Ubwenzi wa Upainiya kwa Moyo Wonse
M’chipinda chaudongo chokongoletsedwa mopepuka mu Cardiff, Wales, Phunziro la Bukhu la pa Mpingo langotha kumene. Wotsogoza phunziroyo anayamikira alongo aŵiri achipainiya, Maud Clark ndi Mary Grant, tsopano m’zaka zawo za mu ma 90, chifukwa cha kuchereza kwawo ndi kuwalimbikitsa iso kupitirizabe . . .
Maud: Tsopano ziri zaka 65 kuyambira pamene Mary ndi ine tinakumana choyamba ndi kuyamba kuchita upainiya pamodzi.
Mary: Inde, munali mu 1923, pa usiku wozizira, wa chipale chofewa wa January! Kodi umakumbukira, Maud? Ndinakutenga iwe kuchokera ku malo oima sitima a Much Wenlock kupita ku chipinda changa. Tinali ndi chinachake chakudya, ndipo kenaka tinaphunzira pamodzi Tabernacle Shadows. Mmawa wotsatira tinanyamuka pa njinga zathu kukalalikira kwa alimi a ku Shropshire.
Kudziwana Koyambirira
Maud: Ndithudi, tinali onzokera kaamba ka ichi. Mudziŵa, tonse aŵirife tinakhala tikuchita upainiya kwa kanthaŵi. Ngakhale pamene ndinali mtsikana wachichepere, Mawu a Mulungu nthaŵi zonse anandikondweretsa ine. Nkulekeranji, popeza ndikhoza kukumbukira ndikumanena mobwereza masalmo asanu ndi aŵiri pa tchalitchi kotero kuti ndipeze Baibulo laulere! Munali mu 1908, pamene ndinali ndi zaka 11, kuti mkulu wanga wamkulu anaŵerenga bukhu la The Divine Plan of the Ages ndi kusiya tchalitchi chimene tinali kupezekako, kukhala Wophunzira Baibulo. Zowonadi za Baibulo zinakhala nkhani ya kukambitsirana kwathu panyumba. Koma pamene bambo wanga anamwalira, ndinayamba kudabwa, ‘Kodi akufa ali kuti?’
Chinali chosangalatsa chotani nanga kupeza yankho pamene ndinapita kukawona Chitsanzo cha Zithunzithunzi za Chilengedwe, choperekedwa mu tauni yakwathu ya Sheffield! M’zithunzithunzi zoyenda zimenezo, zolongosoledwa ndi marekodi ojambulidwa, ndinawona kuchitiridwa chitsanzo kwa kuwuka kwa mwana wa mkazi wa ku Suname. Inde, ndinaphunzira kuti akufa ali mu mkhalidwe wa kusadziŵa kanthu kufikira chiwukiriro.—2 Mafumu 4:32-37.
Mwamsanga ndinasiya Tchalitchi cha Anglican ndi kutenga yomwe tinaitcha ntchito ya upasitala, kugawira mabukhu a Baibulo m’gawo lenilenilo kumene ndinali kukhala komwe ndinadziŵika kaamba ka kugawira magazini a tchalitchi. Ndinasonyeza kudzipereka kwanga kwa Yehova mu August 1918 pa msonkhano mu mzinda wapafupipo wa Leeds.
Pambuyo pa kuthera nthaŵi yambiri ya tchuthi ndi alongo achikoputala aŵiri mu Derbyshire, ndinapanga maganizo anga kupanga utumiki waupainiya kukhala ntchito yanga ya moyo wonse. Mu August 1922, ndinatenga gawo langa loyambirira: Biggleswade mu Bedfordshire.
Mmodzi wa akoputalawo ananena kwa ine: “Ngati ungamamatire ku iyo kwa miyezi isanu ndi umodzi yoyambirirayo, udzakhala bwino.” Miyezi yoyambirira imeneyo sinali yopepuka. Ndinali ndi ngozi pa njinga yanga. Kenaka mnzanga wa chipainiya woyambirira anabwerera kumudzi. Koma ndinali wogamulapo kupitiriza, chotero ndinalembera Sosaite kufunsa kaamba ka mnzanga. Ndipo Yehova anandipatsa ine Mary!
Mary, unatenga kaimidwe kaamba ka chowonadi moyambirira kuposa ine, kodi sunatero?
Mary: Inde, Maud. Pa nthaŵiyo tinali kukhala mu Cardiff, South Wales. Pamene ndinali ndi zaka 16, agogo anga akazi anandiitana ine kukaŵerenga bukhu la The Divine Plan of the Ages, lomwe analipeza pa msonkhano wapoyera wolinganizidwa ndi Ophunzira Baibulo. Nthaŵi zonse ndinafuna kumvetsetsa Baibulo ndi kukhala m’mishonale pamene ndinakula. Pamene ndinali kuŵerenga volyumu imeneyi, ndinadziŵa kuti ndapeza chowanadi.
Ndinayamba kupezeka pa misonkhano ya Ophunzira Baibulo, mosasamala kanthu za kupanda, chivomerezo kokulira kwa amayi anga. Mudziŵa, makolo anga anali olemera, ndipo popeza iwo sanandilole ine kugwira ntchito, ndinapeza mikhalidwe panyumba kukhala yotsekereza koposa. Mosasamala kanthu za chimenecho, ndinakhoza kupeza zothandizira zonse za phunziro la Baibulo. Pamene amayi anga anazipeza, iwo mwaukali anatentha mabukhuwo ndi kundiwuza ine kuti ndinali wachichepere koposa kudziŵa ponena za zinthu zoterozo. Kuti ndibwezeretse iwo ndinayenera kuzembetsa mabukhuwo m’nyumba yanga limodzi ndi limodzi, pambuyo pa maulendo a m’mawa kwambiri ku nyumba ya mmodzi wa Ophunzira Baibulo makilomita atatu kutali. Ndinali kuŵerenga izi mofulumira onse a m’nyumbamo asanawuke, kuzibisa izo mu msasa wosungiramo zinthu kumunda mkati mwa tsiku.
Mu 1913, pamene ndinali ndi zaka 17, ndinapita ku London kaamba ka tchuthi chowona malo. Mwachimwemwe, ichi chinawombana ndi ulendo wa Mbale Russell ku msonkhano wochitidwa pa Kingsway Hall. Kumeneko ndinasonyeza chikhumbo changa cha kufuna kubatizidwa. Mlongo wachikoputala yemwe anagwira ntchito mu Cardiff anafikira Mbale Russell kumfunsa iye ngati analingalira kuti ndinali wachichepere koposa. Iye anandifunsa ine zaka zanga ndi kundifunsa kuti awone ngati ndinamvetsetsa Malemba ndi kugamulapo ngati ndinali ndinapereka moyo wanga kwa Yehova. Monga chotulukapo chake, ndinavala chovala chachitali chakuda ndi kugwirizana ndi ophunzira enawo kaamba ka kumizidwa pa London Tabernacle. Ndikumbukira bwino kwambiri mawu amene tinaimba pamene tinali kutuluka m’madzi:
“Kuikidwa ndi Kristu
ndi kuwukitsidwa limodzi naye,
Nchiyani chomwe chatsalira kwa ine kuchita?
Kokha kusiya
kulimbana ndi mkwiyo,
Kokha kuyenda mu utsopano wa moyo.”
Pambuyo pake, mbale anandifikira ndi kunena kuti: “Uyenera kukhala womalizira wa 144,000 kubwera; uli kokha ndi nthaŵi yochepa yoteroyo kuti utsimikizire kuitanidwa ndi kusankhidwa kwako.” Amenewo anali malingaliro a ambiri omwe anawona chaka chomayandikiracho, cha 1914, ndi chiyembekezo chachikulu. Kwa ine, ngakhale ndi tero, iyi inatsimikizira kukhala nthaŵi ya kuyesedwa pamene ndinali kuchita ndi chitsutso chachikulu kunyumba. Ndinapezeka pa misonkhano mwa kaŵirikaŵiri monga mmene ndinathera. Mu 1916, ndinasangalala ndi mwaŵi wotumikira monga woperekera pa kuwonetsedwa kwa Chitsanzo cha Zithunzithunzi za Chilengedwe mu Cardiff. Pambuyo pa kumaliza maphunziro anga a unamwino mu Manchester, ndinayamba utumiki wa upainiya wa nthaŵi zonse mu 1922.
Kuchitira Umboni M’midzi
Maud: Ife ndithudi tinayenera kudziyambira tokha kumbuyoko. Tinawuza aliyense kuti tinadzilowetsa mu ntchito ya Chikristu. Anthu masiku amenewo anali aŵerengi. Tinagawira Zeze wa Mulungu ndi mipambo ya Studies in the Scriptures. Ndithudi, tinafunikira chola chachikulu chimene tinganyamulire mabukhu onsewa. Changa chinali chachikulu koposa kotero kuti pamene ndinafika ku munda wakutali tsiku limodzi, mkazi wa mlimiyo anaganiza kuti ndinali wachibale wobwera kudzacheza kuchokera ku Canada. Tinaseka chotani nanga!
Popeza kuchita upainiya kunali moyo wathu, tinalandira malipiro athu kuchokera ku ntchito yogawira mabukhu okhala ndi uthenga wa Ufumu. Tinagwiritsira ntchito chuma chathu mosamalitsa ndi kukhala osmalira, tikumasinthanitsa mabukhu kaamba ka bata, ndi zotulutsidwa zina za m’munda ndi kutola mbatata, swedes, ndi kabichi zomwe zinagwa kuchokera ku ngolo za pa munda m’misewu yosasalala, ya fumbi. Tinakhala a luso m’kukonza magudumu akuphwa a njinga zathu, ndipo tinakhala osoka, tikumapanga zovala zathu zathu.
Pamene abale amene anatumikira monga abale olankhula oyendayenda anapereka nkhani za Baibulo m’matauni, Mary ndi ine tinali kubwera pambuyo pawo kutsatira chikondwerero chimene kulalikira kwawo kunadzutsa. Magulu ang’ono a okondwerera anawonekera mu Shrewsbury ndi matauni ena. Ndipo ndimotani nanga mmene tinayanga’anira kutsogolo ku misonkhano! Ndiganiza kuti msonkhano wa ku Londan wa 1926 unali wapadera. Kumeneko tinasangalala ndi mwaŵi wowonjezereka wa kugawira kabukhu ka The Standard for the People pa makwalala a likululo. Kenaka chikondwerero chathu chinakula pamene tinaŵerenga za mkati mwa kalata yochokera ku Sosaite. Kunali kusintha kwa gawo kaamba ka ife: Northern Ireland.
Kuchita Upainiya M’magawo Atsopano
Tinafika mu County Antrim, Northern Ireland, kukachita upainiya pakati pa anthu ogawanikana mwa chipembedzo. Poyamba tinakhala pa Greenisland. Kunali konyowa ndi kozizira, ndipo tinalibe moto kwa milungu ingapo chifukwa cha kuleka kugwira ntchito kwa opanga malasha mu England. Ndinagadzichitire chithunzi ife tsopano, titakhala ndi makoti athu ndi zovala kumanja madzulo, kuyesera kuphunzira pamene tikunjenjemera ndi kuzizira. Kenaka chirimewe chinafika, ndipo tinali oyamikira chotani nanga kwa Yehova kaamba ka mwaŵi wa kugwira ntchito m’malo okongola a Antrim. Anthu anamvetsera bwino lomwe ku uthenga wa Ufumu. Oo, inde, iwo kaŵirikaŵiri anali kuwutsa mkangano, koma anali achifundo. “Lowani,” iwo ankatero, ndipo ankaika ketulo pa greesha (chitsulo chofiira cha moto) kuti iwire, ndipo kukambitsirana kwathu kunapitiriza.
Mary: Popeza tsopano tinali atsikana achipainiya anayi tonse pamodzi m’gawo lathu, tinamamatira ku ndandanda yokwanira ya teokratiki ya misonkhano. M’mawa mulimonse tinakambitsirana lemba la Malemba ndi kuŵerenga “Chigamulo Changa cha M’mawa,” chimene chinanena, m’mbali ina kuti, ‘Tsiku lirilonse ndidzakumbukira pa Mpando Wachifumu wa Chisomo cha Kumwamba zikondwerero za chisawawa za ntchito yotuta, makamaka kugawanamo kumene ine mwini ndiri ndi mwaŵi wosangalala nako m’ntchito imeneyo, ndi ogwira nawo ntchito limodzi pa Beteli ndi kulikonse.’ Lachitatu usiku tinali ndi Msonkhano wathu wa Pemphero, Chitamando, ndi Umboni. Sande tinkaphunzira Nsanja ya Olonda pamodzi, ndipo tinali kusonkhana mozungulira choimbira chaching’ono chimene kaŵirikaŵiri chinali kupezeka m’nyumba za anthu kuimba kuchokera ku Hymns of the Millennial Dawn, monga ngati:
“Ne’er think the victory won,
Nor once at ease sit down
Thine arduous task will not be done
Till thou hast gained thy crown.”
Maud: Kunali kusintha kotani nanaga pamene tinagawiridwa ntchito yapadera yomwe inatseguka—tinakhala “apainiya a nyumba za malonda.” Ndimotani mmene tikanachitira umboni kwa amuna a malonda, amanejala a mu banki, ndi ofanana nawo? Nyumba zazikulu zimenezo mu Belfast zinawoneka zowopsya. Koma tinakumbukira Afilipi 4:13: “Ndikhoza zonse mwa iye wondipatsa mphamvuyo.” Ndipo sitinali kungalira za kusiya ntchito yathu. Ndi zokumana nazo zazikulu chotani nanga zimene tinali nazo kulankhula kwa amuna amenewa ndi kugawira mabukhu ambiri ndi iwo! Pofika 1931 tinali titamaliza nyumba za malonda ndipo tinathera zaka zisanu mu Northern Ireland. Tinadabwa za kumene kudzakhala gawo lathu lotsatira. Ku kuzizwitsidwa kwathu zinali nyumba za malonda za ku Dublin.
Ku Tarisi kapena Nineve?
Tiyenera kuvomereza kuti, poyamba, tinadzimva ngati Yona, yemwe anagawiridwa kukalalikira ku Nineve ndipo m’malomwake kulunjika ku Tarisi. Tikanakonda gawo losiyanako. Mwamsanga tinazindikira mmene tinafunikira kudalira pa Yehova. Komabe, chinali chowopsya chotani nanga kuimirira pafupi ndi Nelson’s Pillar mu Dublin ndi kuwona makwalala odzaza ndi ansembe ndi avirigo, amuna akumatukula zisote zawo ndipo akazi akumadzipingasa iwo eni m’kulemekeza ‘Namwali wodalitsidwa.’ Pa nthaŵi imeneyo panali kokha Ophunzira Baibulo anayi mu Dublin.
Tinakhoza kupeza zipinda ndi banja la Chiroma Katolika. Ndithudi, tinayenera kubisa mabukhu athu pansi pa kama, popeza wansembe anali kupanga ulendo wokhazikika ku nyumbayo. Tsiku limodzi mwamuna wa malonda wa mu Dublin anaitanira pa malo athu ogona, akunena kuti: ‘Munasiya mabukhu pa banki yanga.’ Iye anasangalatsidwa ndi iwo kotero kuti anapita ku shopu iriyonse kukawona ngati anagulitsa mabukhu a Judge Rutherford. Iye kenaka analembera ku New York ndipo anapatsidwa keyala yathu. Iye anakonza phwando kaamba ka mabwenzi ake onse kuwauza iwo ponena za zimene anaziphunzira.
Pambuyo pake chaka chimenecho, tinapezeka pa msonkhano mu Liverpool, England, kumene tinaphunzira za dzina lathu latsopano, Mboni za Yehova. Pa kubwerera kwathu kupita ku Dublin, tinagawana m’ndawala yogawira kabukhu ka The Kingdom, the Hope of the World, komwe kanali ndi chigamulo cha msonkhanowo. Tinapanga maulendo pa malo onse a abambo achipembedzo, nyumba za avirigo, ndi nyumba za malonda, kupereka makope aulere a kabukhuko. Onse analandiridwa!
Mary: Tsiku limodzi tinawona bwato likuyenda mothamanga kutsika ndi mtsinje wa Liffey, ndipo ichi chinatipatsa ife lingaliro la kuchitira umboni kwa anthu a pa sitima ya pamadzi pa makochezi. Pamene tinayesera kulowa m’malo a makochezi, anatsekedwa ndi wapolisi, yemwe anatifunsa chimene tinali kuchita. Pamene tinamuwonetsa iye mabukhuwo, iye ananena kuti, “Pitirizani.” Tinapeza atsogoleri a masitima a pamadzi ambiri ochokera ku maiko ena omwe anadziŵa Mboni. Pamene tiyang’ana m’mbuyo ponena za zokumana nazo zimenezo, timazizwa pa njira imene Yehova anatisamalira ife pamene aliyense wa ife anapita yekha kukwera sitima za pamadzizo.
Kuchitira Umboni Mkati mwa Nkhondo ya Mlengalenga
Maud: Mu 1939 pamene nkhondo inawulika tinabwerera ku Liverpool ndi kugwirizana ndi apainiya ena 20 omwe amakhala panyumba ya apainiya. Tsopano tinakhala mkati mwa kuwukira kwa mlengalenga ndi kuphulitsa mabomba ndi kuchitira umboni kulikonse kumene anthu anamvetsera. Kaŵirikaŵiri tinadzipeza ife eni titaika marekodi pa makina athu oseŵerera uthenga wojambulidwa, kukambitsirana uthenga wa Ufumu, ndipo kenaka kuthamanga kubwerera ku nyumba ya apainiya, kapena kumathamanga kuchokera ku msasa wobisalirako kuwukira kwa mlengalenga umodzi kupita ku unzake. Mkati mwa nyengo yonseyi, sitinachititsidwe mantha, popeza tinali kuchita ntchito ya Ambuye.
Nthaŵi zambiri pamene tinali kupita kutsika m’makwalala, anthu anatitonza ife chifukwa cha kaimidwe ka uchete kamene Mboni zinasungirira mkati mwa nyengo ya kuwombana imeneyi. Ndimakumbukira kuti panyumba imodzi mwamuna wachichepere anamvetsera ku zojambulidwa zathu ndi kulandira phunziro la Baibulo lokhazikika. Vuto linabuka. Iye anali atangodzipereka mwaufulu kugwirizana ndi gulu Lankhondo Lapamadzi la chiBritish. Iye analemba kalata kwa maulamuliro kunena ponena za kaimidwe kake ka uchete ndipo analandira m’kubwezeredwa kupatulidwa kotheratu kuchoka ku utumiki wa nkhondo. Iye pambuyo pake anagwirizana nafe mu utumiki wa nthaŵi zonse.
Mary: Sindidzaiwala nkomwe masiku a nkhondo amenewo, Maud. Kodi umakumbukira chimene chinachitika pamene tinasamukira ku Knutsford mu Cheshire mu 1942? Mkazi anafuula kwa ife, ‘Nchiyani chimene mukuchita kaamba ka zoyesayesa za nkhondo?’ Tisanayankhe, munthu wodutsa anayankha kuti, ‘Iye akuchita ntchito imene tiribe kulimba mtima kwa kuichita.’ Mwamuna wachikulire anawonjezera kuti, ‘Iwo akuchita ntchito yabwino.’
Maud: Ndithudi, ntchito ya phunziro la Baibulo inali chinthu chachikulu. Ndinali ndi chokumana nacho chachikulu pamene ndinaitanira pa munda ndi kupeza mkazi yemwe anandiuza ine kuti mnyamata wake wachichepere anaphedwa pa ngozi ya pa msewu. Ndinagawira kwa iye kabukhu ka Hope for the Dead ndi kuyambitsa phunziro la Baibulo. Patapita kokha maphunziro asanu ndi aŵiri, mkazi ameneyu anayamba kutsagana nane m’ntchito ya umboni. Miyezi yoŵerengeka pambuyo pake mwamuna wake analandira chowonadi, ndipo mkati mwa zaka ziŵiri okwatirana amenewa anagulitsa munda wawo ndi kuyamba upainiya. Mwana wawo wamkazi pambuyo pake anagwirizana nawo mu ntchito ya nthaŵi zonse, ndipo tsopano iye ndi mwamuna wake akutumikira mu Beteli ya pa London.
Pa msonkhano wa mu 1941 pa Leicester, Mbale Shroeder analengeza kuti apainiya apadera adzayenera kulandira ndalama zochepa zowathandiza iwo ndi zofunikira za moyo. Kwa chifupifupi zaka 20, Yehova anakhala akudalitsa ntchito yathu wogawira mabukhu ndipo mwa njira imeneyi kutipatsa ife zimene tinafunikira. Yehova santigwiritse mwala. Tinatsimikizira kuti “sanataika mawu amodzi a mawu ake onse abwino, amene analankhula.”—1 Mafumu 8:56.
Kupeza “Nkhosa” mu Wales
1954 inatipeza ife mu Milford Haven, Wales. Mosasamala kanthu za chitsutso cha atsogoleri a chipembedzo, tinalalikira ndi kupeza ena onga nkhosa omwe anavomereza. Awa tinawalinganiza m’gulu ndi kuwasonyeza iwo mmene angatsogozere misonkhano ndi kupereka ndemanga zazifupi, za tanthauzo. Chinali chochitika cha chimwemwe chotani nanga kuwona asanu ndi aŵiri akubatizidwa m’malo osambitsira nkhosa odzazidwa ndi madzi otentha othiridwa mmenemo ndi zitini za mkaka!
Mu chigwa cha chiWelsh cha mzinda wa Abercynon, kuitanira pa njira ya magazini kunabweretsa zotulukapo zabwino. Ngakhale kuti mkaziyo yemwe mokhazikika analandira makope a magazini ananena kuti, “Sindikukhulupirira zimene mukundiuza ine,” iye anavomereza kuŵerenga magaziniwa. Pa ulendo wa pambuyo pake, ndinapeza mwamuna wake ali wotanganitsidwa kukongoletsa nyumba. Pambuyo pa kukambitsirana kwa ubwenzi, makonzedwe anapangidwa a kuyambitsa phunziro la Baibulo mlungu wotsatira. Tinapanga ubwenzi ndi ana amuna atatu omwe anabwera kugwirizana nawo m’phunzirolo. Kenaka, amayiwo ndi ana awo amuna anapereka miyoyo yawo kwa Yehova ndipo anabatizidwa. Kufikira lerolino, ziwalo 35 za banja limenelo zalandira chowonadi, zina zikutumikira monga apainiya othandizira, okhazikika, kapena apadera ndipo ena monga akulu.
Tsopano lino tiri mu Cardiff, kukumbukiranso ponena za miyoyo yathu. Sitiri ndi zodandaula. Yehova wapereka kaamba ka zosowa zathu zirizonse m’njira ya kuthupi. Tinakhala ndi moyo wosangalatsa kutumikira pamodzi monga apainiya, ndipo tidakali kuŵerengera utumiki wa ntahŵi zonse monga chuma chachikulu koposa m’moyo.
Tsopano mitima yathu imasangalatsidwa kuwona mathayo omakula a upainiya. Ndipo kuwona achichepere onsewo akumatenga utumiki wapadera umenewo—timsangalala chotani nanga! Mary ndi ine tachita upainiya pamodzi kwa zaka 65. Miyoyo yathu yakhala yopepuka koma yotanganitsidwa, yolimba koma yopatsa mphoto. Ife ndithudi tingayamikire upainiya kwa moyo wonse.
[Chithunzi patsamba 23]
Maud (kumanzere) ndi Mary akupezabe chuma chokulira choposa mu utumiki wawo wa nthaŵi zonse kwa Yehova