Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 10/15 tsamba 24-28
  • Zosankha Zolimba Mtima Zipereka Madalitso mu Suriname

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zosankha Zolimba Mtima Zipereka Madalitso mu Suriname
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Chosankha Chimene Chinapulumutsa Moyo Wake
  • Chikondi Chinamsonkhezera Kulanditsa Abale Ake
  • Iye Sanalolere Molakwa
  • Kukwatira pa Lachitatu, Kubatizidwa pa Loŵeruka
Nsanja ya Olonda—1989
w89 10/15 tsamba 24-28

Zosankha Zolimba Mtima Zipereka Madalitso mu Suriname

PA NTHAŴI ina, Suriname anali “limodzi la maiko olemera koposa m’Caribbean,” inatero nyuzi magazine yamitundu yonse yotchedwa South. Ndalama zopezeka kuchokera ku chiziro, nsomba zotchedwa shrimps, mpunga, nthochi, ndi matabwa, kuphatikizapo chithandizo cha chitukuko, zinapatsa nzika zokwanira 400,000 za chisumbu ichi chimene kale chinali kulamulidwa ndi Adatchi kukhala zolemerera kwambiri koposa oyandikana nawo ena.

Komabe, mkati mwa ma 1980, chuma chawo chinatchipa. Mkhalidwe wa mwana alirenji unasanduka njala, ndipo mizere yaitali yofuna chakudya inafikira kukhala paliponse. Mu 1986 kuwulika kwa nkhondo yachizembera kunakakamiza nzika zokwanira zikwi khumi kuthaŵa kuchokera kum’mawa kwa Suriname kunka ku French Guiana yokhala pafupipo, kukayambiranso konko moyo chatsopano m’misasa ya othaŵa. Pa nthaŵiyo, mbali yaikulu ya malo a nkhalango​—kokhala pafupifupi Anegro Amthengo ndi Amwenye a ku Amereka 50,000​—inayamba kulamulidwa ndi omenya nkhondo yachizembera, akumapangitsa kuyenda ulendo wopita ku midzi kukhala waupandu. Magazine yotchedwa South, inanena kuti, masinthidwe amenewa anasiya dzikolo lowonongeka.

Kodi mikhalidwe imeneyo inadodometsanso ntchito ya Mboni za Yehova? Kutalitali, iwo awonjezera ntchito yawo. Mwachitsanzo, chiŵerengero cha Mboni chawonjezereka kuchoka pa 920 mu 1980 kufika pa oposa 1,400 lerolino. Mu April 1989 panali apainiya othandiza 338​—pafupifupi 25 peresenti ya Mbonizo pa nthaŵiyo. Komabe, madalitso otero, anadza kokha chifukwa cha kulimba mtima, umphumphu, ndi chikondi zimene Mbonizo zinasonyeza poyesedwa. Nazi zitsanzo zina zaposachedwapa za mmene zosankha zolimba mtima zinabweretsera madalitso olemerera mu Suriname.

Chosankha Chimene Chinapulumutsa Moyo Wake

Lumey Hoever, ofisala wapolisi wojintcha wokhala ndi zaka zakubadwa za chakumapeto kwa ma 30 amenenso ali mmodzi wa Mboni za Yehova, anagamula kuti akasiya ntchito yake mosasamala kanthu za umphaŵi m’zachuma. Chifukwa ninji kusintha? Lumey akulongosola kuti:

“Kuyambira pamene ndidaŵerenga nkhani ya mu Nsanja ya Olonda yotichenjeza za maupandu ogwirizanitsidwa ndi kunyamula mfuti, ndinadziŵa kuti ndikafunikira kusiya ntchito imeneyi.a Komabe, ndinazengereza chifukwa chakuti ndifunikira kusamalira mkazi wanga ndi ana. Komabe, pamene ndinakankhira chosankha changacho mtsogolo, ndipamenenso chikumbumtima changa chinandivutitsa kwambiri. ‘Ngati gulu la Yehova likundilimbikitsa kulingalira mwamphamvu kusayenerera kwa ntchito ya mtundu uwu, payenera kukhala chifukwa chabwino,’ ndinadzikumbutsa motero. Chotero m’January 1986, ndinapanga chosankha.”

Komabe mkulu wa apolisi sanafune kumulola kupita, anafikira pa kumulonjeza kumpatsa gawo ku Tamanredjo, siteshoni yolakalakika kwambiri yokhala chifupi ndi malikulu. Koma Lumey anali wotsimikiza. Iye analembera nduna ya polisi, nalongosola zikhulupiriro zake za chipembedzo, napempha chilolezo cha kuchoka. Mu April 1986 yankho linadza lakuti: ‘Pemphero laloledwa!’

Mwamsanga Lumey anapeza ntchito ku Dipatimenti yowona Zankhalango. Malipiro ake anali ocheperapo, koma anali ndi nthaŵi yowonjezereka ya kupita ndi banja lake ku misonkhano ku Nyumba Yaufumu. Miyezi khumi idapita. Tsiku lina, pambuyo pa kugwira ntchito tsiku lonse pa fama la banjalo, Lumey ndi mbale wake anali pa njira yobwerera kunyumba. Iye akusimba kuti:

“Titayandikira nyumba ya pa famayo, ndinawona amuna aŵiri ovala nsanza, atavala mikuzi pa mitu yawo. ‘Kon dja (Bwera kuno),’ iwo anaitana motero Mchisuriname. Pamene ndidayenda kumka kwa iwo, mwamuna wachitatu wokoloweka mfuti yachifefe pa pheŵa anawonekera. Panali kokha pa nthaŵi iyi chakuti ndinazindikira amene anali: ankhondo achizembera!

“Anandiyang’ana kuyambira kumutu mpaka kumapazi. Ndiyeno mmodzi wa amuna ovala mkuzi anafuula kuti: ‘Ndimdziŵa munthuyu. Ngwapolisi!’ Nkhope zawo zinakwiya. Kwa mphindi zochepa, tinayang’anizana dwii. Ndinagwira mpweya. Ndiyeno ndinamva phokoso la pansipansi. Khetche, khetche​—mwamuna wachitatuyo anatchera mfuti yake. Mwapang’onopang’ono, iye anailoza pa chifuwa changa, atakonzekera kundipha. ‘Musalase! Mwalakwa. Ine sindirinso wapolisi,’ ndinabwetuka motero.

“Ndiyeno ndinawona ankhondo achizembera owonjezereka khumi ndi aŵiri kumbuyo kwa nyumba. Mmodzi wa iwo​—mwamuna wojintcha wovala theŵera, malamba aŵiri odzala mpholopolo opingasana pachifuwa pake popanda malayapo, ndipo atagwiririra kasinja m’dzanja lake​—anamka patsogolo. ‘Iwe ukuti sulinso wapolisi. Chifukwa ninji?’ iye anafunsa motero. Mwamsanga ndinadzidziŵikitsa kuti ndine mmodzi wa Mboni za Yehova. ‘Mboni sizimanyamula mfuti,’ ndinalongosola motero, ‘chotero ndinasiya ntchito ya polisi ndipo tsopano ndikugwira ntchito ku Dipatimenti yowona Zankhalango. Ife tiri auchete mu ndale zadziko zonse,’ ndinawonjezera motero.

“Atamva kuti ndinali Mboni, nkhope yake inamasuka pang’ono. ‘Kodi ameneyu adzandikhulupirira?’ ndinalingalira. Kenako mng’ono wanga anafika. Mwamuna wovala theŵerayo, mwachiwonekere ndiye amene anali komandala, anayamba kumfunsa. Mbale wanga atatsimikiza zimene ndidanena, komandalayo anawonekera kukhala atakhutira. ‘Saka yu gon! (Tsitsa mfuti yako)’ iye analamula wankhondo wachizembera winayo. Ndinapepukidwa. ‘Zikomo, Yehova, ponditetezera!’ ndinapemphera motero.”

Masiku ochepekera pambuyo pake, Lumey analandira uthenga wina wochititsa mantha. Onyamula mfuti osadziŵika anali atapha maofesala apolisi atatu ku siteshoni ya polisi ya Tamanredjo, malo enieniwo kumene mkulu wa apolisi anali atalonjeza kumtumizako! “Ngati ndikananyalanyaza uphungu wa nkhani ya Nsanja ya Olonda imeneyo, panopa ndikanakhala wakufa,” akutero Lumey. Ndiyeno moyamikira akuwonjezera kuti: “Yehova amatetezeradi atumiki ake.”

Chikondi Chinamsonkhezera Kulanditsa Abale Ake

Pamene nkhondo inawulika pakati pa asilikali a boma ndi ankhondo achizembera mu tauni ya mgodi wa chiziro yotchedwa Moengo mu October 1986, Frans Salaoema, m’Negro Wamthengo wa zaka zakubadwa za kuma 40, anafunikira kusankha chochita. Pomalizira pake, iye, mkazi wake wokhala ndi mimbayo, ndi ana ake aamuna asanu ndi aŵiri, limodzi ndi ena ochokera ku tauniyo, anathaŵa kudzera mu tinjira ta m’nkhalango ndi kudutsa Mtsinje wa Maroni wotakatawo kuloŵa m’French Guiana ku chitetezo.

Frans, anali wovutikabe maganizo. Iye sanapeze Mboni zirizonse zochokera ku mpingo wake pakati pa othaŵawo. ‘Kodi iwo ali kuti? Kodi ndibwerere kukawafunafuna?’ iye analingalira. Koma kutero kukakhala kwaupandu. Unyinji wa omenya nkhondo yachizemberayo anali Anegro Amthengo. ‘Ngati asilikali a boma andiwona ndikumaloŵa mozemba kudzera pa nkhalango, ndidzathera pompo,’ iye anasinkhasinkha motero. Komabe, anasankha kubwerera kukafunafuna abale ake Achikristu. Anauza Mboni zingapo m’French Guiana kuti: “Mlungu wamawa, dzawolokeni mtsinje mudzandichingamire.”

Mlungu umodzi pambuyo pake iwo anapita kutsidyako, koma kunalibe Frans. Iwo anayembekeza kufikira tsiku lotsatira. Kunalibenso Frans. “Tiyeni tiyembekezere usiku wina umodzi,” iwo anatero. Ndiyeno Frans ndi gulu la Mboni anafika. Kodi chidachitika nchiyani?

“Pambuyo pa kupeza abalewo,” Frans anasimba, “tinawolokera pamalo omenyanirana nkhondo kwadzawoneni, tidaloŵa m’nkhalango ndi kuthaŵira chakumalire.” Koma kodi anachedweranji? Frans anasonya makatoni atatu amene adabwera nawo. Iye anali atapita kulikulu kukanyamula mtokoma wa mabukhu olongosola Baibulo kaamba ka Mboni zothaŵazo. Abale oyembekezerawo anakondwera. Tsiku lomwelo, Frans, Mboni zolanditsidwazo, ndi makatoni atatu anawoloka malire ali osungika.

Pambuyo pake Frans anapanga ulendo wina wokathandiza Mboni zowonjezereka. Pomalizira, Mboni 37 zidawoloka malire ndi kukhazikika m’misasa ya othaŵa. Frans anaikidwa m’chimene kale chinali chigawo cha akhate m’French Guiana, kumene othaŵa sayenera kuchita kanthu kali konse kusiyapo kuzendewera pamakama awo ndi kuyingitsa udzudzu.

Komabe, Frans ndi banja lake, sanali a manjalende. Mwamsanga atafika pamsasapo, Frans (amene pa nthaŵi ino analinso ndi mwana wina wamkazi) anatanganitsidwa m’kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu kwa anthu okanthidwawo. Chifukwa cha chisonkhezero chake chabwino, anali wokhoza kupatsidwa chilolezo kuyenda pa njinga ya moto kukalalikira m’misasa ina. Ndi chotulukapo chotani? Lerolino akuchititsa maphunziro Abaibulo 14 kwa othaŵa anzake. Atatu a iwo abatizidwa kale!

Iye Sanalolere Molakwa

“Ndidzabweranso m’mirungu iŵiri ndi zakudya zatsopano,” anatero Victor Wens, mpainiya wapadera wa zaka 58 zakubadwa. Anali kusiya mkazi wake ndi ophunzira Baibulo ena mu mudzi wa m’nkhalango cha pakati pa Suriname. M’menemo munali mu June 1987, pamene anali kupita kulikulu.

Pamene mkazi wa Victor ndi ena anatsazikana naye, matumba awo a mpunga anali pafupifupi opanda kanthu. Nkhondo ya chizembera inali itadula kufika kwa zakudya zonse. Mwamsanga kukakhala njala. Komabe, iwo anazindikira kuti ulendo wa Victor ndi mwadiya unali waupandu. Iye akanakhoza kufera cha pakati pa magulu olimbanawo kapena kukaikiridwa kukhala womenya nkhondo yachizembera. ‘Kodi iye adzabwerako mosungika?’ iwo anakaikira pamene injini ya mwadiya inazimiririka.

Mirungu iŵiri pambuyo pake, mkazi wa Victor maso anali ku mtsinje​—koma kunalibe chithunzi cha Victor. Mirungu yowonjezereka inapita. Chakudya chinatha, ndipo mkaziyo anadwala. “Chonde, Yehova, tetezerani mwamuna wanga,” iye anapemphera motero. “Abwereretu kuno!” Miyezi itatu inapita. Komabe Victor sanabwere. Kodi chinalakwika nchiyani?

“Atafika kulikulu,” akusimba motero Victor pambuyo pake, “ndinapatsidwa chilolezo cha kugula zakudya zotha miyezi isanu ndi umodzi ndi petulo. Ndiyeno ndinapempha phaso loti ndibwererere kumudzi. Ofesala woyang’anira anati: ‘Ungapite, koma kafufuze kumene ankhondo achizembera akubisala, ndiyeno ukabwerere udzatiuze.’ Mtima wanga unachita mantha. ‘Sindingachite zimenezi,’ ndinatinso, ‘Yehova samafuna kuti titenge mbali m’ndale zadziko. Ife Mboni ndife auchete.’ Iye anayankha kuti: ‘Ngati ziri choncho, sudzapita kumudzi.’

“Mlungu uliwonse ndinabwerera kukafunsira chilolezo, koma yankho linali lofanana. Pa nthaŵiyo, ndinamva kuti mkazi wanga anali kudwala. Ndidafuna kuti ndikanapita kumudzi ndi kukamusamalira. Komabe, sindinafune kulolera molakwa. Ndinasowa chochita.

“Pamene ndinapitanso kachiŵiri, ndinadabwa kuti iwo anati ungapite. Iwo anafotokoza kuti anali atapatsa chilolezo kwa apasitala ena Apentekosite ochokera ku chigawo cha kwathu kukhala pa ulendo wobwerera, ndipo ine ndikadapitira nawo limodzi. Ndinakondwera, ndinayamba kuchita makonzedwe kufikira nditamva kwa bwenzi lina kuti atsogoleri achipembedzo amenewo anali atavomera kukhala azondi. Chifukwa chakuti sindinafune kupereka chithunzi chakuti Mboni za Yehova zinali zogwirizana ndi kakonzedwe kameneko, sindinayende ulendowo. Kachiŵirinso ndinasoŵa chochita.”

Potsirizira pake akuluakulu a bomawo anazindikira kuti Victor sanali kufuna kulepa zikhulupiriro zake. Nthaŵi yotsatira imene anawafikira, anampatsa chilolezo.

Pomalizira pake, m’October 1987, kagulu kochepako ka Mboni kanamva injini ndipo kanawona mwadiya wodzazidwa ndi zinthu akufika. “Ndinamva chisoni pamene ndinawona mkazi wanga,” akusimba motero Victor. “Anali atawonda kwambiri. Komabe, iyenso anali wachimwemwe kuti sindinalolere molakwa.”

“Chosankha cholimba mtima cha Victor chakhala dalitso kwa ife,” akutero minisitala woyendayenda wogwirira ntchito kumidziko. “Akulu akulu a boma ndi omenya nkhondo yachizembera azindikira kuti Mboni za Yehova ziri zauchete. Tsopano amalemekeza mkhalidwe wathu, ndipo ntchito yathu ikupita patsogolo.”

Kukwatira pa Lachitatu, Kubatizidwa pa Loŵeruka

“Musakhale zitsiru,” anakakamiza motero achibale awo. “Musakwatire!” Amuna asanu ndi mmodzi a fuko la Aucaner Anegro Amthengo, ku ngondya ya kum’mwera cha kum’mawa kwa dzikolo, anazindikira malingaliro a achibale awo. Ndiiko komwe, mwambo wa fuko lawo umafunikiritsa kuti mwamuna sayenera kukwatira mwalamulo, kuchitira kuti akhoze kusiya mkaziyo nthaŵi iriyonse imene afuna. Komabe, kukhala ataphunzira kuchokera m’phunziro lawo la Baibulo lingaliro lawo la Yehova lonena za dama la chigololo, amuna amenewa anasintha malingaliro awo, nalaka chipsyinjo cha m’chitaganya, ndipo molimba mtima anapanga chosankha cha kukwatira mwalamulo.

Komabe, panali zopinga. Mikhalidwe ya nkhondo inachititsa kutsekedwa kwa Ofesi Yakawundula cha kumidzi, ndipo ulendo wopita ku likulu unali pafupifupi wosatheka. Akwatibwi amtsogolo asanu ndi mmodzi analinso ndi chikhumbo cha kuvala malaya eni eni a ukwati pa tsiku lawo la ukwati. Zimenezi zinasonyeza chikondwerero cha anthu a m’malowo ponena za kavalidwe kotero, ngakhale kuti diresi lotero siliridi chinthu chofunika kwa Akristu.b ‘Kodi tidzawapeza kuti madiresi aukwati m’nkhalango yokhuthalayi?’ anadabwa motero amunawo. Komabe, zosankha zolimba mtima zopangidwa mogwirizana ndi malamulo a makhalidwe abwino a Baibulo zinabweretsa madalitso. Pa Lachitatu, September 16, 1987, akwatibwi asanu ndi mmodzi ovala magawuni okongola ndi akwati asanu ndi mmodzi ovala masuti okongola anakwatirana. Kodi zinatheka motani?

“M’September, tinachita makonzedwe a msonkhano wachigawo mu St. Laurent, French Guiana, ndipo tinapempha Mboni za kumidzi kufikapo,” akulongosola motero Daniël van Marl, mmodzi wa aminisitala oyendayenda amene anakwatitsa maukwatiwo. “Msonkhano umenewo unapereka mpata wa maukwatiwo.”

Cecyl Pinas, chiŵalo cha Komiti Yanthambi chosamalira ntchito m’magawo a kumidzi akulongosola kuti: “Ndinakachezetsa banja la Beteli ku Netherlands kuchiyambiyambi kwa chakacho ndipo ndinawauza za maukwati amene analinkudzawo. Nditatchula mfundo yakuti tikagwitsira ntchito gawuni limodzi mobwerezabwereza, tikumasintha nthaŵi zonse kuti liyenerane ndi mkwatibwi wotsatira, alongo a pa Beteli anayi nthaŵi imodzi anandipatsa madiresi awo a ukwati monga mphatso kwa ‘alongo’ awo mu Suriname. Ndinagwidwa mtima kwambiri. Pambuyo pake, pa msonkhano wina mu Netherlands, magawuni owonjezereka anaperekedwa.”

Pa mamawa a tsiku laukwati, masinthidwe ena pa zovalazo anali ofunikirabe kupangidwa. “Mwamsanga tinakulitsa chiwuno cha madiresi ena ndi kusuntha kutalika kwa ena, koma tinamaliza pa nthaŵi yabwino,” akutero Margreet van de Reep.

Maukwatiwo atachitidwa, asanu mwa okwatirana chatsopanowo anali atakonzekera kaamba ka sitepi ina. Pa Loŵeruka la mlungu umodzimodziwo, iwo anabatizidwa mu Mtsinje wa Maroni. Iwo anali ofunitsitsa kubwerera monga okwatirana ku midzi yawo ya kunkhalango kukagawanamo m’ntchito ya kulalikira. Kodi Yehova anadalitsa chosankha chawo?

“Okwatirana amenewo anasonyeza chitaganyacho kuti Mbonife timagwiritsira ntchito zimene timalalikira,” akutero Nel Pinas, amene anayamba ntchito yolalikira m’gawo limodzimodzi limenelo mu 1967. “Chosankha chawo cha kukwatirana mwalamulo kuti akhale Akristu owona chadzutsa chikondwerero ku midzi yakutali. Tsopano Mboni kumeneko zikuyendetsa amwadiya awo m’mitsinje kumene sitinalalikireko konse kalelo, akumapeza anthu owonjezereka amene ali ofunitsitsa kuphunzira za Yehova.”

Ndithudi, zosankha zolimba mtima za Lumey, Frans, Victor, ndi ena ambiri zabweretsa madalitso olemerera kwa iwo eni ndi kwa Akristu anzawo m’Suriname ndi kwina kulikonse. Zokumana nazo zonga izi zimatsimikizira mobwerezabwereza kuwona kwa mwambi wa Baibulo wakuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola mayendedwe ako.”​—Miyambo 3:5, 6.

[Mawu a M’munsi]

a Wonani nkhani yakuti “Funafunani Mtendere ndi Kulondola” Nsanja ya Olonda ya January 1, 1984, masamba 17-24.

b Wonani “Maukwati Achikritsu Amene Amabweretsa Chisangalalo,” mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 1985, masamba 11, 12.

[Mapu/​Chithunzi patsamba 24]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

ATLANTIC OCEAN

GUYANA

SURINAME

PARAMARIBO

Tamanredjo

Moengo

St. Laurent

Maroni River

FRENCH GUIANA

BRAZIL

300 km

200 mi

[Chithunzi patsamba 25]

Mbali ziŵiri za Nyumba Yaufumu yabwino kwambiriyo kumadera a kumidzi a dzikolo

[Chithunzi patsamba 26]

Bwato lenileni losema mu Suriname

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena