Kutsegula Njira ku Chiwonjezeko mu Gibraltar
BWALO la maseŵera liri lowonekera bwino pa Gibraltar—kokha chifupifupi mailosi imodzi kutali. Komabe, kwa zaka zoposa 13, anthu a ku Gibraltar anayenera kupanga ulendo wa chifupifupi maora khumi kukafika kumeneko. Chimenecho chinaphatikizapo ulendo wa pamadzi choyamba kupita Kumpoto kwa Africa, kenaka kupita ku Spain, ndipo pomalizira kukwera basi. Nchifukwa ninji ulendo wautali chotero kupita ku malo apafupi chotero?
Mu 1969 ulamuliro wa chiFrench wa Spain unatseka malire pa malo ochepa a pamtunda m’madzi olumikiza Spain ndi Gibraltar. Chinali chotulukapo cha mkangano pakati pa Spain ndi Britain pa ulamuliro wa gawolo ponena za Rock, monga mmene Gibraltar amadziŵikira kaŵirikaŵiri. Kusokoneza koteroko, ngakhale kuli tero, sikunali kwachilendo kwa anthu a ku Gibraltar. Chifukwa cha ubwino wake wokhala ndi cholinga chapadera, Gibraltar wakhala linga kaŵirikaŵiri wopatulidwa kuchokera ku maiko oyandikana nawo.
Kumayambiriro kwa zana lachisanu ndi chitatu, olowerera a chiMoor pansi pa Ṭārik analanda chidutswa cha dziko chimenechi ndi kuchitcha “Jabal Ṭāriq” (phiri la Ṭārik), chimene kuyambira panthaŵi imeneyo chinawonongedwa kukhala “Gibraltar.” Anthu a chiMoor mwamphamvu analimbitsa Rock, yomwe inakwera chifupifupi 430 m pamwamba pa nyanja. Mkati mwa zaka mazana, iwo anali malo a kulandidwa kosaŵerengeka ndi maMoors ndi anthu a ku Spain. Anthu a ku Spain pomalizira anatenga Gibraltar mu 1462, kuisunga iyo kufikira 1704, pamene anthu a ku Britain anailanda iyo ndi kumanga malo a zida za nkhondo kumeneko.
M’kuwonjezera ku kukhala malo ochinjirizira, anthu ochokera ku maiko ambiri anakhazikika mu mzinda womwe uli m’munsi mwa Rock, kupereka chiŵerengero chachikulu cha anthu osakanizana ochokera makamaka kwa maMoors, Spanish, British, Ayuda, ndi Genoese. Chiŵerengero chachikulu cha anthuwo tsopano amalankhula chiSpanish ndi Chingelezi.
Chowonadi cha Baibulo Chifika ku Gibraltar
M’nthaŵi zamakono, mbewu za chowonadi cha Baibulo zinabzyalidwa choyamba mu Gibraltar m’chirimwe cha 1958. Mboni za Yehova zoyenda kukapezeka ku msonkhano mu London, England, zinatenga mwaŵi wa kucheza kwawo pa doko la Gibraltar kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu. Nzika zina zinalandira kulembetsa kwa Nsanja ya Olonda.
Amishonale aŵiri okwatirana anafika mu Gibraltar chaka chotsatirapo kudzatsirira “mbewu” zimenezo. Koma olamulira anapereka chitsenderezo chochokera kwa atsogoleri a zipembedzo ndi kuthamangitsa okwatirana aŵiriwo pambuyo pa zaka ziŵiri. Komabe, gulu lochepa la Mboni 25 linapangidwa, ndipo ntchito yawo yokhulupirika mkati mwa zaka yafupidwa ndi chiwonjezeko chokulira, kufikira ku ofalitsa a Ufumu 132 mu March 1987. Ndithudi, kukula kumeneku kumatsimikizira kupirira kwa mpingo pamaso pa mavuto odziŵika ku Gibraltar.
Kupatulidwa—Vuto Lapadera
Pambali pa mavuto a za chuma ndi za mayanjano amene mokulira anabuka kuchokera ku kutsekedwa kwa malire, Mboni za Yehova zinatsekerezedwa kwambiri m’kuyanjana ndi ena achikhulupiriro chawo m’mipingo yoyandikana nayo ya mu Spain. Mkati mwa zaka 13 za kutsekedwa kwa dziko kumeneko, ngakhale kuli tero, iwo sanaphonye pa chakudya chauzimu cholemera choperekedwa ponse paŵiri pa misonkhano yadera ndi misonkhano yachigawo. Programu ya nthaŵi zonse inali kubwerezedwa pambuyo pake ku Nyumba ya Ufumu ya kumaloko mu Gibraltar.
Kupatulidwa kokakamiza kunapereka chiyeso chapadera kwa achichepere a mu mpingowo. Otsenderezedwa kokha ku gawo la mu Gibraltar la 5.8 sq km, iwo anayenera kuchita mwanzeru m’kuyang’anizana ndi mkhalidwe wa utundu, kukondetsa zakuthupi, ndi ukwati.
Ukwati? Inde, popeza kukhala otsekeredwa kokha ku mpingo wawo waung’ono kunapereka mwaŵi wochepa wa kupeza anzawo a mu ukwati oyenerera. Ziwalo zazikazi za mpingowo zinali kugwidwa ndi ziitano za achichepere a kudziko omwe anafuna kukacheza ndi iwo. Mboni zachichepere za mu Gibraltar zinayenera kutenga ku mtima uphungu wanzeru wa Baibulo wa kukwatira “kokha mwa Ambuye.”—1 Akorinto 7:39; yerekezani ndi Genesis 24:1-4.
Pa chochitika chimodzi Mboni yachichepere, ikunyalanyaza uphungu wochokera kwa Mkonzi waukwati, inayamba kucheza ndi mtsikana wa kumaloko yemwe sanali chiwalo cha mpingo. Koma thandizo loleza mtima la akulu mu mpingowo linamupangitsa iye kulingalira mosamalitsa ponena za ngozi zolowetsedwamo. Pomalizira pake, iye anafikira bwenzi lake lachikazilo ndi kuliuza kuti ngakhale kuti anali ndi chikondi chokulira kaamba ka iye, chidziŵitso chake cha Baibulo chinamukakamiza iye kuthetsa unansi wawo. ‘Ndikufuna kukwatira mtsikana amene ndidzakhala naye ndi moyo kosatha, osati kokha kwa zaka zochepa,’ iye analongosola.
Ngakhale kuti anadodometsedwa ndi kukhumudwa, iye anafulumizidwa kudziŵa kokha nchiyani chimene chinamusangalatsa iye koposa unansi wawo. Kenaka anayamba kuphunzira Baibulo. Chimene chinayambika monga kufunitsitsa kunakula kukhala chikondwerero chenicheni, ndipo anapanga kupita patsogolo kofulumira m’chowonadi ndipo anabatizidwa. Pambuyo pa chisonyezero chowonekera bwino ichi cha chikhumbo chake cha kutumikira Yehova, mbaleyo anayambitsanso ubwenziwo. Nthaŵi ina pambuyo pake iwo anakwatirana mwachimwemwe, akumatuta madalitso a kutsatira uphungu wanzeru wa Yehova pa ukwati.
Kutsegula kwa Malire Kutsogolera ku Chiwonjezeko cha Teokratiki
December 14, 1982, inawona kutsegula kwa chipata cha oyenda pansi pa malire. Kenaka pa February 6, 1985, njira yaufulu inabwezeretsedwa kotheratu. Anthuwo anagwera m’mkhalidwe wa mpumuloko. Kutengera mwaŵi pa kukula kumeneko, mpingo wa kumaloko unapititsa patsogolo ntchito ya kuchitira umboni ndi kugwiritsira ntchito mwaŵi wa kukumana pamodzi m’magulu okulirapo. Anthu okhala ndi chiyanjo chabwino tsopano anali ndi mwaŵi wokulira wa kufika kukudziŵa chikondi ndi chigwirizano chomwe chiri pakati pa magulu osonkhana a Yehova.
Mwachitsanzo, mwamuna amene mkazi wake anali Mboni kwa zaka 20 analingalira za kulandira chiitano cha kutsagana ndi mkazi wake ndi ana pamene anapita kukapezeka pa msonkhano wadera mu Spain. Iye anasangalala ndi programu ndi mayanjano mokulira kotero kuti anasankha kukhala kaamba ka tsiku lachiŵiri. Pamene msonkhanowo unatsirizidwa, iye anagawiridwa phunziro la Baibulo la panyumba. “Nchifukwa ninji ayi?” iye anayankha, kuwonjezera kuti, “Bwanji kuyamba mlungu uno?” Mkazi wake, pambuyo pa zaka zambiri za kupemphera kaamba ka chotulukapo choterocho, anakondwera koposa.
Kuti agwiritsire ntchito mokwanira mwaŵi wowonjezereka wa kulalikira, chiŵerengero cha Mboni chotumikira monga apainiya othandizira (awo amene amapereka maora 60 pa mwezi ku utumiki wa poyera) chinawonjezereka. Ntchito ya changu yoteroyo inabweretsa chiwonjezeko cha chifupifupi 35 peresenti mu mipingo chiyambire 1982.
Kuchitira umboni mwamwaŵi kwachitanso mbali yaikulu m’kukula kwa mpingo. Mboni ziŵiri zofufuza pa gombe mkati mwa ntchito yawo yakuthupi zinawona New World Translation Bible yomwe inali kuwonekera pang’ono kupyolera mu m’bowo wa pa gombe la sitima ya pamadziyo. Mwamsanga, iwo anafunafuna mwiniwake. Zinapezeka kuti iye anali woyendetsa sitimayo, yemwe anali ataphunzirapo ndi Mboni za Yehova ku Britain asanabwere posachedwapa kudzakhazikika mu Gibraltar. Iye mofulumira anayambitsanso phunziro lake ndipo anapanga kupita patsogolo limodzi ndi mnzake wa mkazi. Mwamsanga iwo anakhazikitsa mwalamulo kaimidwe kawo ka mu ukwati ndipo anabatizidwa. Okwatirana aŵiri a ku Britain amenewa tsopano amapereka yochulukira ya nthaŵi yawo kuithera mu utumiki kugwira limodzi ndi gulu lolankhula Chingelezi ndipo akhala othandiza m’kukhazikitsa gulu la phunziro kumeneko.
Phunziro limodzi la Baibulo lomwe analiyambitsa linali kwa Tim ndi Tracy, achichepere okwatirana aŵiri okhala mu malo a ankhondo. Ngakhale kuti Tim anali kuseŵera trombone mu oimba a gulu la nkhondo, iye anakhala wotsimikiza kudzipereka iyemwini kotheratu ku zikondwerero za mtendere za Ufumu wa Yehova. Achibale anabweretsa chitsenderezo pa okwatirana aŵiriwo, kuwakakamiza iwo kusiya kuyanjana ndi Mboni. Ngakhale kuli tero, iwo anapitirizabe phunziro lawo la Baibulo ndi kukhala abwinopo m’chikhulupiriro chawo.
Tim anafunsa kuti achotsedwe, ngakhale kuti iye poyambirira anali atandandalitsidwa kaamba ka nyengo ya utali wa zaka zisanu ndi chimodzi. Pamene kubwereramo m’nkhani yake kunawoneka kuti kunali kuchedwetsedwa mosayenerera, Tim anatenga kulimba mtima kwa kulankhula kwa dokotala wa asilikari, kulongosola kuti kusatsimikizirika kwa mtsogolo mwawo kunali kuyambukira mkazi wake mokulira. Dokotalayu anavomereza ndi kugwiritsira ntchito chisonkhezero chake kufulumiza kubwereramoko. Mwamsanga Tim anatumizidwa ku England ndi gulu lake lankhondo, kumene iye pomalizira anapeza chipambano chake cha kuchotsedwa. Tsopano onse aŵiri akutumikira monga Mboni zodzipereka.
Ziyembekezo za Mtsogolo
Okhala ndi malire otsegulidwa, Mboni mu Gibraltar zakhalanso zokhoza kupereka dzanja la thandizo ku mipingo ya pafupipo ya chiSpanish. Iwo amalalikira m’mbali mwa Costa del Sol (Gombe la Dzuŵa), kumene anthu ambiri olankhula Chingelezi amapezeka.
Ngakhale kuti “funso la Gibraltar” likuwoneka kukhalabe losayankhidwa kuchokera ku kayang’anidwe ka ndale zadziko, Mboni za Yehova mu Gibraltar ndi Spain ziri zogwirizana kotheratu mwauzimu, monga mmene ziri zowona padziko lonse lapansi. Izo zimaika chidaliro chawo mu “Thanthwe” limene mphamvu yake iri yosatha, akufuula mawu a wamasalmo: “Tiyeni tiyimbire Yehova mokondwera; tifuule kwa Thanthwe la chipulumutso chathu.”—Masalmo 95:1.