Chidziŵitso pa Nyuzi
“Nsanganizo Yaupandu Koposa”
Milandu yobweretsedwa kukhoti ndi odwala otenga matenda oopsa kupyolera mwakupoperedwa mwazi yayambitsa nkhaŵa yatsopano kumalo osungira mwazi ambiri. Podzafika pakati pa 1989 kwanenedwa kuti milandu yoposa 300 inazengedwa kukhoti motsutsana ndi eni malo osungira mwazi mu United States. Gilbert Clark, mtsogoleri wamkulu wa American Association of Blood Banks, anavomereza kuti “anthu amafuna mwazi wotetezereka kotheratu kumatenda,” komatu iye anavomerezanso kuti sikungatsimikiziridwe.
Mofananamo, Parade Magazine ikusimba kuti katswiri wina wamwazi Dr. Charles Huggins akuvomereza kuti mwazi “uyenera kulingaliridwa kukhala wosatetezereka mosapeweka.” Iye akulongosola mwazi kukhala “nsanganizo yaupandu koposa imene timagwiritsira ntchito monga mankhwala.” Kuyambira kuchiyambi kwa 1989 chiŵerengero cha nthenda zopatsirana zopezedwa m’malo osungira mwazi chakwera kufika ku zisanu (HTLV-I, yogwirizanitsidwa ndi T-selo Lukemiya ya akulu, chindoko, kutupa chiŵindi B, Edzi [AIDS], ndi kutupa chiŵindi C). Komabe, mogwirizana ndi katswiri wa American Red Cross, S. Gerald Sandler, “kukuwoneka kuti m’kupita kwanthaŵi tidzatulukira matenda ena achilendo ofalikira mwakupoperedwa mwazi.” Mosasamala kanthu za kuthekera kwake kwaupandu kwakukulu, pafupifupi mamiliyoni anayi a Amereka Akumpoto akuyembekezeredwa kulandira kupoperedwa mwazi mkati mwa 1990. Mogwirizana ndi mkonzi wa nyuzipepala W. Gifford-Jones, vuto nlakuti “kusiyapo Mboni za Yehova zokha, odwala ambiri samalankhula konse za kuthekera kwakupoperedwa mwazi.”
Kwazaka makumi ambiri Mboni za Yehova mokhulupirika ‘zasala mwazi’ wa mtundu uliwonse monga momwe Mawu a Mulungu amalamulirira pa Machitidwe 15:28, 29; 21:25. Chitetezo chimene zachipeza ku matenda akupha opatsirana mwakupoperedwa mwazi chikuperekadi chitsanzo chakuti kumvera kwawo malamulo a Yehova Mulungu nkolondola.
Kuzimiririka Mosadziŵika?
Kadinala Joachim Meisner, mwamuna wokaikiridwa pamene anaikidwa kukhala akibishopu watsopano February wapitawu, m’Cologne, Jeremani, posachedwapa ananena kuti nkhaŵa yake yaikulu koposa njakuti tsiku lina tchalitchi “chikazimiririka—ndipo mwinamwake kutha mosadziŵa chitaganya.” Mogwirizana ndi nyuzipepala Yachijeremani Rheinische Post, Meisner adaati: “Moyo wanga ukupsinjika kuti chitaganya chikuwona tchalitchi kukhala chosanunka kanthu.” Chifukwa chothekera, iye akutero, nchakuti “timalankhula zochuluka ponena za dziko lapansi koma zochepa ponena za kumwamba, zochuluka kwambiri ponena za nthaŵi ino koma zochepa kwambiri ponena za umuyaya.”
Mwakupalana chibwenzi ndi magulu a ndale zadziko ndi a zamalonda mmalo mwakukhulupirira m’mphamvu yakumwamba kuthetsa mavuto adziko, zipembedzo za Chikristu Chadziko zanamiziradi kudzinenera kwawo kukhala zoimira zabwino za Mulungu. Izi zidzakhala ndi zotulukapo zoopsa. Mogwirizana ndi Baibulo, zipembedzo zonyenga zonse zidzazimiririka mwamsanga—chochitika chimene chidzawonedwa ndi “mafumu a dziko” ndi “ochita malonda a m’dziko,” amene adzalira chifukwa cha chochitika chimenechi. Chifukwa chake, okonda chilungamo afunikira kulabadira mawu awa: “Tulukani m’menemo [m’chipembedzo chonyenga] . . . ; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake.”—Chivumbulutso 18:4, 9, 11.
Chimaliziro Chayandikira
“Kuphedwa ndi Boma” ndimo mmene manyuzipepala ena amalongosolera kupha kwambanda kochitidwa ndi maboma kapena magulu otetezeredwa ndi iwo. Kwenikweni, mu 1988, akutero wolankhulira Amnesty International wotchedwa Gerry O’Connel, “panali kuwonjezereka kwa kuswa malamulo a ufulu, kumene kwapitirizabe mu 1989.” Ndiyeno akuwonjezera kuti: “Kupha anthu moswa malamulo ovomerezedwa kulikonse kwafikira mlingo wapamwamba kuposa ndi kaleronse.”
Mogwirizana ndi lipoti lapachaka la Amnesty, ziŵerengerozo zikuziziritsa m’nkhongono: Mkati mwa 1988 pakati pa anthu okwanira 50,000 ndi 100,000 m’maiko 29 aphedwa pamanja a Boma. Mwa amenewa munali ana, anthu okalamba, ndi akazi, amene upandu wawo unali kokha kukhala ziwalo za zipani zina zandale zadziko kapena mafuko aang’ono kapena kaamba kokhala m’malo amene zipani zotsutsana zimakanganira. Okhala ndi liwongo lakupha kumeneku amaphatikizapo magulu aboma akupha ambanda, opandukira boma, ogulitsa anamgoneka, ndi magulu ena ochita chiwawa chokhala ndi zolinga zandale zadziko. “Kaŵirikaŵiri Boma lenileniro limabisala kumbuyo kwa magulu onyamula zida kuphera adani kapena anthu osafunidwa,” ikutero La Repubblica.
Motero, pali chifukwa chabwino kuti, Mawu owuziridwa a Yehova akuyerekezera boma la anthu ndi “chirombo.” (Chivumbulutso 13:2) Komabe, nkhalwe yosonkhezeredwa ndi ndale zadziko yoteroyo siidzakhala kosatha. Monga momwe Salmo 92:7 limanenera kuti: “Pophuka oipa ngati msipu, ndi popindula ochita zopanda pake; chitero kuti adzawonongeke kosatha.” Ufumu wakumwamba wa Mulungu m’manja mwa Kristu Yesu, “Kalonga wa Mtendere,” udzachita zimenezi.—Yesaya 9:6; Danieli 2:44.