Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 9/15 tsamba 31
  • Womenyera Wokhulupirika wa Chowonadi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Womenyera Wokhulupirika wa Chowonadi
  • Nsanja ya Olonda—1988
Nsanja ya Olonda—1988
w88 9/15 tsamba 31

Womenyera Wokhulupirika wa Chowonadi

MARTIN POETZINGER, chiwalo cha Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, anamaliza ntchito yake ya padziko lapansi monga Mkristu wodzozedwa kumayambiriro kwa madzulo a Lachinayi, June 16, 1988. Iye anali ndi umoyo wovutikira kwa kanthaŵi koma anafa popanda kubweteka kulikonse pa Beteli ya Brooklyn. Mkazi wake, Gertrud, anali pambali pake kwa nthaŵi yonse ya kudwala kwake.

Mbale Poetzinger anabadwa pa July 25, 1904, mu Munich, Germany. Iye anabatizidwa pa October 2, 1928, ndipo analowa utumiki wa upainiya pa October 1, 1930. Mu mphakasa ya 1933, Watch Tower Society inamugawira iye kuyang’anira zikondwerero za Ufumu mu Bulgaria, koma mkati mwa chaka Mboni zomwe sizinali za mtunduwo zinathamangitsidwa m’dzikolo. Ulendo wotsatira wa Mbale Poetzinger unali wa ku Hungary. Atamangidwa, mwachinyengo ndi kuthamangitsidwa m’dziko limenelo, iye chotsatira anapatsidwa kuyang’anira gulu la apainiya mu Yugoslavia. Pambuyo pa kudwala kowopsya, koyenerera kukhala kwa ntahŵi yaitali m’chipatala mu Zagreb, iye anabwerera ku Germany.

Mbale ndi Mlongo Poetzinger anakwatirana mu 1936, koma m’chaka chimodzimodzicho iye anatumizidwa ku ndende ya chibalo chifukwa chokana kukana chikhulupiriro chake. Mkazi wake anaikidwa m’ndende kwina kwake, koma iye anatumizidwa ku Dachau ndipo kenaka ku msasa wophera pa Mauthausen, Upper Austria. Kumeneko a Gestapo anagwiritsira ntchito chakudya chodzetsa njala, kukwapula, ndi nkhalwe yosalongosoleka kum’pangitsa iye ndi Mboni zina kuswa umphumphu wawo kwa Yehova Mulungu. Koma Mbale Poetzinger anamamatira ku chikhulupiriro chowona.

Pambuyo pa zaka zisanu ndi zinayi za kuikidwa m’ndende kwa nkhalwe, Mbale ndi Mlongo Poetzinger anagwirizananso mu 1945. Mwamsanga pambuyo pa ichi, iye anayamba kutumikira mu ntchito yadera mu Germany, ndipo pambuyo pake Gertrud anayenda limodzi naye, mwachangu akumagwira ntchito m’munda pamene iye anatumikira mipingo. Mu 1958 iye anapezeka pa Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower, ndipo pa kubwerera kwake ku Germany, iye ndi mkazi wake anapitiriza mu ntchito yoyendayenda kufikira iwo analowa mu utumiki wa pa Beteli kemeneko mu 1977. Mu September 1977, Mbale Poetzinger anaikidwa mu Bugnwe Lolamulira ndipo anali wokhoza kubwera ku malikulu a dziko lonse a Sosaite mu Brooklyn, New York, patapita chaka chimodzi. Iye anatumikira ndi Komiti ya Utumiki ya Bungwe Lolamulira ndi Dipatimenti ya Komiti ya Utumiki.

Mbale Poetzinger anali womenyera wolimba mtima kaamba ka chowonadi. Kuchirikiza kwake kokhulupirika ndi kwachangu kwa gulu la Yehova ndi ntchito ya Ufumu zinalidi zopereka chitsanzo. Chotero tiri ndi chidaliro kuti iye ali pakati pa awo kwa amene mawu awa amagwira ntchito: “Odala akufa akumwalira mwa Ambuye . . . Inde, unena mzimu, . . . pakuti ntchito zawo zitsatana nawo pamodzi.”​—Chivumbulutso 14:13.

[Chithunzi patsamba 31]

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena