Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 5/15 tsamba 31
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Nkhani Yofanana
  • Mulungu Anaulula Cholinga Chake
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulira
  • ‘Nzeru ya Mulungu Imaonekera mu Chinsinsi Chopatulika’
    Yandikirani Yehova
  • Jehova Mulungu wa Chifuno
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Kodi Nchiyani Chimene Chiri Chifuno Chaulosi?
    Nsanja ya Olonda—1987
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 5/15 tsamba 31

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

◼ Mose anauza a Israyeli kuti “zinthu zovumbuluka nza ife ndi ana athu kosatha.” (Deutronomo 29:29) Kodi “zinthu zimenezo zovumbuluka“ zingaphatikizepo kuwala komwe kukuperekedwa pa Mawu a Mulungu mkati mwa masiku ano omaliza?

Ayi, sichingakhale cholondola kunena kuti kumvetsetsa kwa maulosi komwe tapatsidwa mkati mwa masiku ano otsiriza kuli pa mlingo umodzimodzi ndi “zinthu zovumbuluka“ zomwe Mose anali kulongosola.

Malinga ndi nkhani ya mawu a Mose, “zovumbuluka“ zomwe iye anali kulankhula ponena za izo zinayenera kuchita ndi pangano la Chilamulo. (Deutronomo 29:25) Mose anasonyeza kuti “zinthu zovumbuluka“ zimenezi zinali ndi mathayo. Kulephera kukhala ndi moyo kulinga ku mathayo amenewa kungapangitse Yehova kulanga anthu ake.

Pangano la lamulo, ngakhale kuli tero, linali vumbulutso lochokera kwa Yehova Mulungu. Ilo linatsatizidwa ndi zivumbulutso zina kwa makolo, kwa Nowa, ndi kubwerera m’mbuyo kwa Adamu. Mose anagwiritsidwa ntchito kulemba zinthu zovumbuluka kufika ku nthawi yake, ndipo zinasungidwa kaamba ka ife mu mabukhu asanu oyambirira a Baibulo. Pambuyo pake, monga mmene nkhani ya “Zinthu Zovumbulutsidwa Nzathu” (Nsanja ya Olonda, November 1, 1986) inalongosolera, “zinthu zovumbulutsidwa“ zimenezi zinabwera kuphatikizapo chidziwitso cholembedwa mu Baibulo.​—2 Timoteo 3:16.

Chotero, Baibulo liri ndi [“zonenedwa zopatulika NW] za Mulungu zinthu zovumbulutsidwa ndi iye. (Aroma 3:2) Pamene Ayuda achibadwa anatsimikizira kukhala osakhulupirika, Akristu odzozedwa anakhala athenga a “zinthu zovumbulutsidwa“ zimenezi, ndipo mpingo Wachikristu unakhala “mzati ndi mchirikizo” wa iwo. (1 Timoteo 3:15; 1 Akorinto 4:1) Chotero, ziwalo za mpingo umenewo lerolino moyenerera zingafuule mawu a Mose, kuti “zinthu zovumbuluka nzathu.”

Lerolino, Yehova waika kuwala kwambiri pa “zinthu zovumbuluka“ zimenezi. Monga kunanenedwera ndi Danieli, anthu a Yehova ‘afunafuna’ m’Mawu ouziridwa, ndipo ’chidziwitso chenicheni chakhala chochuluka.’(Danieli 12:4) Chotero, ife tsopano timadziwa chizindikiritso cha “nkhosa zina.” (Yohane 10:16) Timazindikiranso “khamu lalikulu.” (Chivumbulutso 7: 9-17) Timawona kukwaniritsidwa kwa fanizo la nkhosa ndi mbuzi. (Mateyu 25:31-46) Zinthu zoterozo zavumbulidwa, kapena kudziwikitsidwa, kwa ife osati mu lingaliro la “zinthu zovumbuluka“ monga zalembedwera m’Mawu ouziridwa a Yehova.

Chotero, sichingakhale cholondola kuika kupita patsogolo kumeneku mwa kumvetsetsa pa mlingo wofanana ndi zivumbulutso zouziridwa zomwe zimapanga “zinthu zovumbuluka“ zolembedwa mu Baibulo. M’malo mwake, kupyolera mu kuphunzira kosamalitsa kwa Baibulo, anthu a Yehova mwapemphero afuna kumvetsetsa kulondola kwa “zinthu zovumbuluka“ zimenezo. Yehova, kupyolera mwa mzimu wake woyera, wapereka kumvetsetsa kumeneku mu nthawi yake.

Baibulo limatiuza ife kuti “mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbanda kucha, kunkabe kuwala kufikira usana woti mbe.”(Miyambo 4:18) Kuwonjezeka kwa kuwala kumene Yehova akupereka pa “zinthu zovumbuluka“ kumasonyeza kuti “tsiku“ limenelo likuyandikira ndi kutsimikizira kuti dalitso lake liri pa mpingo Wachikristu lerolino.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena