Chidziŵitso pa Nyuzi
Chiŵaŵa Chonenedweratu
“Anamwali akukhala achiŵaŵa kwambiri kuposa mmene iwo analiri m’zaka zingapo zapitazo,” akudziŵitsa tero James Fox, katswiri wa upandu pa University ya Northeastern. “Ndikuwona kusintha kwenikweni mu mtundu wa achichepere omwe tikupeza,” akulongosola tero Faye Harrison, woweruza wa ku Michigan. “Ali olimba kwambiri, ofulumira kwambiri (ku chiŵaŵa), ozama kwambiri ku mkhalidwe wa kusamvera pa msinkhu wa uchichepere.” M’chenicheni, a zaka za pakati pa 13 ndi 19 okulira ali ndi “thayo la chifupifupi 300 ya upandu wa parricides (kupha kwa makolo) kochitidwa ndi anamwali chaka chirichonse,” ikusimba tero Detroit Free Press.
Nchifukwa ninji pali kuwonjezeka kwa chiŵaŵa pakati pa achichepere a lerolino? Fox akutchula kukhalapo kokulira kwa zida, chiŵaŵa cha pa wailesi ya kanema, ndi “mwachisawawa, kusoweka kwa ulemu kaamba ka ulamuliro,” mogwirizana ndi USA Today. Akumalunjikitsa chidwi pa makolo, David Ramirez, woweruza wa ku Denver, akukhulupirira kuti “mapindu ndi malingaliro a mwambo aulemu sakuperekedwa kwa ana ndipo makolo ambiri akuwoneka kukhala akusowa kudzipereka kotheratu kwa achichepere awo,” ikudziŵitsa tero The Denver Post.
Apanthaŵi yake kwenikweni ali mawu olembedwa ndi mtumwi Paulo pamene, zaka mazana angapo apitawo, iye ananeneratu “kuti m’masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zowawitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, . . . osamvera akuwabala, . . . opanda chikondi chachibadidwe, . . . osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino.” (2 Timoteo 3:1-3) Akristu angakhoze kudzichinjiriza molimbana ndi kulowerera kwa mikhalidwe yotereyi mwa kumangilira unansi wa banja wachikondi, monga mmene kwasonyezedwera mu ndime za Baibulo zonga ngati Deuteronomo 6:4-9 ndi Akolose 3:12-14, 18-21.
Kulipira Mtengo
“Sitiŵerenga Baibulo ndipo sitidziŵa zimene ziri mu ilo,” anatero wosonkhanitsa chidziŵitso wa ku America George Gallup, Jr. “Tikulipira kaamba ka ichi ndipo tikuvutika mofananamo mu liŵiro la chisudzulo, kuipsya ana, kugwiritsira ntchito molakwa anamgoneka, ndi kunama ndi kusawona mtima pa miyezo yonse ya chitaganya.” Mogwirizana ndi kusonkhanitsa chidziŵitso cha chitaganya, 40 peresenti ya anthu a ku America amapezeka mu tchalitchi pa Sande ndipo chifupifupi 80 peresenti amakwatiwa mu tchalitchi, komabe liŵiro la chisudzulo lawirikiza nthaŵi zitatu kuyambira 1960, chiŵerengero cha anthu osakwatirana okhala pamodzi chawonjezeka chifupifupi nthaŵi zisanu, ndipo chiŵerengero cha ana obadwira m’tchire chawirikiza chifupifupi nthaŵi zinayi. Kuchotsa mimba kwawonjezeka nthaŵi zitatu pakati pa 1972 ndi 1979.
Akumaloza mwachindunji ku muzu wa vutolo, Gallup anawona kuti: “Mwachiwonekere matchalitchi sakulowerera ku mlingo weniweni wa kuzamitsa mapindu. Tikukhala m’chipembedzo ku mlingo wa pamwamba koposa. Icho sichikusintha moyo ndipo sichikutsogozanso. Ndiponso sichiri chozikidwa pa Baibulo.”
Komabe Chikristu chiyenera kukhala chosintha moyo, kutsogozanso ndi chozikidwa pa Baibulo. Pa chiyambi icho chinali tero. Akristu oyambirira anaphunzitsidwa “kuvula umunthu wakale.” Paulo analemba kuti: “Adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsya ndi amuna, kapena mbala, kapena osirira, . . . sadzalowa Ufumu wa Mulungu. Ndipo ena a inu munali otere.”—Aefeso 4:22; 1 Akorinto 6:9-11.
“Munthu Woyamba Anali Munthu”
Anthanthi ya chisinthiko ena amanena kuti chisinthiko chiri chokhulupiririka “maperesenti zana limodzi” ndipo kuti chiri “nthanthi imene wina angaitsimikizire m’chipinda chofufuzira zinthu.” Koma pa Msonkhano Wachiŵiri wa Mitundu Yonse wa Human Paleontology, posachedwapa wochitidwira mu Turin, Italy, chinamvekera kuti asayansi ambiri anali kukaikirabe pa nkhaniyo.
M’malo motsimikizira chisinthiko kukhala chokhulupiririka “maperesenti zana limodzi,” msonkhanowo mwachiwonekere unavumbula kusiyana kokulira kwa kawonedwe pakati pa asayansi ponena za ndi liti ndipo ndimotani mmene munthu anasinthikira. Katswiri wodziŵa za moyo wakale kupyolera mu Zofukulidwa pansi Bernard Vandermeersch, mwachitsanzo, anamveketsa nsonga yakuti, molingana ndi mmene chiyambi cha munthu chikukhudzidwira, zotulukapo za sayansi yodziwa moyo wakale kupyolera mu zofukulidwa pansi “imatsutsana ndi chidziŵitso choperekedwa ndi sayansi yodziwa za chiyambi cha munthu,” imene imaloza ku kholo limodzi.
Ngakhale kuli tero, kutsutsana koteroko kulipo kokha pakati pa anthu omwe amalephera kulandira chowonadi chopepuka chakuti Mulungu “ndi mmodzi analenga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pa nkhope ya dziko lapansi.” (Machitidwe 17:26) Ndimotani mmene iye anachitira motero? Genesis 2:7 amatiwuza ife kuti “Mulungu anawumba munthu ndi dothi lapansi, nawuzira mpweya wamoyo mphuno mwake,” akumupangitsa munthuyo kukhala “wamoyo.”
Mosadabwitsa, katswiri wodziwa za moyo wa zolengedwa Giuseppe Sermonti, akuchitira ndemanga pa mapeto ofikiridwa ndi msonkhanowo, anavomereza kuti “zoyesayesa zonse zotipangitsa ife kutsika ku mitengo ya anyani zatulutsa zotulukapo zosakondweretsa. Munthu woyambirira anali munthu.”