Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 7/15 tsamba 26-29
  • Ulendo Wathu Wosaiwalika ku Vanuatu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ulendo Wathu Wosaiwalika ku Vanuatu
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Msonkhano mu Port-Vila
  • Kukumana ndi “Manamba a Ang’ono”
  • Kupulumuka Mphepo ya Mkuntho ya Uma
  • Zochitika za Pambuyo Pake
Nsanja ya Olonda—1988
w88 7/15 tsamba 26-29

Ulendo Wathu Wosaiwalika ku Vanuatu

PAMENE ndege yathu inanyamuka pa bwalo la ndege la Port-Vila kutitenga ife kubwerera ku Nouméa, New Caledonia, tinayamba kuzindikira kuti zambiri zomwe tinakumana nazo pa ulendo wathu zinali zosayembekezeredwa. Zomwerekera mozama m’chikumbukiro chathu sizinali zowoneka zokha ndi mawu a zisumbu zokongola za Vanuatu ndi anthu ake aubwenzi komanso chokumana nacho chowopsya cha kupulumuka mphepo ya mkuntho yowononga pa chisumbu cha kumalo otentha.

Vanuatu iri gulu la chifupifupi zisumbu 80 zopangidwa monga Y kum’mwera cha kumadzulo kwa Pacific, chifupifupi makilomita 400 kumpoto cha kum’mawa kwa New Caledonia. Zomwazikana pakati pa zisumbuzo ziri mboni zinzathu za Yehova 84 m’mipingo iŵiri. Mkazi wanga ndi ine tinasangalatsidwa pamene makonzedwe anapangidwa kaamba ka ife kuchezera iwo. Mwachibadwa, mafunso ambiri anabwera m’malingaliro athu. Kodi ndi mtundu wanji wa mikhalidwe imene tikakumanizana nayo? Kodi anthu a pa chisumbu ali onga chiyani? Ndipo, chofunika koposa, ndimotani mmene akavomerezera ku mbiri yabwino ya Ufumu?

Msonkhano mu Port-Vila

Tinali odera nkhaŵa pamene tinadziŵa kuti ngakhale kuti zambiri za nzikazo zinali za chiMelanesia mwa fuko, pali zinenero zoposa zana limodzi zolankhulidwa pa chisumbucho. Koma tinapatsidwa mpumulo kupeza kuti mtundu wa Chingelezi cha Pidgin chotchedwa Bislama chiri chinenero chofala. Chotero sipakakhala vuto lalikulu m’kulankhula ndi anthuwo.

Malo athu oima oyambirira anali Port-Vila, likulu la Vanuatu. Pano, tinayenera kupezeka pa Msonkhano wa Chigawo wa “Mtendere wa Umulungu.” Mboni za kumaloko zinagwira ntchito molimbika kukonzekera. Chinali chotenthetsa mtima kukumana ndi nthumwi zochokera ku zisumbu zakutali zomwe zinasunga ndalama kwa miyezi yambiri kaamba ka kupanga ulendowo.

Holo ya msonkhano inadzazidwa kuyambira pa tsiku loyamba la msonkhano. Anthu oposa 300 anabwera kudzawona zitsanzo za Baibulo zoperekedwa kupyolera m’matepi a video. Ichi chinali chosangalatsa koposa, kulingalira kuti pali kokha ofalitsa a Ufumu 84 m’zisumbu zonsezo. Ndithudi, Yehova akukonzekera kututa kwabwino m’mbali zochepera za dziko zimenezi mkati mwa Nyanja ya Pacific.

Kukumana ndi “Manamba a Ang’ono”

Tsiku lotsatira, mbale wa kumaloko ndi ine tinatenga ndege yaing’ono ndi kulowera ku chisumbu cha Malekula. Pambuyo pa kuwuluka koipa ndi kovuta, tinatera pa South West Bay. Mnzangayo anapita kufunafuna msuwani wake kuti apeze bwato kaamba ka ife. Inali njira yokha ya kufikira mudzi wa Letokas, malo athu oima omalizira.

Pamene tinanyamuka m’bwato lathu ndi kutsatira gombe, ndinadabwitsidwa ndi kukongola kwa chilengedwe kwa chisumbucho. Malo otsetsereka kuthera m’nyanja anali ozizwitsa kowopsya. Zomera zosangalatsa zinali paliponse, zokongoletsedwa ndi maluwa owala kapena kukutidwa ndi ziyangoyango, zomera zopanda maluwa, ndi maluwa ofewa. Zikumalumpha kuchokera ku mtengo kupita ku mtengo zinali mbalame zokongola, monga ngati coconut lories.

Kuchokera ku bwato lathu tinawonanso ulemerero wa nyanja​—gombe la miyala, malo otsikira a mwambo a anthu a pachisumbuwo. Anthu ochokera ku dziko lonse amabwera kudzasambira ndi kukhumbira kukongola kwa gombelo ndi nsomba za ku malo otentha. Nkhono ndi lobsters zirinso zambiri, ndipo anthu a kumaloko amazitchera ukonde kapena kuzilasa ndi nkondo kaamba ka chakudya.

Mwamsanga tinawona utsi ukukwera kuchokera pa malo odzala ngole kutali. Unasonyeza malo athu oimira, malo okongola a chidikha pafupi ndi Bamboo Bay. Pamene tinafika pafupi ndi gombe, maporpoise ambiri anabwera kudzaseŵera motizungulira ife. Kenaka tinawona amuna ena atanyamula mauta ndi mivi akumapanga magesicha okondweretsedwa ambiri. Pakati pawo, tinawona abale athu, akusangalala pa kufika kwathu.

Awa anali ma Namba Ang’ono a kum’mwera kwa Malekula, limodzi la mafuko okhala kutali koposa mu South Pacific. Iwo amakhala m’midzi yaing’ono pamwamba pa mapiri ulendo woyenda masiku ambiri kuchokera ku gombe. Amunawo ankakonda kuvala “namba,” chophimba m’chiuno chopangidwa ndi masamba omangiliridwa ku lamba la khungwa. Akazi amavala masiketi a afupi a udzu. M’mudzi uliwonse, kaŵirikaŵiri pamakhala malo apakati amwambo kumene kuvina kwa nsembe ndi miyambo ina imapangidwa. Ngakhale kuti ambiri a anthu a m’mudziwo atengera njira ya moyo ya Kumadzulo, kukhulupirira malaulo ndi machitachita a mizimu zidakali zofala.

Chinali chosangalatsa kukumana ndi kupatsa moni abale athu. Amunawo anali a matupi ang’ono m’kawonekedwe koma amphamvu kwambiri. Manyazi awo achibadwa ndi kukoma mtima kwawo kunakhudza mtima wanga. Ena a anawo anali kundiwopa ine chifukwa amuna oyera amene anawadziŵa mokulira anali adokotala, ndipo anawo anali kukumbuka bwino kulasidwako!

Mudziwo unagawidwa m’mbali ziŵiri ndi malo ang’ono odzala ngole pakatipo. Theka limodzi la mudziwo linasungidwa kaamba ka awo omwe analandira chowonadi, ndipo mwamsanga ndinaphunzira chifukwa kaamba ka ichi. Ndi cholinga chofuna kutenga kaimidwe kaamba ka chowonadi ndi kupitiriza phunziro lawo la Baibulo, ena anafunikira kukhala modzipatula kwa anthu ena a m’mudziwo.

Tinyumbato tinamangidwa pamwamba pa miyulu ya nsungwi. Pamene tinalowa mu imodzi ya izo, mwamsanga ndinayambukiridwa ndi kuda kwa utsi wochokera pa moto pakati pa chipindacho. Utsiwo unapangitsa maso anga kunyerenyetsa, komabe iwo unathamangitsanso udzudzu ndi ntchentche. Chapafupipo, m’kanyumba kakang’ono kena, mkazi anali kusamalira nthuli ya buluk, kapena nyama, yoikidwa pa masamba a laplap, yakuda ndi ntchentche.

Tinaitana anthu kudzapezeka ku programu ya zithunzithunzi pa madzulo a Lachitatu. Inali kuperekedwa kwa mbiri ya Mboni za Yehova yokhala ndi mutu wakuti Kumapita Patsogolo Dziko Lonse Mosasamala Kanthu za Chizunzo. Mmodzi wa ofalitsawo anali atapita patsogolo pa ulendo wa tsiku limodzi kukaitana anthu a mmudzi ena m’mapiri. Ndinali wodera nkhaŵa kuwona ngati iwo akabwera. Pamene kunayamba chisisira, mwamuna wachichepere anafika ndi uta ndi mivi yake. Iye anatsatiridwa ndi anthu ena angapo. Ndinakondweretsedwa kuwona kuti mtundawo sunawaletse iwo kubwera ku msonkhanowu.

Mwamsanga, tinazungulidwa ndi mauta ndi mivi. Chifupifupi anthu 80 anali atabwera, ndipo tinayamba programu. Chinali chokondweretsa kumvetsera ku phokoso limene iwo ankapanga m’chilankhulo chawo pamene anazizwitsidwa ndi chinachake chimene iwo anawona pa zithunzithunzizo.

Pambuyo pa programu ya zithunzithunziyo, kukambitsiranako kunazikidwa pa miyambo ndi machitachita a anthu a kumaloko. Anthu a m’mudziwo anamvetsera mosamalitsa ndipo mwachimwemwe analandira chenjezo la Baibulo lotsutsana ndi ziwanda pa 1 Akorinto 10:20, 21. Kwa nthaŵi ina, iwo anakana zoyesayesa za amishonale a matchalitchi a Chikristu cha Dziko kuwapanga iwo kutsatira njira yamoyo yotchedwa ya Chikristu. Mwapang’ono ichi chinali chifukwa chakuti iwo sanavomerezane ndi zina za ziphunzitso zophunzitsidwa ndi amishonalewo ndipo kumbali ina chifukwa anadabwitsidwa ndi khalidwe la ena omwe anadzinenera kukhala Akristu. Tsopano, anthu a m’mudziwo anali achimwemwe kuphunzira ponena za lonjezo la Mulungu la kubwezeretsa paradaiso wa pa dziko lapansi ndi kuwukitsa akufa. Sindikanatha kuleka kulingalira za mawu a Yesu pa Yohane 8:32: “Mudzadziŵa chowonadi, ndipo chowonadi chidzakumasulani.”

Chikhulupiriro cha anthuwa ndi chikondi chawo kaamba ka Baibulo chinatanthauzanso chitsutso kaamba ka iwo. Mafumu ena a chipembedzo anakakamiza anthu a kumaloko kukhomerera mabroshuwa athu pa zitseko zawo monga chizindikiro chotanthauza kuti ‘sitikuzifuna izi pano.’ Koma mtundu uwu wa chididikizo unangopangitsa kokha ena a eninyumbawo kufuna phunziro la Baibulo ndi cholinga chofuna kupeza ponena za chowonadi. Chinali chovuta kwambiri kwa ine kusiya anthu abwino awa amene anakonda chowonadi. Ndinalonjeza kuti ndidzabwereranso ndi kuchezera midzi yawo m’mapirimo.

Kupulumuka Mphepo ya Mkuntho ya Uma

Ulendo wathu unaphatikizapo kuima pa Espíritu Santo, chisumbu china kumpoto kwa Vanuatu. Kumeneko tinachezera Mpingo wa Luganville. Ngakhale kuti kunali chabe mkulu mmodzi mu mpingo umenewo, panali mzimu wabwino pakati pa mabwenzi. Pa nkhani ya Baibulo pa Sande, tonse mosangalala tinadabwitsidwa kuwona anthu 150, kuwirikiza nthaŵi zitatu chiwerengero cha ofalitsa a Ufumu.

Tinayenera kubwerera ku Port-Vila kukakwera ndege yomwe ikatitenga ife ku mudzi ku Nouméa, New Caledonia. Pamene tinali mu Port-Vila, tinamva nkhani Lachisanu masana kuti mphepo ya mkuntho ya Uma inali pa ulendo wake. Anthu sanali odabwitsidwa kwambiri, popeza mtundu wa kachitidwe ka mphepo woterewu uli wofala pa nthaŵi imeneyo ya chaka. Kenaka chinasimbidwa kuti mphepo ya mkunthoyo inayenera kufika pa 7:00 p.m. Mwamsanga tinatumiza mauthenga kupyolera pa nyumba ya wailesi ya kumaloko kuti misonkhano yathu idzaimitsidwa. Ndipo ndinali kudandaula ponena za ulendo wathu kubwerera ku Nouméa pa Sande.

Pofika 5:30 p.m., mphepo inakhala yamphamvu kotero kuti inayamba kuswa mazenera ena. Tinazindikira kuti tinayenera kutchingirira mazenera ndi zitseko kotero kuti mphepo yonse isalowe ndi kuchotsa denga la nyumba. Mamatiresi, makama, nsalu za matabwa, ndi matebulo zinawunjikidwa moyedzamitsa mazenera ndi zitseko. Tinakhoza kumva mphamvu ya mphepo yomagunda pa nyumba, koma mwachimwemwe chirichonse chinali m’malo ake. Pambuyo pake tinadziŵa kuti mphepoyo inali yofika ku makilomita 240 pa ora limodzi usiku umenewo.

Mwamsanga panali bata. Tinatenga mwaŵi wa ichi ndi kuthamangira kunja kukawona mmene Mboni pa khomo lotsatira zinali kuchitira. Tinali odabwitsidwa kupeza kuti mitengo pabwalo pawo inagwetsedwa ndipo chipupa cha chipinda chimodzi chinagwera mkati. Alongo atatuwo anawunjikana m’chipinda china, kudikira kaamba ka thandizo. Tinayamba kudabwa kuti ndimotani mmene analiri abale athu ena. Tonse tinapemphera kwa Yehova kuti awasunge iwo.

Pofika pakati pa usiku, pambuyo pa chifupifupi maora otopetsa asanu ndi atatu, mphepo ya mkunthoyo inali kupita kum’mwera kwa chisumbucho. Koma zing’aning’ani ndi mvula zinapitiriza. Ndi kung’anima kokhazikikako, tinakhoza kuwona malata akuwuluka paliponse. Ndipo mwamsanga mvula inayamba kudonthera mkati mwa nyumba. Tsopano inali 2:30 a.m., ndipo tinalingalira za kupita ndi kuwona mmene abale athu anali kuchitira.

Zochitika za Pambuyo Pake

Makwalala anadzazidwa ndi masamba ndi nthambi za mitengo, zidutswa za mipando, madenga a malata ndi zinthu za m’nyumba. Mizati ya magetsi yachitsulo inapotozedwa ndi kugwetsedwera pansi. Tinayenera kudumpha mulu wa zinyalala zonsezi. Malo oipa a kusakaza anali patsogolo pathu. Kenaka tinapeza woyang’anira wotsogoza wa kumaloko ndi banja lake akunjenjemera m’galimoto lawo laling’ono. Denga la nyumba yawo linawulutsidwa ndi mphepo ya mkunthoyo, ndipo nyumbayo inawonongedwa. Chinali chodzetsa mpumulo kuwapeza iwo osavulazidwa.

Mphepo ya mkuntho imeneyo inafikira kukhala yosakaza koposa imene Vanuatu inakumanizana nayo mu zaka 25. Nyanja zaukalizo zinaimitsa masitima onse a m’madzi, ndipo tinaphunzira kuti anthu 46 anaphedwa kapena anali kusowa, mochulukira pakati pa awo omwe anali pa sitima ya m’madziwo. Chifupifupi anthu 4,000 anataya nyumba zawo, ndipo kuwonongedwa kwa mbewu ndi katundu kunaikidwa pa chiŵerengero cha $200 miliyoni. Tinali achimwemwe kudziŵa kuti palibe ndi mmodzi yemwe wa abale athu amene anaphedwa kapena kuvulazidwa.

Mwamsanga, komiti ya chithandizo inakhazikitsidwa. Mboni za Yehova mu New Caledonia zinatumiza zoposa mapaundi chikwi chimodzi a zopereka, kuphatikizapo chakudya, zovala, ndi zinthu zowathandiza abale kumanganso nyumba zawo. Gulu la anthu okondwerera ku mbali ina ya chisumbucho anatikupatira ife pamene anatiwona. Mbewu zawo zinawonongedwa, ndipo kokha nyumba imodzi yomangidwa mwa mtundu wakale inalaka mkunthowo. Tinatsimikizira kuti iwo anali ndi chakudya chokwanira masiku aŵiri, ndipo kenaka tinabwerera ku Port-Vila.

Maulamuliro a kumaloko anayambanso kupereka thandizo, ndipo thandizo lochokera ku maiko oyandikana nawo linayamba kubwera. Pamene kununkha kwa zinthu zowonongedwazo kunayamba kukwera, boma linalangiza anthuwo kuyeretsa mzindawo mwamsanga monga momwe kungathekere. Tinapereka malingaliro ena pa kugwiritsira ntchito madzi kotero kuti apewe kufalitsa matenda onga ngati malungo a typhoid ndi cholera.

Lachinayi lotsatira, ku chisangalatso cha aliyense, tinakhoza kupereka programu ya zithunzithunzi. Pambuyo pa msonkhanowo, tinkamva kukambitsirana kosangalatsa pakati pa mabwenzi. Ambiri a iwo anali adakamvabe kuwopsyedwa kwa kukhala atataya katundu wawo yense. Koma aliyense anasonyeza mzimu wozizwitsa wofunitsitsa kuthandiza ndi kusamalira kaamba ka zosowa za ena. Chinali chisonyezero cha umodzi wa Chikristu chotani nanga!

Pomalizira, inali nthaŵi kaamba ka ife ya kusiya abale ndi alongo athu okondedwa. Tinalimbikitsidwa mokulira ndi chikondi chawo ndi changu. Zovuta zomwe tinakumana nazo zinangotikokera ife kokha kufupi wina ndi mnzake. Pamene ndege yathu inatitulutsa kunja kwa Port-Vila, chikhumbo chathu cha mtima wonse chinali chakuti tingadzabwererenso ndi kuwawona onse a iwo kachiŵiri.​—Inaperekedwa.

[Mapu/​Zithunzi patsamba 26]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

VANUATU

ESPÍRITU SANTO

Luganville

MALEKULA

EFATE

Port-Vila

NEW CALEDONIA

Nouméa

[Zithunzi]

Port-Vila, likulu la Vanuatu

Kulalikira kwa nzika ya kumaloko

Mudzi wa kumaloko

[Chithunzi patsamba 29]

Achimwemwe kumva mbiri yabwino

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena