Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 3/1 tsamba 14
  • ‘Nkhosa Zimva Mawu Ake’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Nkhosa Zimva Mawu Ake’
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Iye Anamva Potsirizira Pake
  • Pemphero la Mkazi Wopembedza Liyankhidwa
  • Amene Angatitonthoze
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Mbusa Wachikondi
    Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • M’busa Wabwino Komanso Makola Awiri a Nkhosa
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Ndimasangalala Kuti Ndine M’busa
    Galamukani!—2011
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 3/1 tsamba 14

Lipoti la Olengeza Ufumu

‘Nkhosa Zimva Mawu Ake’

◻ YESU anati: ‘Nkhosa zimva mawu [a mbusa]; ndipo aitana nkhosa za iye yekha maina awo, nazitsogolera kunja.’ (Yohane 10:3) Iye anawonjezera kuti: “Ndizindikira zanga, ndi zanga zindizindikira Ine.” (Yohane 10:14) Anthu onga nkhosa amamva mawu a Yesu pamene alankhula kwa iwo kupyolera m’Baibulo. Onani mmene anthu aŵiri owona mtima a ku Italiya anatsatirira njirayi.

Iye Anamva Potsirizira Pake

◻ Alberto akulemba motere: “Ndinali wazaka 16 pamene ndinayamba kusuta mbanje ndikumwa LSD, ndipo pamene ndinafika zaka 18 ndinayamba kugwiritsira ntchito heroin. Kuti ndisasoŵe mankhwala ogodomalitsawo, ndinkachita chirichonse chimene ndinaganizira. Ndinkaba, ndinkagulitsa mankhwala ogodomalitsa, ndinkachita uphyuta, ndinagulitsa katundu wanga yense. Ndinalephereratu kuleka. Matchuthi akutali, kukhala nyengo zazitali kumudzi, kapena kudziloŵetsa m’ndale zadziko ndi magulu ofunitsitsa kuthetsa chisalungamo​—palibe nchimodzi chomwe cha izi chinathandiza. Ndinayesa ukwati, koma pambuyo pa nthaŵi yochepa ndinabwereranso pamene ndinayambira. Ngakhale kubadwa kwa mwana wamkazi sikunandiletse kugwiritsira ntchito mankhwala ogodomalitsa. Kwenikweni, zinthu zinaipirabe, popeza kuti tsopano ndinafunikira ndalama zowonjezereka. Kenaka mkazi wanga anandisiya, ndipo m’zaka ziŵiri zokhala ndekha, ndinamuwona kaŵiri kokha mwana wanga wamkazi. Ndinkakhala wothaŵathaŵa kuzemba ogulitsa mankhwala ogodomalitsa omwe ndinali nawo ngongole, ndipo nthaŵi zambiri ndinavutika ndi kusungulumwa.

“Ndiyeno ndinakumbukira bukhu limene Mboni za Yehova zinandipatsa zaka zingapo kalelo. Ndinali nalobe ndipo ndinayamba kuliŵerenga pamodzi ndi Baibulo. Mwanjirayi ndinadziŵa Mulungu wowona, Yehova, ndipo ndinapemphera kwa iye kaamba ka thandizo. Pamene ndinkagwiritsira ntchito pang’onopang’ono zimene ndinaziphunzira, kusungulumwa kwanga kunachepekera. Ndinapeza ntchito, ndipo ndi thandizo la Yehova ndinabwezeretsa banja langa pamodzi. Ndinapita ku Nyumba Yaufumu, ndipo kumeneko ndinakazindikira kuti Mboni za Yehova ziri ndi chowonadi. Titagwirizananso, mkazi wanga ndi ine tinaphunzira Baibulo ndi Mboni ndipo potsirizira pake tinabatizidwa. Tsopano, nkosangalatsa chotani nanga kugaŵana chiyembekezo chathu ndi ena monga apainiya okhazikika!”

Pemphero la Mkazi Wopembedza Liyankhidwa

◻ Mkazi wina akusimba motere: “Mu 1958, ndinali wokangalika m’machitachita atchalitchi, makamaka m’maulendo amwambo wachipembedzo opita ku Malo Opatulika a Namwali Mariya wa Chikondi Chaumulungu m’Roma. M’kupita kwa nthaŵi ndinakhala bwenzi lapamtima la kadinala yemwe anali nduna yoimira tchalitchi m’Roma, ndipo ndinakhala ndi makambitsirano amseri ambiri ndi Papa Paul VI ndi Papa John Paul II. Pambuyo pa zaka 25 zakulinganiza maulendo amwambo wachipembedzo, ndinalandira dipuloma ya mfupo. Komabe, m’kupita kwanthaŵi chikhulupiriro changa monga Mkatolika wamphamphu chinayamba kufooka. Ndinawona kuba, uphyuta, tsankho, ndi kuyendetsa zinthu kokaikitsa. Ndinayamba kuwona tchalitchi ndi malingaliro osiyanasiyana pamene ndinazindikira kuti lamulo la Mulungu linkaponderezedwa kaŵirikaŵiri. Zinthu zoterozo zinandivutitsa maganizo, ndipo ndinapempha Mulungu kundithandiza chifukwa chakuti ndinkataya chikhulupiriro changa. Ndinkalira kaŵirikaŵiri.

“Kenaka, zaka zinayi zapitazo, mwana wanga wamwamuna anandibweretsera makope a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! omwe anawatenga kwa Mboni za Yehova. Magaziniwo anali osangalatsa kwambiri kwakuti ndinampempha kunditengera enanso. Mwamsanga pambuyo pa zimenezo ndinapeza Nyumba Yaufumu ya Mboni za Yehova ndipo ndinasiya kalata pakhomo yopempha kuti wina andichezere. Mbonizo zinabwera pambuyo pa masiko anayi. Ndinayamba phunziro Labaibulo ndikupita patsogolo kufika paubatizo. Tsopano ndine wotsimikiza kuti potsirizira pake ndachipeza chimene ndakhala ndikuchifunafuna nthaŵi zonse​—chowonadi!”

Anthuŵa anamva mawu a Mbusa Wabwino, Yesu Kristu, ndipo ‘chowonadi chinawamasula.’​—Yohane 8:32.

[Mawu a Chithunzi patsamba 14]

Garo Nalbandian

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena