Chidziŵitso pa Nyuzi
“Kuyang’ana Kwachiŵiri”
Genesis 1:1 imanena kuti: “Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.” Kwa nthaŵi yoposa zana limodzi, asayansi omwe amayanja nthanthi ya chisinthiko asuliza vesi limeneli la Baibulo. Ngakhale kuli tero, “ambiri a iwo tsopano akutenga kuyang’ana kwachiŵiri pa nkhani ya kuchiyambi kwenikweni, yamphamvu kwenikweni kaamba ka kukhalako kwa Mlengi,” ikusimba tero The Orange County Register, nyuzipepala ya ku California.
Mwachitsanzo, nkhaniyo ikudziŵitsa chomwe chikunenedwa ndi katswiri wa zolengedwa zamoyo Michael Denton m’bukhu lake Evolution: A Theory in Crisis. Iye akusungirira kuti kuchokera pa nthaŵi imene Darwin anafalitsa bukhu lake lakuti On the Origin of Species kufikira tsopano, sipanakhale chidutswa nchimodzi chomwe cha umboni wochirikiza nthanthi ya Darwin.
Mofananamo, Register ikugwira mawu bukhu lakuti The Mystery of Life’s Origins: Reassessing Current Theories, lolembedwa ndi asayansi atatu. Mogwirizana ndi pepalalo, iwo akulongosola kuti moyo sukanayamba mwamwaŵi ndipo “akutsutsa kuti ‘Mlengi kupyola m’thambo’ ali kalongosoledwe kowona kokha ka chiyambi cha moyo.” Kuchirikiza lingaliro limeneli, nkhaniyo ikutchula kuti katswiri wa zakuthambo wa ku Britain Fred Hoyle “wagwidwa mawu mofala kaamba ka ndemanga yakuti kukhulupirira kuti selo loyambirira linayambika mwamwaŵi kuli kofanana ndi kukhulupirira kuti kavuluvulu womasesa kupyola malo osungira zinthu odzala ndi zidutswa za ziwiya za ndege akakhoza kupanga ndege ya Boeing 747.”
Kwa unyinji wa asayansi, umboni wa kuchirikiza Kupangitsidwa ndi Wokulira uli wosalakwika. Koma bwanji ponena za awo omwe amaumirira kukana kukhalapo kwa Mlengi? Anthu oterowo akachita bwino kulingalira mawu awa olembedwa ndi mneneri Yesaya: “Ozolitsa inu! Kodi woumba adzayesedwa ngati dothi; kodi chinthu chopangidwa chinganene za iye amene anachipanga, iye sanandipange ine konse?”—Yesaya 29:16.
Kupambanitsa Kwakupha
Mu January wa chaka chino, wakupha wotchuka Theodore Robert Bundy, anaikidwa mu mpando wamagetsi mu Ndende ya Boma la Florida ndi kuphedwa. Iye anagwirizanitsidwa ndi imfa zankhalwe za akazi ochulukira kufika ku 36, ngakhale kuti maulamuliro akulingalira kuti chiŵerengerocho chingakhoze kukhala chachikulu kufika ku 100.
Pa kufunsidwa kuphedwa kwake kusanachitike, Bundy anavomereza kuti zithunzithunzi zosonyeza umaliseche zinali chochititsa chachikulu chothandizira ku mkhalidwe wake wa upandu. Mogwirizana ndi Dr. James Dobson, yemwe anatsogoza kufunsako, “pa zaka 12 kapena 13 iye anayamba kupeza zithunzithunzi zosonyeza umaliseche m’masitolo a anam’goneka, ngakhale m’mbali mwa msewu, ndipo anakhala womwerekera, wopambanitsa,” ikusimba tero Daily News.
Kuvomereza kwa Bundy kukumveketsanso mawu a Arthur Gary Bishop, wakupha wina wozengedwa mlandu, yemwe anaphedwa chaka chatha kaamba ka kugonana kodzetsa imfa kwa anyamata asanu. Mogwirizana ndi The Tribune, nyuzipepala, ya ku San Diego, California, Bishop anavomereza kuti zithunzithunzi zosonyeza umaliseche “zinali ‘zosakaza’ kwa iye monga m’nyamata ndipo zinatsogolera ku kugwa kwake.” Bishop anagwira mawu katswiri wa zamaganizo yemwe anachitira umboni pa kuzengedwa mlandu kwake kuti “pamene anthu akhala omwerekera [ku zithunzithunzi zosonyeza umaliseche] zikhumbo zawo zimakulirako, kudzimva kwawo kwachibadwa kumazimiririka ndipo amakhoterera kuchita pa zimene awona.” Bishop anavomereza kuti: “Zinali tero ndi ine. Ndine womwerekera m’kugonana kwa ofanana ziŵalo wozengedwa mlandu wakupha, ndipo zithunzithunzi zosonyeza umaliseche zinali chochititsa chogamulirapo m’kugwa kwanga.”
Ngakhale kuti akupha odziwulula avomereza kuti zithunzithunzi zosonyeza umaliseche ziri zosakaza, pali anthu ambiri omwe akuziwona izo monga zosangulutsa zosavulaza. Kwa oterowo chenjezo loperekedwa pa Yesaya 5:20 limagwira ntchito bwino lomwe: “Tsoka kwa iwo amene ayesa zoipa zabwino, ndi zabwino zoipa; amene aika mdima m’malo mwa kuyera, ndi kuyera m’malo mwa mdima!”
Palibe Chinsinsi
Minisitala wa United Church Phyllis Smith akudzinenera kuti chikhulupiriro cha atsogoleri ena a chipembedzo chikuwopsyezedwa mwachiwonekere ndi mafunso a odwala matenda akupha, ikusimba tero The Toronto Star, nyuzipepala ya ku Canada. Mogwirizana ndi Smith, “anthu omwe ali pafupi kufa amafunsa mafunso onena za zinsinsi za moyo ndi imfa zimene palibe aliyense yemwe amazimvetsetsa.” Mkaziyo akunena kuti: “Sitifunikira kudzimva owopsyezedwa kokha chifukwa chakuti tikudzimva kuti tifunikira kukhala ndi mayankho onse.” Pamene mafunso ovuta auzimu adzutsidwa, Smith akusungirira kuti atsogoleri a chipembedzo “safunikira kuchinjiriza Mulungu.”
Pamene chiri chowona kuti anthu sangakhale ndi mayankho onse nthaŵi zonse ku mafunso onena za moyo ndi imfa, Baibulo liri nawo. Kodi awo odzinenera kukhala aminisitala a Mulungu sayenera kudziŵa chimene Mawu ake amanena? Mtumwi Petro ananena kuti akhulupiriri anzake ayenera nthaŵi zonse kukhala “okonzekera kupanga kuchinjiriza pamaso pa aliyense yemwe akafunsa chifukwa cha chiyembekezo chiri mwa inu.” (1 Petro 3:15, NW) Akristu oyambirira analibe vuto la kumvetsetsa mkhalidwe wa akufa kapena ziyembekezo zamtsogolo zomwe zasungidwa kaamba ka mtundu wa anthu womafa. Iwo anadziŵa kuti Mlaliki 9:5 imanena kuti: “Pakuti amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi.” Ndipo Yesu anauza atsatiri ake kuti: “Ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira.” (Yohane 5:28, 29) Kwa aminisitala owona a Mulungu, moyo ndi imfa ziribe chinsinsi.