Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 5/1 tsamba 26-29
  • Mphamvu ya Dziko ya Chisanu ndi Chimodzi—Roma

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mphamvu ya Dziko ya Chisanu ndi Chimodzi—Roma
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Gulu la Nkhondo la Roma
  • Misewu ya Roma ndi Maina Aulemu
  • Ufumu ndi Chikristu
  • Akaisara
  • Kugwa kwa Ufumu wa Roma
  • Mafumu Aŵiriwo Asintha
    Samalani Ulosi wa Danieli!
  • Buku Limene Mungathe Kulikhulupirira—Gawo 6
    Galamukani!—2011
  • Mmene Dziko Lachikristu Linakhalira Mbali ya Dzikoli
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Sanaganize za Kulolera Molakwa!
    Nsanja ya Olonda—1993
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 5/1 tsamba 26-29

Mphamvu ya Dziko ya Chisanu ndi Chimodzi​—Roma

Ufumu wa Roma unalamulira panthaŵi imene Chikristu chinayamba. Chidziŵitso chabwino cha Roma wakale chidzakuthandizani kumvetsetsa mkhalidwe pa umene Yesu analalikira ndi mkhalidwe umene unalipo pamene otsatira ake oyambirira anafalitsa Chikristu kupyola m’dziko lodziŵika kalelo.

ROMA, mphamvu ya dziko ya chisanu ndi chimodzi ya mbiri ya Baibulo, inali kulamulira pamene Yesu anabadwa ndi pamene atumwi ake ankalalikira. Grisi, mphamvu ya dziko yapapitapo, inapereka chinenero cha dziko lonse mu chimene kuphunzitsa kwa Chikristu kunkachitidwira kupyola mbali imeneyo ya dziko​—Koine, kapena chodziŵika mofala monga, Chigriki. Tsopano Roma anapereka mkhalidwe ndi njira zimene zinathandiza m’kufalitsa kofulumira kwa chowonadi cha Chikristu.

Roma, yomwe pa nthaŵi imodzi unali mzinda waung’ono mu Latium, Italy, unakula kulamulira ufumu waukulu koposa wa dziko lonse wa nthaŵi zakale wa Baibulo. Kuti tiyambe, iwo unafutukuka kulamulira gawo la Italy. Iwo unagonjetsa Carthage wamphamvu cha ku gombe la kumpoto kwa Africa. Spain, Makedoniya, ndi Grisi inadzakhala pansi pa ulamuliro wake. Kenaka iwo unalanda Yerusalemu mu 63 B.C.E. ndipo unapanga Igupto chigawo cha Roma mu 30 B.C.E. Pa ukulu wake, ufumu waukulu umenewo unafalikira kuchokera ku Britain kupyola kupita ku Igupto ndi kuchokera ku Portugal kupita ku Mesopotamiya, dziko la Babulo wakale. Iwo unazinga kotheratu Mediterranean, yomwe unaitcha Mare Nostrum (Nyanja Yathu).

Zowonongedwa zambiri za Roma zingachezeredwebe mu ulamuliro wonse waufumu wolamulira kwanthaŵi yaitaliwo. Inu mungawone Hadrian’s Wall mu Britain, mtsinje waukulu pa Segovia mu Spain, bwalo la maseŵera la Roma pa Orange, ndi bwalo lina mu Arles, (zonse ziŵiri kum’mwera kwa France). Inu mungayende kupyola mu mabwinja okhala chete a Ostia Antica, pafupi ndi Roma, ndi kuzizwitsidwa pa Pompeii wakale, kum’mwera kwa Naples. Mu Roma inu mungayerekeze gulu lokondweretsedwa mu Colosseum ndi kuwona Arch ya Titus yomwe imakumbukira kuwononga kwake kwa Yerusalemu ndi kachisi wake mu 70 C.E., konenedweratu ndi Yesu zoposa zaka 35 pasadakhale.

Mu Roma wakale olemera anali ndi mabanja a akulu ndi ogwira ntchito ndi akapolo omwe nthaŵi zina anafika m’chiŵerengero cha mazana angapo. Osauka anawunjikidwa m’nyumba zosanjika zomwe zinandandama mwauve, m’makwalala okhotakhota. Ochepera kwambiri anakhoza kuitanidwa olemera pang’ono. Boma linkapereka zaulere ponse paŵiri zoperekedwa za chimanga ndi zosangalatsa kotero kuti osauka asadzetse chiŵaŵa. Misonkho yosonkhetsedwa m’mizinda inalipirira zowonongedwa zimenezi.

Gulu la Nkhondo la Roma

Gulu lolimba la nkhondo la Roma linapangidwa ndi chiŵerengero ndithu cha magulu. Gulu lirilonse, lokhala ndi amuna 4,500 kufika ku 7,000, linali gulu la nkhondo lathunthu mwa ilo lokha. Mtsogoleri wake anali ndi thayo lokulira kwa wolamulira. Gululo linagawidwa m’magulu mazana 60, nthaŵi zambiri lokhala ndi amuna zana limodzi gulu limodzi. Zanalo linali pansi pa utsogoleri wa Kenturiyo, wotchedwa “nduna ya gulu la nkhondo” mu New World Translation. Anali Kenturiyo yemwe anali ndi lamulo la asilikari anayi omwe anapha Yesu ndi omwe, powona mikhalidwe ndi zochitika zozizwitsa pa imfa yake, ananena kuti: “Ndithudi uyu anali Mwana wa Mulungu.” (Mateyu 27:54; Yohane 19:23) Analinso Kenturiyo, Korneliyo, yemwe anali woyamba wosakhala m’Yuda wosadulidwa woyamba kukhala Mkristu.​—Machitidwe 10:22.

Maguluwo anali ndi miyezo, mwachiwonekere mafano kapena zizindikiro zopangidwa ndi matabwa, kapena zitsulo, zomwe zinatumikira chifuno chofanana ndi chija chotumikiridwa ndi mbendera zamakono. Polingaliridwa zopatulika, izi zinalondedwa pa imfa ya moyo wa munthu. Encyclopædia Britannica yanena kuti: “Miyezo ya Roma inalondedwa ndi kuyera kwa chipembedzo m’makachisi a Roma. Sichinali chosakhala cha nthaŵi zonse kaamba ka nduna kulamulira muyezo kuti uikidwe m’mathayo a mdani, m’malo mwa kuwonjezera changu ku kachitidwe ka asilikari ake mwa kuwasonkhezera iwo kupeza chimene kwa iwo chinali chinthu chopatulika kwenikweni chomwe dziko lapansi linali nacho.”

Misewu ya Roma ndi Maina Aulemu

Roma anapanga mitundu yomwe anailamulira kukhala ufumu wa dziko. Iye anapereka misewu kupangitsa mbali zonse zaufumu umenewo kukhala zofikirika. Anthu anayenda! Tangoyang’anani kokha pa ndandanda ya malo kumene anthu anachokera omwe anabwera ku Yerusalemu kaamba ka Phwando la Pentekoste wa 33 C.E. Iwo anachokera ku Media kutali kumpoto cha kum’mawa kuchokera ku Roma ndi Kumpoto kwa Africa kutali cha kumadzulo, ndi kuchokera ku malo ochulukira apakati.​—Machitidwe 2:9-11.

Zochulukira za njira zake zokhazikitsidwa ndi opanga njira a ku Roma zikali kugwiritsiridwabe ntchito lerolino. Chakum’mwera kwa Roma, inu mungayende cha mphepete mwa Appian Way yakale, pamene mtumwi Paulo iyemwini analowera mu Roma. (Machitidwe 28:15, 16) Chanenedwa kuti misewu ya Roma “inapereka ziŵiya kaamba ka kayendedwe ka dziko losalakidwa kufikira kudza kwa njira za njanji.”​—The Westminster Historical Atlas to the Bible.

M’kulamulira ufumu wawo waukuluwo, Aroma kaŵirikaŵiri anasungilira miyambo ya kumaloko. Chotero, maulamuliro m’madera osiyanasiyana anadziŵika ndi maina ambiri osiyanasiyana kapena maina aulemu. Mu Modern Discovery and the Bible, A. Rendle Short wanena kuti ngakhale “odziŵa mbiri yakale ozindikirika a ku Roma” sanayesere “kupatsa nduna zimenezi magulu awo olondola.” Komabe, iye akunena kuti, wolemba wa Baibulo Luka “nthaŵi zonse anayesera kufikira kulondola kwangwiro” m’nkhaniyi. Mwachitsanzo, Luka amatcha Herode kukhala “chiwanga,” Herode Agrippa kukhala “mfumu,” nduna za ku Tesalonika kukhala “andale,” ndi Sergio Paulo, wolamulira wa Cyprus, kukhala “kazembe.” (Luka 3:1; Machitidwe 25:13; Machitidwe 17:6; Machitidwe 13:7; onani mawu a mmunsi mu New World Translation Reference Bible) Nthaŵi zina panali kokha ndalama yopezedwa pano kapena mawu ozokotedwa pamenepo omwe anachitira umboni kuti wolemba Baibulo ameneyu anagwiritsira ntchito mawu aulemu olondola panthaŵi yoyenera. Kusamalira koteroko ndi kulongosoka kuli umboni wowonjezereka wa kuwona kumene Baibulo limandandalitsa zenizeni za m’mbiri ya moyo ndi nthaŵi ya Yesu Kristu.a

Ufumu ndi Chikristu

Mpingo Wachikristu womakula unalimo mu Roma. Iwo mwachidziŵikire unapangidwa ndi aja omwe anabwerera ku Roma pambuyo pa kulandira Chikristu mu Yerusalemu pa tsiku la Pentekoste wa 33 C.E. (Machitidwe 2:10) Bukhu la Baibulo la Aroma linalembedwa ku mpingo umenewu chifupifupi chaka cha 56 C.E. Pambuyo pake, Paulo anabwera ku Roma monga wandende, ndipo kwa zaka ziŵiri iye anapereka umboni wotheratu kwa anthu omwe anachezera nyumba yake ya m’ndende. Chotero, ziwalo za nduna Zolonda za Mfumu zinaphunzira ponena za uthenga wa Ufumu, ndipo ngakhale ziwalo za “nyumba ya Kaisara” zinakhala Akristu.​—Afilipi 1:12, 13; 4:22.

Miyambo, malamulo, ndi miyezo ya Ufumu wa Roma zimatchulidwa kaŵirikaŵiri m’Baibulo. Lamulo la Augustus linabweretsa Yosefe ndi Mariya ku Bethlehem, kumene Yesu anabadwira. Yesu anatsimikizira kulondola kwa kulipira msonkho umene Kaisara anaufuna. Ansembe a Chiyuda anadzinenera kukhala okhulupirika kwa Kaisara m’malo mofuna kupha Yesu. Ndipo pansi pa lamulo la Roma, mtumwi Paulo Wachikristu anachita apilu mlandu wake kwa Kaisara.​—Luka 2:1-6; 20:22-25; Yohane 19:12, 15; Machitidwe 25:11, 12.

Chovala cha nkhondo cha msilikari wa Roma​—chisoti chake, cha pachifuŵa, chikopa, choveka mapazi, ndi lupanga​—zinagwiritsiridwa ntchito kuchitira chitsanzo phindu la chowonadi, chiyembekezo cha chipulumutso, chilungamo, chikhulupiriro, kulalikira mbiri ya bwino, ndi Mawu a Mulungu monga zochinjiriza zomwe zimatithandiza ife kuima olimba molimbana ndi kumenyera kwa Satana. (Aefeso 6:10-18; 1 Atesalonika 5:8) Kunali ku chitsanzo cha m’silikari wachiRoma wophunzitsidwa bwino kumene Paulo analozerako pamene anauza Timoteo kukhala “msilikari wabwino wa Kristu Yesu.” (2 Timoteo 2:3, 4) Komabe, nkhondo ya Chikristu inali yauzimu, osati ya kuthupi. Chotero, Akristu oyambirira anakana kutumikira m’gulu la nkhondo la Roma. Justin Martyr (110-165 C.E.) ananena kuti Chikristu “chinasintha zida zathu zonga za nkhondo,​—malupanga athu kukhala zolimira, ndi nthungo zathu kukhala zosakulira.” Akristu ambiri anataya miyoyo yawo kaamba ka kukana ntchito ya m’gulu la nkhondo.

Akaisara

Roma anafikira ukulu wa ulemerero wake pansi pa Akaisara. Chikakhala bwino kubwerera mu nsonga zokulira za oŵerengeka a iwo, popeza kuti anali ophatikizidwa m’mbiri ya Baibulo.

M’chaka cha 44 B.C.E., Julius Caesar anaphedwa. Potsirizira pake Octavian anadzakhala wolamulira wamkulu. Mu 30 B.C.E., Octavian anagonjetsa Igupto, akumabweretsa mapeto ku ufumu wa Griki Ptolemaic kumeneko. Ichi chinabweretsa mapeto otsirizira ku mphamvu ya dziko ya Grisi imene inalipo chiyambire nthaŵi ya Alexander Wamkulu, zaka 300 zoyambirirazo.b

M’chaka cha 27 B.C.E., Octavian anadzakhala mfumu. Iye anatenga dzina laulemu lakuti “Augustus,” kutanthauza “wokwezeka, wopatulika.” Iye anapatsanso dzina mwezi kaamba ka iyemwini ndipo anabwereka tsiku kuchokera ku February kotero kuti August akhale ndi masiku ochulukira olingana ndi mwezi wopatsidwa dzina la Julius Caesar. Augustus anali mfumu pamene Yesu anabadwa, ndipo analamulira kufikira chaka cha 14 C.E.​—Luka 2:1.

Tiberiya, wolowa m’malo mwa Augustus, analamulira kuchokera mu 14 mpaka 37 C.E. M’chaka cha 15 cha kulamulira kwa Tiberiya, Yohane Mbatizi anayamba kulalikira. Munalinso mkati mwa kulamulira kwake pamene Yesu anabatizidwa, kuchita utumiki wake wa zaka zitatu ndi theka, ndi kupereka moyo wake monga nsembe. Iye anali kulamulirabe pamene atsatiri a Yesu anayamba kufalitsa Chikristu kupyola m’dziko lodziŵika kalelo.​—Luka 3:1-3, 23.

Gaius, wopatsidwa dzina lopeka lakuti Caligula, analamulira kuchokera mu 37 mpaka 41 C.E. Claudius (41-54 C.E.) anamulowa iye m’malo ndipo anapitikitsa Ayuda kuchoka mu Roma, monga mmene zanenedwera pa Machitidwe 18:1, 2. Iye pambuyo pake, anapatsidwa mankhwala akupha ndi mkazi wake, ndipo mwana wake wamwamuna wachichepere Nero anakwera pa mphando wachifumu. Moto waukulu unasesa kupyola Roma mu July 64 C.E., ukumapha chifupifupi kota ya mzindawo. Wodziŵa za mbiri yakale Tacitus wanena kuti kuchotsapo mlandu pa iye, Nero anapatsa mlandu wa motowo pa Akristu, omwe pambuyo pake “analumidwa ndi agalu ndi kufa” ndipo “anasakazidwa ndi makala a moto ndi kupsya, kutumikira monga chowunikira usiku, pamene kuwunika kwa masana kunatha. Nero anapereka minda yake kaamba ka chochitikacho.” Mkati mwa chizunzo chake, Paulo, yemwe analalikira kuchokera ku Yerusalemu mpaka Roma ndipo mwinamwake ngakhale ku Spain, anaikidwa m’ndende kwa nthaŵi yachiŵiri. Iye mwachidziŵikire anaphedwa ndi Nero chifupifupi 66 C.E.

Mafumu ena a Roma omwe amatikondweretsa ife amaphatikizapo Vespasian (69-79 C.E.) amene pa kulamulira kwake Titus anawononga Yerusalemu, Titus iyemwini (79-81 C.E.), ndi mbale wa Titus Domitian (81-96 C.E.), yemwe anawukira kuzunza kwa lamulo kwa Akristu. Molingana ndi mwambo, munali mkati mwa chizunzo chimenechi pamene mtumwi wachikulire Yohane anaikidwa m’ndende pa chisumbu cha Patmos. Pamenepo iye anapatsidwa masomphenya odabwitsa a mapeto a dongosolo loipa iri la zinthu ndi kulowedwapo m’malo kwake ndi Ufumu wakumwamba wolungama wa Mulungu, umene Yohane anaulemba m’bukhu la Baibulo la Chivumbulutso. (Chivumbulutso 1:9) Yohane mwachiwonekere anamasulidwa mkati mwa kulamulira kwa mfumu yotsatira, Nerva, 96-98 C.E., ndipo Uthenga wake ndi makalata ake atatu anatsirizidwa pambuyo pa kuyamba kulamulira kwa Trajan (98-117 C.E.)

Kugwa kwa Ufumu wa Roma

Mu zana lachinayi, Mfumu Constantine anagamulapo kugwirizanitsa anthu pansi pa “Chikatolika” chimodzi, kapena chipembedzo, cha dziko lonse. Miyambo ya kunja ndi madyerero anapatsidwa maina a “Chikristu,” koma kuipitsa kofananako kwa kale kunapitirizabe. M’chaka cha 325 C.E., Constantine anatsogolera pa bungwe la tchalitchi lokhala pa Nicaea ndipo anagamulapo mokomera chiphunzitso cha Utatu. Kutalitali ndi kukhala Mkristu wowona, Constantine mwamsanga anapeza chifukwa cha kuphera mwana wake wamwamuna wamkulu, Crispus, ndi mkazi wake, Fausta.

Constantine anasamutsa boma lake ku Byzantium, limene analipereka monga Roma Watsopano ndipo pambuyo pake Constantinople (Mzinda wa Constantine). Mzinda umenewo wokhala pa Bosporus, kumene Europe ndi Asia amakumanira, unakhala likulu la Ufumu wa Roma chakum’mawa kwa mazana 11, kufikira unagwa kwa Ottoman Turks mu 1453.

Kubwerera ku Roma, chigawo cha kumadzulo cha Ufumu wa Roma chinagwa mu 476 B.C.E., pamene mfumu inasakazidwa ndi Mfumu Odoacer, nduna ya mbadwa ya chiGerman, ndipo mpando wachifumu unasiidwa wopanda munthu. Pambuyo pake Charlemagne anayesera kubwezeretsa ufumu wa kumadzulo ndipo m’chaka cha 800 C.E. iye anapatsidwa chisoti cha ufumu ndi Papa Leo III. Kenaka, mu 962 C.E. Papa John XII anaveka chisoti cha ufumu Otto I mfumu ya Ufumu Woyera wa Roma wa mtundu wa chiGerman​—dzina la ulemu lomwe linakanidwa kokha m’chaka cha 1806.

Komabe, panthaŵi imeneyo mphamvu ya dziko yachisanu ndi chiŵiri ndi yothera ya mbiri ya Baibulo inkatuluka. Monga momwe kunaloseledwera, iyo nayonso ikapita, kuti ikalowedwe m’malo ndi boma lokhazikika, Ufumu wa kumwamba wa Mulungu.​—Chivumbulutso 17:10; Danieli 2:44.

[Mawu a M’munsi]

a Onani “All Scripture Is Inspired of God and Beneficial,” masamba 340-1.

b Chotero, mkati mwa kulamulira kwa Roma mngelo anakhoza kunena ponena za mphamvu zadziko zimenezi: “Ndipo ali mafumu asanu ndi aŵiri: asanu adagwa [Igupto, Asuri, Babulo, Medi-Peresiya, ndi Grisi], imodzi iriko [Roma], inayo [Anglo-America] siinadze.”​—Chivumbulutso 17:10.

[Mapu patsamba 26]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Ukulu wa Ufumu wa Roma

Nyanja ya Atlantic

BRITANNIA

GAUL

SPANYA

ITALIYA

Roma

GRISI

Nyanja ya Mediterranean

Black Sea

Nyanja ya Caspian

IGUPTO

Yerusalemu

Tigrisi

Firate

[Chithunzi patsamba 28]

Appian Way pamene Paulo anayendapo pa ulendo wake wopita ku Roma

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena