Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 10/1 tsamba 27-29
  • ‘Akapanda Kumanga Nyumba Yehova . . . ’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Akapanda Kumanga Nyumba Yehova . . . ’
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kumanga Nyumba
  • Kumanga Banja Kwachipambano
  • Kuphunzirira pa Ntchito
  • Khalani ndi Cholinga cha Chigwirizano Chaumodzi wa Banja
  • Kumanga Banja Lolimba Mwauzimu
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Kukwaniritsa Udindo wa Kusamalira Banja
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Banja Lachikristu Limachitira Zinthu Pamodzi
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Mabanja Aakulu Ogwirizana Potumikira Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1999
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 10/1 tsamba 27-29

‘Akapanda Kumanga Nyumba Yehova . . . ’

MOSASAMALA kanthu za kumene mukukhala, pali malo amene, inu, mumawatcha kwanu. Mitundu ya nyumba zokhalamo ndi njira zozimangira zimasiyana kambiri. Nyumba za dothi, za mitengo, za konkire​—ndandanda ikuwoneka kukhala yosatha. Ena amamva kukhala okondwa m’nyumba yaudzu monga mmene ena amachitira m’nyumba zamataya. Kodi nchifukwa ninji izi ziri choncho?

Kumasuka mokondwa, kukhala wokhutira, kumadalira kwakukulukulu pa atsamwali a munthuwe. (Miyambo 18:24) Mosasamala kanthu za zonyezimira ndi zokongola zimene dziko limapereka, kwanu ndiko kumene munthuwe mwachibadwa umatembenukira kaamba ka mtendere ndi chisangalalo. Komabe, titapenda mothandizidwa ndi maripoti a moyo wamakono wakwathu, palibe chitsimikiziro chakuti munthuwe nthaŵi zonse udzapeza mtendere ndi chisangalalo kwanuko. Ku mlingo wokulira, amene mumakhala nawo​—banja lanu​—angagawane nanu mtendere wanu kapena kuuwononga. Pamenepa, kodi nchiyani chimene chiri chinsinsi cha kumanga nyumba yachimwemwe, ndi yamtendere?

Kumanga Nyumba

“Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwira ntchito chabe,” likutero vesi loyamba la Salmo 127. Otengamo mbali m’kumanga nyumba zolambiriramo Mulungu wowona, Yehova, amapeza chimenechi kukhala chowona. Ngakhale kuti antchito aukatswiri amapereka mwaufulu nthaŵi yawo ndi zoyesayesa zawo kumanga mofulumira Nyumba Zaufumu zokongola, liri dalitso la Yehova limene limatsimikizira chipambano. Kaŵirikaŵiri ngakhale openyerera angawone kuti chinthu chachilendo chikuchitika. Mwachitsanzo, magazine ena anasimba imodzi ya nyumba zoterozo mu Colchester, Ingalande, ikumagwiritsira ntchito mutu wakuti “Yehova Akutukula Tsindwi.”

Komabe, chipambano m’zochitika zina kuwonjezera pa ntchito zomanga zenizenizo chimadalira pa dalitso la Yehova. Lingalirani mawu a Solomo mu vesi lachitatu la Salmo 127: “Tawonani, ana ndiwo cholandira cha kwa Yehova; chipatso cha m’mimba ndicho mphotho yake.” Yehova alinso katswiri Womanga wopambana onse pa zokhudza mabanja, ndipo makolo ali ndi mwaŵi wodabwitsa wa kukhala antchito anzake, kapena ogwirizana naye.a (Ahebri 11:10) Kodi makolo Achikristu angapindule motani ndi mwaŵi wa kugwirira pamodzi umenewu ndi kumanga mwachipambano banja lachimwemwe, ndi la mtendere, lomwe lidzabweretsa ulemu kwa Mlengiyo, Yehova Mulungu?

Kumanga Banja Kwachipambano

Chinthu chofunika kwambiri m’kamangidwe kachipambano ndicho kulinganiza kwabwino, kapena chitsanzo cholembedwa. Kuti mupange atamandi achichepere a Mulungu, palibe chitsanzo cholembedwa chabwinopo koposa Mawu ake owuziridwa, Baibulo. (2 Timoteo 3:16, 17) “Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo,” analemba motero Solomo. (Miyambo 22:6) “Njira yake” iri njira ya Yehova, ndipo pamene makolo aitsatira, amapereka kwa achichepere awo chiyembekezo cha kukhala atumiki okhulupirika a Mulungu.

Nyumba yolimba imafuna mirimo yabwino. Mlendo wina wa ku Afirika ku Yuropu anakupeza kukhala kovuta kukhulupirira kuti nyumba zina zimene anawona zinali ndi zaka mazana angapo zitamangidwa. Chinali chidziŵitso chachilendo kwa iye kuwona mirimo yokhalitsa yogwiritsiridwa ntchito m’nyumba zimenezi. Ku mbali ina, pamene omanga achepetsa mirimoyo, kaŵirikaŵiri zotulukapo zake zimakhala zangozi, ngakhale zakupha. Zimenezi zingakhalenso zofanana m’kulera ana.

Pa nthaŵi ya kutenga mimba, ana amalandira cholowa chamajini chokhala ndi kupanda ungwiro chifukwa cha uchimo. (Salmo 51:5) M’mawu ena, iwo amaipitsidwa kuyambira pa chiyambi penipeni. Makolo Achikristu ayenera kulimbana ndi zimenezi mwa kuyesayesa kukulitsa mwa ana awo, mikhalidwe yaumulungu yokhalitsa. (1 Akorinto 3:10-15) Kusiyapo ngati zimenezi zichitidwa, mosasamala kanthu zakuti makolo akugwira ntchito zolimba m’mbali zina, zonga ngati kupezera ana awo aamuna ndi aakazi zakudya zabwino, zovala, ndi nyumba, zoyesayesa zawo za kumanga zidzakhala zachabe.

Ndicho chifukwa chake chilangizo cha Mulungu kwa makolo, makamaka atate, nchakuti: “Ndipo atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha [Yehova, NW].” (Aefeso 6:4) Maleredwe ndi chilangizo cha Yehova zimaloŵetsamo zitsanzo zolembedwa zabwino koposa ndi mirimo. Kuzigwiritsira ntchito kudzatulukira m’madalitso osatha kaamba ka banja lonse.

Kuphunzirira pa Ntchito

Mosasamala kanthu za maplani olembedwa bwino, nthaŵi zonse pamakhala mavuto osayembekezereka mkati mwa nthaŵi ya kumanga kulikonse. Mofananamo, makolo ayenera kuphunzira kuyembekezera mavuto osayembekezereka m’moyo wa tsiku ndi tsiku wa ziŵalo za banja ndi kukhala okonzekera kuchita nawo. Kodi chimenechi chingachitidwe motani?

Kukambitsirana kwabwino pakati pa makolo aŵiri kuli kofunika. Pamene atate ndi amayi akambitsirana mwapemphero za kupita patsogolo kwa achichepere, adzapeza mbali zoyenerera chiyamikiro ndi zina zofunikira “kumanga” kowonjezereka. Pamene zofooka zoterozo zadziŵika, makolowo angachitire pamodzi ndi kuchitapo kanthu moyenerera kuzithetsa.

Komatu mwinamwake inu muli ndi banja lalikulu, ndipo mungadabwe kuti: ‘Kodi tingachititse motani zoyesayesa zathu kuyenerera zosoŵa za mmodzi ndi mmodzi wa ana athu ambiriwo?’ Bwanji osapereka maphunziro a pa ntchito kotero kuti ana anu athandizane? Ophunzira ntchito amatumikira kwa zaka zambiri akuphunzira maluso mogwirira pamodzi ndi akatswiri aluso. Mwinamwake pa phunziro lanu labanja, mungayese kupempha ana anu achichepere kulongosola zinthu zina kwa ocheperapowo. Kuwona mtima, kusankha mabwenzi, kukaniza zisonkhezero zoipa ku sukulu, ndi zina zotero, ziri nkhani zimene ponse paŵiri ana achikulire ndi ochepera angasimbe bwino lomwe. Mwa kugawira ana okulirapowo kusimba zochitika zenizeni zoterozo, mungathandize kuwaphunzitsa kukulitsa mphamvu zawo za kuganiza ndi luso lophunzitsa pamene akuphunzitsa ocheperawo zimene afunikira kudziŵa. (Ahebri 5:14) Zimenezi ziri ndi phindu lowonjezereka la kukulitsa chibale chowona pakati pa ana.

Mwinamwake banja lanu n’laling’ono, lokhala ndi mwana mmodzi yekha. Pamenepo, muli ndi mwaŵi wochuluka wofuna kudziŵa ndi kuzindikira mwana wanu. Komabe, peŵani ngozi ya kuwononga mwana wanu mwa kupereka chisamaliro chopambanitsa kwa iye. Nonsenu muli atatu, kodi sichoncho? Chotero chitirani zinthu pamodzi. Zimenezi zidzamthandiza kukambitsirana ndi ena ndi kupereka chisamaliro kwa ena, mwakutero kumchinjiriza iye kusakhala wodzigangira.

Khalani ndi Cholinga cha Chigwirizano Chaumodzi wa Banja

Ndithudi, pali zowonjezereka pa kumanga banja kuposa kuchititsa phunziro la Baibulo ndi kupereka uphungu ndi chilango. Solomo ananena kuti: “Kodi sichabwino kuti munthu adye namwe, nawonetse moyo wake zabwino m’ntchito yake?” (Mlaliki 2:24) Mosakaikira banja lanu limasangalala ndi chakudya pamene chaphikidwa bwino. Kodi mumalinganiza kudyera pamodzi chakudya chanu monga banja? Zimenezi sizingakhale zothekera nthaŵi zonse pamene ziŵalo zina zabanjalo ziri kuntchito, kusukulu, kapena kukachita zinthu zina. Komabe, kaŵirikaŵiri pali chakudya chimodzi pa tsiku chimene mungadyere pamodzi monga banja. Kodi nchiyani chimene chingathandizire kukhalapo kwa mkhalidwe wabwino pa chakudya cha banja?

Mbale wina amadzutsa funso la Baibulo pa nthaŵiyo kuti onse alipo akambitsirane. Ndithudi, iye amapeŵa kuchititsa manyazi awo amene angakhale osadziŵa yankho. Ena amasimba zokumana nazo zauminisitala wakumunda. Mwa kupereka chisamaliro ku nkhani zauzimu, nthaŵi za chakudya zimakhala nthaŵi zolimbikitsira banja lonse. (Wonani Aroma 14:19.) Ndithudi, m’mbali zina za dziko, sichamwambo kukambitsirana kwambiri panthaŵi yachakudya. Komabe, kuyesayesa kwamphamphu kusunga mkhalidwe wachimwemwe kuli kofunika. Miyambo 15:17 imati: “Kudya masamba, pali chikondano, kuposa ng’ombe yonenepa pali udani.”

Kusanguluka ndi kupuma zirinso ndi malo ake mu umoyo wabanja Lachikristu. Makolo anzeru amagwiritsira ntchito nthaŵi zoterozo kumanga banja lolimba lateokratiki. Motani?

Pamene kuli kwakuti nkosavuta kulola achichepere kupita ndi kukafunafuna zowakondweretsa, zimenezi ziri ndi ngozi. Mwachitsanzo, kungakhale kupanda nzeru kotani nanga kulola achichepere kuphatikizidwa mwakuya m’maseŵera opereka chiwopsyezo ku moyo kapena chiŵalo chathupi! (1 Timoteo 4:8) Ku mlingo wothekera, sankhani zochita zoloŵetsamo chiŵalo chirichonse cha banja. Atate angapemphe malingaliro awo ndi ziganizo ndi kugawira aliyense mbali yochita kukonzekera.

Kodi inu monga banja mungakulitse chikondi chanu ndi kuitana ziŵalo zina za mpingo kugawanamo zisangalalo za banja lanu? Kaŵirikaŵiri ziŵalo zokalamba za mpingo zimasangalala kugawana chikondwerero chabanja, makamaka pamene mabanja a iwo eni sali panyumba kapena sakhala ndi moyo mogwirizana ndi malamulo a makhalidwe abwino Achikristu. (Yakobo 1:27) M’mipingo yambiri, pali mabanja a kholo limodzi. Mwakulingalira bwino umutu wateokratiki ndi kulemekeza maumunthu Achikristu, akulu ndi ena angapereke mthunzi wauzimu ku ziŵalo za mabanja oterowo. (Yesaya 32:1) Ana “amasiye” ambiri achita bwino kukhala mitu ya banja yokhazikika monga chotulukapo cha chikondwerero chachikondi chosonyezedwa ndi wachikulire mwauzimu Wachikristu.​—Salmo 82:3.

Kumanga banja Lachikristu ndiko ntchito yakalavulagaga. Koma mwa chithandizo cha Yehova, mudzafikiradi pa kuyamikira kuti “ana ndiwo cholandira cha kwa Yehova; chipatso cha m’mimba ndicho mphotho yake.” (Salmo 127:1, 3) Iwo angakhale magwero a chitamando osati kokha kwa makolo Achikristu komanso kwa Mlengi wawo, Yehova Mulungu.

[Mawu a M’munsi]

a M’chenicheni, mawu Achihebri otanthauza ‘omanga’ (vesi 1) ndi “ana” (vesi 3) onse aŵiri akulingaliridwa kukhala ochokera ku tanthauzo lamaziko lakuti “kumanga.” Ndiponso, m’Chihebri liwu lakuti “nyumba” lingatanthauze kaya “malo okhala” kapena “banja.” (2 Samueli 7:11, 16; Mika 1:5) Motero, kumanga nyumba kuli kogwirizanitsidwa ndi kulera banja. Dalitso la Yehova liri lofunikira m’zochitika zonse ziŵirizi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena