Kututa Kubweretsa Chisangalalo mu Japan
“CHINALI chowonekeratu kuti Amishonale anali kumva mlingo winawake wa kulefulidwa.” Anatero Charles T. Russell, prezidenti woyamba wa Watch Tower Bible and Tract Society, pambuyo pa kufufuza kwake kwaumwini kwa mkhalidwe wachipembedzo mu Japan mu 1912. Iye ankalankhula za kulephera kwa amishonale a Dziko Lachikristu ndipo ananena kuti: “Chimene anthu a ku Japan akufuna ndicho ‘Uthenga Wabwino wa ufumu.’”
Kodi chosoŵachi chikakwaniritsidwa konse? Kuwunika kwa chowonadi kunaŵalikira pa anthu a ku Japan kudzera mwa Mboni za Yehova zokhulupirika zochepera mkati mwa ma 1920 ndi ma 1930. Ngakhale mkati mwa Nkhondo ya Dziko ya II, ochepera anapitiriza kubukitsa mbiri yabwino mosasamala kanthu za chitsutso kuchokera ku boma lotsendereza. Komabe, ntchito yofutukuka mokulira ya kututa inali kutsogolo kaamba ka m’dadada wa zisumbu zimenezi mu Far East.
Ndi kufika kwa amishonale 15 a Watchtower mu 1949, Yehova anauzira moyo watsopano mu ntchito yolalikira Ufumu mu Japan. Amishonale ofika chatsopanowo anawona zotulukapo za Nkhondo ya Dziko ya II kulikonse: Mizinda yosandutsidwa bwinja, ndipo anthu anali osokonezeka popeza kuti dongosolo lawo lakale la mikhalidwe linali litasinthiratu. Amishonale a Dziko Lachikristu nawonso anayambitsa chatsopano ntchito yawo mu Japan pa nthaŵi imodzimodziyo, koma analephera kupanga Akristu enieni mwa anthu a ku Japani amenewo. Ofika mu “49wo” ndi amishonale oposa 150 a Mboni za Yehova omwe anaŵatsatira anayang’anizana ndi chitokoso chachikulu cha kufesa m’maganizo ndi m’mitima ya anthu a ku Japan chikhulupiriro mwa Mlengi, Yehova Mulungu. Kodi anachifikira motani chitokoso chimenechi?
Kuyala Maziko
Kuyesayesa kwawo kwaumishonale kunayambira pa nyumba yosanjikana ya nyumba ziŵiri mu Tokyo. M’ma 1950, kututako kunadzachedwerako. ‘Ocheperadi ndiwo adzabwera m’chowonadi mu Japan Harmagedo isanadze,’ adaganiza choncho mmodzi wa anthu a ku Japan woyambirira yemwe anavomereza ku mbiri yabwino masiku amenewo. Mmodzi wa oyang’anira amadera oyambirira amakumbukira kukhala akuyang’ana kunja pa zenera la sitima ndi kukaikira kaya ngati nyumba zokhala m’midzi yaing’ono zimene iye anapitirira zikafikiridwadi ndi mbiri yabwino.
Chinatenga chifupifupi zaka khumi za kuyesayesa kwaumishonale kuti chiŵerengero cha ofalitsa a Ufumu mu Japan chifike pa chikwi chimodzi. Koma podzafika mu 1963, chifukwa cha kuwonjezeka kokhazikika, nthambi yosalimba ya ku Tokyo inagwetsedwa ndipo nyumba yosanjikana yakonkiri ya nyumba zisanu ndi imodzi inamangidwa m’malo mwake.
Amishonalewo anayala maziko abwino a mtsogolo mwa kuika mzimu wa upainiya m’mitima ya ophunzira Baibulo awo. Yehova anadalitsa kuyesayesa kogwirizana kwa amishonalewo ndi apainiya a ku Japan, ndipo chiŵerengero cha Mboni chinakula kufika pa zikwi khumi mu 1970. Mu 1972, kuti achite ndi kuwonjezekako, nyumba yosanjikana yosindikizira yokhala ndi nyumba zitatu ndiponso yogonamo yokhala ndi nyumba zisanu zinamangidwa mu Numazu, chifupifupi makilomita 120 kum’mwera koma chakumadzulo kwa Tokyo. Tsopano, m’malo molola kampani yakunja kusindikiza magazine, Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ankatulutsidwa pa makina osindikizira a nthambi ya Japan kutumikira ntchito yolalikira Ufumu ya kumaloko.
Kodi ndani yemwe anayembekezera kuti ntchito yotuta ikakula kupangitsa nyumba za pa Numazu kuchepa m’zaka khumi zotsatira? Koma zimenezo ndizo zidachitika, ndipo Yehova anali adakali ndi ntchito yowonjezereka yofutukula nyumba yosamalira kututa komawonjezerekako.
Chiwonjezeko Mosasamala Kanthu za Mavuto
Nyumba yocholoŵana yatsopano ya nthambi ya mlingo wowirikiza nthaŵi zitatu kuposa ija ya mu Numazu inatsirizidwa mu 1982 mu Ebina, cha kum’mwera pang’ono kwa Tokyo. Podzafika nthaŵi imene inaperekedwa mu May chaka chimenecho, Yehova anali atadalitsa Mboni mu Japan ndi ziŵerengero zapamwamba zotsatizanatsatizana za mwezi ndi mwezi kwa zaka zoposa zitatu. Chiwonjezeko chimenechi chinapitirizabe, ndipo mu May 1985 chiŵerengero cha ofalitsa a mu Japan chinafika pa zikwi zana limodzi. Inde, Yehova ankafulumizitsa ntchito m’nthaŵi yake, chotero kufutukula kowonjezereka kwa malo a nthambi kunali kosapeŵeka. (Yesaya 60:22) Zaka zoŵerengeka zokha pambuyo pa kuperekedwa kwa nyumba yocholoŵana yoyamba mu Ebina, Bungwe Lolamulira linavomereza kumanga fakitale yatsopano yosanjikana ya nyumba zisanu ndi imodzi yokhala ndi malo apansi ndiponso nyumba zina zosanjikana zisanu ndi zitatu zogonamo.
Mosakaikira, Satana sanakondwere ndi kukula kumeneku pakati pa atumiki a Yehova chifukwa chakuti mwezi wotsatira pambuyo pa kufikira chiŵerengero cha ofalitsa zikwi zana limodzi, nkhani yaikulu ya kuthira mwazi inabuka m’Japan. Mnyamata wa zaka khumi zakubadwa anamwalira pambuyo pake—koma osati chifukwa chakuti—makolo ake anakana kuti athiridwe mwazi. (Machitidwe 15:29) Monga chotulukapo, owulutsa nkhani mwaukali anawukira Mboni. Ngakhale kuti atate a mnyamatayo panthaŵiyo sanali Mboni yodzipereka, iye analimbana ndi kuvutitsidwa kopanda chifundo kochitidwa ndi amtola nkhani. Pambuyo pake iye anabatizidwa ndipo tsopano akutumikira ndi mkazi wake monga apainiya okhazikika.
Kodi kuwukira kumeneko kunayambukira motani ntchito yotuta? Mochepera kwambiri. Ophunzira a Baibulo ena analeka maphunziro awo, koma ziŵerengero zapamwamba za mwezi ndi mwezi za ofalitsa zinapitirizabe mosalekeza, ndipo December 1988 inapanga zaka khumi za ziŵerengero zapamwamba zotsatizanatsatizana. Mkati mwa nyengo ya zaka zisanu ndi ziŵiri pakati pa kuperekedwa kwa nyumba yocholoŵana yoyambirira mu Ebina ndi kuperekedwa kwa yatsopanoyo, chiŵerengero cha ofalitsa chawirikiza kaŵiri kuchokera pa 67,000 kufika ku oposa 135,000, pamene kuli kwakuti chiŵerengero cha apainiya okhazikika chawirikiza katatu kuchokera pa 12,000 kufika ku 36,000, ndipo chiŵerengero cha maphunziro a Baibulo apanyumba chawirikiza chifupifupi kaŵiri kuchokera pa 97,000 kufika ku 172,000. Ndi umboni wowonekera wotani nanga wa chilakiko cha Yehova pa ziwukiro za Satana kwa anthu ake!—Miyambo 27:11.
Kumanga Nyumba Zatsopano
Mboni za Yehova sizimamanga nyumba zokongola kuti zikondweretse anthu. Koma pamene zikuchita ndi chiwonjezeko cha alengezi a Ufumu, kaŵirikaŵiri nyumba zawo zimafunikira kukhala zazikulu kwambiri. Fakitale yatsopano ya ku Japan iri chitsanzo chabwino. Iyo iri ndi malo apansi a chifupifupi mamita 22,500 mbali zonse zinayi, kuwirikiza kaŵiri kuposa malo apansi a fakitale yoyamba. Moikira Zikuto ku Mabukhu, Shopu ya Makina, ndi Dipatimenti Yosamalira Zinthu Zotuluka m’Dziko/Yotumiza Katundu zinasamutsidwira ku fakitale yatsopanoyo, ndipo chifupifupi nyumba zosanjikana ziŵiri zikugwiritsiridwa ntchito kusungiramo zinthu. Ngakhale pokhala ndi zonsezi, fakitale yatsopanoyo iri ndi ukulu wokhoza kutengabe zinthu zambiri. Maziko anayalidwa m’malo apansiwo kaamba ka makina aŵiri osindikizira a liŵiro lalikulu, ndipo nyumba zosanjikana ziŵiri zidakali zopanda kanthu, zoyembekezera kufutukuka kwa mtsogolo.
Nyumba yatsopano ya nyumba zogonamo zisanu ndi zitatu zosanjikana iri ndi pofikira alendo pokongola ndi pokometsedwa bwino. Pali zipinda za pambali 128 za ogwira ntchito pa Beteli ndi pansi pa ukulu wa mamita 8,980 mbali zonse zinayi—wofanana ndi mlingo wa malo a pansi a chingalaŵa cha Nowa. Mnansi anafunsadi ogwira ntchito pa nyumbayo mmene iye angalembereko kufunsira kukhala “mu umwini wa malowo” mwa kuphatikiza pamodzi ndi malo ake!
Onse omwe anatengamo mbali m’kumangako anazindikira Yehova kukhala wotsogoza ntchito yomangayo. (Salmo 127:1, 2) Unyinji wa antchitowo anali achichepere ofunitsitsa kugwira ntchito a m’zaka zawo za kuchiyambi kwa 20, odzala ndi changu koma opanda luso la ntchito yomanga. “Poyamba,” akusimba tero mmisiri womanga yemwe anagwira ntchito pa projekitiyo, “chinali chovuta kwa ine kulemba pulani m’njira yomwe inali yomveka kwa abale opanda luso la ntchitoyo.” Komabe, ndi mzimu wa chigwirizano ku mbali zonse, zopingazo zinalakidwa.
Kufunitsitsa kugwirizana kumeneku kunalola mzimu wa Yehova kugwira ntchito pakati pa antchitowo mosavuta. “Pamene tinkakumba,” mmodzi akukumbukira tero, “nthaŵi iriyonse kunkagwa mvula—mukhale m’mawamawa kapena usiku—ndinkapita ku malo omangakowo kukaŵona ngati zogwira makoma zinkagwiririrabe. Nthaŵi iriyonse, ndinapezako nkhope zankhaŵa, ndipo tonsefe tinagwirira ntchito limodzi, titanyowa kwa dzawoneni, kuchita ndi ngozi iriyonse. Zokumana nazo zoterozo zinatipangitsa kudzimva aubale moposerapo.”
Chirikizo la Kututa kwa Mitundu Yonse
Popeza kuti nyumba zatsopanozo zinamangidwa kotero kuti zichirikize ntchito yokolola ya Yehova, kunali koyenerera kuti izo ziperekedwe kwa iye zitamalizidwa. Programu ya kuperekedwa inachitidwa pa May 13, 1989, ndi Carey Barber, John Barr, ndi Lloyd Barry a Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, limodzi ndi akazi awo, akupezekapo. Anthu a ku Japan oyambirira kubatizidwa oposa chikwi chimodzi anaitanidwa kupezeka pa programu ya kuperekedwayo, ndipo anasangalala kupeza mabwenzi akale akutumikirabe Yehova mokhulupirika. Oimira kuchokera ku maiko 13 analandira chiitano chokapezekapocho ndi kugawanamo m’chochitika chosangalatsa chimenecho. “Chinalidi ngati msonkhano wa mitundu yonse waung’ono,” inatero nthumwi ina.
Chomwe chinapangitsa programuyo kukhaladi ya mitundu yonse anali maripoti ochokera ku maiko asanu ndi anayi amenewo. Pamene oimira ochokera ku maiko osiyanasiyana a ku Asia anasimba zitsanzo za chigwirizano cha mitundu yonse ndi kusonya kuti fakitale yatsopanoyo ikutumikira zosoŵa za maiko awo limodzinso ndi munda wa Japan, anadzimva kukhala ogwirizanitsidwa ndi chomangira cholimba cha ubale. Nthambi ya Japan tsopano imasindikiza zofalitsidwa m’zinenero 13 ndipo imatumiza maoda a mabukhu ku maiko ambiri.
Masana, Mbale Barber analankhula ku gululo ndi kugogomezera kufunika kwa kukwaniritsidwa kwa maulosi a Ezekieli. Kenaka Mbale Barr anapereka nkhani pa mutu wakuti “Kudzaza Dziko Lapansi ndi Ulemerero wa Yehova,” akumathandiza gululo kumvetsetsa mphamvu yoloŵerera mozama ya chowonadi.
Nkhani ya kuperekedwa inapatsidwa ndi Mbale Barry, yemwe kale anatumikira monga m’mishonale mu Japan kwa zaka zoposa 25. M’nkhani yake ya mutu wakuti “Muyenera Kusangalala Pamaso pa Mulungu Wanu, Yehova,” iye analimbikitsa gululo kusangalala pokhala ndi moyo m’nyengo ya nthaŵi yochitiridwa chithunzi ndi Madyerero a Misasa, kapena a Kututa, mu Israyeli wakale. Iye anasonyeza zifukwa zosangalalira pamene anafotokoza mbiri yachidule ya ntchito mu Japan. Pamene Mbale Barry anavomereza kuti nyumba zatsopanozo ziperekedwe kwa Yehova, onse opezekapo anavomereza ndi kuwomba m’manja kwa mtima wonse.
Tsiku lotsatira, oimira a Bungwe Lolamulira analankhula kwa gulu la 233,780 osonkhana m’malo 46 ogwirizanitsidwa ndi kulunzanitsa kwa telefoni m’zisumbu zonse za Japan. Ndithudi, monga mmene Pasitala Russell ananenera mu 1912, anthu a ku Japan afunikiradi mbiri yabwino ya Ufumu. Yehova anakwaniritsa chosoŵa chimenecho mwa kuyala maziko kupyolera mu ntchito yaumishonale ndi kuloŵetsa mzimu wa upainiya mwa Mboni za ku Japan. Nyumba zoperekedwa chatsopanozo ziri umboni wa ‘kufulumizitsa’ kwa Yehova ntchito yotuta mkati mwa Madyerero a Misasa ophiphiritsira.—Yesaya 60:22.
[Zithunzi patsamba 24]
Kulamanzere: nyumba ya fakitale yatsopano pa Ebina ndi (m’munsi kumanzere) programu ya kuperekedwa ikuchitidwa ndipo (m’munsi kulamanja) pofikira alendo pa nyumba yokhalamo yatsopano
[Zithunzi patsamba 25]
Nyumba yokhalamo yatsopano ndi (pakati) laibulale pa chipinda chosanjikana chachiŵiri cha nyumba ya ofesi
[Zithunzi patsamba 26]
Amishonale 19 a kalasi la 11 la Gileadi ameneŵa anapezeka pa kuperekedwako. Utumiki wanthaŵi zonse wa ameneŵa—kuphatikizapo uja wa ena asanu a kalasi la 11 omwe anamwalira okhulupirika pa gawo lawo mu Japan—umafikira chiwonkhetso cha zaka 1,023
Ziŵalo zitatu za Bungwe Lolamulira—Carey Barber, John Barr, ndi Lloyd Barry—anatengamo mbali mu programu ya kuperekedwayo