Chidziŵitso pa Nyuzi
“Kuzembetsa Zinthu Zakale Zokwiriridwa Pansi”
Pansi pamutu wankhani umenewo, magazine a tsiku ndi tsiku Achifrench Le Monde anasimba nkhani ya katswiri wofufuza zamoyo zamakedzana m’mabwinja mu India amene mwachiwonekere “kwa zaka 20 . . . ananyenga anzake ponena za kumene kunachokera zofukulidwa pansi zimene anazipereka kwa iwo kuti azipende.” Kwanenedwa kuti “kuzembetsako” kunaphatikizapo kuwatumizira zofukulidwa pansi zimene zinapezedwa mu United States, Afirika, Chekoslovakia, ndi Zisumbu za Briteni, akumanena kuti zinatumbidwa m’Mapiri a Himalaya. Wasayansi ameneyu anafalitsa zotumba zakezo m’nkhani zoposa 300. Chinyengocho chinavumbulidwa ndi wasayansi wina wa ku Australia kupyolera m’magazine yasayansi ya ku Briteni yotchedwa Nature. Iye ‘anadabwa mmene zinathekera kuti unyinji wotero wa zotumbidwa zokaikitsa zikhale zosaululidwa kwa nthawi yaitali chotero.’
Chifukwa chimodzi chothera, malinga ndikunena kwa Le Monde, chinali lamulo losunga chinsinsi lolabadiridwa ndi ziwalo zambiri za asayansi. Nkhaniyo inanena kuti “kuzembetsa” zinthu zakale zokwiriridwa pansi kumeneku “kwapangitsa pafupifupi maumboni onse onena za mkhalidwe wadziko ku Himalaya osonkhanitsidwa [zoposa zaka 20 zapitazo] kukhala opanda pake.”
Mwachiwonekere, chochitika chatsopanochi cha chinyengo m’sayansi sichimapereka chikaiko pa sayansi yonse. Komabe, chimapereka umboni wowonjezereka wakuti mutayerekezera zigomeko za sayansi ya zofukulidwa pansi ndi kulondola kwa cholembedwa cha Baibulo kaŵirikaŵiri izo sizimakhala kanthu kena kusiyapo chimene mtumwi Paulo anachitcha “kutsutsana kwa ‘chidziŵitso’ chimene sichiri konse chidziŵitso.”—1 Timoteo 6:20, The New Jerusalem Bible.
“Okhathamira ndi Mwazi”
Mu Colombia, South America, ngwazi zankhanza zogulitsa mankhwala ogodomalitsa zimapangana ndi anyamata kuti afafanize okangana nawo kapena kuyambitsa kuda nkhawa pakati pa andale zadziko ndi anthu onse. Mmodzi wotero sicario, kapena wambanda wolipiridwa, anauza atola nkhani a Tiempo, magazine osimba nkhani Achispanya, kuti ‘kupha munthu wopanda liwongo nkovuta.’ Kodi iye amatonthoza bwanji chikumbumtima chake? Iye akulongosola kuti: “Ndidziŵa kuti limodzi la malamulo a Mulungu limati usaphe, koma kwa ine iri nkhani ya munthu amene afunikira kupha kuti apeze zakudya. Ndimapha dala chifukwa chofuna ndalama. Kodi simunawone kuti ndikugwira ntchito chifukwa chakuti ndifunikira kudzisamalira? . . . Ndisanapite kukapha munthu, ndimapemphera kwa Mulungu ndi kwa Namwali kuti anditetezere.”
Ngakhale kuti mosakaikira lingaliro la mtundu uwu lingakanidwe kotheratu ndi akatswiri a maphunziro a zaumulungu a Chikatolika, atsogoleri atchalitchi avomereza mwalamulo nkhondo zomenyana ndi zida “kukhala kachitidwe komalizira ka kuthetsera ulamuliro wa nthawi yaitali wankhalwe.” Ngati akatswiri a maphunziro a zaumulungu alekelera chiwawa kuthetsera chisalungamo cha ndale zadziko, kodi zingatidabwitse kuti Akatolika ena, monga sicario uyu, akulungamitsa kupha chifukwa cha chisalungamo chazachuma? Nkwaupandu chotani nanga kusukulutsa Mawu a Mulungu!
Pausikuwo chisalungamo chachikulu koposa ndi kalelonse chiri pafupi kuchitidwa—chophatikizapo kumangidwa, kuyesedwa, ndi kuphedwa kwa Yesu Kristu—Yesu iyemwini anakana kugwiritsira ntchito chiwawa cha mtundu uliwonse. Iye anauza Petro kuti: “Onse ogwiritsira ntchito lupanga adzafa ndi lupanga.” (Mateyu 26:52, Revised Standard Version, kope Lachikatolika) Ndithudi, kodi otembenukira ku chiwawa angayembekezere bwanji Mulungu Wamphamvuyonse kuwamvera m’mikhalidwe iriyonse, popeza kuti ulosi wa Yesaya umanena mosabisa kuti: “Ngakhale mutapanga mapempero ambiri, sindidzamvetsera; manja anu ndi okhathamira ndi mwazi”?—Yesaya 1:15, RS, kope Lachikatolika.
“Perekani zake za Kaisara kwa Kaisara”
Vuto la kupewa kukhoma misonkho likuwonjezerekawonjezereka mmaiko ambiri. Mwachitsanzo, m’Spanya, nyuzipepala yotchedwa El Diario Vasco ikusimba kuti ponse paŵiri ogula ndi ogulitsa ali ndi chizolowezi chobisa mtengo weniweni wogulira chinthu. Pamene kuli kwakuti wogula ndi wogulitsa angavomerezane pamtengo umodzi weniweni wogulira, mtengo waung’ono kwenikweni ndiwo umene umalembedwa pa pepala lamalonda. Malondawo atamalizidwa, msonkho umalipiridwa molingana ndi mtengo wa chinthu wolembedwawo. El Diario Vasco ikusimba za zifunsiro za ofesala wa malumbiro José María Segura Zurbano kuti pamene kuli kwakuti maofesala a malumbiro samakhaladi ndi phande m’chinyengocho, iwo amadziŵa kuti mtengo wa chinthu chimene akulemba ngwabodza. Pofotokoza anthu okha amene sakukhudzidwa ndi chizoloŵezi chosawona mtima ichi, Zurbano ananena kuti: “M’dziko lino aliyense ndi mnansi wake amanena bodza, kusiyapo Mboni za Yehova zokha. Pamene agula kapena kugulitsa, mtengo [wa chinthu] umene amalemba umakhala wowonadi.”
Mboni za Yehova nzodziŵika bwino lomwe kaamba ka kuwona mtima kwawo. Iwo amadziŵa kuti Yehova Mulungu amayembekezera atumiki ake kusonyeza mikhalidwe imeneyo m’zochita zawo zonse. Mulungu amada “lirime lonama” ndi “mboni yonama yonong’ona mabodza.” Pankhani ya kukhoma misonkho, Yesu Kristu anaikira muyezo atsatiri ake owona pamene ananena kuti: “Perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma zinthu za Mulungu kwa Mulngu.”—Miyambo 6:6-19; Marko 12:17.