Minda Yayera Kuti Imwetedwe mu Brazil
‘KWEZANI maso anu, nimuyang’ane m’minda, kuti mwayera kale kufikira kumweta. Wakumweta alandira kulipira, nasonkhanitsira chobala ku moyo wosatha.’ (Yohane 4:35, 36) Mawu aulosi amenewo a Yesu Kristu ali owona lerolino m’malo akutali a dziko lalikulu la Brazil la Kum’mwera kwa Amereka.
Kwazaka zingapo Mboni za Yehova m’Brazil zakhala zikusangalala ndi ziwonjezeko zabwino. Mu April 1991, chiŵerengero chapamwamba cha omweta a Ufumu 308,973 anachititsa maphunziro Abaibulo apanyumba 401,574. Pa March 30, 1991, chiwonkhetso cha anthu 897,739 anasonkhana kukumbukira imfa ya Yesu, amene anayamba ntchito yomwetayi.
Mosasamala kanthu za zotulukapo zabwino zoterozo, mbali ya munda idakali kuyembekezera kumwetedwa. Anthu oposa mamiliyoni asanu amakhala m’madera ameneŵa a Brazil kumene ntchito yolalikira ikuchitidwa pang’ono kapena siikuchitidwa konse ndi Mboni za Yehova. Kodi nchiyani chimene chikuchitidwa kufutukulira kumwetako kumadera ameneŵa?
Apainiya Akhala ndi Phande m’Kumweta
Mkati mwa nyengo yaposachedwapa ya miyezi isanu ndi umodzi, ofesi yanthambi ya Watch Tower Society m’Brazil inatumiza olengeza Ufumu anthaŵi zonse—apainiya apadera ogwirizira 100 ndi apainiya okhazikika 97—ku matauni 97, makamaka kumadera a kum’maŵa a dzikolo okhala ndi anthu ochuluka kwambiri. Olengeza Ufumu ochokera m’mipingo yosiyanasiyana nawonso anadzipereka kukagwira ntchito m’madera ameneŵa kwa nyengo yaifupi. Mosasamala kanthu za zopinga zofunika kulakidwa, zotulukapo zakhala zosangalatsa.
Mwachitsanzo, ku São João da Ponte, m’dera la Minas Gerais, apainiya anafikira mphunzitsi wazachipembedzo pasukulu yakumaloko. Atamva uthengawo, iye anaoda makope 50 a bukhu la Your Youth—Getting the Best Out Of It kugulira kalasi yake yakatikizimu. Mphunzitsi winanso anauza apainiya omwe anali kupita kuti: “Simuyenera kupita, popeza kuti mukuchita ntchito yabwino chotere kuno. Ndinu nokha amene mukhoza kulifotokoza momvekera bwino Baibulo.”
Sialiyense anakondweretsedwa ndi ntchito yabwino imeneyi. Mwachitsanzo, talingalirani kalata yomwe inafalitsidwa m’nyuzipepala yakumaloko (Diário de Montes Claros) pansi pamutu wankhani patsamba loyamba wakuti “Wansembe Azengedwa Mlandu Wakusonkhezera Chiwawa ndi Tsankho.” Kalatayo inati: “M’tchalitchi, [wansembeyo] ali ndi chizoloŵezi chakusuliza anthu amene amatsatira timagulu tina tampatuko ndi zipembedzo, ngakhale kuti atsogoleri achipembedzo kuno kwathu samapereka chitsogozo chokwanira Chachikatolika ndi Chachikristu cha Uthenga Wabwino kwa okhulupirika. Pochita Misa, iye anaukira Mboni za Yehova zimene ziri m’tauni, ngakhale kuti izo sizimachitira Akatolika zoipa.” Posasonyeza chidani chotero, wolemba nkhaniyo (katswiri wa maphunziro azaumulungu) anapezekapo pa nkhani Yabaibulo yoperekedwa ndi apainiyawo ndipo anabwera limodzi ndi okondwerera ena. Onsewo anasangalala ndi msonkhanowo.
Abale anayi ochokera ku Fortaleza anakwera ndege kupita ku Chisumbu cha Fernando de Noronha, mtunda wa makilomita 400 kuchokera ku mtunda. Anthu 1,500 okhala ku chisumbucho sanalandirepo umboni wabwino kwa zaka zoposa 15. M’masiku khumi abalewo anagaŵira mabuku 50 ndi magazini ndi mabrosha 245, ndipo anayambitsa maphunziro Abaibulo apanyumba 15. Anthu khumi ndi aŵiri anapezekapo pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu, chomwe chinachitika mkati mwakucheza kwawo. Apainiyawo akhulupirira kuti ndi chithandizo cha Yehova ntchitoyo idzakhazikitsidwa zolimba kumeneko posachedwapa. Abale ena alingalira zakusamukira ku chisumbucho.
Chisonkhezero cha Atsogoleri Achipembedzo Chiyambukira Kumweta
Gulu la alaliki a Ufumu a Mpingo wa Arpoador ku Rio de Janeiro anadzipereka kuthera milungu iŵiri akulalikira m’matauni angapo m’dera la Minas Gerais, pafupifupi mtunda wa makilomita 200. Choŵasangalatsa chinali chakuti anapeza kuti anthu akumaloko ngochereza ndi okoma mtima. Amuna anali ndi ulemu wovula chipewa paliponse pamene Mulungu kapena dzina lake, Yehova, zinatchulidwa. Komabe, chifukwa cha ulemu wawo kaamba ka Mulungu, anthuwo anasonkhezeredwa mosavuta ndi atsogoleri achipembedzo.
M’tauni ina wansembe anauza anthu kusamvetsera kwa Mboni za Yehova kapena kufika pamisonkhano imene zinali kukonzekera kuchita. Iye anandandalitsanso Misa yapadera panthaŵi imodzimodziyo ya msonkhano, ndipo Misayo inachitidwa mofuula pa zokuzira mawu kunja kwa tchalitchi chake. Komabe, mosasamala kanthu za zoyesayesa zake, anthu 29 okhala kumaloko, kuwonjezerapo alendowo anapezekapo pamsonkhanowo.
Tauni yapafupi inali yosiyana kotheratu. Wansembe anauza anthu kumeneko kumvetsera pamene Mboni zinkaŵafikira. Chotulukapo chinali chakuti anthu 168 anapezekapo pamsonkhano woyamba. Pambuyo pake, iye anawauza kupereka chisamaliro ku njira yomwe Mboni za Yehova zimachitira Chikumbutso chifukwa chakuti, “izo zimachita mwa njira yoyenera,” iye anatero. Mkati mwa milungu iŵiri ya ntchito yolalikira Ufumu m’dera limenelo, mabuku 1,014 ndi magazini ndi mabrosha 1,052 anagaŵiridwa.
Zoyesayesa Zomapitirizabe Zinadzetsa Madalitso
Mwezi umodzi pambuyo pake ofalitsa a Ufumu 34 anapitanso kukasamalira maphunziro Abaibulo oyambitsidwa mkati mwa kuchezera koyamba. Mkulu Wachikristu wowatsogolera analemba kuti: “Kunali kosangalatsa kuwona anthu okondwerera akutilandira ndi chiyamiko ndi misozi yachimwemwe m’maso mwawo.” Mlongo wina akukumbukira kuti mkazi wina anamfikira iye ndi Mboni zina m’karesitilanti “akutichonderera, misozi iri m’maso mwake, kuti tipite kukaphunzira naye.” Dona wina anaphunzira katatu mkati mwa mlungu umene Mboni zinali komweko. Nthaŵi iriyonse, iye anakonzekera phunziro lake ndipo ankayembekezera kuphunzira. Donayo ananena kuti adayamba kupemphera kwa Mulungu wowona, Yehova. “Nthaŵi zonse ndakhala ndikuyembekezera chimenechi mumtima mwanga,” anawonjezera motero.
Pambuyo pake, apainiya aŵiri anagaŵiridwa kusamalira okondwerera m’dera limenelo. Mofanana ndi m’zaka za zana loyamba C.E., “omwe anali ndi mitima yowongoka kaamba ka moyo wosatha anakhala akhulupiriri.” (Machitidwe 13:48, NW) Ndipo mofanana ndi mkazi Wachisamariya kwa amene Yesu anachitira umboni pa chitsime cha Yakobo, iwo anayamba kuuza ena zimene anaphunzira. (Yohane 4:5-30) Lerolino apainiya 2 amenewo alinso ndi ena 6 amene akutumikira nawo, ndipo avareji ya anthu 20 amapezeka pamisonkhano mlungu uliwonse.
Posangalatsidwa ndi chipambano cha ntchito yapadera imeneyi, ofalitsa 29 a Mpingo wa Arpoador anapita kukalalikira m’tauni ya Mutum, pafupifupi mtunda wa makilomita 500. “Tinalandiridwa mwapadera zedi,” anatero mkulu wotsogoza gululo. “Anthu ambiri anamvetsera mosamalitsa ndipo mwachidwi kwambiri kwakuti maphunziro Abaibulo 170 anayambitsidwa, ndipo tikulingalira kuti ambiri a iwo adzapitirizabe.” M’milungu iŵiri, ofalitsawo analalikira avareji ya maola 90 aliyense ndi kugaŵira anthu pafupifupi mabuku 1,100. Chiŵerengero chapamwamba cha anthu 181 anapezekapo pa nkhani zapoyera zoperekedwa ndi abalewo.
Miyezi ingapo pambuyo pake, mpingo unachita lendi nyumba yabwino mkati mwa tauni ya Mutum yogwiritsira ntchito monga Nyumba Yaufumu ndi nyumba ya apainiya. Lipoti loyamba lotumizidwa ku Sosaite ndi alongo achipainiya aŵiri ogaŵiridwa kumeneko linasimba izi m’mbali yake: “Pokhala kuti maphunziro ambiri ayambitsidwa, tikufuna apainiya owonjezereka. Ngakhale ndi chithandizo cha abale ochokera ku Rio de Janeiro pamwezi, ntchito njaikuludi. Asanu ndi anayi mwa eninyumba khumi amene timalankhula nawo amatipempha kubwererako. Tifunikiranso chithandizo kutsogoza misonkhano.” Mpainiya wina wagwirizana nawo tsopano.
Miyoyo Isinthidwa
Kuwona chowonadi chikuzika mizu ndi kubala zipatso zabwino kwakhala kopereka chilimbikitso kwabasi. Munthu wina wokondwerera analemba kuti: “Kupeza chidziŵitso chimenechi cha Baibulo nchinthu chabwino koposa chimene chinandichitikira. Moyo wanga wasinthidwa kukhala wabwinopo, ndipo sindifunikiranso kumwa mankhwala ogoneka tulo. . . . Yehova akufupenitu kaamba ka zonse zimene mwandichitira.”
Munthu wina ananena kuti: “Ndimadabwa zedi mmene Yehova watsegulira maso anga. Ngakhale kuti ndinaferedwa agogo anga aakazi mlungu uno, ndiri nchiyembekezo tsopano chakuŵawonanso. Ndikufuna kubatizidwa, koma choyamba ndifuna kukonzekera bwino lomwe. Yehova akudalitsenitu kaamba ka kubwera kuno kudzatisonyeza njira yopapatiza yotsogolera ku moyo wamuyaya.” Munthu winanso anati: “Ndifuna kuti mudziŵe kuti ndinaleka kusuta mwezi umodzi wapitawo. Ndiri wosangalala ndi magazini amene munanditumizira. Anali ndi zinthu zabwino zambiri zomwe zandithandiza kutero.” Ndithudi, kumweta kumapereka zifukwa zambiri zokhalira wachimwemwe.
Komabe, madalitso oterowo sanadze popanda kulimbana. Mwachitsanzo, pamene dona wina ndi mwana wake wamkazi anayamba kuphunzira, wansembe wakumaloko anaŵachenjeza kuti ngati akapita ku misonkhano ya Mboni, iye akaŵachotsa m’tchalitchi. Akunyalanyaza chiwopsezo chimenecho, iwo anapita ku misonkhano. Pamenepo anadedwa ndi mabwenzi awo akale, ena a iwo ananena kuti anachita misala chifukwa chakuti dzina “lakuti Yehova” silimapezeka m’Baibulo Lachikatolika. Popeza kuti donayo sanathe kulipeza dzina la Yehova m’Baibulo lake Lachikatolika, anaitanira anansi ake kumchezera patsiku la kuphunzira ndi apainiyawo. Mkazi wina anabwera ndi matembenuzidwe a Paulinas a Baibulo lake Lachikatolika. Pamene iye anaŵerenga dzina la Mulungu m’mawu amtsinde pa Eksodo 6:3, analandira phunziro Labaibulo m’nyumba yake.
Khalani ndi Phande Mokwanira m’Kumweta
Kodi kutumikira m’gawo losagwiridwa ntchito kaŵirikaŵiri kunakhala ndi chiyambukiro chotani pa antchitowo? Wofalitsa Waufumu wina anati: “Ntchito imeneyi inalimbikitsa chikhulupiriro chathu ndi unansi wathu ndi Yehova ndikutithandiza kubwereramo m’zinthu zathu zofunika koposa.” Wofalitsa wina ananena kuti: “Nyengo ija yamasiku 14 inawonjezera chikondi changa kaamba ka abale, omwe amatumikira monga banja limodzi lokhala ndi cholinga chimodzi: kufunafuna ofatsa owonjezereka. Inandipangitsa kukonda moposerapo aja omwe kaŵirikaŵiri amalandira uthenga wathu ali ndi misozi m’maso mwawo, kusonyeza ludzu lenileni la chowonadi. Ndipo koposa zonse, ndinachimva chikondi cha Yehova potipatsa mwaŵi wakumtumikira.”
Mkulu yemwe anakhala ndi phande m’kulalikira m’gawo losagwiridwa ntchito kaŵirikaŵiri anasonyeza kusiyana pakati pa moyo kumeneko ndi m’mizinda yaikulu. Iye anati: “Ndimangolingalira mmene moyo wa abale ambiri ukhoza kulemeretsedwera mwakusamukira ku malo akutali. Kunoko kulibiretu chiwawa. Moyo m’matauni aang’ono ndi achikatikati ngwotitheketsa osati kokha kukhala ndi moyo ndi ndalama zochepa komanso kukhala ndi mayanjano owonjezereka ndi abale athu ndikuthera nthaŵi yowonjezereka m’zinthu zauzimu. Kodi abale oleka ntchito, achichepere okhala ndi mathayo ochepa abanja, kapena abale amene ntchito yawo imaŵalola kusamuka angalandire mwaŵi wapadera umenewu ndi kudzetsa chimwemwe kwa iwo eni, kwa Yehova, ndi kwa anansi awo?”
Lipoti limeneli lonena za gawo losagwiridwa ntchito kaŵirikaŵiri m’Brazil limatsimikizira kuti minda yayera kaamba ka kumweta. M’zaka ziŵiri zokha, ntchito m’munda umenewu yatulukapo mipingo yatsopano 191 ndi magulu akutali. Zochuluka zikuyembekezeredwabe, koma Yehova ndithudi adzapitirizabe kuikapo dalitso lake pamene ofalitsa Ufumu ochuluka atengamo mbali m’kumweta kobala zipatso. Kodi inuyo mukhoza kukhalamo ndi phande lokulira?
[Mapu/Chithunzi patsamba 25]
Mboni zachimwemwe za ku Rio de Janeiro zikhala ndi phande m’kumweta
[Mapu]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
BRAZIL
[Chithunzi patsamba 26]
Kuchitira umboni m’malo akumidzi ku Minas Gerais