Kodi Helo Ngotentha?
“PA NTHAŴI inayake m’ma 1960, Helo anazimiririka.” Adatero mkonzi Wachibritish David Lodge m’bukhu lake lakuti Souls and Bodies, ndipo mawu ake amasonyeza kulingalira kwa Akatolika ndi Aprotesitanti ambiri mkati mwa zaka makumi angapo pambuyo pa nkhondo ya dziko yachiŵiri. Kwakanthaŵi, matchalitchi ambiri aakulu anafooketsa chiphunzitso chawo chalamulo cha helo wamoto m’zoyesayesa zawo za kusinthira ku dongosolo la kalingaliridwe lamakono.
Lingaliro lakuti pamakhala chilango pambuyo pa imfa linali losalandirikadi kwa anthu chifukwa chakuti ganizo la chimo lenilenilo linakhala lozimiririka m’maganizo mwawo. Pamene anafunsidwa mu 1984, Kadinala Ratzinger wa ku Roma ananena kuti: “Kutsungula kwathu . . . kumasumika maganizo pa mikhalidwe yovuta ndi kudzikhululukira m’kuyesera kuchotsera anthu lingaliro la liwongo, la chimo . . . , zenizeni zimenezo pa zimene chikhulupiriro cha helo ndi Purigatoriyo chiri chogwirizana nazo.”
Kodi nchotheka lerolino kukhulupirira m’kukhalapo kwa chimo popanda kuvomereza chiphunzitso cha chilango pambuyo pa imfa mu purigatoriyo ndi helo? Bukhu laposachedwapa, Abrégé de la foi catholique (Chidule cha Chikhulupiriro Chachikatolika), lolongosoledwa ndi Kadinala Wachifalansa Decourtray, limalemba funsolo mwachindunji kuti: “Kodi nchoyenerera kukhulupirira helo?” Yankho liri lakuti: “Nchosatheka kuchotsa funso lochititsa mantha la helo.” Bukhu lakuti Vatican Council II—More Postconciliar Documents (1982) likugwira mawu “Chikhulupiriro cha Anthu a Mulungu” kukhala likunena kuti: “Timakhulupirira . . . [kuti] awo amene avomereza ku chikondi ndi chifundo cha Mulungu adzapeza moyo wamuyaya. Awo amene amazikana adzaponyedwa m’moto womwe sudzazimidwa konse.”
Chotero, mosasamala kanthu za zoyesayesa zonse za maphunziro a zaumulungu za kutsimikizira zosiyanako, moto wa helo udakali mbali yaikulu ya chiphunzitso choikidwiratu Chachikatolika. Komabe A New Dictionary of Christian Theology (1983) ikunena ponena za “kunyazitsidwa” ndi “kusoŵa mtendere” kumene chiphunzitso cha chilango chamuyaya chimapangitsa ziŵalo zambiri za matchalitchi a Dziko Lachikristu lerolino. Iwo amavutika m’kugwirizanitsa chiphunzitso choikidwiratu chimenechi ndi lingaliro la Mulungu wachikondi. Iwo amazizwa kuti: ‘Kodi helo ngotentha alidi chiphunzitso Chachikristu ndi Chabaibulo? Ngati ayi, nkuti komwe chinachokera?’
[Chithunzi patsamba 3]
Bourges Cathedral, Falansa