Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 10/15 tsamba 22-24
  • Caymans—Zisumbu Zoiwalidwa ndi Nthaŵi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Caymans—Zisumbu Zoiwalidwa ndi Nthaŵi
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Nkhasi, Mbala za Panyanja, ndi Luso Lapamwamba la Zopangapanga
  • Alendo a Mtundu Wina
  • Anthu a ku Cayman Amva Mbiri Yabwino
  • Chitsutso Chigonjetsedwa pa Cayman Brac
  • Kukumbukiridwa ndi Yehova
Nsanja ya Olonda—1988
w88 10/15 tsamba 22-24

Caymans​—Zisumbu Zoiwalidwa ndi Nthaŵi

INU mungasambire m’madzi abata, obiriŵira. Inu mungadumphe kuyendera zosakazidwa zochulukira pansi pa nyanja. Kapena mungachezere munda wa nkhasi. Kuti? Mu Zisumbu za Cayman​—Grand Cayman, Cayman Brac, ndi Little Cayman.

‘Koma ndi kuti padziko lapansi kumene kuli Zisumbu za Cayman?’ inu mungafunse tero. Limenelo ndi funso lomveka chifukwa chakuti izo ziri zochepera kotero kuti sizimasonyezedwa kaŵirikaŵiri pa mapu a dziko. Ngati zawonekera, izo zingangosonyezedwa kokha monga madontho atatu ochepera m’Nyanja ya Kumadzulo ya Caribbean, makolimita 240 chakum’mwera kwa Cuba, kapena makilomita 800 kum’mewra kwa Miami, Florida.

Zopezedwa mu 1503 ndi Christopher Columbus pa ulendo wake womalizira wa pamadzi kudzera ku West Indies, zisumbuzo​—Cayman Brac ndi Little Cayman, popeza kuti Columbus sanawonepo Grand Cayman​—zinkatchedwa Las Tortugas (Nkhasi). Chimenecho chinali chifukwa cha chiŵerengero chochulukira cha nkhasi zomwe zinkawonedwa pa zisumbupo ndi mozungulira. Mu 1670, ndi Pangano la Madrid, Spain inalekera zisumbuzo kwa Britain, ndipo zakhala pansi pa ulamuliro wa chiBritish chiyanmbire pamenepo.

Nkhasi, Mbala za Panyanja, ndi Luso Lapamwamba la Zopangapanga

M’masiku a masitima oyenda pamadzi, zisumbu zimenezi zinali gombe lokondedwa la kuitanira la masitima a pamadzi akulu omayenda m’madzi a Caribbean. Unyinji wokulira wa nkhasi zobiriwira za m’nyanja zinakhala magwero a nyama yosaumikidwa kaamba ka amalinyero anjala. Nkhasi zinkadyedwa zosaumikidwa, kapena kunyamulidwa pa ulendo zowumitsidwa kapena zoikidwa mchere. Izo zinakhala magwero okulira a zakudya zomangirira thupi mkati wa ulendo wa pamadzi wautali.

Koma zisumbuzo zinadziŵidwa kaamba ka chinachakenso. Malo osalala ndi doko la bata linakoka amuna ena okonda za m’nyanja. Achinsinsi otchuka ndi mbala za panyanja, zonga ngati Sir Henry Morgan ndi Edward Teach, wodziŵikanso monga Ndevu zakuda, anagwiritsira ntchito zisumbuzi monga pobisalira kapena magwero ogwirirako ntchito kaamba ka zolinga zawo molimbana ndi masitima a malonda. Kuchepera kumeneku kwa mbiri yabwino kumakumbukiridwa ndi madyerero a pa chaka otchedwa Mlungu wa Mbala za Panyanja, wolingaliridwa kumaloko kukhala nthaŵi yapadera ya pa chaka.

Pamene chiŵerengero cha nkhasi chinacheperachepera ndi pamene masitima ogwiritsira ntchito mafuta analowa m’malo masitima a pamadzi, masitima ocheperachepera anaitanira. Ndipo popeza kuti nzika zochepera za pa zisumbuzo zinali ndi mawailesi, kaamba ka zifuno zogwira ntchito zonse Zisumbu za Cayman zinalekedwa ndi kuiwalidwa ndi dziko lonse. Izo zinadzipezera zeni zokha dzina laulemu lakuti “Zisumbu Zoiwalidwa ndi Nthaŵi.”

Podzafika mu ma-1960, ngakhale kuli tero, chithunzi chinayamba kusintha. Kusunga ndalama kwa kumaloko ndi malamulo a msonkho, mogwirizana ndi kufika kwa zopangapanga zapamwamba za dongosolo la kukambitsirana, zinatembenuzira gawo loiwalidwa panthaŵi imodzili kukhala limodzi la malo osungitsa ndalama odziŵika a mitundu yonse. Zisumbuzo zinaŵerenga banki lawo la 500 lotsegulidwa mu June 1987. Kupita patsogolo kunasangalatsanso ochezera a malonda. Bungwe la ochezera la kumaloko linapangidwa pamene unyinji wonse pamodzi wa ochezera 8,244 unabwera mu 1966. Chiŵerengero chimenecho chinawonjezeka kufika ku 430,000 mu 1986, kupangitsa kuchezera kukhala chinthu chachiŵiri kokha m’kufunika ku indastri ya za ndalama. Pali, ngakhale kuli tero, gulu lina la anthu omwe ali okondweretsedwa mwachidwi m’zisumbuzi.

Alendo a Mtundu Wina

Mboni za Yehova, zomwe zimatenga mosamalitsa mawu a Yesu akuti mbiri yabwino ya Ufumu idzalalikidwa ku mitundu yonse, sizinanyalanyaze Zisumbu za Cayman. (Mateyu 24:14) Mofulumira mu 1929, Patrick Davidson, yemwe anali kuyang’anira ntchito yolalikira mu Jamaica, anachezera Grand Cayman. Mosasamala kanthu za chitsautso, iye anakhoza kuwoka mbewu za chowonadi cha Ufumu.

Davidson anapanga kuchezera kwachiŵiri mu 1937, koma sichinali kufikira mu 1950 pamene kukwaniritsa kotheratu kwa Grand Cayman kunachitidwa ndi Aleck Bangle ndi m’mishonale mnzake. Mazana a zidutswa za mabukhu a Baibulo angawiridwa m’nthaŵi yochepera. Amishonalewo anasimba kuti anapeza anthuwo kukhala aubwenzi, osavuta kulankhula nawo, ndipo ofunitsitsa kumva mbiri yabwino.

Anthu a ku Cayman Amva Mbiri Yabwino

Mokhazikika ndi moleza mtima, amishonalewo ndi atumiki ena a nthaŵi zonse anapitirizabe ntchito yawo. Podzafika 1959 panali gulu lochepera la ofalitsa a Ufumu 12, ndipo mpingo unalinganizidwa. Mmodzi wa nzika za kumaloko yemwe analandira chowonadi cha Baibulo anali Wilbert Sterling. Iye angakumbukire bwino lomwe masiku pamene unyinji wochepera wa Mboni unakhoza kukuta gawo lawo ndi miyendo. Nakhale kuti tsopano iye ali wakhungu ndipo m’zaka zake za ma-80, Mbale Sterling akali kutumikirabe monga mkulu mu Mpingo wa Georgetown.

Kuyesayesa kwakhama kwa olengeza a Ufumu oyambirira amenewo kwadalitsidwa ndi Yehova. Pali tsopano avereji ya ofalitsa a Ufumu 60 pakati pa chiŵerengero chonse cha anthu cha chifupifupi 17,000. Ambiri a nzika za pa zisumbuzo ayamikira kuti Mboni ziri zosiyana chifukwa chakuti kulambira kwawo kuli kozikidwa pa Baibulo.

Mwachitsanzo, mkazi wogwira ntchito m’nyumba yodyeramo anawona Mboni ikulalikira kuchokera kunyumba ndi nyumba. Iye anamfikira iye ndi kumukunsa chimene anayenera kuchita kuti akhale mmodzi wa Mboni za Yehova. Iye anauzidwa kuti iye akafunikira kutenga chidziŵitso cholongosoka cha Yehova Mulungu ndi Mwana wake, Yesu Kristu, ndipo kenaka kuziika izo m’kugwira ntchito. (Yohane 17:3) Pamene anamva chimenecho, iye analandira phunziro la Baibulo la panyumba. Lerolino, iye akutumikira Yehova monga mmodzi wa mboni zake.

Ambiri a awo omwe alandira chowonadi ali ochokera ku maiko ena. Iwo apanga Cayman mudzi wawo kapena ali alendo a pa kanthaŵi pa malonjezano a ntchito. Chotero, mlongo mmodzi analongosola chikhumbo chowona nzika zambiri za ku Cayman mu mpingo. Iye anapemphera kwa Yehova kumthandiza iye kupeza nzika yomwe inafuna kuphunzira Baibulo. Pasanapite nthaŵi yaitali pambuyo pa chimenecho, iye anakumana ndi mkazi wachichepere yemwe anali kale ndi bukhu la Chowonadi Chimene Chimatsogolera ku Moyo Wamuyaya, ndipo mlongoyo anayamba phunziro la Baibulo ndi iye. Mkati mwa miyezi yoŵerengeka, mkaziyo anayamba kupezeka pa misonkhano, analeka chipembedzo chake chakale, ndipo anayamba kugawana chimene anali kuphunzira ndi ena. Mkati mwa chaka iye anakhala mboni yodzipereka, yobatizidwa ya Yehova.

Ntchito yolalikira inalandira kufutukuka kowonjezereka mu 1952, pamene amishonale okwatirana aŵiri anagawiridwa ku Grand Cayman. Iwo anatsogoza maphunziro a Baibulo a panyumba ambiri ndipo anakhazikitsa maziko abwino kaaamba ka chiwonjezeko chotsatira.

Chitsutso Chigonjetsedwa pa Cayman Brac

Chisumbu cha Cayman Brac chiri chifupifupi makilomita 140 kumpoto cha kum’mawa kwa Grand Cayman. Kuchokera ku nthaŵi ndi nthaŵi, amishonale ndi ogwira ntchito a nthaŵi zonse ena kuchokera ku Grand Cayman anaima kwa kanthaŵi kubweretsa mbiri yabwino ku nzika zake 1,700. Koma zinthu zosangalatsa zinayamba kuchitika kumeneko mu1986.

Aŵiri okwatirana ogwira ntchito kumeneko pa pangano anayamba kuphunzira ndipo anapita patsogolo kumlingo wa kudzipereka ndi kubatizidwa. Kenaka, Mboni zina ziŵiri zinasamukirako kuchokera ku maiko ena. Ntchito yowonjezereka mwamsanga inabweretsa mkwiyo wa otsutsa, omwe anayesera kupangitsa okhala ndi malamulo a anthu olowa m’dziko kuthetsa chilolezo cha ntchito za aŵiri okwatirana obatizidwa chatsopanowo. Ngakhale kuli tero, zoyesayesa zawo zinasokonezedwa, pamene nduna yaikulu yoyang’anira za olowa m’dzikomo mu Georgetown, Grand Cayman, inatenga malo akuti ngati otsutsa achipembedzowo anakalipitsidwa ndi ntchito ya Mboni, nawonso afunikira kupita kuchokera kunyumba ndi nyumba kuti alimbane nayo. Palibe kuwukira kowonekera komwe kwamvedwa chiyambire pamenepo.

Kukumbukiridwa ndi Yehova

Anthu a Zisumbu za Cayman motsimikizirika sanaiwalidwe ndi Yehova, Mlengi Wamkulu. M’malomwake, iye akuchipangitsa icho kukhala chothekera kaamba ka mbiri yabwino kulalikidwa m’zisumbu zazing’ono zimenezi, mwakutero kukwaniritsa ulosi wa Yesaya: “Yimbirani Yehova nyimbo yatsopano, ndi matamando ake kuchokera ku malekezero a dziko lapansi, inu amene mutsikira kunyanja ndi zonse ziri mmenemo, zisumbu ndi okhala mommo.”​—Yesaya 42:10.

Zisumbu za Cayman zingasangalale kuti kuchokera ku kayang’anidwe ka Yehova, izo siziri “Zisumbu Zoiwalidwa ndi Nthaŵi.”

[Mapu patsamba 22]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Caribbean Sea

LITTLE CAYMAN

CAYMAN BRAC

[Mapu]

GRAND CAYMAN

[Mapu]

CUBA

LITTLE CAYMAN

GRAND CAYMAN

CAYMAN BRAC

JAMAICA

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena