Kukondwera mwa Mlengi Wathu Wamkulu
“Akondwere Israyeli mwa iye amene anamlenga; Ana a Ziyoni asekere mwa Mfumu yawo.”—SALMO 149:2.
1. Mosasamala kanthu ndi mfuu zakuti “tsopano ufulu wafika,” kodi nchiyani chimene chiri mkhalidwe weniweni wa anthu?
DZIKO lamakono lakanthidwa ndi ‘zoŵawa za nsautso.’ Ndiwo mawu amene Yesu anagwiritsira ntchito mu ulosi wake wonena za “mapeto a dongosolo lazinthu,” nyengo ya tsoka imene inayamba ndi nkhondo yoyamba yadziko mu 1914. (Mateyu 24:3-8) Andale zadziko ambiri sakuwona chirichonse mtsogolomo kusiyapo mdima. Mosasamala kanthu za mfuu zakuti: “tsopano ufulu wafika” Kummaŵa kwa Yuropu, amene kale anali pulezidenti m’chigawo chimenecho ananena mwachidule mkhalidwewo pamene anati: “Kuchuluka kochititsa mantha kwa chiŵerengero cha anthu ndi kuyambukiridwa moipa kwa dziko lapansi chifukwa cha kutentha kosalamulirika kwa dzuŵa, ziboo mu muyalo wa mpweya wa ozoni ndi AIDS, chiwopsezo cha uchigaŵenga wa zida za nyukliya ndi kusiyana kwakukulu kochititsa manthako pakati pa maiko akumpoto olemera ndi maiko akummwera osauka, chiwopsezo cha njala, kucheperachepera kwa malo oyenerera kukhalidwa ndi anthu ndi chuma cha m’nthaka cha pulanetili, kuwonjezereka kwa anthu amene makhalidwe awo aumbidwa ndi kupenyerera wailesi yakanema ndi chiwopsezo chomakulakula cha nkhondo za chiweniweni—zonsezi, zitaikidwa pamodzi ndi zochititsa zina zikwi zambirimbiri, zimapereka chiwopsezo chachikulu kwa anthu.” Palibe ulamuliro wa anthu umene ungachotse chiwopsezo cha tsoka lochititsa imfa limeneli.—Yeremiya 10:23.
2. Kodi ndani amene ali ndi njira yachikhalire yothetsera mavuto a anthu, ndipo nchiyani chimene iye wachita kale?
2 Komabe, tingathe kusangalala, kuti Mlengi wathu Wamkulu ali ndi njira yothetsera yachikhalire. Muulosi wa Yesu “mapeto a dongosolo la zinthu” ngogwirizanitsidwa ndi “kukhalapo” kwake kosawoneka. (Mateyu 24:3, 37-39, NW) Kuti alenge “miyamba yatsopano,” Yehova anayika Yesu pampando wake wachifumu monga Mfumu Yaumesiya, umboni waulosi umasonyeza kuti chochitika cha m’mbiri chimenechi chinachitika kumwamba m’chaka cha 1914.a (2 Petro 3:13) Monga wolamulira limodzi ndi Ambuye Mfumu Yehova, Yesu tsopano walamulidwa kuweruza mitundu ndi kulekanitsa anthu ofatsa, onga nkhosa adziko lapansi kwa anthu ouma khosi onga mbuzi. “Mbuzi” zosapembedzazo zikupita ku “kudulidwa kosatha” ndipo “nkhosa” kumoyo wosatha mmalo apadziko lapansi a Ufumuwo.—Mateyu 25:31-34, 46.
3. Kodi nchifukwa chiti chimene Akristu owona ali nacho chakukondwerera?
3 Otsalira a Israyeli wauzimu padziko lapansi, amene tsopano khamu lalikulu la nkhosa zomvera limeneli lagwirizana nawo, ali ndi chifukwa chirichonse chakukhalira okondwerera Yehova, Mfumu yamuyaya, pamene akufikitsa zifuno zake zazikulu pakukwaniritsidwa kotheratu kupyolera mwa Ufumu wa Mwana wake. Iwo angathe kunena kuti: ‘Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti iye wandiveka ine ndi zovala zachipulumutso, nandifunda chofunda chachilungamo, . . . monga dziko liphukitsa mphundu zake, ndi monga munda umeretsa zobzalamo, momwemo Ambuye Yehova adzaphukitsa chilungamo ndi matamando pamaso pa amitundu onse.’ (Yesaya 61:10, 11) ‘Kuphukira’ kumeneku kukuwonekera mwa mamiliyoni ambiri amene tsopano akusonkhanitsidwa kuchokera ku mitundu kuimbira Yehova chitamando.
‘Kufulumizitsa’
4, 5. (a) Kodi kusonkhanitsidwa kwa anthu a Mulungu kunanenedweratu motani? (b) Kodi ndichiwonjezeko chapadera chotani chimene chinawoneka mkati mwa chaka chautumiki cha 1992?
4 Kusonkhanitsako kukufulumira pamene mapeto a dongosolo la Satana akuyandikira. Mlengi wathu Wamkulu akuti: “Anthu ako adzakhalanso onse olungama . . . nthambi yowoka ine, ntchito ya manja anga, kuti ine ndikuzidwe. Wamng’ono adzasanduka chikwi, ndi wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu; ine Yehova ndidzafulumiza ichi m’nthaŵi yake.” (Yesaya 60:21, 22) Kufulumizitsa kumeneku kwasonyezedwa modabwitsa mu Lipoti lautumiki la Chaka cha 1992 la Mboni zaYehova Padziko Lonse, lofalitsidwa pamasamba 12 mpaka 15 a magazini ano.
5 Chapadera m’lipoti lino ndicho chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha olengeza Ufumu 4,472,787 chiwonjezeko cha 193,967—4.5 peresenti kuposa chaka chatha. Chiŵerengero chapamwamba cha obatizidwa 301,002 mkati mwa 1992 nachonso chikusonyeza umboni wakuti ambirimbiri akuvomereza chowonadi cha Baibulo. Tikukondwera chotani nanga kuti mu ‘tsiku lamdima wandiweyani, tsiku la mitambo, . . . gulu lalikulu lankhondo,’ limene, mofanana ndi thenje la dzombe, likuwonjezera kuchitira umboni Ufumu “kumalekezero adziko lapansi”! (Yoweli 2:2, 25; Machitidwe 1:8) Kuchokera ku Alaska wozizirayo—kumene ndege ya Watch Tower Society yapanga maulendo oposa 50 kumagawo achipale chofeŵa—kufikira ku zipululu zoŵaula za Mali ndi Burkina Faso ndi zisumbu zotalikirana za Micronesia, atumiki a Yehova akuŵala monga ‘kuunika kwa amitundu, kuti akhale chipulumutso [chake] mpaka kumalekezero adziko lapansi.’—Yesaya 49:6.
6, 7. Kodi ndikusintha kosayembekezereka kwa zinthu kotani kumene kunawonedwa m’zaka zaposachedwapa, ndipo kodi atumiki a Yehova akulabadira motani?
6 Yehova wakhala monga ngaka ndi linga lolimba m’kutetezera ndi kulimbikitsa anthu ake. M’mbali zambiri za dziko lapansi, Mboni za Yehova zifunikira kupirira zaka makumi ambiri za chitsenderezo chokakala ndi chizunzo. (Salmo 37:39, 40; 61:3, 4) Koma posachedwapa, monga ngati mwachozizwitsa, ziletso ndi zopinga zachotsedwa m’maiko pafupifupi 21, kotero kuti tsopano anthu a Mulungu angathe kulengeza mwaufulu kuti Mlengi wathu Wamkulu waika pampando wachifumu Kristu monga Mfumu yolamulira dziko lapansi.—Salmo 2:6-12.
7 Kodi anthu a Yehova akugwiritsira ntchito bwino lomwe ufulu wawo wopezedwa chatsopano? Tawonani patchati ziwonjezeko za Bulgaria, Romania, ndi yomwe kale inali Soviet Union Kummaŵa kwa Yuropu ndi za Angola, Benin, ndi Mozambique mu Afirika. Mu Zairenso, chiwonjezeko nchodabwitsa. Ali ndi chikondwerero m’mitima yawo, abale athu opeza ufuluwo akulabadira chiitano chakuti: ‘Yamikani Yehova pakuti ndiye wabwino; . . . amene yekha achita zodabwitsa zazikulu: pakuti chifundo chake nchosatha.’ (Salmo 136:1, 4) Zithokozo zimenezi zikusonyezedwa mwa utumiki wachangu mwakusonkhanitsira anthu onga nkhosa ena kumbali ya Ufumuwo.
8. Kodi ndimotani mmene atamandi atsopano a Yehova ‘afikira akuuluka mtambo’ Kummaŵa kwa Yuropu? mu Afirika?
8 Mkati mwa chilimwe chapitachi cha ku Yuropu, misonkhano ya anthu a Yehova yochitidwira m’maiko amene kale anali Achikomyunizimu inali ndi ziŵerengero zozizwitsa za ofikapo. Zozizwitsadi kwambiri ndizo ziŵerengero za obatizidwa, m’maiko amenewo. Mofananamo, m’Togo, Afirika, chiletso chinachotsedwa pa December 10, 1991. Mwezi wotsatira kunali kunachitidwa msonkhano wamtundu. Poyerekezera ndi avareji ya mwezi ndi mwezi ya ofalitsa 6,443 mu utumiki wakumunda, chiŵerengero cha ofika pamsonkhanowu chinakwera kufika ku 25,467, ndi okwanira 556 akubatizidwa—8.6 peresenti ya chiŵerengero cha ofalitsa. Monga momwe Yesaya 60:8 amasonyezera, atamandi atsopano a Yehova amabwera ‘akuuluka ngati mtambo, ndi monga nkhunda ku mazenera awo’ m’mipingo ya anthu a Yehova.
9. Kodi ndimakonzedwe otani amene apangidwa kotero kuti Akristu m’maiko amene apeza ufulu posachedwapa akhoze ‘kudya ndi kukhuta’?
9 Njala yachakudya chauzimu Kummaŵa kwa Yuropu ndi mu Afirika ikukhutiritsidwanso. Mafakitale a Watch Tower Society m’Jeremani, Italiya, ndi South Africa anatumiza malole ambirimbiri odzala mabukhu, m’zinenero zingapo, ku maiko okanthidwa ndi njala yauzimu. Papitapo, ambiri a Mboni anali kubwerekana magazini othaitha, koma tsopano akulandira mwana alirenji wachakudya chauzimu. Iwo akukondwera kukhala ndi phande m’kukwaniritsidwa kwa ulosi wakuti: ‘Ndipo mudzadyaidya ndi kukhuta, nimudzalemekeza dzina la Yehova Mulungu wanu, amene anachita nanu modabwitsa.’—Yoweli 2:26.
Kusamalira Chifutukuko Chowonjezereka
10. Chifukwa cha kuchuluka kwa ofika pa Chikumbutso, kodi ndichiitano chotani chimene chikuperekedwa kwa anthu onse okondwerera?
10 Ndithudi chodabwitsa ndicho chiŵerengero cha dziko lonse lapansi cha ofika pa Chikumbutso cha imfa ya Yesu, cha 11,431,171, chiwonjezeko cha 781,013, kapena 7.3 peresenti kuposa chaka chatha. Tikukulandirani, inu nonse atsopano! Kukakhala kokondweretsa chotani nanga ngati anthu onse okondwerera chatsopano amenewa angapindule mwa phunziro la Baibulo lapanyumba ndi mmodzi wa Mboni za Yehova! (Wonani Yesaya 48:17.) Lipoti la Chaka Chautumiki limasonyeza 4,278,127 amaphunziro amenewa kukhala akuchititsidwa mwezi uliwonse, chiwonjezeko chabwino kwambiri cha 8.4 peresenti. Komabe, ambiri angakhoze kupeza thandizo lautumiki umenewu. Mboni za Yehova ziri zokondwera kufika mokhazikika kwa anthu okondwerera kukachita phunziro la Baibulo laulere m’nyumba mwawo, chotero kuthandiza amenewa kuti azike zolimba mapazi awo panjira yomka kumoyo wosatha. (Yohane 3:16, 36) Kodi mulekeranji kupempha phunziro lotero? Ndipo kumbukirani, kuchingamiridwa kwaubwenzi kukukuyembekezerani pa Nyumba Yaufumu!—Salmo 122:1; Aroma 15:7.
11, 12. (a) Kodi anthu akukumana ndi mavuto otani m’maiko ena? (b) Kodi ndim’njira yotani imene ‘kulinganiza’ kukuchitikira pakati pa maiko okhupuka ndi osauka?
11 Mipingo imene iri ndi Nyumba Zaufumu zabwinozo njodalitsidwa molemerera. Mkhalidwewo ngwosiyana m’maiko kumene Mboni zokhulupirika zapirira zaka zambiri ziri zoletsedwa, zikumasonkhana mobisa m’timagulu tating’ono. M’malo ambiri otero, iwo tsopano ngomasuka koma ali ndi Nyumba Zaufumu zochepekera. Mwachitsazo, m’dziko lina la mu Afirika, Pa mipingo 93, pali Nyumba Zaufumu zitatu zokha. Chotero kaŵirikaŵiri misonkhano imachitidwira pamabwalo aakulu apoyera. Mpingo wa ofalitsa 150 ungakhale ndi ofikapo mokhazikika ofikira ku 450 pa misonkhano imeneyi.
12 Kaŵirikaŵiri, Kummaŵa kwa Yuropu kuli kovuta kugula malo kapena nyumba, koma kupita patsogolo kukupangidwa. Kuperekedwa kwa nyumba yatsopano ya ofesi ya nthambi kunalinganizidwa kuchitidwa pa November 28, 1992 mu Poland. Zopereka zaufulu kuntchito ya dziko lonse ya Mboni za Yehova zikugwiritsidwa ntchito kumanga maholo ndi nyumba zina. Chotero, ‘kulinganiza’ kumachitika m’chakuti kuwolowa manja kwa abale amene amapereka zopereka kuchokera pa zinthu zawo zakuthupi “zowonjezerekazo” kumathandiza kugaŵira zosoŵa zauzimu za mipingo m’maiko okhala ndiumphaŵi.—2 Akorinto 8:13, 14.
Maola Mamiliyoni Chikwi!
13. Kodi ndimaola angati amene anagwiritsidwa ntchito m’kulalikira ndi kuphunzitsa mu 1992, ndipo ndizoyesayesa zamphamvu zayani zimene zikusonyezedwa ndi ziŵerengerozi?
13 Kodi mukachitanji ndi maola mamiliyoni chikwi? Onse olandira moyo wosatha adzakhoza kuthera maola ochuluka chotero, ndipo ngakhale oposerapo, mu utumiki wopindulitsa, ndi wokhutiritsa kwa Yehova. Koma tayerekezerani kudzaza thothotho maola ochuluka chotero m’chaka chimodzi! Ndizo zimene anthu a Yehova anachita mkati mwa 1992. Kuwonkhetsa pamodzi malipoti a aliyense payekha a ofalitsa Aufumu onse, tikupeza chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha maola 1,024,910,434 ogwiritsiridwa ntchito m’njira yabwino koposa—kutamanda Mlengi wathu Wamkulu, “kuphunzitsa . . . poyera ndi kunyumba ndi nyumba.” (Machitidwe 20:20, NW) Pa avareji, Mboni zokwanira 4,289,737 zinali kuchitira lipoti mwezi uliwonse. Iwo anachokera ku mikhalidwe yonse yamoyo. Ena ali ndi nthaŵi yochepa imene angapereke ku ntchito ya Ufumu. Amenewa amaphatikizapo mitu yabanja, imene iyenera kugaŵira apabanja; okalamba; ndi ambiri okhala ndi mavuto athanzi; kuphatikizapo ana amene akadali pa sukulu. Komabe, lipoti loperekedwa ndi aliyense limayamikiridwa monga chisonyezero chake cha kukonda Yehova.—Yerekezerani ndi Luka 21:2-4.
14. Kodi ndimotani mmene achichepere ‘akumbukirira Mlengi wawo Wamkulu’?
14 Mbadwo wa achicheperepo ukusinkhukira mu utumiki wa Yehova, ndipo mosangalatsa unyinji wa amenewa ukugwiritsira ntchito mawu a Solomo pa Mlaliki 12:1, NW akuti: “Kumbukira, tsopano, Mlengi wako Wamkulu m’masiku aunyamata wako.” Iwo akupindula ndi maphunziro awo akusukulu, kuphatikizapo kuphunzitsidwa zinthu zauzimu ndi makolo odzipereka. Kwakhala kosangalatsa kwambiri kuwona chiŵerengero chachikulu cha achichepere a zaka 13-19 akuimirira pamisonkhano yaikulu yaposachedwapa kudzipereka ku ubatizo. Kulinso kosangalatsa kudziŵa kuti ambiri, mwakuphunzira ntchito iriyonse kapena luso, akupanga chikonzekero chothandiza podzachita upainiya pamene amaliza sukulu. Chotero, iwo adzakhoza kudzichirikiza, monga momwe anachitira mtumwi Paulo panthaŵi ndi nthaŵi mwa kusoka mahema.—Machitidwe 18:1-4.
15, 16. Kodi ndimotani mmene apainiya ndi atumiki ena anthaŵi yonse athandizira kupita patsogolo kwa ntchito ya Ufumu, ndipo ndi dalitso lotani limene ena a iwo akhala nalo?
15 Nchithandizo chachikulu chotani nanga chimene apainiya ndi atumiki ena anthaŵi yonse akupereka m’kupititsa patsogolo ntchito ya Ufumu! Apainiya anawonjezereka kufikira chiŵerengero chapamwamba cha 931,521 chaka chathachi. Pamene amenewa akulalikira tsiku ndi tsiku kunyumba ndi nyumba ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo apanyumba m’nyumba za anthu, amafikira kukhala ogwira mtima kwambiri pofotokoza Malemba mosadodoma. Ndiponso, ambiri ayeneretsedwa kuloŵa Sukulu Yautumiki wa Apainiya ya masabata aŵiri, imene imawathandiza kukulitsa maluso okulirapo ndi chisangalalo pochita ntchito ya Mulungu.
16 Aliyense wa apainiya okhulupirika amenewa angathe kuvomereza mawu a pa Yesaya 50:4: ‘Ambuye Yehova wandipatsa ine lirime la ophunzira, kuti ndidziŵe kunena mawu akuchirikiza iye amene ali wolema.’ Pali anthu ambirimbiri lerolino amene ali otopa ndi dziko lopanda chilungamo lowazinga koma amene akupeza mpumulo kupyolera mwa mawu olankhulidwa ndi apainiya athu okhulupirika.—Yerekezerani ndi Miyambo 15:23; Ezekieli 9:4.
Programu Yaikulu Yakumanga
17. Kuwonjezera pa kumanga kwauzimu, kodi ndikumanga nyumba zenizeni kotani kumene kwachitika m’zaka zaposachedwapa?
17 Chiwonjezeko chauzimu cha padziko lonse cha Mboni za Yehova chimachititsanso kufunika kwa chiwonjezeko cha zinthu zakuthupi. Kuwonjezeredwa kwa nyumba zosindikizira, maofesi, ndi nyumba za Beteli ndi kumangidwa kwa Nyumba Zaufumu ndi Nyumba Zamisonkhano kumakhala kofunika. Chotero Mboni za Yehova zimafunikira kukhala amisiri omanga nyumba zenizeni. Kumanga kofananako kunachitika m’tsiku la Mfumu Solomo. Solomo anamanga kachisi wolambirira Yehova mogwirizana ndi ‘pulani la mmisiri . . . limene analipeza mwachiuziro,’ Yehova anali atapereka limeneli kwa atate wake, Mfumu Davide. (1 Mbiri 28:11, 12) Chotero, sikokha kuti Solomo analimbikitsa omvetsera ake ndi mawu anzeru amtengo wapatali komanso anatsogolera m’kumangidwa kwa nyumba yeniyeni yaulemerero imene sinamangidwepo konse ndi dzikoli.—1 Mafumu 6:1; 9:15, 17-19.
18, 19. (a) Kodi ndintchito zomanga zopita patsogolo mofulumira kwambiri ziti zimene zikuchitidwa ndi gulu la Yehova? (b) Kodi mzimu wa Yehova wawoneka motani m’ntchito yakumanga kwauzimu ndi nyumba zenizeni?
18 Lerolino, Mboni za Yehova sizimamanga mogwiritsira ntchito mapulani aumisiri ouziridwa ndi Mulungu, koma izo ziri nawo mzimu wa Mulungu. Mofanana ndi m’masiku a Israyeli, mzimuwo umawasonkhezera kumanga mwanjira imene imazizwitsa anthu adzikoli. (Zekariya 4:6) Nthaŵi njaifupi. Nyumba Zaufumu ndi nyumba zina ziri zofunika mofulumira. M’maiko ena nyumba Zaufumu zomangidwa mofulumira nzofala. Mwachitsanzo, m’zaka 10 zapitazo, Canada ikusimba lipoti la kumangidwa kwa maholo 306, iriyonse ikumamangidwa m’masiku osafikira aŵiri. Chifukwa cha chiwonjezeko chofulumira cha ntchito ya Yehova padziko lonse lapansi, nyumba za nthambi zatsopano zokwanira 43 kapena kuwonjezeredwa kwa nthambi pakali pano zikumangidwa kapena kulinganizidwa. Ndiponso, nyumba yokhalamo yosanja zipinda 30, imene antchito odzifunira a pa Beteli pafupifupi chikwi adzakhalamo iri pafupi kutha m’Brooklyn. Ndiponso mu New York, ku Patterson, kumangidwa kwa likulu la Maphunziro a Baibulo, ntchito yomanga yolinganizidwa yaikulu koposa imene Watch Tower Society sinayambe yachitapo, ikupita patsogolo bwino kwambiri kuposa nthaŵi yoikidwa.
19 Ntchito yomanga imeneyi ikupita patsogolo bwino lomwe ndiponso ndintchito yochitidwa mwaluso imene ikuzizwitsa makampani omanga odziŵa bwino adzikoli. Chifukwa ninji? Chifukwa cha chithandizo chachikulu choperekedwa ndi Mboni zodzipatulira za Yehova. Mzimu wake umazisonkhezera osati kokha kupereka chichirikizo chakuthupi komanso kupereka ndi mtima wonse nthaŵi yawo ndi nyonga. Malo omangapo nyumbawo amadzala ndi antchito odzipereka ophunzitsidwa bwino. Palibe masitaraka a antchito, ndipo palibe ukamberembere pantchito. Mzimu wa Yehova umapereka chisonkhezero, monga momwedi unasonkhezerera omanga chihema m’nthaŵi ya Mose ndi awo amene anamanga kachisi m’masiku a Solomo. Mkhalidwe wauzimu ndiwo khalidwe lapadera lofunika mwa antchito amenewa.—Yerekezerani ndi Eksodo 35:30-35; 36:1-3; 39:42, 43; 1 Mafumu 6:11-14.
20. (a) Kodi nkumlingo wotani kumene mbiri yabwino idzalalikidwabe? (b) Kodi nchiyembekezo chadalitso chotani chimene chikuyembekezera anthu a Yehova?
20 Solomo anapitiriza programu yake yakumanga pambuyo pakumaliza kachisi. (2 Mbiri 8:1-6) Kuti nkumlingo wotani kuumene Mboni zamakono zidzawonjezerabe—limodzi ndi kufunika kokhalapo kwa kumanga maholo ndi nyumba zina—sitidziŵa. Komabe, chimene tidziŵa nchakuti, pamene mbiri yabwino ya Ufumu yalalikidwa kumlingo umene Yehova walamula, pamenepo mapeto, “chisautso chachikulu,” adzafika. (Mateyu 24:14, 21) M’dziko lapansi losaipitsidwanso ndi anthu aumbombo, kakonzedwe ka Yehova ka “miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano” kadzatsanulirano madalitso osaneneka pa anthu. Chifukwa chake ife ‘tikondwere ndi chisangalalo kosatha m’zimene Mulungu alenga,’ tikumapereka chitamando chonse kwa Mlengi wathu Wamkulu!—Yesaya 65:17-19, 21, 25.
[Mawu a M’munsi]
a Wonani “Let Your Kingdom Come,” lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., tsamba 105-16, 186-9.
Kodi Mungafotokoze?
◻ Kodi nzifukwa ziti zimene tiri nazo za kukondwerera Mlengi wathu Wamkulu?
◻ Kodi ndiziwonjezeko zotani zimene zinachitiridwa lipoti mkati mwa chaka chautumiki cha 1992?
◻ M’maiko amene kuchitira umboni poyamba kunali koletsedwa, kodi ndimadalitso olemerera otani amene asimbidwa?
◻ Kodi ndimotani mmene achichepere ndi apainiya athandizira chiwonjezeko m’gulu la Yehova?
◻ Kodi anthu a Yehova akhala otanganitsidwa motani m’kumanga kwauzimu ndi nyumba zenizeni?
[Bokosi patsamba 17]
Chaka chathachi maola oposa mamiliyoni chikwi anaperekedwa kuntchito yolalikira ndi kuphunzitsa
[Tchati pamasamba 12-15]
LIPOTI LAUTUMIKI LA CHAKA CHA 1992 LA MBONI ZA YEHOVA PADZIKO LONSE
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
[Chithunzi patsamba 10]
Oyembekezera ubatizo zikwi mazana ambiri chaka chatha anasonyeza dalitso la Yehova pa ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa
[Chithunzi patsamba 16]
Achichepere ambirimbiri ‘akukumbukira Mlengi wawo Wamkulu’