Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 8/1 tsamba 31
  • “Mankhwala Olelera Mwana Wachimwemwe ndi Wachipambano”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Mankhwala Olelera Mwana Wachimwemwe ndi Wachipambano”
  • Nsanja ya Olonda​—1990
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 8/1 tsamba 31

“Mankhwala Olelera Mwana Wachimwemwe ndi Wachipambano”

PANSI pamutuwu, magazine a Medical Aspects of Human Sexuality anafalitsa nkhani mu imene Dr. Irene Jakab, profesa wa pa yunivesiti ya maganizo, anandandalitsa chimene analingalira kuti chinali choyenerera ngati mwana adati aleredwe kukhala mkulu wachipambano. Pakati pa zinthu zolowetsedwamo za “mankhwala” ake panali kufunika kwa makolo kukonda mwana wawo, kumtsogolera ku chimene chiri chabwino ndi choipa, ndi kumphunzitsa kupanga zosankha. Iye analingalira kuti “mankhwala” amenewa sayeneradi kuphatikizapo kukhala ndi mtima wapachala kwa makolo, ungwiro wopambanitsa, kuda nkhaŵa kopambanitsa, kapena kulekerera.

“Mankhwala” a Dr. Jakab ngabwinodi atagwiritsiridwa ntchito. Ndithudi, zaka zikwi zambiri zapitazo, Baibulo linapereka uphungu wofananawo kwa makolo. (Onani, mwachitsanzo, Miyambo 4:1; 13:24; 22:6; Akolose 3:21.) Komabe, Baibulo limaphatikizapo chinachake chimene Profesa Jakab anasiya: kufunika kwenikweni kwa kuphunzitsa ana kukonda Mlengi wawo ndi kuzoloŵerana ndi Mawu ake. Mtumwi Paulo analemba motere: ‘Atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha [Yehova, NW].’​—Aefeso 6:4; Deuteronomo 6:4-7.

Popanda kuphunzitsa koteroko, ana angakule bwino popanda nangula wa makhalidwe abwino. Chotulukapo chingakhale chatsoka m’dziko lachisembwere ndi loipitsidwa ili.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena