Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 6/1 tsamba 25-27
  • Kupeza Ufulu pa “Chisumbu cha Anthu Osungulumwa”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupeza Ufulu pa “Chisumbu cha Anthu Osungulumwa”
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • “Chisumbu cha Anthu Osungulumwa”
  • Wandende, komabe Womasuka
  • Mboni pa San Lucas
  • Ufulu Wowona Pomalizira
Nsanja ya Olonda—1989
w89 6/1 tsamba 25-27

Kupeza Ufulu pa “Chisumbu cha Anthu Osungulumwa”

BWATO loyenda kupyola m’mafunde aang’ono a Gulf ya Nicoya silinali lodzala. Ngakhale ndi tero ichi sichinali chifukwa cha kupereŵera kwa alendo ocheza. Pano pa gombe la Pacific la Costa Rica, thambo lopanda mitambo, madzi obiriŵira, doko la mchenga woyera, ndi mitengo ya ngole yondenguma silinalephere konse kucheutsa aja otsatira paradaiso ya kumalo otentha. Koma ine sindinali kuno pa tchuthi​—ndipo osatinso ngakhale ena okweramo.

“Chisumbu cha Anthu Osungulumwa”

Tinali kupita ku Chisumbu cha San Lucas, dziko lolangirako lolamulidwa ndi dziko lina lotsogozedwa ndi Bungwe la Chilungamo la ku Costa Rica. Pa nthaŵi ina, Chisumbu cha San Lucas chinali imodzi ya ndende za mbiri yoipa mu Latin America. Apandu owuma mitu anapanga mbali yaikulu koposa ya chiŵerengero chake cha anthu, ndipo awo otumizidwa kuno mwamsanga anaphunzira zenizeni zolimba za kupulumuka. Aulamuliro anapereka zofunikira wamba, pamene kuli kwakuti akaidi anakhazikitsa dongosolo lawo la ulamuliro ndi kumenyera kuwongolera mwaŵi wawo waumwini. Kaŵirikaŵiri, awo omwe anayesera kuthaŵa anakokedwera ku nyanja ndi madzi oyenda amphamvu, kapena kuphedwa ndi nsomba zazikulu zotchedwa shark.

Kuchiyambi kwa ma 1950, yemwe kale anali mkaidi pa Chisumbu cha San Lucas, José León Sánchez, analemba bukhu lozikidwa pa moyo wake waumwini m’dziko lolangirako lolamulidwa ndi dziko lina. Nkhani yake, yolunjika, ya nkhalwe, koma yeniyeni, La Isla de los Hombres Solos (Chisumbu cha Anthu Osungulumwa), mwamsanga inadzakhala yogulidwa koposa mu Mexico ndi Central America. Mu Costa Rica iyo inadzutsa phokoso la unyinji.

Pa nthaŵiyo, bomalo linali m’njira ya kukonzanso malo ake a olangira. Chigogomezero chinaikidwa pa kusintha mmalo mwa chilango, ndipo chilango cha imfa chinachotsedwa. Ndi chisamaliro chosonkhezeredwa ndi bukhu la Sánchez, kusintha kunabweranso ku Chisumbu cha San Lucas. Andende anaphunzitsidwa kuŵeta ng’ombe ndi nkhumba, kusodza nsomba, ndi maluso ena a umisiri. Iwo analimanso mbewu zogulitsa ndipo analoledwa kutengamo mbali mu phindu lopezedwa. Kuwongolera nakonso kunapangidwa m’nyumba zokhalamo. Podzafika ku chiyambi kwa ma 1960, San Lucas inadzakhala malo apakati a kusintha a chitsanzo kaamba ka akaidi oyang’aniridwa mochepera.

Pamene ndinatuluka m’bwatolo kutsikira pa doko laling’ono, ndinali wodziŵa bwino lomwe za mbiri yoipa ya chisumbucho. Koma ine ndinali pano monga mlonda wa ndende, osati monga wandende. Ndinayamba kugwira ntchito ndi National Police Force pamene ndinali wa zaka 18, ndipo chifukwa chakuti ndinali wamkulu kaamba ka msinkhu wanga, ntchito yanga yoyambirira inali ntchito ya ulonda pa Chisumbu cha San Lucas.

Wandende, komabe Womasuka

Woleredwa ndi avirigo a Chikatolika ndi ansembe, nthaŵi zonse ndinali wochititsidwa mantha ndi lingaliro la helo wotentha. Kwa ine, chinthu chofunika koposa m’moyo chinali kupeŵa kukathera mu helo. Koma ndinadabwitsidwa kuwona kuti anthu ambiri koposa anawoneka kukhala osasamala kwenikweni ponena za icho. Wansembe angalankhule ponena za icho m’kalasi, koma kunja kwa kalasi, palibe aliyense anafuna kulankhula ponena za chipembedzo kapena Baibulo. Iwo anadzinenera kukhulupirira m’helo wamoto, koma chimenecho chinachita zochepera kuletsa khalidwe lawo.

Mkhalidwe pa San Lucas sunali wosiyana kwambiri. Ngakhale kuti ambiri a alonda ndi akaidi ananenera chikhulupiriro chimodzimodzicho, chinawoneka kukhala ndi chiyambukiro chochepera pa iwo. Kalankhulidwe kotukwana ndi machitachita odetsedwa zinali zofala. Nthaŵi ina mlonda mnzanga anagwidwa akuba chamba kuloŵetsa pa chisumbucho ndipo anathera kukhala mkaidi iye mwiniyo! Woyang’anira wanga wachifupi anali wokwiya msanga wowopsya ndipo kaŵiri anatokosa kumenyana zibakera ndi akaidi. Popeza ndinali nayo nthaŵi kwa inemwini, kaŵirikaŵiri ndinalingalira mwakuya ponena za zinthu zimene ndinali kuwona pa chisumbucho. Monga mwamuna wachichepere wosazoloŵera, ndinali wosokonezeka ndi wokhumudwitsidwa.

Madzulo ena, Franklin, mkaidi wodalirika, anandiitanira kumvetsera ku kukambitsirana kwa Baibulo. Ngakhale kuti sindinali wokondwerera kwambiri, mwamsanga kukambitsirana kunakula.

“Chiyenera kukhala chovuta kukhala wandende ndi kuphunzira Baibulo,” ndinachitira ndemanga tero. Sindinaiwale konse yankho la Franklin.

“Mwakuthupi ndiri wandende,” iye anatero, “koma mwauzimu ndiri womasuka.”

Ndimotani nanga mmene ine ndinafunira kumvetsetsa mtundu wa ufulu umenewo!

Mboni pa San Lucas

Chinadzatembenuka kuti Franklin anali kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Pa masiku a Sande, achibale ndi mabwenzi anali kuloledwa pa chisumbucho. Kaŵirikaŵiri, mabwato aŵiri kapena atatu ankabweretsa Mboni zochulukira kufika ku 30 kudutsa chigwegwe (bay) cha nyanja kuchokera ku Mpingo wa Puntarenas. Pokhala watsopano kumeneko, ndinali wodabwa kuwona nduna zikumangopereka chilolezo kwa Mboni kupita pamalo ofufuzira pamene wina aliyense anafufuzidwa kotheratu. Ngakhale chodabwitsa mowonjezereka kwa ine chinali chenicheni chakuti Mboni zinachita mwaulemu kwa akaidi ndi alonda mofananamo ndipo zinalankhula kwa aliyense ponena za uthenga wawo wozikidwa pa Baibulo.

Akaidi oŵerengeka anali ndi maphunziro a Baibulo aumwini, okhazikika ndi Mbonizo pa masiku a Sande amenewa. Franklin anali mmodzi wa iwo, ndipo panali chinachake ponena za iye chimene chinandikondweretsa ine. Ndinaphunzira kuti Franklin anali ataweruziridwa ku chilango cha zaka 12 m’ndende chifukwa cha kupha wopikisana naye wa malonda. M’ndendemo iye anaphunzira za maakaunti mwa kulemba makalata. Chifukwa chakuti iye sanali kumwa, kusuta, kapena kugwiritsira ntchito anam’goneka, iye anaikidwa pa chiyang’aniro cha laibulale ya ndendeyo. Pambuyo pake, iye anapatsidwa chipinda cha iyemwini ndipo ngakhale thayo lowonjezereka.

Akali ku sukulu, Franklin anali atakhala ndi mabwenzi omwe anali Mboni za Yehova. Iye anadziŵa kuti iwo sanadziloŵetse konse m’mikangano kapena ndewu, ngakhale pamene ena anawayamba iwo. Ngakhale kuti sanatenge chipembedzo mosamalitsa, iye anadziŵa Mboni kukhala anthu a mtendere ndi a makhalidwe oyera. Chotero pamene iye anamva kuti kunali Atalaya (“Wachitawala,” monga mmene ena anatchera Mboni za Yehova) pakati pa akaidiwo, iye anakhala wolakalaka kudziŵa.

Tsiku lina chakudya chamasana chisanakhale, Franklin anawona wandende atakhala yekha kunja kwa nyumba yodyeramo. Mawonekedwe ake audongo anapangitsa Franklin kufunsa ngati iye anali Atalaya. Pamene iye anawuzidwa kuti iye analidi, kachitidwe koyambirira ka Franklin kanali kakuti: “Nchifukwa ninji iwe uli pano?” Mwamunayo analongosola kuti choyamba iye anaweruzidwira ku Ndende Yokhaulitsira Yapakati mu San José, likulu, ndipo anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova pamene anali kumeneko. Pambuyo pa kusamutsidwira ku San Lucas, iye anapitirizabe maphunziro ake ndi Mboni yochokera ku Puntarenas. M’kupita kwa nthaŵi iye anabatizidwa kumeneko pa Coco Beach pa Chisumbu cha San Lucas.

Kukumana kumeneko kunali posinthira m’moyo wa Franklin. Kuchokera nthaŵi imeneyo kumkabe mtsogolo, nthaŵi iriyonse pamene Mboni zinabwera kudzacheza, iye ankaziloŵetsa izo m’kukambitsirana kwaumoyo. Iye anayambanso kulankhula kwa akaidi ena ndi alonda ponena za zinthu zimene iye anali kuphunzira. Mkhalidwe wake, kavalidwe, ndi kapesedwe zinayamba kuwongokera. Onse aŵiri iye ndi mnzake wobatizidwa anapeza ulemu wa aliyense.

Potsirizira pake, chiweruzo cha Franklin cha zaka 12 chinachepetsedwa ku zaka 3 ndi miyezi 4. Iye ndi mnzakeyo anapitirizabe kuphunzira Baibulo. Mosasamala kanthu za mkhalidwe woipa m’ndende, iwo anali achimwemwe, ndipo nkhope zawo zinasonyeza icho. Mwachiwonekere iwo anadziŵa kuti ine ndinali wosiyana kuchokera kwa alonda ena, popeza kuti sindinatengeko mbali mu ziphwete zodetsedwa ndi njerengo zodetsedwa. Chotero iwo anandiitanira ine ku zipinda zawo kaamba ka kukambitsirana kwa Baibulo. Zomwe ndinamva kuchokera kwa iwo ndi kuchokera kwa Mboni zochezerazo zinali zokondweretsa kwambiri kwa ine, makamaka ponena za mkhalidwe wa akufa ndi kuti m’chenicheni kulibe helo yotentha. Ndinapatsidwa kope la bukhu la Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya ndi kuyamba kuliŵerenga ilo. Ngakhale kuti sindinazindikire icho nthaŵi imeneyo, mbewu za chowonadi zomwe pambuyo pake zikatulutsa chipatso zinali kufesedwa mu mtima mwanga.

Ufulu Wowona Pomalizira

Pambuyo pa kusiya National Police Force, ndinakhala mwachidule mu Miami, Florida. Tsiku lina wogwira ntchito mnzanga anayamba kulankhula kwa ine ponena za Baibulo. Kalankhulidwe kake, kavalidwe, ndi kapesedwe zinandiwuza ine kuti ndinakumana ndi Mboni za Yehova kachiŵirinso. Ichi chinabwezera ku chikumbukiro changa Chisumbu cha San Lucas, ndipo ndinamfunsa iye chifukwa chimene palibe aliyense anawoneka kukhala wokondweretsedwa m’kukambitsirana zinthu zauzimu. Iye anandipatsa yankho lachidule ndi kulingalira kukambitsirana m’nyumba yanga. Chimenechi chinatsogolera ku phunziro la Baibulo lokhazikika ndipo pambuyo pake kudzipereka ndi ubatizo.

Ndinabwerera ku Costa Rica mu 1975 ndi kupezekapo pa msonkhano wachigawo mu San José. Ndidakali wosatsimikiza za yemwe anali wodabwitsidwa koposa pamene Franklin ndi ine tinakumana mwamwaŵi pa msonkhanowo. Iye tsopano anali womasuka mwa kuthupi ndiponso wobatizidwa. Pamene ndinasiya San Lucas, Franklin sanali wotsimikiza za mmene chikondwerero changa m’Baibulo chinaliri cholimba. Koma tinalipo, wandende wakale ndi yemwe anali mlonda, mowonadi ogwirizana mu ufulu umene umabwera kuchokera ku kulambira Mulungu wowona Yehova!

Kwa ena “Chisumbu cha Anthu Osungulumwa” cholangirako chinatanthauza kokha zikumbukiro zoipa. Kwa ine chinatanthauza chiyambi cha ufulu wauzimu. Tsopano, monga mkulu Wachikristu, ndimatengamo mbali m’kubweretsa ufulu kwa awo omwe amaganiza kuti ali omasuka koma omwe m’chenicheni ali m’ndende monga mmene analiri amuna aja omwe ndinali kulonda pa nthaŵi ina.​—Monga momwe yasimbidwira ndi David Robinson.

[Mapu patsamba 25]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Nicaragua

CARIBBEAN SEA

Costa Rica

Puntarenas

Gulf of Nicoya

San José

PANAMA

PACIFIC OCEAN

Km 0 50 100

mi 0 50 100

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena