Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 11/15 tsamba 7
  • Chidziŵitso pa Nyuzi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chidziŵitso pa Nyuzi
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kungokhala Nalo Baibulo Sikokwanira
  • Womwerekera m’Kusayeruzika
  • Yesu ndi Ndale Zadziko
  • Mmene Mankhwala Oletsedwa Amakhudzira Moyo Wanu
    Galamukani!—1999
  • Kodi Tingapambane Pankhondo Yolimbana ndi Mankhwala Osokoneza Bongo?
    Galamukani!—1999
  • N’chifukwa Chiyani Anthu Amagwiritsa Ntchito Mankhwala Osokoneza Bongo?
    Galamukani!—2001
  • Vuto la Mankhwala Osokoneza Bongo Lingathetsedwe!
    Galamukani!—2001
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 11/15 tsamba 7

Chidziŵitso pa Nyuzi

Kungokhala Nalo Baibulo Sikokwanira

Phunziro laposachedwapa linapeza kuti kwa anthu okhala ndi Mabaibulo, theka la iwo ananena kuti sanaliŵerengepo. Ichi chinaphatikizapo ambiri odzidziŵikitsa kukhala Akristu obadwanso. Chifupifupi 30 peresenti ya odzinenera kukhala Akristu ofunsidwa sanadziŵe kuti Yesu anabadwira m’Betelehemu. Mogwirizana ndi The Detroit News, “maperesenti khumi limodzi mphambu zisanu ndi zitatu anayankha kuti ndi ku Yerusalemu, pamene 8 peresenti anati ndi ku Nazarete.” George Barna, mtsogoleri wa gulu lofufuzalo, ananena kuti: “Ngati iwo ali osadziŵitsidwa zinthu zoyambirira zonga zimenezi, kodi angayembekezeredwe motani kukambitsirana mwaluntha za mkati mwa Malemba ndi munthu wosakhulupirira kapena kukhala ndi moyo mogwirizana ndi malamulo a makhalidwe abwino a Baibulo?”

Mtumwi Paulo anawona mkhalidwe wofananawo pakati pa ena omwe anali ndi “changu cha kwa Mulungu, koma si monga mwa chidziŵitso [cholongosoka].” Iye analozeranso kwa ena omwe anali ndi “mkhalidwe wachinyengo wa kulambira, ndi kudzichepetsa kwa chiphamaso” ndipo ananeneratu kuti “masiku otsiriza” akazindikiritsidwa ndi kukhalapo kwa awo okhala ndi “mawonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana.” (Aroma 10:2; Akolose 2:23; 2 Timoteo 3:1-5) Komabe, Akristu owona amawona Mawu a Mulungu kukhala a mtengo wapamwamba. Iwo amazindikira kuti kungokhala nalo Baibulo sikokwanira. M’malomwake, iwo mwa mtima wonse amagwirizana ndi chilangizo chake “lirani monga makanda alero mkaka woyenera.”​—1 Petro 2:2.

Womwerekera m’Kusayeruzika

Chimodzi cha zochitika zimene Yesu Kristu anandandalitsa monga mbali ya “chizindikiro” cha masiku otsiriza a dongosolo iri la zinthu ndicho “kuchuluka kwa kusayeruzika.” (Mateyu 24:3, 12) Kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala ogodomalitsa kwakhala ndi chisonkhezero champhamvu pa kuwonjezeka kwa kusayeruzika lerolino. Mwachitsanzo, nyuzipepala ya ku Australia The Sydney Morning Herald ikusimba kuti maupandu asanu ndi aŵiri mwa khumi ochitidwa mu New South Wales ali ogwirizanitsidwa ndi mankhwala ogodomalitsa, ndipo chifupifupi 85 peresenti ya kuba kogwiritsira ntchito mfuti m’bomalo kukuchitidwa ndi ogwiritsira ntchito heroin. Ndipo vuto la kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala ogodomalitsa likukulabe.

U.S. News & World Report ikunena kuti “kulibe malo mu Europe amene ali osakhudzidwa ndi mliriwo.” Mu Soviet Union, chiŵerengero cha ogwiritsira ntchito molakwa mankhwala ogodomalitsa chikuyerekezedwa kukhala m’mamiliyoni. M’kuyesayesa kosowa chochita kuti athetse funde la kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala ogodomalitsa, boma la Soviet layamba kukambitsirana ndi mabungwe oletsa kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala ogodomalitsa m’maiko 25. Komabe, ziyembekezo zakuti maboma adzazifikira zonulirapo zoterozo zikuwoneka kusakhala zenizeni powona maripoti osonyeza kuti ndalama zopindulidwa mu mankhwala ogodomalitsa zikugwiritsiridwa ntchito kunyenga apolisi, oimba milandu, ndipo ngakhale oweruza. Nduna ina ya boma yogwiritsidwa mwala inanena kuti: “Palibe bungwe la polisi m’dziko limene lakhoza mpang’ono pomwe kuletsa kuperekedwa kwa [mankhwala ogodomalitsa] kufalikira tero m’makwalala.” Iye anawonjezera kuti: “Kuli kopsyinja maganizo chifukwa chakuti palibe njira iriyonse yothetsera vutolo yomwe ikuikidwa.”

Mawu oterowo amatikumbutsa ulosi wa Yesu wonena za masiku otsiriza. Iye ananeneratu kuti panthaŵiyi ‘anthu adzakomoka ndi mantha, osadziŵa njira yotulukira.’​—Luka 21:25, 26.

Yesu ndi Ndale Zadziko

Mutu wa nkhani mu nyuzipepala ya ku South Africa, yotchedwa The Star ya ku Johannesburg, unali wakuti: “Tchalitchi cha Katolika Chivumbula Makonzedwe a Upasitala a SA.” Makonzedwewo ali a “kubweretsa ufumu wa Mulungu” mu South Africa kupyolera mwa “chosankha champhamvu cha tchalitchi kuchotsapo tsankho la fuko.” Kukwaniritsa cholinga chimenechi, Jude Pieterse, mlembi wamkulu wa South African Catholic Bishops Conference, akunena kuti tchalitchicho chikufunafuna chirikizo la matchalitchi ena limodzinso ndi “mbali zonse za chitaganya cha anthu a South Africa.” Komabe, Akatolika ena akulingalira kuti makonzedwewo ali “chinyengo chochitidwa ndi Abishopu cha kusintha Akatolika kukhala achangu a ndale zadziko,” akusimba tero bishopu wa ku Johannesburg, Reginald Orsmond. Pamene kuli kwakuti Pieterse anavomereza kuti makonzedwewo anali ndi zolinga za ndale zadziko, Orsmond anati sanali “chinthu chachilendo” koma anali “akale monga Yesu iyemwini.”

M’chenicheni, Yesu Kristu sakalangiza konse ophunzira ake kukhala achangu a ndale zadziko. Pamene anafunsidwa ndi Pontiyo Pilato, Yesu mwamphamvu anayankha kuti: “Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi.” (Yohane 18:36) Ndiponso, Mboni za Yehova zoposa mamiliyoni atatu zimasangalala ndi kugwirizana kwaufuko m’mathayo awo chifukwa chakuti amakhala mogwirizana ndi lamulo la Yesu ‘latsopano, kuti akondane wina ndi mnzake; monga Yesu anawakondera iwo’​—osati mu South Africa mokha, koma kuzungulira dziko lonse!​—Yohane 13:34.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena