Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 11/15 tsamba 24-27
  • Mbiri Yabwino Ifika Kumadera Akumidzi a South Africa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mbiri Yabwino Ifika Kumadera Akumidzi a South Africa
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • “Sukulu ya Sande” m’Zululand
  • M’chipalamba Chafumbi Kwambiri
  • Mfumu Ipereka Lamulo!
  • Kuthandiza Ofunafuna Chowonadi Ambiri Mwachimwemwe
  • Zipatso za Ntchitoyo
Nsanja ya Olonda—1991
w91 11/15 tsamba 24-27

Mbiri Yabwino Ifika Kumadera Akumidzi a South Africa

MAGULU okwiya, apolisi oletsa chiwawa, utsi wokhetsa misozi wotchedwa tear gas. M’zaka zaposachedwa, matauni a m’South Africa ndi mizinda akanthidwa ndi chipwirikiti choterocho. Ngakhale madera akumidzi okongola​—kumene yoposa 40 peresenti ya chiŵerengero cha anthu akukhala​—sanapulumuke kusakazidwa ndi chiwawa cha ndale zadziko. Komabe, mkati mwa zonsezi, Mboni za Yehova zapitirizabe kulengeza “Uthenga Wabwino wa mtendere.”​—Aefeso 6:15.

Kwa zaka zambiri Mbonizo zakhala ndi ndawala ya miyezi itatu pachaka yakulalikira makamaka kwa anthu a m’madera akumidzi. Mwachitsanzo, mu 1990 ofalitsa Ufumu oposa 12,000 ochokera m’mipingo 334 anakhala ndi phande m’ndawalayo. Mwachibadwa, pamafunikira kulaka zopinga zambiri kuti afikire anthu akumidziwa okhala momwazikana a kum’mwera kwa Afirika.

Pakati pa zinthu zina, Mbonizo ziyenera kuchita ndi miyambo ndi zinenero zambiri zosiyanasiyana. Ndipo ndiunyinji wa zosiyanasiyana chotani nanga! Mwachitsanzo, pali alimi olankhula Chingelezi ndi olankhula Chiafrikaans, limodzinso ndi Apedi, Asotho, Atsonga, Atswana, Avenda, Axhosa, ndi Azulu. Gulu lirilonse liri ndi mwambo wakewake ndi chinenero. Palinso mitunda yaitali ndi misewu ya majidumajidu. Zonsezi zimafunikira mzimu wodzimana ndi kuwonongedwa kwa nthaŵi yochuluka ndi ndalama. Komabe, Yehova wadalitsa zoyesayesazo molemera. Lekani tikusimbireni pang’ono zovuta ndi zipambano za mbali yapadera imeneyi ya ntchito yolalikira.​—Yerekezerani ndi Malaki 3:10.

“Sukulu ya Sande” m’Zululand

Mkati mwenimweni mwa Zululand motentha pang’ono mumapezeka chigwa chakuya cha mtsinje wa Umvoti. Munthu ataima pamaterezi, akhoza kuwona nyumba Zachizulu zofolera ndi udzu zikundanda mpaka uko. Pa Sande ina mu 1984, ofalitsa Ufumu aŵiri anatsikira m’chigwacho ndi msewu wokhotakhota wafumbi. Ndikotentha ndi kwachinyontho kumeneko kwakuti malowo anapatsidwa dzina lakuti Kwa-Sathane (Malo a Satana)​—chinyengo chowonekeratu cha chiphunzitso chonama cha moto wahelo woikidwa ndi Mdyerekezi!

Ali onyowa ndi thukuta, abalewo anafikira mkazi wotchedwa Doris, yemwe ankachititsa kalasi la sukulu ya Sande. Pambuyo pakumva uthenga wa Ufumu, pompo Doris anaitana Mbonizo kukalankhula kwa gulu lake la achichepere okwanira 40. Chotulukapo? Abalewo anabwerera mlungu wotsatira ndi makope 70 a Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo ogwiritsira ntchito pasukulu yakumaloko. Mkati mwa milungu yoŵerengeka, mkhalidwe wa sukulu ya Sande unasintha kukhala wa gulu la phunziro Labaibulo. Mmalo mwa nyimbo za tchalitchi, nyimbo Zaufumu zinaimbidwa mwanjira ya Chiafirika, ndi mang’ombe achibadwa osangalatsa. Posapita nthaŵi gululo linakula kuposa pa 60. Mbale wina anadzuma kuti: “Chinali chokumana nacho chosangalatsa chotani nanga kukhala ndi phande m’kusintha sukulu ya Sande imeneyi kukhala malo a kulambira kowona!”

M’chipalamba Chafumbi Kwambiri

Chifukwa cha kudziloŵetsa kwa matchalitchi m’chipwirikiti cha ndale zadziko, alimi achiyera ambiri amakhala atcheru kapena okaikira aliyense amene amawafikira ndi uthenga wa Baibulo. Onani lipoti iri loperekedwa ndi gulu la ku Johannesburg limene linayenda makilomita pafupifupi 640 kulalikira mbiri yabwino m’chigawo cha Transvaal.

“Takhala tikuyenda kulinga kumpoto kudutsa m’chipalamba chotambalala kwa pafupifupi maola anayi tsopano. Chizirezire chikuchezima pamsewu wowongoka pansi pa dzuŵa lotentha la mu Afirika. Mwadzidzidzi, msewu wa phula ukutha ndipo kuyamba msewu wafumbi wokumbikakumbika wodzala mayenje. Pomalizira pake, njira yafumbiyo itifikitsa pa famu.

“‘Mwadzuka bwanji, Meneer [Bambo],’ tipereka moni kwa mlimi wojintcha.

“‘Ndadzuka,’ iye ayankha tero mwamphamvu. ‘Kodi ndingakuthandizeni chiyani?’

“Pambuyo podzidziŵikitsa, tifotokoza cholinga cha ulendo wathu. Tilephera kunena kanthu pamene azaza kuti: ‘Dominee [minisitala] wanga anandichenjeza za anthu inu! Nonsenu ndinu a Komyunizimu ndi okana Kristu. Chokani pamalo anga tsopanoli ndisana . . . !’

“Kaimidwe ka mlimiyo kakusonyeza kuti iye akachita chiwawa mphindi iriyonse. Pokhala opanda chochita, tikusankha kuchoka ndi ‘kusansa fumbi m’mapazi athu.’ (Mateyu 10:14) Fumbi nlambiri kwakuti ukhoza kuchita chimenechi m’lingaliro lenileni.

“Pa famu yotsatira, kayankhidwe nkofanana. Ndiyeno tizindikira kuti minisitala wokhala kumeneko wa Dutch Reformed ngwotaganitsidwa kulankhula patelefoni yakumaloko, akuchenjeza ‘nkhosa zake’ ponena za ‘ngozi’ imene yafika m’malowo. Pomalizira pake tikumana ndi mlimi amene, ngakhale kuti iyemwini sali wokondweretsedwa, anena kuti: ‘Inde, mukhoza kulankhula kwa antchito anga.’

“Takhala tikuyembekezera kokha chimenecho. Pafupi ndi mitengo ya wattle pali nyumba zazing’ono zadothi pafupifupi khumi. Tikulingalira kuti maso okaikira akusuzumira kunja kuchokera m’nyumbazo pamene tikuunjika mabuku bwinobwino pa boneti ya galimoto lathu. Mulu wa Mabaibulo, mulu wina wa bukhu la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, mulu wa Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, ndi mabrosha osiyanasiyana akwaniritsa chisonyezerocho. Mmodzi wa anyamata akumaloko athamanga kukauza anthu a m’mudzi za kufika kwathu. Mwamsanga gulu la anthu pafupifupi 30 lisonkhana mozungulira galimoto kuti amve uthengawo.

“Ulaliki wojambulidwa pasadakhale useŵeredwa kwa iwo m’Chitswana. Ha, anthuŵa ali achimwemwe motani nanga kumva m’chinenero chawochawo mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu ndi chiyembekezo cha Paradaiso! Pakukhala kukambitsirana kwachisangalalo pamene mabuku agaŵiridwa. Posapita nthaŵi, zogaŵira zonse zikutha. Mwamuna wina wokalamba apempha kugula tepurekodayo. Tikudzimva osangalala kwambiri pamene chiyamikiro cha mbiri yabwino chikusonyezedwa m’njira zazing’ono zambiri​—kumwetulira kwamanyazi, kukhudza, ndi ‘zikomo’ wofatsa.

“Pa iwo okha, ana apanga mzera wokhotakhota ndi kuimba nyimbo yamwambo yotsazikira. Mwadzidzidzi, misewu yafumbi, yokumbikakumbika ndipo nthaŵi zina kuyankhidwa moipa ziiŵalika. Kwakhala koyenereradi kuyesayesa kulikonse!”

Mfumu Ipereka Lamulo!

Mpingo wina wa ku Soweto unali ndi gawo lakulalikira m’dera la fuko lina pafupi ndi tauni lakum’maŵa la Piet Retief. Mwambo wa kumeneko umafuna kuti mlendo ayenera choyamba kuuza induna (mfumu) ya deralo chimene wayendera. Abalewo anachita malinga ndi makonzedwe amenewo. Ha, zinali zodabwitsa motani nanga pamene mfumuyo inawalandira ndi manja aŵiri ndipo ngakhale kuwapatsa malo ogona m’nyumba mwake! Ndiponso, inalemba kalata yodziŵikitsa ofalitsawo yoisonyeza kukhomo ndi khomo niikapo chidindo chake chalamulo. Kalatayo inati: “Awa ali alaliki a Ufumu wa Mulungu. Alandireni m’nyumba mwanu, ndi kuwamvetsera.”

Chivomerezo chinali chosangalatsa kwakuti Mbonizo zinakonza kukhala ndi nkhani yapoyera yokambidwira m’bwalo la nyumba ya mfumu masana pa Sande imeneyo. “Holo” yapabwaloyo inadzaza anthu, ndipo msonkhanowo unatsegulidwa ndi kutsekedwa ndi nyimbo ndi pemphero. Zokumana nazo zofananazo ndi anthu amalingaliro oyanja zakhala zosangalatsa m’madera ena akumidzi.

Munthu wina woteroyo anali Nathaniel, m’mudzi waung’ono wa Pitsedisulejang m’dera lokanthidwa ndi chilala la kumathero kwa Bophuthatswana. Iye anali wopititsa patsogolo chitaganya wodziloŵetsa m’programu yophunzitsa anthu akumaloko kulima dzinthu mwaluso. Iye ankalota zakutembenuza malo osabala ameneŵa kukhala paradaiso. Koma pamene anaphunzira kuti paradaiso wa padziko lonse akabwera posachedwa, iye anadabwa. Analemba lemba lirilonse limene ofalitsawo anamsonyeza. Nathaniel anagwirizanitsidwa mwamsanga ndi mpingo wapafupi, pamtunda wa makilomita 30.

Kuthandiza Ofunafuna Chowonadi Ambiri Mwachimwemwe

“Yehova anatisonyeza kuti umphaŵi sumaletsa munthu wanjala yauzimu kuphunzira chowonadi,” akutero Monika, mpainiya, kapena wolengeza Ufumu wanthaŵi zonse. Iye anali mbali ya gulu la apainiya amene analalikira ku famu ndi famu m’malo azidikha opanda mitengo a Orange Free State m’chigawo chapakati cha dzikolo. Kodi ndimotani mmene apainiyawo anadzimverera pamene anadzipereka m’kufikitsa mbiri yabwino kwa anthu ameneŵa? “Kodi ndani angaike mtengo pazinthu zimene takumana nazo?” iwo anatero. Ndithudi, apainiyawo anafupidwa kwambiri mwauzimu kaamba ka zoyesayesa zawo.

Ngakhale kusakhoza kuŵerenga sikumaletsa munthu womva njala yauzimu kuphunzira chowonadi Chamalemba. Brosha yokhala ndi zithunzithunzi zokongola ya Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! imalandiridwa bwino kwambiri ndi osadziŵa kuŵerenga kapena okhoza kuŵerenga pang’ono kwambiri. Achichepere ndi okalamba onse amachititsidwa chidwi ndi zithunzithunzi zokopa za Paradaiso. Wantchito wina wa nthaŵi zonse, amene amathandiza kusindikiza zinthu zoterozo ananena kuti: “Brosha imeneyi imathandiza anthu kuwona Paradaiso kukhala weniweni ndipo imakulitsa ulemu wawo wachibadwa ndi mantha ku Baibulo.”

Pachifukwa chimodzimodzicho, Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo lakondedwa kwenikweni. M’dera lakutali la Lebowa la fuko lina, alongo athu auzimu aŵiri anadabwa kupeza kuti mwamuna wokalamba, wowona pang’ono ndi mkazi wake anali ndi kope la bukhu limeneli m’chinenero cha Sepedi. Okwatirana ameneŵa analigwiritsira ntchito monga bukhu lophunzitsira ana akumaloko. Kwenikweni, bukhulo linaphunziridwa kwambiri ndi kuchongedwa kwakuti linali kung’ambika. Ha, iwo anali achimwemwe chotani nanga kupeza kope latsopano!

Chotero nzowona kuti zofalitsidwa Zachikristu chowona zikukwaniritsa chosoŵa chachikulu chakuthandiza awo akumva njala ya chowonadi. Mokondweretsa, mbali yaikulu ya zinthu zonse zosindikizidwa m’zinenero zambiri za kum’mwera kwa Afirika zimafalitsidwa ndi Watch Tower Society. Mu 1990 mokha, mabuku, mabrosha, ndi magazini okwanira 113,529 ofalitsidwa ndi Sosaite anagaŵiridwa m’madera akumidzi a South Africa.

Zipatso za Ntchitoyo

Kodi zokumana nazo zabwino zimenezi ndi kugaŵira mabuku zabala zipatso zokhalitsa m’madera akumidzi a South Africa? Izo zaterodi. Chiyambire 1989 mipingo inayi ndi magulu akutali asanu ndi anayi apangidwa monga chotulukapo chachindunji cha kulengeza mbiri yabwino m’madera akumidzi a South Africa. Apainiya apadera akanthaŵi ndi apainiya okhazikika akupititsa patsogolo yochuluka ya ntchito imeneyi.

Kodi mukumkumbukira Doris ndi sukulu yake ya Sande m’mudzi wa m’chigwa chakutali chija m’Zululand? Lerolino, iye ali Mboni ya Yehova, yodzipereka ndi yobatizidwa. Ndiponso, gulu lokangalika la ofalitsa Ufumu asanu ndi anayi kumeneko likupitabe patsogolo mwauzimu. Atsopano ambiri amafika pamisonkhano yochitidwira m’nyumba ya Doris, ndipo anthu asanu ndi aŵiri kwa amene anachititsa maphunziro Abaibulo anabatizidwa pamsonkhano wachigawo wochitidwira m’Durban mu December 1990.

Zipatso zoterozo zimakondweretsa mitima ya ofalitsa Ufumu mu South Africa. Iwo amakumbukira mosamalitsa mawu a mtumwi Paulo akuti: ‘Chifukwa chake, monga tiri nayo nyengo, tichitire onse chokoma.’ (Agalatiya 6:10) Inde, atumiki a Yehova ali otsimikiza mtima kufikira anthu onse owona mtima, kuphatikizapo awo okhala m’madera akumidzi a ku ‘malekezero ake a dziko.’​—Machitidwe 1:8.

[Mapu/​Zithunzi patsamba 24]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Lebowa

TRANSVAAL

Soweto

Piet Retief

Bophuthatswana

ORANGE FREE STATE

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena