Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?
Ian Boyne, mlembi wachipembedzo wa The Sunday Gleaner, ya ku Jamaica, West Indies, anafotokoza za broshuwa yaposachedwapa yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova, akumati mwapang’ono:
“Mboni ziyenera kupatsidwa ‘A’ kaamba ka kabukhuka kamene, ngakhale kuti nkolembedwa mopepuka kwakuti wachichepere angakaŵerenge, iko kadzazidwa ndi mfundo—mosakuza mawu ndi mkamwa—ndi mawu ogwidwa kuchokera kwa akatswiri otchuka ndi magwero. . . . Bukhuli la Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu? nchida kwa Mboni ndipo tsopano palibe katswiri wa Utatu—kapena katswiri wa aŵiri—yemwe ali ndi chisungiko. Kabukhuka nkodzala ndi mawu ogwidwa ambirimbiri kuchokera ku magwero a mu mbiri ndi a maphunziro a zaumulungu kusonyeza kuti chiphunzitso cha Utatu sichinatengedwe kuchokera m’Baibulo. Iko kamagwira mawu bukhu lalikulu la Encyclopedia of Religion kukhala likunena kuti, ‘Akatswiri a zaumulungu amavomerezana kuti Chipangano Chatsopano nachonso chiribe chiphunzitso chotsimikizirika cha Utatu.’”
Boyne anatinso: “Nkovuta kwenikweni kwa mlembi wachipembedzoyu kuwona mmene ziŵalo wamba za tchalitchi—kapena zapamwamba—zingayankhire mikangano yodzetsedwa ndi yovuta yobweretsedwa ndi Mboni motsutsana ndi lingaliro lakuti Yesu ali Mulungu.”
Ngati mukufuna kulandira kope ya broshuwayi, chonde dzazani ndi kutumiza kapepala kotsatiraka.
Ndingakonde kulandira broshuwa yamasamba 32 yakuti Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu? (Kunja kwa Zambia, lemberani nthambi ya Watch Tower yakwanuko kaamba ka chidziŵitso. Onani tsamba 2.)
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
Musée du Louvre, Paris
Museo Egizio, Turin
Musée des Beaux-Arts de Troyes
Museo Bardini, Florence
Musée du Louvre, Paris