Kubadwa kwa Yesu—Nthano Chabe?
KUBADWA kwa Kristu! Iko kukunenedwa kukhala maziko a madyerero akulu a pa chaka a Chikristu cha Dziko. M’chenicheni, ngakhale kuli tero, atsogoleri a chipembedzo ambiri amaika pambali mbali zosiyanasiyana za zolembedwa za Uthenga Wabwino wa kubadwa kwa Yesu kukhala nthano chabe. The Interpreter’s Bible, mwachitsanzo, imanena ponena za cholembedwa cha Mateyu chonena za kuchezera kwa openda nyenyezi, kapena “amuna anzeru”: “Chotero palibe njira iriyonse yodziŵira kaya chinangopekedwa, kapena m’chenicheni, kaya ‘chinachitika’ nkomwe kukhala nsonga yeniyeni. Mapindu ndi kufunika kwa kulongosola sikumadalira pa kulondola kwake; nkhaniyo m’malomwake imafunikira kulingaliridwa kukhala ntchito ya luso.”
Kusuliza kotereku kaŵirikaŵiri kumatsutsa kuti zolembedwa za Uthenga Wabwino wa kubadwa kwa Kristu zimasowa tsatanetsatane wofunikira kuwonedwa monga mbiri yakale. Koma m’bukhu lake, The Life and Times of Jesus the Messiah, Alfred Edersheim akutsutsa chimenechi, akumanena kuti: “Chinganenedwe mwachisungiko, kuti palibe Zolembedwa Zopeka kapena kulongosola kwa nthano chochitika (cha nthano) choterecho chomwe chikanazindikiritsidwa ndi kusakwanira koteroko, kapena kusoweka kwa tsatanetsatane. Popeza kuti, zochitika zofunika ziŵiri, zofanana ndi nthano ndi mwambo, ziri, zakuti izo nthaŵi zonse zimafuna kuzinga anthu awo otchuka ndi ulemelero wokulira, ndi kuti zimayesera kupereka tsatanetsatane, amene nthaŵi zina amakhala wopereŵera.”
Nchifukwa ninji, ngakhale kuli tero, chimene Mauthenga Abwinowo amaperekera tsatanetsatane wochepera ponena za kubadwa kwa Yesu? Choyambirira chiri chifukwa chakuti imfa yake, osati kubadwa kwake, kuli kofunika koposa. (Mateyu 20:28) Edersheim akutikumbutsa mowonjezereka kuti: “Mauthenga Abwinowo sanalinganizidwe kupereka nkhani ya moyo wa Yesu, kapena ngakhale nsonga ponena za iyo; koma anali kokha ndi cholinga chokhala ndi mbali ziŵiri ichi: kuti aja oŵerenga iwo ‘angakhulupirire kuti Yesu ali Kristu, Mwana wa Mulungu,’ ndi kuti kukhulupirira mwa iye iwo ‘angakhale ndi moyo kupyolera m’Dzina Lake.’”