Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 3/15 tsamba 26-28
  • Kulengeza Mbiri Yabwino mu “Mzinda Wachipolynesia” wa ku New Zealand

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulengeza Mbiri Yabwino mu “Mzinda Wachipolynesia” wa ku New Zealand
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Anthu a ku Samoa Apita Patsogolo
  • Chivomerezo cha ku Niue
  • Zofalitsidwa za Chinenero Chachipolynesia
  • Kusangalala pa Gome Limodzi Lauzimu
Nsanja ya Olonda—1991
w91 3/15 tsamba 26-28

Kulengeza Mbiri Yabwino mu “Mzinda Wachipolynesia” wa ku New Zealand

“MZINDA Wachipolynesia Waukulu Koposa Padziko.” Umo ndimmene ena atchela Auckland likulu la New Zealand. Kodi nchifukwa ninji? Osati kokha chifukwa chakuti ndilo kwawo kwa Apolynesia a ku New Zealand, Amaori, komanso chifukwa chakuti zikwi makumi ambiri za Apolynesia ena zikukhala kumeneko. M’zaka zaposachedwapa, iwo asamuka kuchokera ku Western Samoa, Cook Islands, Tonga, Niue, ndi zilumba zina za Pacific. Eya, tsopano muli Amaori a ku Cook Island ochuluka m’New Zealand kuposa gulu lawo lenilenilo lokhala m’Cook Island! Mofananamo, nzika za ku Niue m’Auckland ziposa mokulira chiŵerengero cha zimene zimakhala m’Niue.

Ngakhale kuti okhala m’zilumba za Pacific ameneŵa asamukira ku Auckland kwakukulukulu kaamba ka zifukwa zachuma, iwo alinso ndi zosoŵa zina zoti zikhutiritsidwe. Chofunika koposa kwa anthu okondadi Baibulo ameneŵa ndicho kusoŵa kwawo kwauzimu. (Mateyu 5:3, NW) Pozindikira ichi, Mboni za Yehova m’New Zealand zapanga kuyesayesa kwakukulu kulengeza “mbiri yabwino ya ufumu” pakati pa okhala m’zilumba ameneŵa. (Mateyu 24:14, NW) Kodi chachitidwa nchiyani ponena za chimenechi, ndipo kodi okhala m’zilumbawo avomerezera motani?

Anthu a ku Samoa Apita Patsogolo

Ndemanga yoperekedwa ndi mishonale m’Samoa ikutiuza kanthu kena konena za mmene okhala m’zilumbawo amawonera zinthu zauzimu. “Mutakumana ndi munthu kwanthaŵi yoyamba m’New Zealand, nchachizoloŵezi kufunsa za ntchito yake yakuthupi,” iye akufotokoza motero. “Mu Samoa funso loyamba kufunsidwa kaŵirikaŵiri limakhudza chipembedzo chomwe wina agwirizana nacho.” Chotero, sizodabwitsa kuti mipingo iŵiri ya Mboni za Yehova yolankhula Chisamoa m’Auckland ikukula mofulumira kuposa mpingo wina uliwonse wachikatikati m’New Zealand.

Mpingo woyambirira wa Chisamoa m’Auckland unakhazikitsidwa mu 1977. Chifukwa cha kufutukuka koperekedwa ndi Mulungu, mpingo wachiŵiri unapangidwa zaka zisanu ndi ziŵiri pambuyo pake. (Yerekezerani ndi 1 Akorinto 3:6.) M’mipingo iŵiri imeneyi, muli chiwonkhetso cha olengeza Ufumu 154, 12 a ameneŵa ngokangalika muuminisitala wanthaŵi zonse. Pafupifupi Sande iriyonse, anthu oposa 275 amapezekapo pa misonkhano yozikidwa pa Baibulo pa Nyumba ya Ufumu.

Abale ndi alongo Achisamoa amatenga chikhulupiriro chawo mosamalitsa, monga kwasonyezedwa ndi changu ndi kutsimikiza mtima kumene iwo amasonyeza m’ntchito yawo yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira. (Mateyu 28:19, 20) Ichi chingawonedwe kuchokera ku chokumana nacho chotsatirachi cha mlongo wa Chisamoa:

Muuminisitala wa kunyumba ndi nyumba, mlongoyu anakumana ndi mkazi yemwe anatsutsa zipembedzo zonse kukhala zonyenga ndipo anatseka chitseko. Ali wodabwa ndi wokhumudwa, mlongoyo analingalira zochita. ‘Sindingamsiye akuganiza kuti Mboni za Yehova nzonyenga,’ iye analingalira motero. Chotero iye anasankha kusiya kakalata. “Ndinafotokoza mwachidule maziko Amalemba a ntchito yanga ndi kupempha ngati angandipatse nthaŵi yomfotokozera chiyembekezo chimene Baibulo limapereka. Ndinaphatikizamonso nambala yanga ya foni.”

Ndiyeno mlongoyo anapitirizabe ndi uminisitala wake, akumafikira nyumba zina. Pamene anafika pa nyumba yachinayi m’khwalalamo, anapatsidwa uthenga wapatelefoni wakuti abwerere kukawonana ndi mkazi uja yemwe mwaukali adatseka chitseko poyambirira. “Mkaziyo anapepesa kaamba ka kuyankha kwake koyambirira,” mlongoyo akusimba motero, “ndipo anasonyeza chiyamikiro kaamba ka kakalata komwe ndinasiya. Kukambitsirana kobala zipatso kunatsatirapo, ndipo phunziro Labaibulo lapanyumba linakhazikitsidwa.”

Nkosangalatsanso kuwona mzimu wodzikhutula waumishonale wosonyezedwa ndi zina za Mboni za Chisamoa. Mbale wina ndi banja lake anasamuka kuchoka ku Auckland kupita ku Wellington mu 1981 kukathandiza kagulu kogwira ntchito pakati pa anthu Achisamoa kumeneko. Kuchokera kukagulu ka ofalitsa Ufumu okwanira 11 pa nthaŵiyo, kwapangidwa mpingo wa ofalitsa 47. “Mphotho zinaposadi nsembe,” anatero mbaleyo. Posachedwapa, iye ndi banja lake anayankha ‘chiitano cha ku Makedoniya’ ndipo abwerera ku Western Samoa. (Machitidwe 16:9, 10) Enanso abwerera ku malo awo komwe ankakhala ndipo atenga ntchito ya upainiya wapadera, umishonale, kapena utumiki wa pa Beteli.

Chivomerezo cha ku Niue

Ntchito yolalikira ikupitanso patsogolo pakati pa anthu a ku Niue m’Auckland. Woyang’anira woyendayenda akusimba kuti: “Muuminisitala wa kunyumba ndi nyumba, nkwachizoloŵezi kuitanidwira m’nyumba. Baibulo la banja kaŵirikaŵiri limakhala pafupi, ndipo kumalingaliridwa kukhala chinthu chachibadwa kukambitsirana za ilo.”

Tsopano pali mpingo wa Chiniue wokangalika m’Auckland. Mkati mwa kuchezetsa kwa woyang’anira woyendayenda chaka chatha, ofalitsa Ufumu okwanira 76 ogwirizana nawo anali okhoza kulandira anthu 127 ku nkhani ya Baibulo yapoyera pa Sande. Ndipo pali mzimu wabwino pakati pa abale ndi alongo.

“Kuchezetsaku kumawonedwa kukhala mlungu wapadera wa chilimbikitso kwa onse,” akunena motero woyang’anira woyendayendayo. “Chakudya chirichonse nchochitika champingo. Ndipo izi ndinthaŵi zoperekera zakudya zokondeka za Chiniue zonga ngati takihi (chakudya chosanganizana ndi mapapaya, taros [ndiwo zamizu za kumalo otentha], ndi mafuta a ngole okulungidwa m’masamba anthochi), pitako (mkate wopangidwa kuchokera ku taros, nthochi, ndi chinangwa), ndi punu povi (nyama yang’ombe yokonzedweratu ndi yokoleretsedwa), nthaŵi zina moseka imatchedwa nthuli yanyama ya anthu a m’zilumba.”

Zofalitsidwa za Chinenero Chachipolynesia

Kuti ikhutiritse zosoŵa zauzimu za anthu ochuluka Achipolynesia m’Auckland ndi kwina kulikonse, Watch Tower Society yalinganiza kutulutsa zofalitsidwa Zabaibulo zosiyanasiyana m’zinenero Zachipolynesia. Mwachitsanzo, Nsanja ya Olonda ya Chirarotongan, kapena Chimaori cha ku Cook Island imafalitsidwa kaŵiri pamwezi. Nsanja ya Olonda ya Chiniue yotulutsidwa kamodzi pamwezi nayonso imalandiridwa bwino lomwe. Kugaŵiridwa kwa makope aŵiri a Nsanja ya Olonda Achirarotongan ndi Chiniue tsopano kuli pafupifupi makope 1,000 iriyonse, ndipo makope 900 Achisamoa akugaŵiridwa m’New Zealand.

Kuwonjezera pa Nsanja ya Olonda, mabuku angapo ndi mabrosha alipo m’zinenero zosiyanasiyana za Chipolynesia. Bukhu la Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya, lofalitsidwa m’Chiniue mu 1989, ndilo chofalitsidwa choyambirira m’chinenerocho lopereka kumvetsetsa kwa ziphunzitso zamaziko za Baibulo. Logwira mtima mwapadera m’munda wa Chimaori cha ku Cook Island (Chirarotongan) ndilo bukhu la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi m’chinenerocho. Kwakukulukulu maphunziro Abaibulo apanyumba onse akutsogozedwa mothandizidwa ndi bukhulo. “Cholikhalira umboni wakukhala kwake chiŵiya chogwira mtima chothandizira kuphunzitsa,” akufotokoza motero mkulu wina, “ndicho chikondwerero chimene ophunzira amayamba nacho kupezeka pamisonkhano yampingo.”

Kuwonjezera pakugaŵira kwawo kwamasiku onse zofalitsidwa zimenezi kwa kunyumba ndi nyumba, anthu a Yehova amagaŵira mabuku ochulukira muumboni umene ungatchedwe wa pa msika wapabwalo. Chifukwa cha kukula kofulumira kwa chiŵerengero cha anthu Achipolynesia m’Auckland m’zaka zaposachedwapa, misika yaikulu yokhala ndi masitolo apakanthaŵi ogulitsirapo zakudya za ku Pacific Island ndi zopangapanga yachuluka. Anthu ambiri ofika ku 25,000 angabwere ku msika woterowo pa Loŵeruka m’maŵa. Zikumagwiritsira ntchito mwanzeru mwaŵi umenewu, Mboni zimapita ku misika imeneyi ndi kulankhula kwa eni masitolo ndi ogula ponena za Ufumu wa Mulungu.

Kupyolera muutumiki wawo, Mboni za Yehova zakhoza kufesa mbewu za Ufumu zochuluka ndi kugaŵira mabuku Abaibulo m’ziŵerengero zazikulu kwa anthu Achipolynesia. Ofesi ya nthambi ya Watch Tower Society ikusimba kuti mkati mwa chaka chautumiki cha 1990, mabuku achinenero cha Chipolynesia okwanira 23,928 anatumizidwa kuchokera ku fakitale.

Kusangalala pa Gome Limodzi Lauzimu

Pokhala zozindikira kusoŵa kwawo kwauzimu, Mboni za Chipolynesia zimaika chisamaliro choyamba pa kumapezeka pamisonkhano Yachikristu yamlungu ndi mlungu ku Nyumba za Ufumu, limodzinso ndi pamisonkhano yadera ndi yachigawo. (Ahebri 10:23-25) Pa Msonkhano Wachigawo wa “Chilungamo Chaumulungu” umene unachitidwira m’Auckland m’December 1988, panakhala magawo osiyanasiyana mu Chisamoa, Chiniue, ndi mu Chimaori cha ku Cook Island. Mfundo yaikulu ya programu ya Chisamoa inali drama Yabaibulo yoyeseredwa bwino kwambiri ndi yochititsa nthumanzi. Mboni za Chiniue ndi za ku Cook Island zokhala ku Auckland zinasonyeza kuchereza kwawo Kwachikristu mwa kutumikira monga ochereza achisomo kwa alendo ochokera ku zilumba za kwawo. Msonkhanowu unakhaladi nthaŵi ya phwando ndi kusangalala pa gome lauzimu la Yehova. Pa Msonkhano wa “Chinenero Choyera” wa mu 1990 m’Auckland, chiŵerengero chapamwamba cha anthu 503 anapezekapo pa magawo a Chisamoa.

Chivomerezo chabwino ku uthenga wa Ufumu chiri umboni wowonekera bwino wakuti anthu a ku zilumba za Chipolynesia za South Pacific akhala ‘akuyembekezera lamulo la Yehova.’ (Yerekezerani ndi Yesaya 42:4, 12.) Nawonso mwachimwemwe amakhala ndi phande m’kulengeza mbiri yabwino mu “mzinda Wachipolynesia” wa ku New Zealand.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena