Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 9/15 tsamba 32
  • “Munali Mulungu Amene Ndinali Kufunafuna”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Munali Mulungu Amene Ndinali Kufunafuna”
  • Nsanja ya Olonda—1989
Nsanja ya Olonda—1989
w89 9/15 tsamba 32

“Munali Mulungu Amene Ndinali Kufunafuna”

Kuti? Kodi munthuyo anali kulankhula za chiyani?

Nkhaniyi imabwerera m’mbuyo pamene mphatso inaperekedwa ya bukhu la Life​—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? Bukhulo linaperekedwa kwa woleka ntchito ya uphunzitsi wa zofukula m’mainja wa ku Sipanya. Pambuyo pake, pamene munthu wopereka mphatsoyo anali kucheza ku Sipanya, mphunzitsi woleka kugwira ntchito ameneyu anati: “Edwin, zikomo chifukwa cha kutumiza bukhu lija. Ndinaliŵerenga komano ndinalipatsa mnyamata wina wachichepere wa Chisipanya.”

Msipanya wachichepere ameneyo anali wogwiritsira ntchito anam’goneka, wa ndevu ndi tsitsi lalikulu. Komabe, pamene mnyamatayo analandira bukhulo, mnyamatayo anali ndi masinthidwe aakulu. Iye anameta ndevu zake, ndi tsitsi lake, ndi kuleka kugwiritsira ntchito anam’goneka. Atamva zimenezi, Edwin analakalaka kukumana naye.

Atakumana ndipo mnyamatayo atamva kumene bukhulo linachokera, iye anakupatira Edwin ndi kunena kuti: “Kwa zaka zisanu ndakhala ndikufunafuna Mulungu, ndipo pamene ndinatsegula bukhulo, munali Mulungu amene ndinali kufunafuna.” Mnyamatayo adapanga kupita patsogolo ku mlingo wa kugawana chikhulupiriro chake chopezedwa chatsopano ndi ena.

Tilingalira kuti nanunso mungapindule ndi bukhu labwino koposa limeneli lomwe layambukira miyoyo ya anthu mopindulitsa. Inu mungalandire kope la bukhu losanthulidwa mosamalitsa limeneli mwa kulemba ndi kutumiza kapepala pansipa limodzi ndi K48 yokha.

Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, bukhu lachikuto cholimba, lamasamba 256 la Life​—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? Ndatumiza K48 (Zambia).

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena