Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 1/1 tsamba 3-4
  • “Liwu Lawo Linatulukira ku Dziko Lonse Lapansi”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Liwu Lawo Linatulukira ku Dziko Lonse Lapansi”
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Nkhani Yofanana
  • Perekani Chilengezo Chapoyera cha Chipulumutso
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Ziwerengero Zonse za 2012
    Buku Lapachaka la Mboni za Yehova 2013
  • Kukondwera mwa Mlengi Wathu Wamkulu
    Nsanja ya Olonda—1993
Nsanja ya Olonda—1989
w89 1/1 tsamba 3-4

“Liwu Lawo Linatulukira ku Dziko Lonse Lapansi”

MU SALMO 19, Davide akulemekeza ulemerero wa chilengedwe cha kuthupi cha Mulungu ndi kupitiriza kulongosola chiyamikiro chotentha cha lamulo la Yehova, zokumbutsa, malangizo, malamulo, ndi maŵeruzo. Mtumwi Paulo nayenso anasonyeza chiyamikiro kaamba ka zinthu zimenezi. Iye anagwira mawu kuchokera ku salmo limeneli ndi kufutukula kugwiritsira ntchito kwake ku ntchito yofunika koposa ya Akristu owona. Za izi iye ananena kuti: “Liwu lawo linatulukira ku dziko lonse lapansi, ndi maneno awo ku malekezero okhalamo anthu.”​—Aroma 10:18.

“Maneno” amenewa ali chodetsa nkhaŵa cha moyo ndi imfa kwa mtundu wonse wa anthu lerolino, popeza kuti ziŵeruzo za Yehova ziri pafupi kuperekedwa pa dongosolo iri la kachitidwe ka zinthu loipa pa dziko lapansi. (Zefaniya 2:2, 3; 3:8) Mtundu wa anthu ndithudi ufunikira kudziŵa ponena za mbiri yabwino ya Ufumu wa Yehova. Kulikonse kumene mungayang’ane lerolino, pali kusagwirizana, kusayeruzika, upandu, chisembwere, nyumba zosweka. Oh, inde, pali kulankhula kwa mtendere, koma mphamvu zazikuluzo zikupitiriza kumangirira zida zomwe ziri zapamwamba koposa, pamene ziwalo za ‘gulu la nyukliya’ zikupitirizabe kufutukukira ku mitundu yochulukira koposa. Mikhalidwe pa dziko lapansi imayenerera mowonekera bwino “masiku otsiriza” olongosoledwa ndi Paulo pa 2 Timoteo 3:1-5.

Ndani adzapulumutsidwa kuchoka ku zoipa zimenezi, ndipo motani? Paulo akuyankha mosabisa, akumagwira mawu ulosi pa Yoweli 2:32: “Amene aliyense adzaitanira pa dzina la Yehova adzapulumuka.” (Aroma 10:13) Koma ndimotani mmene anthu a pa dziko lapansi ‘angaitanire pa dzina la Yehova’? Nkulekeranji, ambiri ochulukira sadziŵa nkomwe kuti Yehova ndilo dzina la Mulungu! Ndimotani mmene anthu amenewa angathandizidwire? Paulo akuyankha kuti olalikira ayenera kutumizidwa kwa iwo.​—Aroma 10:14-16.

Mwachimwemwe, Yehova watumiza Mboni zake kudziŵitsa anthu kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi ndipo kuti udzatanthauza chipulumutso ku moyo wosatha kaamba ka awo omafika ku kudziŵa Mulungu ndi Mwana wake, Yesu Kristu. (Yesaya 43:10, 12; Luka 21:25, 26, 31; Yohane 17:3) Mbiri yabwino imeneyi ikumveketsedwa “ku dziko lonse lapansi.”

Mamiliyoni akupereka chilabadiro ku kulalikira kumeneko, monga momwe kwachitiridwa umboni ndi chiwonkhetso cha dziko lonse cha 9,201,071 omwe anapezekapo pa msonkhano womwe unakumbukira imfa ya Yesu, pa April 1, 1988. Mkati mwa chaka chimenecho, chiŵerengero chapamwamba cha ofalitsa a Ufumu cha 3,592,654 chinafikiridwa kaamba ka munda wa dziko lonse, ndipo atumiki atsopano 239,268 anabatizidwa​—chiwonjezeko cha 3.6-peresenti kuposa chaka chapita. Amishonale okhulupirika anayala maziko a ntchito yokulira kaamba ka chiwonjezeko chimenechi, monga momwe kwalongosoledwera kutsogoloku m’magazini iyi. Koma m’zaka za posachedwapa, mazana a zikwi za Mboni za kumaloko, awo omwe ‘aika chikhulupiriro m’zinthu zomvedwa,’ nawonso akulitsa mzimu wa upainiya ndipo tsiku ndi tsiku ‘akulalikira mbiri yabwino ya zinthu zabwino.’ Avereji ya Mboni 455,561 yakhala ikuchitira ripoti monga apainiya, chiwonjezeko kaamba ka chakacho cha 4.4 peresenti. Monga chotulukapo chake, chiwonkhetso chachikulu cha maora 785,521,697 chinawonongedwa m’kulalikira, kuposa kuwirikiza nthaŵi ziŵiri chiwonkhetso cha maora chonse kokha zaka 6 zapitazo.

Chati cha pa masamba anayi otsatira a magazini ino chikusonyeza mwatsatanetsatane mmene kulalikira kumeneku kwachitidwira mokulira. Tikukuitanani kuphunzira za ripoti la 1988 limeneli la ntchito Yachikristu ya dziko lonse.

[Tchati patsamba 4-7]

RIPOTI LAUTUMIKI LA CHAKA CHA 1988 LA MBONI ZA YEHOVA DZIKO LONSE

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena