Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 5/15 tsamba 20-23
  • Chikristu Chowona Chikuwongolera Moyo m’Sweden

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chikristu Chowona Chikuwongolera Moyo m’Sweden
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Chidziŵitso cha Baibulo Chimathandiza!
  • Chiyambukiro Chamafunde
  • Kuchitira Umboni Pasukulu
  • Kumenyera Ufulu Wachipembedzo
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 5/15 tsamba 20-23

Chikristu Chowona Chikuwongolera Moyo m’Sweden

SWEDEN amagaŵira anthu ake umodzi wa miyezo yokhalira moyo yapamwamba koposa m’dziko. Kuwonjezera pa zakudya zochuluka ndi malo omangapo nyumba, magalimoto, mabwato oseŵerera, mawailesi akanema, ndi makompyuta aumwini, nzika za Sweden zimasangalala ndi chisamaliro cha kupatsidwa pafupipafupi mankhwala aulere, penishoni ya ukalamba ndi ya kupunduka, kulandira ndalama ngati muli ndi ana, ndi mautumiki ena ochirikizidwa ndi boma.

Chotero inu mungaganize kuti mwinamwake palibe munthu amene angafunikire kuwongolera mkhalidwe wa moyo m’dziko loterolo. Komabe, pamapindu onse a chuma chake chakuthupi, Sweden ali ndi mavuto ake: chisudzulo, uchidakwa, kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala, upandu, ndi kudzipha. Chipembedzo, chomwe chingayembekezeredwe kupereka chisonkhezero champhamvu cha makhalidwe abwino, nchoferatu m’Sweden. Zoposa 90 peresenti za nzika zadzikolo nza Tchalitchi cha Boma cha Lutheran, koma 2.1 peresenti okha ndiwo amene amapita ku maulaliki ake mokhazikika. Wansembe wina akuti: “Tchalitchi chiri mumkhalidwe wa kuleka kugwira ntchito. . . . Mphamvu yake yofunika yataika ndipo chadzilekanitsa chokha ndi zosoŵa za anthu.”

Komabe, kulephera kwa tchalitchi kuwongolera moyo mu Sweden, sikumatanthauza kulephera kwa Chikristu chowona mpang’ono pomwe. Mboni za Yehova zokwanira 22,000 m’mipingo 331 zikupeza chipambano m’kuthandiza anthu kugwiritsira ntchito miyezo ya Baibulo kuubwino wawo. Ntchito imeneyi siinachitidwe popanda kuwonedwa.

“Tiyenera kusirira Mboni za Yehova kaamba ka changu chawo chakutuluka ndi uthenga wawo!” akutero mphunzitsi wina wachipembedzo m’nyuzipepala ya m’dzikomo ya Pentekoste Dagen (Tsiku). Nkhaniyo ikuwonjezera kuti: “Mboni za Yehova zapanga kagulu kamene kakopa chiŵerengero chachikulu cha ziŵalo zatsopano chaka chirichonse ndipo kali ndi khamu lalikulu la achichepere . . . Tiyenera kuphunzira kwa Mboni za Yehova!”

Ndithudi, awo ofunitsitsadi kuphunzira kwa Mboni za Yehova adzatulukira chinthu chinachake. Kodi chimenecho nchiyani? Mmene chowonadi cha Baibulo chingawongolerere mofulumira mkhalidwe wa miyoyo yawo.

Chidziŵitso cha Baibulo Chimathandiza!

Tangolingalirani kalata imene ofesi ya nthambi ya kumeneko ya Watch Tower Society inalandira kuchokera kwa nakubala wina wachichepere wosakwatiwa. Iye analemba kuti: “Ndikufuna kusonyeza kuthokoza kwanga kaamba ka moyo wabwino umene ndakhala ndikusangalala nawo chiyambire pamene ndinayamba kuphunzira ndi Mboni za Yehova. Ndiri ndi nyumba yopanda utsi wa fodya. Ndayamba kuzindikira kufunika kwa kuthera nthaŵi yowonjezereka ndi mwana wanga wamkazi. Mkhalidwe wanga wa zachuma wawongokera, ngakhale kuti ndikadalandirabe malipiro apamwezi ofananawo. Ndiri ndi mavuto ochepa pogona. Ndirinso ndi mabwenzi enieni osangalala nawo. Inde, sindikanasinthanitsa njira yanga yatsopano ya moyo ndi yomwe ndinali nayo poyamba.”

Chitsanzo china chikuphatikizapo nkhani yachisudzulo​—yofala kwambiri mu Sweden. Komabe, Baibulo linathandiza okwatirana otchedwa Arne ndi Ketie. Iwo anali okwatirana kwa zaka 13 ndipo anali ndi ana aŵiri pamene kusamvana kwawo kunawapangitsa kusudzulana. Iwo anadana.

Arne, yemwe anasamuka kukakhala yekha, anawonana ndi Mboni za Yehova ndipo anayamba kuphunzira Baibulo. Iye anasangalala kwambiri ndi zimene anaphunzira kotero kuti tsiku lina anathamangira kwa Ketie ndi kuyesa kumkakamiza iye ndi anawo kuti nawonso aphunzire! Pamene mkaziyo anakana, iye anamkankhira kukhoma naati: “Phunzira, apo phuluzi n’dzakupha!” Ketie anaitana Mboni za Yehova ndi kudandaula, kuti: “Kodi Yehova ameneyo ndi Mulungu wankhalwe wotani?”

Ketie anauzidwa moleza mtima kuti Yehova ndi Mulungu wachikondi amene samakakamiza aliyense. Iye anachita chidwi nafuna kuphunzira zochuluka. Pamene Arne anapeza chidziŵitso chowonjezereka cha malamulo a Mulungu amakhalidwe abwino, iye anazilala nayambanso kulankhulana bwino ndi Ketie. Iwo anawonana mokhazikika pamisonkhano m’Nyumba Yaufumu. Chotulukapo chake? Pamene aŵiri onsewo anakhala Mboni zobatizidwa, anakwatirananso! Iwo akhala okwatirana kwa zaka zisanu ndi zitatu, ndipo Arne akutumikira monga mkulu mumpingo. “Ukwati wathu sunakhalepo wabwino kwambiri kuposa mmene uliri tsopano,” iwo akutero. “Tiri nzambiri zothokozera Yehova.”

Chowonadi cha Baibulo chikuthandizanso achichepere kuwongolera mkhalidwe wa miyoyo yawo. Mnyamata wina wotchedwa David akukumbukira kuti: “Makolo anga anali osudzudzulana, ndipo chirichonse chinawonekera kukhala chisakuyenda bwino m’moyo wanga. Sindinadere nkhaŵa ndi chirichonse. Kaŵirikaŵiri ndinkajomba kusukulu ndipo sindinali kuchita homuweki iriyonse m’zaka zitatu zomalizira. Nthaŵi zina ndinapeza kuti kunali kosayenerera kukhala ndi moyo. Ndinkavala masanza amajini ndi nsapato zakalekale. Tsitsi langa linali lotalika kwambiri kumbuyo. Ndinayesa masitayelo osiyanasiyana a moyo, monga ngati mpanki woimba ndi wachiwawa ndi mpanki wokonda zachifwamba. Ndinkasuta ndi kumwa ndipo ndinaphatikizidwa muupandu.

“Mu 1986 mmodzi wa Mboni za Yehova anandifikira. ‘Chimodzi cha zipembedzo zonyenga zija,’ ndinaganiza motero. ‘Lekani ndimufunse mafunso amene sadzatha kuŵayankha.’ Mondidabwitsa, iye anawayankha. Ndinapita pa amodzi a maphunziro ake a Baibulo ndikupeza kuti iye anali ndi yankho lotsimikizirika pafupifupi la funso lirilonse​—kotero kuti panalibetu chokaikiritsa m’chowonadi. Ndinafika pa msonkhano waukulu ndipo ndinadabwa kuwona anthu audongo kumeneko, ndi aubwenzi amenewo. Ndinayamba kufika pamisonkhano ya Mboni za Yehova ndipo ndinadabwa pamene ambiri anadza ndi kundipatsa moni wa pamanja. Ha ndiumodzi wotani nanga pakati pa anthu amenewa!”

Chaka chimodzi ndi theka pambuyo pake, David anabatizidwa monga mmodzi wa Mboni za Yehova. Achibale ake, mabwenzi ake akale, aphunzitsi, ndi ena sanakhoze konse kukhulupirira kuti mnyamata wovala mwaudongo ndi wopesa tsitsi bwinoyu anali David amene iwo anadziŵa poyambirira.

Chiyambukiro Chamafunde

Kulalikira kukhomo ndi khomo m’Sweden kungakhale kolefula nthaŵi zina. Mswede amatetezera mwachangu ufulu wake wakufuna kukhala yekha. Atamva kugogoda pakhomo, iye angasuzumire pachibowo chosuzumilira, ndipo zitseko zambiri zimakhala zotsekedwa kwa Mboni za Yehova. Koma izo sizimalefulidwa. Mbonizo zimadziŵa kuti angelo angafufuze anthu owongoka mtima. (Chivumbulutso 14:6; yerekezerani ndi Mateyu 13:41.) Chowonadi chitangoloŵa m’moyo wa munthu woteroyo, kaŵirikaŵiri chimafalikira​—mofanana ndi mafunde pamadzi​—kwa achibale ndi mabwenzi.

Mkazi wina m’Stockholm akukumbukira nthaŵi ina pamene anali khale pathebulo ya m’kitchini yake akumalira chifukwa cha mavuto amoyo wake . “Ndinalibe chochita,” anatero. “Mwadzidzidzi, ndinayamba kupemphera kuti: ‘Mulungu, ndikufuna kulankhula nanu ponena za moyo.’ Belu linalira pakhomo. Kudzera pachibowo chosuzumilira, ndinawona mwamuna wovala bwino, motero ndinatsegula chitseko. Iye anati anafuna kugaŵana nane mfundo zolimbikitsa kuchokera m’Mawu a Mulungu. Iye anali mmodzi wa Mboni za Yehova. Ndinafunsa ngati anali atafikira anthu ena pachipinda chosanja cha nyumba yangayo. ‘Ayi,’ iye anatero, ‘ndimamka kunyumba kuchokera kuphunziro la Baibulo pamene ndinaganiza za kulalikira pang’ono. Zangochitika kuti ndayambira pano.’ Ndinadabwa chifukwa chakuti ndinali kukhala pachipinda chosanja chachiŵiri pamwambapo. Ndinakonda zimene anandisonyeza.”

Mwamsanga mkazi ameneyu anayamba kuphunzira Baibulo. Motenthedwa maganizo, iye anayamba kugaŵana zimene anaphunzira ndi achibale ndi mabwenzi ake. Iye anagaŵira Mabaibulo 28 ndi mabukhu 96. Chotulukapo chake? Mwamuna wake, aŵiri a alongo ake, mwana wamkazi ndi mwana wamwamuna wa mbale wake, mlamu wake, atate wake ndi amake, mwana wamwamuna wopeza wa mwamuna wake, wapantchito mnzake, ndi wogwira naye ntchito wa mwamuna wake limodzi ndi mkazi wake mwamsanga anali kuphunzira Baibulo ndi kukonzekera ubatizo. Kufikira pano, anthu 13 akhala ndi mwaŵi wa kuwongolera njira ya moyo wawo kupyolera mu ulendo umodzi pakhomolo wochitidwa ndi mmodzi wa Mboni za Yehova. Mkaziyu akuti: “Kuchita mogwirizana ndi chifuniro cha Yehova kwachita zabwino zambiri m’miyoyo yathu kwakuti tiyenera kumthokoza titagwada m’pemphero tsiku lirilonse!”

Kuchitira Umboni Pasukulu

Mu Sweden muli mavuto aakulu ofunikira kuperekedwa kwa chilango m’masukulu ambiri. Koma Mboni zachichepere zikutsimikizira kukhala chisonkhezero chabwino mwa kugaŵana chowonadi cha Baibulo ndi aphunzitsi ndi apasukulu anzawo. Mwachitsanzo, Jorgen wachichepere anawauza poyera aphunzitsi ake ndi anzake amkalasi kuti anali mmodzi wa Mboni za Yehova. Iye analemekezedwa kaamba ka kukhala kwake wosabisa mawu ndi makhalidwe abwino. Nthaŵi zonse Jorgen anayankha modekha ngakhale mafunso okwiyitsa ndi kusonyeza ku Baibulo. Ichi chinapangitsa chikhomerezo chachikulu pa anzake amkalasimo. Jorgen akusimba motere:

“Chaka chimodzi pambuyo pa kumaliza sukulu, ndinakumana ndi Peter, yemwe anali mnzanga wamkalasi. Pambuyo pa kukambirana, ndinayamba kuchita naye phunziro la Baibulo. Popeza kuti amake anali otsutsa, tinaphunzirira kugombe. Peter anabatizidwa mu March 1988. Amake anawona kuti mwana wawo anasintha kukhala wabwino kwambiri, motero nawonso anayamba kuphunzira. Patapita kanthaŵi, iwo anabatizidwa.

“Mzanga winanso wamkalasi, Torbjorn, anayamba kuphunzira Baibulo. Amake anateronso. Nawonso tsopano ngobatizidwa.” Onse pamodzi, anzake a Jorgen anayi amkalasi anayamba kuphunzira Baibulo, ndipo wachisanu wasonyeza kukondwerera. “Ndikuyembekezera kuti chokumana nacho chimenechi chidzalimbikitsa Mboni zachichepere m’masukulu kusaleka kulankhula,” akumaliza motero Jorgen. “Mkhalidwe wawo Wachikristu ndi kuima nji kaamba ka chowonadi zingafese mbewu zimene pambuyo pake zingabale zipatso.”

Kumenyera Ufulu Wachipembedzo

Mboni za Yehova zachitanso mbali yaikulu m’kukhazikitsa ufulu weniweni wa chipembedzo m’Sweden. Izi zapindulitsa aliyense.

Mwachitsanzo, mofanana ndi m’maiko ena onse, aliyense wa Mboni za Yehova m’Sweden wasankha kusunga uchete Wachikristu. (Yohane 17:16) Monga chotulukapo, ambiri anapatsidwa chilango cha kukhala m’ndende kwa nyengo yaitali. Koma mu 1966 nkhondo inamenyedwa ya ufulu wa chipembedzo pamene akuluakulu aboma anasankha kuti poyembekezera kufufuza kochitidwa pa anthuwo, Mboni sizikaitanidwira ku utumiki wa nkhondo. (Yesaya 2:2-4) Kulekerera chipembedzo kwa m’Sweden kwatumikira kukhala chitsanzo kumaboma ena.

Nkhani ina inaphatizapo ufulu wa odwala. Mboni za Yehova zimawona lamulo la Baibulo la ‘kusala mwazi’ mwamphamvu ndipo motero zimakana kuthiriridwa mwazi. (Machitidwe 15:28, 29) Ngakhale kuti simadokotala ndi ogwira ntchito m’zipatala onse amene alemekeza kaimidwe aka ka m’Malemba, magazini otchuka koposa a zamankhwala m’Sweden posachedwapa analengeza mutu wankhani uwu: Palibe Kukana Kuthiridwa Mwazi Kumene Kuyenera Kulemekezedwa ngati Wodwalayo Akudziŵa Zotulukapo Zake.”

Mawu amenewa anali mutu wankhani wa lipoti la msonkhano wa National Board of Health and Welfare ndi Delegation for Medical Ethics of the Swedish Society of Medicine. Pambuyo pokambitsirana mkhalidwe wa Mboni za Yehova, akuluakulu ameneŵa anagamula kufulumiza madokotala onse kuvomereza pamene wodwala wodziŵa mogwirizana ndi lamulo​—kuyambira pa zaka 15 zakubadwa ndi kuposerapo​—akana kuthiriridwa mwazi. Iwo anavomereza kuti tsopano pali zoletsa kuthirira mwazi zazikulu chifukwa cha upandu wa kupatsirana matenda. Komabe, chofunika koposa nchakuti, chosankha chawo chanzeru chimachirikiza ufulu weniweni wa wodwala aliyense wa kukana mtundu winawake wa mankhwala.

Ndithudi, nzika zambiri za Sweden, zimasangalala ndi moyo wabwino mwakuthupi. Koma ambiri afunikira kulimbikitsidwa mwa makhalidwe abwino ndi mwauzimu. Mosakaikira, Akristu owona m’dziko limenelo akuthandiza kuwongolera miyoyo ya onse omwe ali ofunitsitsa kuphunzira ndi kugwiritsira ntchito Mawu a Mulungu. Anthu olabadira oterewa amasangalalanso ndi chiyembekezo cha moyo wosatha m’dziko latsopano likudzalo la Mulungu.​—Yohane 17:3; 2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:3, 4.

[Mapu patsamba 22]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

NORWAY

SWEDEN

FINLAND

U.S.S.R

DENMARK

WEST GERMANY

EAST GERMANY

POLAND

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena