Kodi Mukukumbukira?
Kodi mwapeza makope a posachedwapa a Nsanja ya Olonda kukhala a phindu logwira ntchito kwa inu? Bwanji osayesa kukumbukira kwanu ndi mafunso otsatirawa?
◻ Nchiyani chomwe chiri yankho ku mavuto a lerolino a mimba za a zaka zapakati pa 13 ndi 19?
Achichepere ayenera kupatsidwa chitsogozo cha makhalidwe abwino ndi chauzimu. Baibulo limasonyeza kuti makolo ali ndi thayo la kuchita ichi. (Aefeso 6:4)—4/15, tsamba 4.
◻ Nchiyani chimachipangitsa icho kukhala chovuta kulera ana mwachipambano?
Makolo ndi ana ali opanda ungwiro ndipo, chotero, amapanga zophophonya. (Aroma 5:12) Ndiponso, ana omakula amasonkhezeredwa kwambiri ndi zikhoterero zoipa za chitaganya cha masiku ano; ichi chimayambukira moipa mapindu awo ndi kawonedwe pa moyo. (2 Timoteo 3:1-5)—5/1, tsamba 4.
◻ Ndi kusiyana kunayi kosangalatsa kotani kumene kulipo pakati pa Akristu owona ndi awo odzinenera kukhala Akristu?
Akristu owona amasala mwazi. (Machitidwe 15:28, 29) Iwo amasungirira miyezo yapamwamba ya makhalidwe abwino. (1 Akorinto 6:9, 10) Akristu owona amakhala a uchete kulinga ku ndale zadziko ndi kuwombana kochulukira kwa utundu. (Yohane 17:16) Awo amene amatsatira Yesu amagwiritsira ntchito chitsanzo chake monga chitsanzo kaamba ka maunansi awo a panyumba. (Aefeso 5:21-25)—5/1, masamba 17-19.
◻ Nchifukwa ninji Ayuda anatcha Yesu m’Samariya? (Yohane 8:48)
Ayuda anadana ndi Asamariya. Chotero, liwulo linagwiritsiridwa ntchito ndi iwo monga ka longosoledwe ka kuputa ndi kutonza Yesu.—5/15, tsamba 8.
◻ Kodi nchiyani chomwe chiri “chinerero choyera” cholankhulidwa pa Zefaniya 3:9?
Ichi chiri chinerero cha chowonadi cha m’Malemba chomwe chimatheketsa anthu owopa Mulungu a mitundu yonse ndi mafuko kutumikira Yehova mogwirizana.—5/15, tsamba 16.
◻ Ndi maufulu otani amene amatulukapo kuchokera ku kukulitsa unansi ndi Mulungu?
Ufulu ku kukhala akapolo a mantha a munthu ndi ku miyambo yolemetsa imene iribe tanthauzo lenileni kapena phindu. (Miyambo 29:25) Ndiponso, ufulu ku kuwopa imfa. (Mlaliki 9:5, 10; Yohane 5:28, 29)—6/1, masamba 5-6.
◻ Nchiyani chimene Yesu anatanthauza pamene ananena kuti: “Ukudza usiku pamene palibe munthu angakhoze kugwira ntchito”? (Yohane 9:4)
Yesu pano anali kulozera ku nthaŵi pamene iye akapita m’manda ndipo sakakhalanso wokhoza kuchita ntchito zozizwitsa zimene iye anali kuchita pamene iye anali ndi moyo.—6/1, tsamba 8.
◻ Kodi nchiyani chimene ubatizo wa m’madzi umasonyeza?
Kumizidwa kotheratu m’madzi chiri chisonyezero choyenerera cha kudzipereka kwa munthu kwa Mulungu, pamene munthuyo amakhala mtumiki wolikidwa. Pamene ali pansi pa madzi, iye, m’chenicheni, amafa ku njira yakale ya moyo, ndipo pa kutuluka m’madzi, iye amakhala, monga mmene kunaliri, wamoyo ku njira yatsopano ya kudzipereka kwaumwini mu utumiki wa Yehova. (Yerekezani ndi Aroma 6:2-4; 12:1; Afilipi 3:16.)—6/15, tsamba 29.
◻ Kodi ndi ziti zomwe ziri njira zina zosonyezera chiyamikiro kwa Yehova?
Pamene kuyamikira kuli kwamphamvu, chikhumbo chosonkhezera cha kutumikira Mulungu chimadzaza mu mtima woyamikira. Njira imodzi yokhutiritsira chikhumbo chimenechi iri kudzilowetsa mu utumiki, mwinamwake mu utumiki wa upainiya. Njira ina iri kugwirizana mu programu yomanga yomwe ikuchitika tsopano kuzungulira pa dziko lonse lapansi.—7/1, tsamba 11.
◻ Nchifukwa ninji Yesu anapatsa ulamuliro 70 a ophunzira ake wa kuchiritsa odwala pamene anawatumiza iwo pa ndawala yolalikira mu Galileya?
Ophunzira amenewa, mwa kuchita zozizwitsa zimenezo, anakonzekeretsa njira kaamba ka Yesu ya kuchita ntchito yotsatira. Zozizwitsa zimene iwo anazipanga zikapanga eninyumba ambiri kukhala ofunitsitsa kukumana ndi Yesu ndi kumvetsera ku uthenga wake wa Ufumu.—7/1, masamba 16-17.
◻ Kodi Yesu anali kulozera kwa Yudasi pamene anawuza Pilato kuti: “Iye wondipereka ine kwa inu ali nalo chimo loposa”?—Yohane 19:11.
Chikuwoneka kuti Yesu anali kulowezera kwa onse omwe anali ndi thayo kaamba ka kukhala kwake pamaso pa Pilato pa mlanduwo. Chimenecho ndithudi chinaphatikizapo Yudasi Isikariote, yemwe anapereka Yesu. (Luka 22:2-6) Koma wansembe wamkulu Kayafa ndi atsogoleri ena achipembedzo analinso olowetsedwamo m’kubweretsa kumangidwa kwa Yesu. (Mateyu 26:59-65; 27:1, 2, 20-23) Mwachidziŵikire aliwongo onsewa anaphatikizidwamo mu chimene Yesu ananena pa Yohane 19:11.—7/15, tsamba 30.
◻ Ndi ngozi yeniyeni yakupha iti imene iri yogwirizana ndi kulambira mafano?
Wamasalmo ananena ponena za Aisrayeli: “Kutumikira mafano a akunja, iwo anadzipeza iwo eni okodwa m’kupereka nsembe ana awo enieni amuna ndi akazi ku ziwanda.” (Masalmo 106:36, 37, The Jerusalem Bible) Malemba Achikristu a Chigriki amachenjeza za ngozi yofananayo. (1 Akorinto 10:19, 20) Kulambira mafano kwa mtundu uliwonse kumatsegula njira ya kuthekera kwakuti fano lingatumikire monga nsonga yokumanirana ndi mphamvu za ziwanda.—8/1, tsamba 6.