lamadzi obiriŵira, mtandadza wathanthwe loyera lakorali, ndi nyanja yamchere yamawonekedwe athambo! Pokhala tatsitsimulidwa ndi mpweya wosaipitsidwa, wabwino, ndife okonzekera kupita.
Titenga kankwaso kodzera m’minda ndi kudutsa madambo kuti tifikire tinyumba tambiri m’chigwacho. Tilandiridwa bwino panyumba iliyonse ndipo tilankhula ndi eninyumba za madalitso a Ufumu umene udzadza posachedwapa. Posapita nthaŵi tifika mkati mwenimweni mwa chigwacho, ndipo nthaŵi yopita kunyumba yakwana. Kumeneku kufuna maola ochuluka oyenda ndi kukwezeka mapiri, koma anthu ochereza a kunoko atithandiza—atikwezeka kumbuyo kwa galimoto laling’ono lamtundu wa lole.
Pambuyo pa ulendo wotopetsawo, ndife okondwa kuti tabwerera kumalo abwino ku Nyumba Yabeteli yokongola ku Vacoas. Misonkhano iŵiri yatsiku lapadera inalinganizidwa kuchitikira ku Municipal Hall. Patsiku loyamba, anthu okwanira 760 apezekapo. Iwo achokera kumipingo isanu ndi umodzi mwa mipingo 12 pachisumbuchi. Patsiku lotsatira, tikhala ndi programu imodzimodziyo ndi anthu opezekapo 786 ochokera kumipingo inayo isanu ndi umodzi. Pamapeto a mlungu, anayi atsopano abatizidwa. Pali apainiya apadera 30 ndi apainiya okhazikika 50 amene amakhala ndi phande m’kubweretsa mbiri yabwino kwa nzika za chisumbuchi.
Zisumbu za Seychelles Zakutalizo
Tsopano ndinthaŵi yakuti tikwerenso ndege, kupita kumpoto kwenikweni pamtunda wamakilomita chikwi chimodzi mpambu mazana asanu ndi limodzi kudutsa nyanja yotakata kufika kuchisumbu cha Mahé ku Seychelles, chotchedwa Zil Elwannyen Sesel m’Chicreole, kutanthauza “Zisumbu za Seychelle Zakutali.” Chifukwa chamtunda wautaliwo, ofesi yanthambi imalinganiza maulendo aŵiri okha pachaka. Tsiku la msonkhano wapadera ndi msonkhano wadera zimachitika pamasiku atatu otsatizana m’nyengo yangululu. Msonkhano wachigawo umachitika chakumapeto kwa chaka. Tsopano pokhala ndimkati mwa October, tabwera kuno kumsonkhano wachigawo, umene udzatsatiridwa ndi mlungu wakuyendera mipingo. Kunonso tidzagwiritsira ntchito chinenero chathu cha ku Mauritius, Chicreole.
Abale ochokera kuzisumbu zapafupi za Praslin ndi La Digue afika kale. Nkokondweretsa chotani nanga kukhala ndi nthumwi zoimira maiko 12! Msonkhanowo uchitidwira pa Nyumba Yaufumu, garaji yosinthidwa yaikulu yokhala kumbuyo kwa nyumba ya Mboni. Popeza pali abale asanu ndi mmodzi okha, kuphatikizapo alendo, amene ali oyeneretsedwa kukhala ndi phande m’programuyi, ena akhala ndi mwaŵi wakukamba nkhani zingapo m’masiku anayiwo. Ofalitsa okwanira 81 asangalala kuwona opezekapo 216 patsiku lomalizira la msonkhanowo.
Pamene msonkhanowo utha, tikwera chombo kupita ku Praslin, mtunda wamakilomita 40 kumpoto koma chakum’maŵa kwa Mahé. Chombo chimenechi chautali wamamita 18 nchopangidwa ndi matabwa a mtengo wa tacamahac. Chombo chokongolachi chikhoza kunyamula anthu 50 ndi pafupifupi katundu wolemera matani 36. Pamene tichoka padoko la Mahé ndi kulinga ku Praslin wowonekera patali m’chizimezime, tikumva mphamvu yokankha ya injini yadizilo yothandizidwa ndi matanga obvutira kumilingoti iŵiri.
Pambuyo pa maola aŵiri, tizungulira chitunda chamiyala kuloŵa m’chigawo chokongola chamadzi abata cha Bay St. Anne. Potuluka padoko lalitali, tiwona abale athu akutiyembekezera. Pali ofalitsa 13 pachisumbu chaching’ono chimenechi, ndipo alendo 8 anachokera kumadera ena. Choncho tikondwera kwambiri powona holo yaing’ono yodzala ndi anthu 39 odzamvetsera nkhani yapadera. Ha, ndikuthekera kwabwino chotani nanga kwa chiwonjezeko!
Tidakali kunoko ku Praslin, tiyenera kuchezera Vallée de Mai. Kunoko ndiko kumapezeka mtengo wangole wotchedwa Coco-de-mer, umene umabala zipatso zazikulu zoposa zonse za padziko lapansi, chirichonse cholemera makilo 20. Mumthunzi wozizirira wa nkhalango yamsiphu, tiwona mitengo yangole imeneyi yaing’ono ndi yaikulu yonse. Kabukhu kopatsa alendo kamafotokoza kuti mtengo wautali koposa unali wamsinkhu wamamita 31 pamene unapimidwa mu 1968. Ina ya mitengo imeneyi imayerekezeredwa kukhala ndi zaka 800. Pamapita zaka 25 kuti mtengo umodzi uyambe kubala zipatso ndi zaka 7 kuti zipatsozo zikhwime. Mposadabwitsa kuti brosahayo imachenjeza kuti: “Jambulani zithunzithunzi basi, siyani mapazi okha”!
Panthaŵi ya 7 koloko m’maŵa wotsatira, tikwera bwato kupita kuchisumbu chaching’ono cha La Digue. Mabwato ambiri ngokocheza padoko. Ndiwo choyendera chachikulu pakati pa nzika 2,000 ndi anthu ochokera kunja. Tilandiridwa ndi okwatirana aŵiri a ku Switzerland amene akhala m’zisumbu zimenezi chiyambire 1975. Mmalo mokwera “teksi” yagaleta la ng’ombe, tingolamba ndi gombe lamiyala yamawonekedwe ofiirira yosalalizidwa ndi madzi anyanja ndi mvula. Pambuyo pa kapiniki kakufisula, tipitiriza ndi ulendo wathu kupita kwa anthu okondwerera kudutsa nkhalango yosungira zinyama, kumene mbalame yogwira ntchentche imasungidwako, kumene okondwerera ena amakhala. Anthu khumi ndi atatu asonkhana kuti amve nkhani yokambidwa m’Chicreole. Takumana ndi okwatirana aŵiri amene apanga makonzedwe ofunikira akulembetsa ukwati wawo kotero kuti apite patsogolo mwauzimu. Ndithudi, Yehova akubweretsa zofunika za amitundu ngakhale kuzisumbu zakutali zimenezi.
Tipita ku Réunion
Réunion ndichisumbu chotsungula koposa zonse zimene tikuyendera paulendo uno. Pamene tikuyandikira pafupi ndi doko, tiwona msewu waukulu wanjira zinayi, wodzala ndi magalimoto ochokera kumzinda wake waukulu, Saint-Denis. Nyumba zosanja zazitali zikuta malo pakati pa nyanja ndi phiri. Chisumbu chimenechi chiri ndi anthu 580,000 ndipo chakhala munda wobala zipatso wa ntchito yochitira umboni Ufumu. (Mateyu 9:37, 38) Tsopano muli ofalitsa mbiri yabwino achangu pafupifupi 2,000 m’mipingo 21.
Msonkhano wapadera watsiku limodzi uchitikira m’bwalo lamaseŵera lalikulu lokhala ndi denga. Ndife achimwemwe kuwona anthu opezekapo 3,332, ndipo nkosangalatsa chotani nanga kukhala ndi atsopano 67 akubatizidwa! Pambuyo pakucheza ndi amishonale pachisumbuchi, tipitiriza ndi ulendo wathu kuchisumbu chotsatira.
Mayotte—Chisumbu Chonunkhira
Pambuyo pa ulendo wandege wamaola aŵiri, ndege yathu yokwera anthu 40 iyamba kutera pabwalo la ndege la Pamanzi, limene liri pakachisumbu kolumikizidwa ku Dzaoudzi, likulu la Mayotte, ndi chikweza cha msewu wamakilomita 1.9. Thambo lobiriŵira, mitambo yoyera, mapiri okutidwa bwinobwino ndi zomera zamsiphu, ndi nyanja yonga thambo lopanda kanthu zisanganizana kupereka chithunzithunzi chowoneka ngati paradaiso wamtendere wakumalo otentha. Moyenerera, Mayotte amatchedwa dzina lopeka lakuti Chisumbu Chonunkhira chifukwa cha fungo lonunkhira bwino la mtengo wa ilang-ilang. Madzi otengedwa m’maluŵa ake amatumizidwa ku Falansa kukapangira mafuta onunkhira otchuka padziko lapansi.
Ulendo wopita kumalo aakulu a chisumbucho ndi bwato utenga mphindi 15. Titadya takudya tokhwasula ndi kumwa zoziziritsa kunyumba ya amishonale, tiitanidwa kuphunziro labukhu pamtunda wamakilomita 19 kumbali ina ya chisumbuchi. Zimenezi zaswa chiyembekezo chathu cha ulendo woongola miyendo! Tikwera m’galimoto lamtundu walole lotamanga paliŵiro ladzanimuwone m’timisewu topapatiza. Kukuwonekera kuti tikuphonya pang’ono kugunda anthu, ng’ombe, ndi galimoto zina. Koma wotiyendetsa Wachifalansa azidziŵa bwino njirazi. Mwamsanga, tifika ku Chiconi, kumene tikumana ndi banja limene liri ndi nyumba m’mene phunziro limachitidwira.
Atateyo, amene kale anali Msilamu, atisonyeza ana ake asanu ndi atatu. Mwana wake wamwamuna wamng’ono pa onse, wazaka zinayi, atipatsa moni umene tidziŵa pambuyo pake kuti ngwamwambo. Aika kumbuyo kwa dzanja lake m’chikhato cha dzanja lina ndi kutambasulira kwa ife. Choyamba tiyetsa kugwirana naye chanza, ndiyeno mkazi wanga ayesa kuika pamutu wake manja a mwanayo. Mnyamatayo wamaso aakulu akudikhirira moleza mtima, mosakaikira akudabwa ndi zimene tikuchita. Pomalizira pake tikhoza—tiika manja ake pamutu pake. Tiyamba phunziro ndi opezekapo 14. Tiri mkati mwa phunzirolo, munthu wokondwerera aloŵa nagwirana chanza ndi aliyense. Mwachiwonekere, nawonso ndimwambo wawo.
Paulendo wathu wobwerera kudzera m’madera akumidzi kutada kale, tiwona mileme yaikulu yomwe imadya zipatso ikupita ku mitengo kukafuna chakudya chawo chausiku. Tikumvanso fungo lamphamvu la njale zogwera panjira yokhotakhota ndi fungo labwino la mango, mapapaya, ndi magwaŵa. Ameneŵa ndimalo okhala tinyama tonga achanga, tinyama tating’ono tofanana ndi apusi tankhope monga nkhandwe ndi michira yogwirira yaitali, ndi yopindika. Pamene tikweteza pamwamba pa gomo, tiwona zochititsa chidwi. Mwezi wathunthu wofiirira wangotuluka kumene chakuchigwegwe, ukumachezimitsa madzi abata. Ngakhale woyendetsa galimoto wathu asintha liŵiro namayendetsa pang’onopang’ono kuti aupenye bwino. Paulendo wonse tsopano, tifuna kuwona madziwo titafika pokhotera msewu.
Tsiku lotsatira m’maŵa, tipita kukalalikira ndi amishonale. Choyamba, tichezera mwamuna wachichepere yemwe ndimphunzitsi ndipo amalankhula Chifalansa. Iye wakhala pansi, ndipo ife takhala pakama wake. Phunziro lotsatira tirichitanso ndi mwamuna wachichepere, ndipo atiuza kukhala pamatiresi yake pansi m’kachipinda kake kakang’ono. Posapita nthaŵi, tiyamba kutakataka ndi kutopa ngakhale kuti tayesa kunyalanyaza dzanzi la miyendo yathu ndi thukuta lomwe likuyenda kumsana kwathu. Ndi phokoso la nyimbo zatsopano zotchuka zoimbidwa pawailesi m’nyumba yotsatira, tipeza vuto kusumika maganizo paphunziro lochitidwa m’Chifalansa ndi m’Chimahori.
Ulaliki wathu uthera pa mwamuna wina wachichepere wochokera kuzisumbu zapafupi za Comoro. Iye apepesa chifukwa chosakhoza kulankhula bwino Chifalansa, atenga brosha yake, nakonzekera kuyamba phunziro. Pamene mishonale apitiriza kundifotokozera kanthu kena, mwamunayo adudukira nanena kuti adzaŵerenga ndime. Akutiuza mwaulemu kukhala chete. Anthu onseŵa ndi Asilamu, koma amakondadi zimene akuphunzira m’Baibulo.
Tikudabwa kuwona kuti anyamata ambiri amaphunzira, pamene kuli kwakuti ndiakazi ochepa okha kapena asungwana amene amatero. Tiuzidwa kuti zili choncho chifukwa chamiyambo yakakhalidwe ndi yabanja. Popeza kuti mitala imavomerezedwa ndi chipembedzo ndi anthu onse ndipo aliyense wa akaziwo amadzikhalira m’nyumba yakeyake, ulamuliro wa atate ngwochepa; amayiwo ndiwo ali ndi ulamuliro wonse. Tiuzidwanso kuti malinga ndi mwambo, ana aakazi amakhalabe panyumba ya amayi ŵawo kufikira atakwatiwa. Kumbali ina, ana aamuna amachoka panyumba atatha msinkhu nakamanga banga, kapena nyumba, kapena amakakhala ndi anyamata ena m’banga. M’mikhalidwe imeneyi anyamata ali omasuka kuphunzira ngati afuna, koma ndiasungwana ochepa amene ali ndi ufulu wotero.
Pa Sande tidzakhala ndi tsiku la msonkhano wapadera. Kunja kwacha bwino m’maŵa, koma pofika masana mitambo iyamba kusonkhana, ndipo mwamsanga mvumbi uyamba. Palibe amene awoneka kudera nkhaŵa, pakuti mvulayo ingowaziziritsa basi. Kunonso tipeza chuma chochuluka chauzimu pamene ofalitsa 36 ndi apainiya asangalala powona opezekapo 83 ndi atsopano obatizidwa 3.
Kumasulidwa kwa brosha ya Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! m’chinenero chawo kudzetsa chimwemwe chachikulu. Siiri kokha chofalitsidwa chimodzi chokha cha Watch Tower m’Chimahori komanso ili chofalitsidwa chokha m’chinenerocho. Liri ndi zilembo Zachiluya zolembedwa pansi pa zilembo zanthaŵi zonse. Anthu amaphunzira zilembo Zachiluya kusukulu koma samaphunzira chinenero cha Aluya. Akhoza kutchula mapemphero apamtima m’Chiluya ndi kuŵerenga Koran m’Chiluya; komabe samamva zimene amanena. Pamene akuŵerenga zilembo Zachiluya m’broshayo, akudabwa kuti zikumveka. Chimene akuŵerenga kwenikweni ndichinenero chawo Chimahori cholembedwa m’zilembo Zachiluya zoimira mawu a Chimahori. Nkosangalatsa kuwawona akumwetulira pamene amvetsetsa zimene aŵerenga.
Mabrosha amagaŵiridwa kwa anthu mosavuta. M’mudzi wina wakutali, mwamuna wina atifikira pamene tikulalikira kwa mkazi wina. Ayamba kulankhula mwamphamvu kwa mbale wathu m’Chimahori. Kwa ife mwamunayo awoneka kukhala wotsutsa kwambiri. Mwamunayo apitiriza kulankhula kwakanthaŵi, akuponya manja uku ndi uku. Zitatha izi mbale atilongosolera kuti mwamuna uja anali kudandaula kuti: “Kodi tingakumbukire bwanji zimene mumatiphunzitsa ngati mumatichezera kamodzi pachaka kwatha? Tingakumbukire bwanji? Mudzibwera kaŵirikaŵiri kudzatifotokozera zinthu izi.”
Mawu otsiriza amenewo asonyezanso malingaliro athu. Ndithudi Yehova akusonkhanitsa zofunika za amitundu onse kupyolera mwa mbiri yabwino ya Ufumu. Ngakhale kuti nzika za zisumbuzo nzolekanitsidwa ndi nyanja yamchere yotakatayo, zikuwonjezera mawu awo kumfuu yaikulu yachitamando yomwe ikuperekedwa kwa Mlengi wawo ndi Atate, Yehova Mulungu.—Hagai 2:7.
[Mapu patsamba 21]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
SEYCHELLES
INDIAN OCEAN
COMOROS
MAYOTTE
MADAGASCAR
MAURITIUS
RÉUNION
RODRIGUES
[Chithunzi patsamba 23]
Chitunda chamiyala ku Praslin, Bay St. Anne
[Chithunzi patsamba 24]
“Teksi” yagaleta la ng’ombe ku La Digue, Seychelles
[Chithunzi patsamba 25]
Kulalikira ndi brosha yatsopano ku Mayotte