Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 11/15 tsamba 3-4
  • Kodi Amphaŵi Angathe Kukhala Owona Mtima?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Amphaŵi Angathe Kukhala Owona Mtima?
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Nkhani Yofanana
  • “Ndine Wazaka Zisanu ndi Ziŵiri”
    Galamukani!—1999
  • Akapolo a Umphaŵi
    Galamukani!—1998
  • Kupeza Njira Yothetseratu Umphaŵi
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Posachedwapa, Sikudzakhalanso Mmphaŵi!
    Nsanja ya Olonda—1995
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 11/15 tsamba 3-4

Kodi Amphaŵi Angathe Kukhala Owona Mtima?

Amelia adali wamasiku 29 okha akubadwa pamene agogo ake anampereka kwa dokotala. Amayi wa Amelia analephera kuwupanga ulendowo, popeza kuti adali wodwala panyumba ndi ana ena anayi.

Bambo adapita kwinakwake kukafunafuna ntchito. Dokotala anampima mwanayo. Padali zizindikiro zakuti adali ndi matenda omwe amadza ndi kusadya chakudya chokwanira, chomwe sichiri chachilendo Kumadzulo kwa Afirika. Koma vuto lalikulu linali matenda a “cellulitis.” Chifuŵa chochepa cha Amelia chinali choyambukiridwa phaphapha ndi matenda.

Pamene dokotala anawapatsa agogowo kapepala kolembedwapo mankhwala, iwo anafunsa kuti: “Kodi mankhwalawa adzagulidwa ndi ndalama zingati?” “Madola anayi kapena asanu,” iye anawayankha motero.

Agogowo anadandaula mong’ung’udza. Iwo analibe ngakhale ndimadola aŵiri omwe ofunikira utumiki wa dokotalayo. “Kalanga ine tidzaipeza kuti ndalama yochulukayi!” iwo anadzuma motero.

“Mudzafunikira kukaifunafuna kwinakwake,” anaumirirabe tero dokotalayo. “Pemphapemphani mabwenzi ndi achibale anu. Ngati inuyo simudzachiritsa matenda oyambukirawa, iwo adzafalikira ku mitsempha yamwazi, ndipo khandali lidzafa.”

Mwakugwira apa ndi apo banja la Amelia linaipeza ndalamayo, ndipo mwanayo anakhalapobe kufikira m’mwezi wake wachiŵiri. Komabe, mamiliyoni ambiri m’maiko otukuka kumene kuzungulira padziko lonse sangazikongole ndalama kwa mabwenzi ndi achibale. Ndipo kuyembekezera kuti chuma chidzawongokera ndiko loto.

The State of the World’s Children Report 1989 yolembedwa ndi UNICEF (United Nations Children’s Fund) inalengeza motere: “Pambuyo pa zaka khumi za kupita patsogolo kokhazikika kwa chuma, madera aakulu adziko akubwereranso muumphaŵi.” Mu Afirika ndi Latini Amereka, avereji ya malipiro inatsika ndi 10 mpaka 25 peresenti m’ma 1980. Ndipo mkati mwa zaka zoŵerengeka zapitazo, 37 a maiko aumphaŵi kwenikweni, ndalama zawo zowonongeredwa paumoyo zatsika ndi 50 peresenti.

Kodi ichi chikutanthauzanji kwa mamiliyoni omwe akukhala muumphaŵi? Kwa ambiri, chikutanthauza kuti iwo sangagule zakudya zofunikira kapena mankhwala. Chotero, ana awo, anzawo amuukwati, kapena makolo awo angayang’anizane ndi imfa, pokhapo atatembenukira kunjira yopezera ndalama imene akuilingalira kukhala yowatsegukira​—mwakuba! Inde, umphaŵi ungatanthauze kulimbana ndi kupanikizika kowawa kwa makhalidwe uku: kuba kodi kapena imfa? kunama kodi kapena kufa ndi njala? kulipira ziphuphu kodi kapena kumanidwa zinthu?

Kumadzulo kwa Afirika kuli mwambi uwu: “Komwe mumangirira ng’ombe, komweko nkomwe idzadya udzu.” Kuwufotokoza m’mawu ena, anthu adzadyerera mkhalidwe uliwonse umene udzawatheketsa kudzilemeretsa okha. Kaŵirikaŵiri kwambiri, anthu amene ali muulamuliro m’maiko kuzungulira dziko lonse lapansi amagwiritsira ntchito maudindo awo kulandira ziphuphu, kuzembetsa ndalama, kapena kuba. ‘Dzithandizeni nokha mwaŵi utakugwerani,’ ndi mmene amalingalira. ‘Mwaŵi umenewo sungadzakugwereninso pambuyo pake.’ Pamene mkhalidwe wachuma wa maiko otukuka kumene ukuipiraipira, amphaŵi angatembenukire mowonjezerekawonjezereka ku lingaliro lakuti kuwona mtima sindiko kungakhale lamulo labwino kwa amphaŵi.

Baibulo limati: “Musabe.” (Eksodo 20:15) Koma ngati waumphaŵi sangathe kukhaladi wowona mtima, kodi kugwira ntchito kwa malamulo abwino Abaibulo kumakaikiridwa? Kodi malamulo a Mulungu ngosapindulitsa, osazindikira zosoŵa zenizeni za anthu? Zokumana nazo za Akristu zikwi zambiri m’maiko otukuka kumene zikupereka yankho lodabwitsa kumafunso amenewa.

[Mawu Otsindika patsamba 4]

“Komwe mumangirira ng’ombe, komweko nkomwe idzadya udzu”

[Chithunzi patsamba 4]

Amphaŵi ali pakati pa anthu omwe amavutika kwambiri kugwira ntchito m’maiko otukuka kumene

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena