Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 5/15 tsamba 32
  • Anaorda Makope 50!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anaorda Makope 50!
  • Nsanja ya Olonda—1987
Nsanja ya Olonda—1987
w87 5/15 tsamba 32

Anaorda Makope 50!

Pamene bukhu la Life​—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? linatulutsidwa chifupifupi zaka ziwiri zapita, mkazi wina mu England anaganiza kuti lingakhale mphatso yabwino kaambaka amalume ake, mwamuna wa bizinesi wodziwika bwino wa zaka 84 m’derala Yorkshire. Chotero iye anamupatsakope.

Mkati mwa mlungu umodzi iye anamuitana iye ndi kunena: “Chozizwitsa, bukhu limene lija liri kokha chozizwitsa! Kodi ungandipezere makope ena owonjezereka? Ndingakonde kuwapatsa iwo monga mphatso kwa anzanga a bizinesi.”

Makope 25 okha analipo, ndipo iye mwamsanga anagawira amenewa pakati pa mabwenzi ake. Koma analikufuna 25 owonjezereka. Awa mwamsanga anapezedwa, ndipo iye anagawira iwo kwa mabwenzi ake​—onse pamodzi 50!

Mwinamwake mumadzimva ponena za bukhu la Creation mu njira yofanana ndi mmene mwamuna wa bizinesi ameneyu amachitira. Kodi mumadziwa winawake amene mungakonde kugawana naye chofalitsidwa chamalemba chimenechi? Bwanji osamutumizira munthu ameneyo kope la mphatso? Mungachite tero mwakungodzaza ndi kutumiza kapepala kali pansipa, kuikamo kokha K20. 00.

Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, kope la mphatso la bukhu la masamba 256 la Life​—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? limodzi ndi kalata yolongosola kuti iri mphatso yochokera kwa (dzina lanu). Ndatsekeramo K20. 00.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena