Apangidwa Wanzeru mwa “Kukhazikitsa Malipiro”
MIYAMBO 21:11, NW imanena kuti: “Mwa kukhazikitsa malipiro pa wonyoza wachibwana alandira nzeru; naphunzira pa kuyang’ana pa wanzeru.”
“Wachibwana” kaŵirikaŵiri amakhala ndi vuto la kuyamikira chifukwa chimene kachitidwe kenakake ka mkhalidwe kali kolakwika. M’kupita kwa nthaŵi, ngakhale kuli tero, iye angapenyerere pa “wonyoza”—wina yemwe amaseka pa malamulo a Mawu a Mulungu—akumagwidwa m’kuipa kwake ndi kuvutika ndi “vuto ndi nsautso.” (Miyambo 1:27) Pansi pa Lamulo la Mose, ‘chilango’ choyenera (King James Version), kapena m’chenicheni kwambiri “malipiro,” ankalipiritsidwa pa ochita cholakwa.—Yerekezani ndi Eksodo 21:22; Deuteronomo 22:19.
Chiyambukiro pa wachibwana? Potsirizira pake atawona mphoto ya kuchita zoipa iye ankakhoza ‘kukhala wanzeru’ ndi kugamulapo kusatsatira kachitidwe koteroko iyemwini. (Yerekezani ndi Miyambo 19:25.) Mwa njira yosiyanitsa, “munthu wanzeru” amakhala wodziŵa kale kuchokera ku chokumana nacho chapapitapo, kupenyerera, ndi chidziŵitso cha malamulo a Baibulo kuti kachitidwe kenakake ka mkhalidwe kali kosalongosoka kapena kowononga. Iye samafuna nthaŵi zonse kuwona chotulukapo chovulaza cha kachitidwe kenakake kuti akhutiritsidwe za kulakwika kwake. Iye chotero angakhoze kupeza ‘chidziŵitso’ chatsopano mwa kulangizidwa kokha, m’malo mwa zokumana nazo zowawa.