Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 5/15 tsamba 4-7
  • Kodi ndi Mapindu Ena Ati Amene Amachokera kwa Mulungu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi ndi Mapindu Ena Ati Amene Amachokera kwa Mulungu?
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Magwero a Kuunika ndi Chiyembekezo
  • Nchifukwa Ninji Mtundu wa Anthu uli mu Mkhalidwe Wodetsedwa?
  • Mtsogolo Mwaulemerero
  • “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano”
    “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano”
  • Yesu Kristu, kupyolera mwa Amene Mulungu Adzawadalitsa Anthu
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Njira Yokha ya Moyo Wosatha
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Yesu Kristu—Kodi Anatumidwa ndi Mulungu?
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 5/15 tsamba 4-7

Kodi ndi Mapindu Ena Ati Amene Amachokera kwa Mulungu?

KODI MUMASANGALALA ndi maluwa okongola, kununkhira kwa maluwa a rose, nyimbo za mbalame? Kodi inu munasangalatsidwapo ndi kumwetulira koyambirira kwa mwana wanu? Kodi simumayamikira fungo lodzutsa chilakolako cha chakudya? Ndipo kodi ndi ndani amene samasangalala ndi uta wa Leza, kulowa kwa dzuwa kwa ulemerero, kapena nyenyezi pa usiku wopanda mitambo? Zopereka zochititsa chidwi za Mulungu ziri zosatha, kodi sitero?

Komabe, pali umphawi wochuluka. Mosasamala kanthu za kuthekera kwa dziko kutulutsa zochuluka kaamba ka onse, mamiliyoni sadya mokwanira. Mamiliyoni ochulukira apangidwa poizoni ndi kuwononga. Ndipo mabiliyoni lerolino akhudzidwa ndi chiwawa, umbombo, kudzikonda, ndi mantha ponena za nchiyani chimene mtsogolo mudzabweretsa.

Popeza Mlengi wakhala wopereka moolowa manja chotero, kodi nchifukwa ninji pali kupanda chimwemwe kochuluka kotero? Pulaneti iyi iri malo osangalatsa kwambiri, opangidwa kaamba ka ife kuti tisangalale. Koma dziko​—mtundu wa anthu— ​uli mmkhalidwe womvetsa chisoni kwambiri. Kwa nzika zambiri za padziko lapansi, kawonedwe kali kakuda, kochititsa mantha. Kodi nchifukwa ninji? Kodi nchiyani cholakwika chimene chinachitika? Kodi Mulungu anapanga munthu ndipo kenaka kumunyalanyaza iye? Kodi pali kuwala kulikonse pa mkhalidwe wozizwitsa umenewu? Kodi tiri ndi chiyembekezo chiri chonse kaamba ka mtsogolo?

Magwero a Kuunika ndi Chiyembekezo

Chifupifupi zaka 2, 000 zapita mwana wamwamuna wapadera anabadwa​—wapadera chifukwa chakuti mayi wake, Mariya, anali munthu, ndipo atate wake anali Mulungu iye mwini! ‘Nchosatheka!’ kodi ena amatero? Ayi, osati kwa Muyambitsi wakukhalako kwa moyo, Mpangi wambali zonse zocholowanacholowana za moyo. Mnyamata wachichepere ameneyo anakula kukhala wangwiro “munthuyu, Kristu Yesu.”​—1 Timoteo 2:5; Mateyu 1:18-25.

Kunali kubadwa kopanga mbiri. Mchenicheni, mitundu yambiri imavomereza chimenechi mwa kuika madeti ku zochitika za m’mbiri lisanafike tsiku lake monga B. C.​—asanafike Kristu. Koma zaka zake zoyambirira zinawonongedwa mwakachetechete monga wopala matabwa wothandizira wa atate wake olera mu Nazarete. Zaka makumi atatu zinapita. Kenaka, pa Mtsinje wa Yordano, Yesu anadzipereka iyemwini kuchita chifuniro cha Mulungu ndipo anabatizidwa, ndipo mzimu woyera wa Yehova Mulungu unatsika pa iye. (Mateyu 3:13-17) Yesu kenaka anayamba ndawala yamphamvu ya kulalikira ndi kuphunzitsa. Monga kunanenedwera ndi Yesaya, “anthu okhala mumdima anawona kuwala kwakukulu.”​—Mateyu 4:14-17; Yesaya 9:2.

Yesu anakhala Mphunzitsi wotchuka kwambiri ndi wolemekezedwa koposa wanthawi yonse. Palibe mphunzitsi wina aliyense wa munthu yemwe anapereka chisonkhezero champhamvu choterocho pa anthu kapena kupereka kuwala kwauzimu kochuluka ndi chiyembekezo. Kodi nchiyani chimene chinali bukhu lake lophunzirira? Baibulo, monga mmene linaliri nthawiyo​—Malemba Achihebri kapena “Chipangano Chakale.” Yesu anawapanga iwo kukhala amoyo. Maulosi ambiri akale anakwaniritsidwa mwa iye. (Yerekezani Mika 5:2 ndi Mateyu 2:3-6. ) Iye anatsimikizira mbiri ya mu Genesis ponena za chiyambi cha munthu. (Genesis 2:24; Mateyu 19:3-6) Yesu anatenga, kukulitsa, ndi kubukitsa kofala mutu weniweni wa Baibulo​—kuyeretsa dzina la Yehova mwa Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 4:23; 6:10) Kuwonjezerapo, mbiri za moyo ndi ntchito za Yesu Kristu ziri mbali zowonekera za Malemba a Chikristu Achigriki kapena “Chipangano Chatsopano.” Inde, Baibulo linali mphatso yodabwitsa yochokera kwa Mulungu, kuwala konyezimira mumdima, dziko lachisoni.​—Ma salmo 119:105.

Nchifukwa Ninji Mtundu wa Anthu uli mu Mkhalidwe Wodetsedwa?

Kodi Baibulo limayankha funso limenelo? Inde. Limasonyeza kuti sinali nkhani ya Mulungu kunyalanyaza munthu koma, mmalo mwake, ya munthu kunyalanyaza Mulungu. Kachiwirinso, prinsipulo loyambirira la ufulu wa kusankha linaphatikizidwamo. Anthu analengedwa osati monga maroboti, okonzekeretsedwa kumvera. Timasankha kumvera kapena kusamvera.

Pamene Mulungu analenga anthu awiri oyambirira mu Paradaiso wokongola mu Edene, anali achimwemwe chotani nanga ndi aufulu! Popanda matenda, popanda mantha, popanda kudandaula. Mbalame zokongola ndi zinyama zinalipo, ndipo panali chakudya chabwino chochuluka. (Genesis 1:26; 2:7-9) Mkupita kwanthawi, ngakhale kuli tero, mdani wosawoneka anabwera pachochitikacho. Cholengedwa chauzimu champhamvu chinakhala chonyada, kusilira kuyang’anira banja la munthu la mtsogolo. Mwakunena bodza loyamba, iye ananyenga Hava, ndipo Adamu anakakamizidwa kusamvera lamulo la Mulungu lakusadya chipatso choletsedwa. (Genesis 3:1-7) Monga ambiri lerolino, anthu oyambirirawo anaganiza kuti ‘angachite chinthu cha iwo eni.’ Koma mwakutero iwo mchenicheni anadziika iwo eni pansi pa ulamuliro wa Satana, mulungu wa dongosolo la kachitidwe ka zinthu loipa liripoli.​—2 Akorinto 4:4.

Ichi chinadzutsa nkhani yaikulu ndipo yofunika kwambiri: Kodi munthu mwachipambano angadzilamulire iye mwini popanda Mulungu? Chikafunikira nthawi yokulira kuthetsa funso limeneli mokhutiritsa. Panthaŵi ino, Adamu ndi Hava anayenera kulandira chilango chimene Mulungu anali atachinena​—imfa. Ndipo popeza iwo anakhala ochimwa adala, osati iwo kapena mbadwa zawo zinali ndi chiyembekezo chirichonse cha moyo wosatha osadalira pa Mulungu.​—Aroma 5:12; 1 Akorinto 15:21, 22.

Mtsogolo Mwaulemerero

Kuyambira mtsiku la Adamu mibadwo yambiri yabwera ndi kupita. Ndipo mu chochitika chosinthasintha cha zinthu za anthu, mitundu yosiyanasiyana ya maboma a anthu ayesedwa—autokrasi, demokrasi, sosholizimu, komyunizimu, ndi ena. Koma onse alephera. Ndale za dziko, mayanjano, ndi mavuto a dziko lonse ali kupita patsogolo; choteronso zida zopatsa imfa za kusakaza kokulira zomwe zikuwopsyeza kudzipha kwa dziko. Mkati mwa Nkhondo Yadziko II, andale za dziko a Kumadzulo analonjeza kuti chipambano chidzabweretsa ufulu ku kusowa ndi mantha, koma ziwiri zonse zikuwonjezeka.

Kodi yankho nchiyani? Vuto lalikulu kwambiri limafunikira mankhwala okulira koposa​—osati china chake koposa kuyeretsa kwa dziko lonse ndi kubweretsedwa kwa dziko latsopano. Kodi ndani amene angakwaniritse chimenecho? Mwachiwonekere osati Mitundu Yogwirizana kapena kuphatikiza kuli konse kwamphamvu za ndale za dziko kumene kaŵirikaŵiri kumaphwanya mapangano a mtendere chifupifupi mainawo asanaume! Iwo ali kokha tinthu topanda thandizo mu mphamvu yogwira ya Usatana. (1 Yohane 5:19) Yehova yekha, Wamphamvuyonse, angachotse Satana ndi ziwanda zake, kuika kumapeto dziko lovunda liripoli ndi kubweretsa dziko la ulemerero pansi pa Ufumu wa kumwamba wa Mwana wake, Yesu Kristu, monga Mfumu ya mafumu.​—Mateyu 6:9, 10; Danieli 2:44; Chivumbulutso 20: 1-3.

Kodi nchiyani chimene Ufumuwo udzakwaniritsa? Kodi ndani amene adzapulumuka kuyeretsa kosakaza kwa dziko lonse, kapena Armagedo? Nsonga yosangalatsa kwambiri ndi yakuti anthu ochuluka kwambiri akufika ku kuzindikira kuti boma lakumwamba limeneli liri kugwira ntchito lerolino ndipo liri kukonzekeretsa anthu kaamba ka kupulumuka Armagedo! (Chivumbulutso 16:14-16) Kodi ndi mtundu wa anthu otani umene iwo ayenera kukhala? Yesu Kristu anati: “Odala ali akufatsa; [odekha mtima] chifukwa adzalandira dziko lapansi.” (Mateyu 5:5) Iye mwakutero anatsimikizira ulosi wamakedzana: “Lisanakugwereni tsiku la mkwiyo wa Yehova. Funani Yehova, ofatsa inu nonse a m’dziko, amene munachita chiweruzo chake; funani chilungamo, funani chifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.”​—Zefaniya 2:2, 3.

Ofatsa adzapulumuka osati kokha Armagedo koma, mwa kukhalabe okhulupirika kwa Mulungu, adzalandiranso moyo wosatha. Motani? Monga kwatchulidwa kale, banja lalikulu la mbadwa za Adamu linataya ziyembekezo zamoyo wosatha kupyolera mu kuchimwa kwakekwa kusamvera. Imfa inafika pa mtundu wonse wa anthu kupyolera mwa Adamu. Popezaiye anali munthu wangwiro, munthu wina wangwiro anafunikira kaamba ka dipo, kapena kugulanso, chimene Adamu anataya. Yesu Kristu anakwaniritsa chosowa chimenecho ndi kupereka moyo wake “kuti yense wakukhulupirira iye asataike, koma akhale nawo moyo wosatha.”​—Yohane 3:16.

Kupereka kwa dipo kumeneku kuli mphatso yaikulu kwambiri ya Mulungu kwa munthu. Lidzagwira ntchito osati kokha kwa awo amene adzapulumuka kulowa mu dziko latsopano komanso kwa awo obwera kuchokera kwa akufa. Kodi chimenecho chikumvekera kukhala chozizwitsa koposa? Yesu anati: “Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthawi, imene onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira, amene adachita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma amene adachita zoipa kukuuka kwa kuweruza.” Chiri chosangalatsa chotani nanga! Chidzakhala chachimwemwe chotani nanga kwa opulumuka Armagedo, amene adzakhala okhoza kulandira okondedwa awo kuchokera ku imfa!​—Yohane 5:28, 29.

Ndi chiyang’aniro chaulemerero ndi chiyembekezo chotani nanga! Ndipo zonse izi zaperekedwa ndi Mlengi wachikondi, Yehova, kupyolera mwa Mwana wake wokondedwa, Yesu. Ngakhale kuti lerolino kawonedwe kakuwoneka kakuda ndi kochititsa mantha, mtsogolo muli modzaza ndi kuwala ndi chiyembekezo kaamba ka awo amene amaphunzira Baibulo ndi kugwirira ntchito pa uthenga wake wotenthetsa maganizo. Tikukhala mnthawi zosangalatsa. Ufumu wa Mulungu wayandikira. (Mateyu 24:33, 34) Lemekezani Yehova, Mpatsi wa “mphatso iriyonse yabwino, ndi chininkho chiri chonse changwiro”!​—Yakobo 1:17.

Pamene mukusinkhasinkha panjira zambiri zimene tingapindulire kuchokera ku zoperekedwa za Mulungu ndi zifuno zake, mungamve lingaliro lozama la chiyamikiro ndi chikhumbo cha kusonyeza icho mu njira ina yake. Koma ngati mwangoyamba kumene kumvetsetsa ndi kuvomereza chiyembekezo chenicheni kaamba ka mtsogolo, mungamve kufunika kwa kukumba mozama. Tikukulimbikitsani inu kuchita chimenecho. Pitirizani kuphunzira Mawu a Mulungu limodzi ndi zofalitsidwa monga ngati ichi zomwe zingakuthandizeni kuwonjezera chidziwitso chanu ndi chiyamikiro chanu kaamba ka zifuno zaulemerero za Mulungu.

Awo amene ali kale ndi chitsimikiziro chabwino chakuti Ufumu wa Mulungu uli kokha yankho ku adani amtundu wa anthu angadzimve monga anachitira wamasalmo wouziridwa amene anati: “Ndidzabwezera Yehova chiyani chifukwa cha zokoma zake zonse anandichitira?” (Masalmo 116:12) Anthu oterowo angapeze kuti kuuza ena ponena za zimene Mulungu wachita kaamba ka ife ndi mtsogolo mwaulemerero mmene iye amapereka kwa awo amene amakonda ndi kutumikira iye kumabweretsa chikwaniritso chozama ndi chimwemwe chenicheni. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti, monga mmene Yesu ananenera: “Muli chimwemwe chambiri m’kupatsa koposa ndi chimene chiri m’kulandira.”​—Machitidwe 20:35, NW.

[Bokisi pa tsamba 5]

YESU KRISTU—

◆ Anakwaniritsa maulosi ambiri akale, mwachitsanzo, Mika 5:2; Mateyu 2:3-6

◆ Anatsimikizira mbiri ya mu Genesis ya chiyambi cha munthu​—Mateyu 19:3-6

◆ Anakulitsa ndi kubukitsa mutu weniweni wa Baibulo, kuyeretsa dzina la Yehova mwa Ufumu​—Mateyu 4:23; 6: 9, 10; Luka 8:1

◆ Anabwezera chimene Adamu anataya, moyo wa munthu wangwiro, mwakutero kutheketsa awo amene amakhulupirira mwa iye kupeza moyo wosatha —Yohane 3:16

[Bokisi pa tsamba 7]

‘Kodi nchiyani chimene mudzabwezera Yehova kaamba ka mapindu ake onse?’

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena