Mvetserani ku Kuŵerenga kwa Baibulo
Landirani kakaseti a Baibulo mu maalubamu a m’manja
“Ndayamba kuwona kukhala amtengo wapatali makasetiwo,” walemba tero mkazi wina kuchokera ku Germany. “Chifukwa chake?” iye akufunsa tero. “Ndinakhudzidwa m’kugundana kwakung’ono kwa magalimoto ndipo ndinavulaza chigaza changa. Chotero kwa masiku 8 apitawo ndakhala gone m’chipatala ndi mutu wopweteka womwe unandiletsa ine kuŵerenga, kukhala tsonga, ndi zina zotero.
“Ndinali kukhala maso usiku mumdima, makamaka pamene chinali chovuta kugona, ndipo ndinawonerera filimu m’mutu mwanga pamene ndinamvetsera ku Genesis, Eksodo . . . tsopano ndikuzolowerana ndi atumwi onga Petro ndi Yohane kupyolera m’makalata awo, omwe ndimakonda nthaŵi zonse, koma tsopano oyamikiridwa m’tsatanetsatane aliyense pamene ndisewera iwo mobwerezabwereza.
Ndikuyamikani kuchokera pansi pa mtima wanga kuto maora anga a kuvutika ndi kusungulumwa sanali osakhoza kupiririka chifukwa cha kulingalira kwanu kwapasadakhale ndi khama m’kuyang’ana pa zikondwerero zathu zauzimu.”
Inu nanunso mungapindule ndi makaseti ojambulidwa a chinenero cha Chingelezi a New World Translation of the Holy Scriptures. Alubamu yathunthu yokhala ndi Malemba a Chibgriki kuchokera pa Mateyu kufika ku Chivumbulutso (makaseti 18), iri K240.00. Ma alubamu aŵiri a Malemba Achihebri alikonso. Yoyamba iri ndi Genesis mpaka Rute pa makaseti 18 ndipo iri K240.00; alubamu yachiŵiri iri ndi makaseti 21 omwe ali ndi 1 Samueli mpaka Masalmo ndipo iri pa K266.00.
Chonde sonyezani mwakuika chizindikiro pa bokosi lolondola la alubamu ya makaseti omwe mukufuna, ndi kutumiza unyinji wa ndalama wosonyezedwa.
□ Ndatsekeramo K240.00 (Zambia) kaamba ka alubamu ya Malemba a Chigriki.
□ Ndatsekeramo K240.00 (Zambia) kaamba ka alubamu ya Genesis mpaka Rute.
□ Ndatsekeramo K266.00 (Zambia) kaamba ka alubamu ya 1 Samueli mpaka Masalmo. (Kunja kwa Zambia, lemberani ku nthambi ya Watch Tower ya kumaloko kaamba ka chidziŵitso.)