Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 6/15 tsamba 10-15
  • Kodi Mumayamikira Zinthu Zopatulika?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumayamikira Zinthu Zopatulika?
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Dzina la Yehova ndi Dipo​—Zopatulika Koposa
  • Unansi Wathu Ndi Yehova ndi Gulu Lake
  • Mawu a Mulungu, Malamulo, ndi Chiyembekezo cha Ufumu
  • Misonkhano Yopatulika ndi Mwaŵi
  • Ukwati ndi Banja
  • Mzimu Woyera wa Yehova ndi Pemphero
  • Kodi Mumaona Zinthu Zopatulika Monga Mmene Yehova Amazionera?
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Esau Anagulitsa Ukulu Wake
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Akristu Amapeza Chimwemwe Potumikira
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Kulemekeza Misonkhano Yathu Yopatulika
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 6/15 tsamba 10-15

Kodi Mumayamikira Zinthu Zopatulika?

“Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi chiyeretso chimene akapanda ichi palibe mmodzi adzaona Ambuye, ndi kuyang’anira . . . pangakhale wachigololo kapena [wosayamikira zinthu zopatulika, NW], ngati Esau, amene anagulitsa ukulu wake wobadwa nawo mtanda umodzi wa chakudya.”​—AHEBRI 12:14-16.

1. Ndi kusoweka kwa chiyamikiro kotani kumene anthu ambiri amasonyeza, koma kodi ndimotani mmene Akristu aliri osiyana?

YEHOVA Mulungu wathu ali Mpatsi woolowa manja. Iye mwaufulu amapereka zosowa za chilengedwe chake chonse. Unyinji wa mtundu wa anthu, ngakhale kuli tero, umapereka lingaliro lochepa ku ichi. Iwo sayamikira Yehova ndiponso sazindikira ngongole yawo yaikulu kwa iye. Akristu, ku mbali ina, samatenga ubwino wa Yehova mosasamala. Iwo amamulemekeza iye kaamba ka chimene iye amachita m’malo mwawo. Chifukwa cha kudzipereka kwawo kwa iye, Yehova wapereka kwa anthu ake unyinji wa zinthu zopatulika zomwe sizikusangalalidwa ndi mtundu wa anthu mwachisawawa. Izi ziri zinthu za mtengo wapatali, zoikidwa pambali monga zoyera ndipo zoyenera kuchita ndi kulambira Yehova. Kodi mumadziŵa zimene ziri zinthu zopatulika zimenezi? Ndipo kodi inu muli ndi chiyamikiro chozama, chochokera mumtima kaamba ka izo?​—Masalmo 104:10-28; Mateyu 5:45; Chivumbulutso 4:11.

2. Ndani amene anasonyeza kusoweka kwa chiyamikiro kowonekera?

2 Si onse a anthu a Mulungu amene moyenerera ayamikira zinthu zopatulika. Mwana wa Isake Esau, mwachitsanzo, analephera m’mbali imeneyi. Paulo analankhula za iye pamene analembera kwa Akristu odzozedwa Achihebri. Pambuyo pa kuwafulumiza “kulondola mtendere ndi anthu onse,” iye anawachenjeza iwo kutsimikizira kuti pakati pawo patsimikizire kuti “palibe wachigololo, kapena [wosayamikira zinthu zopatulika, NW], ngati Esau, amene anagulitsa [kuyenera kwake monga woyamba kubadwa, NW] mtanda umodzi wa chakudya.”​—Ahebri 12:14-16.

3, 4. Kodi ndi kuyenera kwa kuyamba kubadwa kotani kumene Esau anagulitsa kwa Yakobo ndi mbale ya mphodza?

3 Nchiyani chimene chinali kuyenera kwa woyamba kubadwa kumeneku? Yehova analonjeza agogo a Esau, Abrahamu, kuti kupyolera mwa iye ndi mbadwa zake mmodzi potsirizira pake adzabadwa amene adzakhala Mbewu ya lonjezo, Mesiya, kapena Kristu. Kupyolera mwa Mbewu imeneyi mitundu yonse idzakhala yokhoza kudzidalitsa yokha, kutsogolera ku kupulumutsidwa kwawo kuchokera ku uchimo ndi imfa.​—Genesis 22:15-18; Agalatiya 3:16.

4 Esau, mwana woyamba kubadwa wa Isake, anali ndi mwaŵi wa kukhala ndi mbali ya mzera umenewu umene ukatulutsa Mbewu imeneyo. Imeneyi inali mbali ya ukulu wa kubadwa kwake. Koma ku manyazi ake, cholembera cha Baibulo chimanena kuti: “Esau ananyoza ukulu wake.” Iye mosalingalira anagulitsa iwo kaamba ka chakudya chimodzi cha mphodza zophika ndi mkate. Ndithudi, sitikufuna kutsanzira kusoŵeka kwake kwa chiyamikiro. Ife, m’malomwake, tiyenera kukulitsa kawonedwe ka mbale wa Esau, Yakobo. Iye anali wotsatira mu mzera wa ukulu wa kubadwa, umene iye anaugula m’chiyang’aniro cha umboni wa kusoŵeka kwa chiyamikiro kwa mbale wake. Yakobo mwakutero anatsimikizira kuti kuyenera kwa kukhala kholo la Mbewu yolonjezedwayo kunaperekedwa kwa mmodzi amene moyenerera anawona monga chinthu cha mtengo wapatali chinthu chopatulika chimenechi.​—Genesis 25:27-34.

5. Kodi ndi zinthu zopatulika ziti zimene tidzalingalira, ndipo ndimotani mmene tingapewere kuzitenga izi mosasamala?

5 Mkati mwa mpingo Wachikristu, Yehova wapangitsa kukhalapo zinthu zambiri zopatulika kutisunga ife amphamvu mwauzimu ndipo moyenerera kutikonzekeretsa kaamba ka utumiki wake. Tiyeni tikambitsirane unyinji wa zimenezi. Kenaka, aliyense payekha, tingasinkhesinkhe pa izo ndi kulimbikitsa chiyamikiro chathu kaamba ka izo kotero kuti sitidzazitenga izo mosasamala.

Dzina la Yehova ndi Dipo​—Zopatulika Koposa

6. Ndi mwanjira zotani mmene tingasonyezere kuti sititenga mosasamala kupatulika kwa dzina la Yehova?

6 Choyambirira pa ndandanda yathu ya zinthu zopatulika liri dzina la Yehova. Kodi dzina limeneli liri lokwezeka chotani m’maganizo ndi mtima wanu? M’kupereka pemphero la chitsanzo, Yesu choyamba ananena kuti: “Dzina lanu liyeretsedwe.” (Mateyu 6:9) Pamene tibatizidwa, timakhala mmodzi wa Mboni za Yehova. (Yesaya 43:10, 11) Ndi ulemu wotani nanga! Ndipo pamene tilankhula ponena za ubwino wa Yehova ndi zifuno zake zazikulu, ena amafikira ku kumudziŵa iye ndi dzina lake laumwini, ndipo nawonso amafuna kumutumikira iye. Koma ngati wina anyalanyaza kulankhula ponena za iye kapena, choipa koposa, adziloŵetsa m’kuchita choipa, ichi chimabweretsa chitonzo pa dzina labwino la Yehova ndi ulemu. Mboni za Chikristu zokhulupirika za Yehova zimakalamira nthaŵi zonse kuyeretsa dzina lake loyera pamaso pa ena mwa zimene iwo amanena ndi kuchita.​—Levitiko 22:31, 32; Deuteronomo 5:11.

7. Nchifukwa ninji tiyenera kusonyeza chiyamikiro chotheratu kaamba ka nsembe ya dipo la Kristu?

7 Chomwe chiri pamwamba pa ndandanda ya zinthu zopatulika iri nsembe ya dipo. Kodi nsembe ya Kristu iri ya mtengo wapatali chotani kwa inu? Kokha pa maziko a chikhulupiriro chotheratu mu nsembe ya munthu ya ungwiro imeneyi ndi pamene tingakhale ndi machimo athu akukhululukidwa. (1 Yohane 2:1, 2) Paulo akulankhula ponena za mpingo wodzozedwa kukhala “wogulidwa ndi mwazi wa Mwana weniweni wa [Mulungu].” (Machitidwe 20:28; yerekezani ndi 1 Petro 1:17-19.) Yesu, Mwana wobadwa yekha wa Mulungu, anasiya malo ake kumwamba, kukhala padziko lapansi pakati pa amuna ndi akazi ochimwa, ndipo kenaka kupereka moyo wake wa umunthu wa ungwiro, mu imfa yowawa pa mtengo wozunzirapo ndi cholinga chakuti tikapeze moyo wosatha. (Mateyu 20:28) Ungakhale ukulu wa kusayamikira ngati wina sasonyeza kuyamikira kozama tsiku ndi tsiku kaamba ka mphatso yapadera imeneyi ya Mulungu.​—Ahebri 10:28, 29; Yuda 4, 5.

Unansi Wathu Ndi Yehova ndi Gulu Lake

8. Kodi unansi wathu ndi Yehova uli wamtengo wapatali motani?

8 Ichi chimatibweretsa ife ku nkhani ina yopatulika koposa, unansi wathu ndi Yehova. Ndi mokondeka chotani nanga mmene tiyenera kuwonera unansi wathithithi umenewu umene tiri nawo ndi Atate wathu wakumwamba. Ngati ‘tiyandikira kwa Mulungu, iye adzayandikira kwa ife.’ (Yakobo 4:8) Iye amatikonda ife koposa, ndipo amatifuna ife kuti timukonde iye ndi mtima wathu wonse. (Mateyu 22:37, 38; Yohane 3:16) Davide anapatsa mwana wake Solomo uphungu wabwino ponena za unansi wake ndi Yehova. Lophatikizidwa mu uwu linali chenjezo lakuti: “Ndipo iwe, Solomo mwana wanga, umdziwe Mulungu wa atate wako, umtumikire ndi mtima wangwiro ndi moyo waufulu pakuti Yehova asanthula mitima yonse, nazindikira zolingalira zonse za maganizo; ukamfunafuna iye udzampeza, koma ukamsiya iye adzakusiya kosatha.” (1 Mbiri 28:9) Chotero “mudzisunge nokha mu chikondi cha Mulungu ndi kulindira chifundo cha Ambuye wathu Yesu Kristu, kufikira moyo wosatha.”​—Yuda 21.

9. Ndi mwanjira zotani mmene tingasonyezere kuti sititenga mosasamala mwaŵi wapadera wa kukhala mbali ya gulu la Yehova?

9 Kodi mumayamikiranso kuti ndi mwaŵi wopatulika wotani kukhala mbali ya gulu la Yehova? Tonse a ife tiyenera kukumbukira kuti tiri mu ilo kokha chifukwa cha chifundo chokoma mtima cha Yehova. Ngati munthu atsimikizira kukhala wosayamikira ndi kukhala wochita choipa wosalapa, iye adzataya mwaŵi umenewu. Paulo anachenjeza kuti: “Chifukwa chake iye wakuyesa kuti ali chiriri, ayang’anire kuti angagwe.” (1 Akorinto 10:6-12) Paulo anapereka chenjezo limeneli pambuyo pa kunena kwa Aisrayeli 23,000 omwe anatha psyiti chifukwa cha kulambira mafano ndi chisembwere. Tingasonyeze kuyamikira kwathu kaamba ka kupatulika kwa gulu la Yehova mwa kumachita aliyense wa ife mbali yake m’kukhala maso ku zinthu zoipa, mikhalidwe ya chisembwere, mkwiyo, kukondetsa zinthu zakuthupi, ndi malingaliro a kudzimva kukhala wapamwamba ndi kunyada. (2 Akorinto 7:1; 1 Petro 1:14-16) Tingagwirire ntchito kulimbikitsa zomangira za chikondi cha ubale, pamene mosamalitsa tikusunga malamulo a teokratiki ndi kugwirizana ndi awo otenga chitsogozo.​—1 Atesalonika 4:3-8; 5:12, 13.

Mawu a Mulungu, Malamulo, ndi Chiyembekezo cha Ufumu

10. Kodi ndimotani mmene tingasonyezere kuti timayamikira mokwanira Malemba Oyera?

10 Mawu owuziridwa a Mulungu, Baibulo Loyera, lirinso lopatulika koposa. Ilo liri ndi zilengezo za umulungu, malangizo, uphungu, malonjezo, zivumbulutso, inde, zonse zimene timafunikira ‘kutikonzekeretsa ife kaamba ka ntchito iriyonse yabwino.’ (2 Timoteo 3:16, 17) Kodi ndimotani mmene tingasonyezere chiyamikiro kaamba ka ichi? Choyamba, mwa kuphunzira ilo ndi kugwiritsira ntchito zimene timaphunzira m’miyoyo yathu. Kenaka, mwa kulabadira mosamalitsa “chakudya cha pa nthaŵi yake” chozikidwa pa Baibulo chimene Yehova akupereka kupyolera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wa nzeru.” (Mateyu 24:45) Ndipo kuchokera ku kawonedwe kokhoza kugwirirapo ntchito, tifunikira kusunga makope athu aumwini a Baibulo, limodzinso ndi zofalitsidwa Zachikristu zimene timagwiritsira ntchito mu ntchito yathu yolalikira zaudongo ndi zoyera. Chingabweretse chitonzo pa Yehova ngati tipita kukachitira umboni ndi kugwiritsira ntchito Baibulo lomwe liri lakuda kwambiri kapena losawoneka bwino.

11. Nchifukwa ninji sitifunikira kutenga mosasamala malamulo opatulika a Yehova?

11 M’mawu a Mulungu muli malamulo opatulika. Kodi inu nthaŵi zonse mumawawona iwo kukhala opatulika, kapena kodi nthaŵi zina mumakhoterera ku kuwatenga iwo mopepuka? Malamulo a Yehova ali monga zizindikiro, zoika malire, ndi zochinjiriza zopereka chisungiko pa njira yopita ku moyo. Ngati timvera iwo, tidzayenda mwa chisungiko ndipo potsirizira pake tidzafika ku malo athu amene tikupitako m’dziko latsopano la Yehova; koma ngati titenga malamulo a Yehova ndi zokumbutsa zake mopepuka, ndiye kuti tikulunjika ku tsoka.​—Masalmo 119:10, 11, 35, 101, 102; Miyambo 3:1-4.

12. Kodi ndimotani mmene chiyembekezo chathu cha Ufumu chiriri chinthu chopatulika?

12 Kupyolera m’Baibulo, timaphunziranso za chinthu chopatulika chimene chiyenera kukhala chokondeka m’mitima yathu: chiyembekezo chathu cha Ufumu. Akumalankhula ponena za Abrahamu wokhulupirika, Paulo akunena pa Ahebri 11:10: “Pakuti analindirira mudzi [Ufumu wa Mulungu] wokhala nawo maziko, mmisiri wake ndi womanga wake ndiye Mulungu.” Kodi muli ndi chiyembekezo champhamvu chofananacho, chopyolera mu Ufumu wa Mulungu? Kodi chikhulupiriro chanu chiri champhamvu kotero kuti mtima wanu sumalandira zikaikiro, ndipo kodi changu chanu chimakhalabe chosazimiririka pamene mukuyembekezera kaamba ka zifuno za Mulungu kukwaniritsidwa m’nthaŵi yake yoikika?​—Mateyu 24:20-22, 33, 34, 42.

Misonkhano Yopatulika ndi Mwaŵi

13. Nchifukwa ninji sitifunikira kutenga mosasamala mapindu a misonkhano ya Chikristu?

13 “Tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena,” anachenjeza tero Paulo. Ichi chimasonyeza kuti misonkhano yathu ya Chikristu iri chopereka china chopatulika chosafunika kutengedwa mopepuka. Pa misonkhano, timalandira malangizo ofunika ndi mayanjano otentha amene timawafunikira mwachangu. Pano tingapangenso “chilengezo chapoyera cha chiyembekezo chathu” mwa kulankhula kuchokera pa platifomu pamene tiri ndi mwaŵi kapena mwa kupereka ndemanga mokhazikika. (Ahebri 10:23-25) Ndipo popeza kuti ku Nyumba ya Ufumu kuli kumene yambiri ya misonkhano imachitidwira, kodi inu mokhazikika mumaperekako ndalama ndi kugwira ntchito molimbikira kuipanga iyo kukhala yosungidwa moyenerera?​—Eksodo 35:21.

14. Nchiyani chimene chidzatithandiza ife kuyamikira kuti utumiki wathu Wachikristu uli chuma chopatulika?

14 Mwaŵi wapadera umene Akristu ali nawo wa kulalikira mbiri yabwino wayerekezedwa ndi Paulo ku “chuma m’zotengera zadothi.” (2 Akorinto 4:1, 7) Inde, utumiki Wachikristu ulinso chinthu china chopatulika chimene timayamikira mozama. Pamene kuli kwakuti ambiri kwa amene timalalikirako ali osiyanako, tiyenera kupitirizabe kudzikumbutsa ife eni za mwaŵi wapadera wokwezeka umene tiri nawo wa kuuza ena ponena za Yehova ndi zifuno zake. Mwakutero tidzakwaniritsa ntchito yathu ya kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu ndi kupanga ophunzira. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Kuwona ophunzira atsopano akupita patsogolo chiri chopangitsa chowonjezereka cha chimwemwe. (1 Atesalonika 2:19, 20) Ngati ife timawona utumiki monga chuma, sitidzakhala osakhazikika kapena osakangalika mkulalikira mbiri yabwino.

15. Nchifukwa ninji kusamalira kaamba ka mathayo mkati mwa gulu la Yehova sikufunikira kutengedwa mopepuka?

15 Mwaŵi wapadera mkati mwa gulu la Yehova ulinso wopatulika. M’chenicheni, mwaŵi woterowo uli kukhulupiridwa kopatulika. (Yerekezani ndi Machitidwe 20:28.) Kaya thayolo limaphatikizapo kuyang’anira, kuweta, kuphunzitsa, kapena mautumiki ena kwa Akristu anzathu, lipatseni ilo chisamaliro choposa cha nthaŵi zonse. Ngakhale ngati ntchitoyo iwoneka kukhala yosawonekera kwenikweni, musaitenge iyo mopepuka, koma ichiteni bwino, mwachangu, monga ngati muchita kwa Yehova. Kumbukirani, “iye amene akhulupirika m’chaching’onong’ono alinso wokhulupirika m’chachikulu.”​—Luka 16:10.

Ukwati ndi Banja

16. Kodi ndi mwanjira zotani mmene tingasonyezere kuti timalingalira ukwati ndi banja kukhala zinthu zopatulika?

16 M’kundandalika zinthu zopatulika, osaiwala kuphatikizapo ukwati ndi banja. Zowona, awo omwe sali Akristu amakwatiranso, koma kawonedwe ka Akristu ka ukwati kali kopatulika, koyambukiridwa m’kulambira kwawo Yehova. (Yerekezani ndi 1 Petro 3:1-7.) Kodi ndimotani mmene iwo amasonyezera ulemu kaamba ka chinthu chopatulika chimenechi? Baibulo limanena pa Ahebri 13:4: “Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaŵeruza Mulungu.” Yesu anachenjeza kuti kuyang’ana pa mkazi mopitiriza kotero kuti akhale ndi chilakolako kukafikira ku kuchita chigololo mumtima. (Mateyu 5:27, 28) Ngati musankha kukwatira, chitani tero mwaulemu. Kenaka, musautenge ukwati wanu mosasamala. Mangirirani chikondi chenicheni ndi ulemu wozama tsiku lirilonse. Ngati muli ndi ana, ‘aleleni iwo m’maleredwe ndi m’chilangizo cha Yehova.’ M’njira imeneyi banja lanu lidzakhala “loyera.”​—Aefeso 6:4; 1 Akorinto 7:14.

Mzimu Woyera wa Yehova ndi Pemphero

17. Nchifukwa ninji sitingatenge mosasamala mzimu woyera wa Mulungu?

17 Timafunikira zonse za zopereka za Yehova, ndipo thandizo limodzi lofunika koposa lochokera kwa Yehova liri mzimu wake woyera. (Yohane 14:26) Nthaŵi zonse sitidziŵa njira zimene Yehova amagwiritsira ntchito mzimu wake woyera m’malo mwathu, koma chinthu chimodzi chiri chotsimikizirika: Ife sitingachite chirichonse popanda iwo. Tiyenera kupemphera kaamba ka mzimu woyera kutithandiza ife kumvetsetsa ziphunzitso zowona ndi kupirira mayeso. Timaufunikira iwo kuti utithandize kukulitsa zipatso za mzimu. (Agalatiya 5:22, 23) Ndipo tikuchenjezedwa pa Aefeso 4:30 kuti tiyenera “kusakwiitsa” mzimu woyera, kudziloŵetsa mu zinthu zimene zimaletsa kubwera kwa iwo pa ife. Lolani kuti tipitirizebe kuyamikira mzimu woyera wa Yehova.

18. Nchifukwa ninji pemphero liri mwaŵi wapadera wopatulika?

18 Chinthu chopatulika chomalizira chimene tidzakambitsirana, pemphero, liri ndithudi osati chinthu chofunika chaching’ono. Iwo uli mwaŵi wapadera wotani nanga kulankhulana ndi Mfumu ya chilengedwe, Yehova! Mwachiwonekere, tiyenera kumufikira iye mwaulemu, mosabisa kanthu, ndipo osati mopepuka. Tingakhale ndi chidaliro kuti iye adzamva ndi kuyankha mapemphero athu amene amaperekedwa m’chigwirizano ndi chifuno chake. “Musadere nkhaŵa konse, komatu m’zonse ndi pemphero ndi pembedzero pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu.” (Afilipi 4:6) Pemphero lidzatipangitsa ife kukhala oyamikira za zinthu zopatulika.

19. Kodi ndi madalitso otani amene amabwera kwa awo amene moyenera amayamikira zinthu zopatulika?

19 Takambitsirana zinthu 13 zokha zopatulika zomwe sitiyenera kuzitenga mosasamala. Zowonjezereka zambiri zingatchulidwe. Ngati timayamikira zinthu zoterozo, tidzasunga unansi wabwino ndi Mulungu wathu, Yehova ndi kukhala ndi dalitso lake la tsiku ndi tsiku. Ndi mtendere wa maganizo wotani nanga umene ichi chimabweretsa, limodzi ndi chikumbumtima chabwino! Musatenge konse unansi wapadera umenewu mosasamala! Kondani Yehova ndi mtima wanu wonse, nzeru, moyo, ndi mphamvu, ndipo iye adzakukondani nthaŵi zonse. (1 Yohane 4:16) Palibe china chirichonse kuchotsapo kokha kusakhulupiririka kwanu chomwe chingaswe chomangira chachikondi chimenecho.​—Aroma 8:38, 39.

20. Kodi ndimotani mmene tingayendere mwachipambano pa msewu wopita ku moyo m’dziko latsopano la Yehova?

20 Lolani kuti tipitirizenso kukhala otanganitsidwa mu utumiki wa Ufumu, kusamalira bwino kaamba ka mwaŵi wonse wapadera ndi kuyamikira zopereka zonse zauzimu. Ndi mitima yodzaza ndi chiyamikiro, lolani kuti tikhale ogalamuka kumvera onse a malamulo opatulika a Yehova ndi zikumbutso, kuyamikira kuti izo zaikidwa kutitsogoza ife m’chisungiko pa njira ya kumoyo. Ndipo, pamene tipitirizabe kuyenda pa msewu wopapatiza umenewo ku moyo, chiri chachidziŵikire kuti Yehova sadzatisunga kokha kukhala amoyo kupyola chisautso chachikulu komanso adzatipatsa ife moyo wosatha ndi madalitso opanda malekezero m’dziko lake latsopano, tsopano lomwe liri pafupi kwenikweni. Zonsezi chifukwa timayamikira zinthu zopatulika.

Kodi Ndi Yankho Lotani Limene Mungapereke?

◻ Kodi ndimotani mmene tingapeŵere kutenga dzina la Yehova ndi nsembe ya dipo mosasamala?

◻ Kodi nchiyani chimene chingatinyenge kotero kuti sitikuyamikira unansi wathu ndi Yehova ndi gulu lake?

◻ Kodi ndi zinthu zina ziti zimene zimachitira chitsanzo chiyamikiro chathu kaamba ka Mawu a Mulungu ndi malamulo, ndi chiyembekezo cha Ufumu?

◻ Ndimotani mmene tingasonyezere kuti sititenga misonkhano ya Chikristu ndi mathayo a teokratiki mosasamala?

◻ Kodi ndi zinthu zina ziti zowonjezereka zopatulika kaamba ka zimene tiyenera kukulitsa chiyamikiro chozama?

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena