Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 4/15 tsamba 3-4
  • Nzeru ya Mulungu Kodi Mukuiwona lyo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nzeru ya Mulungu Kodi Mukuiwona lyo?
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Nzeru ya Yehova Izindikiritsidwa
  • Nzeru Yachibadidwe ya Zinyama
  • Nzeru Yakumwamba ya Yehova
  • ‘Nzeru za Mulungu N’zozama’
    Yandikirani Yehova
  • Tamandani Mfumu Yamuyaya!
    Nsanja ya Olonda—1996
  • ‘Wodala Munthu Wopeza Nzeru’
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Kodi Mumagwiritsa Ntchito “Nzeru Yochokera Kumwamba” pa Moyo Wanu?
    Yandikirani Yehova
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 4/15 tsamba 3-4

Nzeru ya Mulungu Kodi Mukuiwona lyo?

ONANI M’MAGANIZO MWANU bwalo la milandu la mfumu yakale. Pamenepo itavala mwinjiro wachifumu yakhala pa mpando wachifumu waulemerero pamene ikuyang’anira. Iye ali wolemekezedwa osati kokha chifukwa cha chuma chake komanso chifukwa chanzeru yake. Atumiki ake a bwalo la milandu ali ogwirizana mwaungwiro. Malo aulemerero ali otenga mpweya. Tawonani: Mfumu Solomo!​—1 Mafumu 10:1-9, 18-20.

Tamverani, tsopano, kwa munthu wozindikiridwa monga Mphunzitsi Wamkulu wanthawi zonse: “Ndipo muderanji nkhawa ndi chovala? Tapenyetsani maluwa a kuthengo, makulidwe awo; sagwiritsa ntchito, kapena sapota; koma ndinena kwa inu, kuti angakhale Solomo mu ulemerero wake wonse sanavala monga limodzi la amenewa.”​—Mateyu 6:28, 29.

Kodi nchiyani chimene Yesu anatanthauza ndi chimenecho? Chabwino, iye mowonadi anali kupereka uphungu ponena zakusakhala wokonda zinthu zakuthupi. Koma kodi mawu ake ponena za Solomo akanakhaladi owona? Kumbukirani, Yesu anagwiritsira ntchito mafanizo a moyo weniweni. Chotero odziwa kulemba a Solomo ndi owumba ake, ngakhale anali ozolowerera, sakanafanana ndi zokonzedwa, kusakaniza kwa mitundu, ndi kugwirizana kwa “maluwa a m’minda” okhazikitsidwa mu malo awo achibadwa.

Nzeru ya Yehova Izindikiritsidwa

Ngakhale kufufuza kochepera kwa maluwa kungakupangitseni inu kutsimikizira mawu a Yesu. Ife sitidziwa ndi mtundu wanji wa kakombo umene Yesu anali nawo m’maganizo, koma maluwa amera mmbali zambiri za dziko lapansi. Yang’anani mosamalitsa pa duwa, duwa liri lonse: kakombo, rose, orchid. Ndi mitundu ya mtundu ndi makonzedwe ocholowanacholowana otani amene mumawona, atasakanizidwa ndi timasamba tamaluwa, masamba, ndi mbali zina za thunthu la duwa. Kodi mungawone umboni wachete koma wamphamvu wakuti Wopanga Wamkulu wanzeru yosayembekezereka ndi malingaliro ali kumbuyo kwa ntchito yokongola ya manja imeneyi? Sikokha kuti maso athu amasangalala mu kukongola kwawo komanso mphuno zathu zimakoka kununkhira kwawo mpweya umene timapuma.

Mtumwi Paulo anawona kuti “zawoneka bwino zosawoneka za Yehova Mulungu ndipo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa.” (Aroma 1:20) Komabe, Mulungu analenga zowonjezereka kuposa maluwa kukongoletsa dziko; iye anapanga zitsamba zosawerengeka ndi mitengo, zonse za zimene zimapanga ufumu weniweni, ndiponso wokongola wobiriwira. Ngati mungafike ku Humboldt National Forest mu California, U. S. A. , mungapeze mtengo waukulu kwambiri wofiira womwe umakhulupiriridwa kukhala mtengo wautali koposa m’dziko lonse lapansi. Ngati mungaime patsinde pake ndi kuyang’ana m’mwamba pa msinkhu wake woposa mapazi 360 (110 m), kodi simungalemekeze mwachete amene anadziwa kapangidwe ka mtengo woterowo?

Nzeru Yachibadidwe ya Zinyama

Padziko ndi mnyanja muli zinyama, zazing’ono ndi zazikulu, zomwe zimasindikiza pa ife nzeru ya Mulungu. Mwachiwonekere iri yonse imatumikira chifuno china chake cha Mlengi. Mfumu Solomo yanzeru inapereka uphungu: “Pita kunyerere, wolesi iwe, penya njira zawo nuchenjere.” (Miyambo 6:6) Awo amene anapenyetsetsa nyerere amazizwa ndi kuthekera kwa kugwirizana kwa nyerere. Nyerere sizimadzipatula; zimakhala muunyinji. Zina ziri alimi ndipo zimatuta mbewu. M’maiko otentha mungawone nyerere zina motanganidwa zikubudula zidutswa zamasamba kuti zitengere ku chisa chawo. Kodi ndimotani mmene zimadziwira kuchita chimenechi? Aguri, mmodzi wa alembi a bukhu la Miyambo, akuyankha kuti nyererezo “ziri zopambana kukhala zanzeru.” Kodi ndani amene anazipanga izo kukhala zotero? Yehova, Mpangi wa kumwamba ndi dziko lapansi.​—Miyambo 30: 24, 25.

Inde, chilengedwe cha zinyama chiri ndi nzeru yachibadwa. Chiri chowonekeratu mwakusamuka kwa mbalame. Mungakhale munamvapo ponena za kusamuka kwa Capistrano swallows. Panthawi ina yake chaka chiri chonse, izo zimayenda zikwi za mamailosi kuchokera ku maenje awo a mu nthawi ya chisanu mu South America kupita ku malo ena ku San Juan Capistrano, California, U. S. A. Mwachibadidwe ndipo mosalakwa izo zimabwera ku malo amodzimodziwo panthawi imodzimodziyo, March.

Ponena za nyanja yaikulu, wamasalmo akunena: “Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru; dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu. Nyanja siyo, yaikulu ndi yachithando, momwemo muli zokwawa zosawerengeka.” (Masalmo 104:24, 25) Kuyambira kutimatemba tating’ono kufika ku zinsomba zazikulu, nzeru ya umulungu imawonekera mukapangidwe kawo ndi kugwira ntchito kwawo.

Kukongoletsa kwa Mulungu kwa chilengedwe chapadziko lapansi anali munthu iyemwini. Tsopano panali cholengedwa chimene sichinachite chinthu kokha chifukwa cha nzeru yoikidwa mkati, kapena nzeru yachibadidwe. Iye anali ndi kuthekera kwakukhala monga Mulungu mnjira zambiri. Chiri chowona motani ponena za iye kuti “chipangidwe chake ndi choopsya” ndipo anapangidwa modabwitsa! Ngakhale kuti sitiri asayansi a mankhwala, tingawerengere ponena za zopeza zawo ndi kupanga chigamulo chofanana ndi cha wolemba wouziridwa. Ntchito za Mlengi zowonekera muthupi la munthu m’zodabwitsa.​—Masalmo 139:14.

Nzeru Yakumwamba ya Yehova

Masalmo 19:1 amanena kuti zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu. Kodi ziri zowonadi motani! Wamasalmo Davide analibe chida chomuthandiza kuwona kutali kapena zida za magetsi, koma iye anali ndi chiyamikiro chenicheni ponena za zimene iye akanatha kuwona. Lerolino munthu wa maphunziro okwanira amadziwa zochulukira kwambiri kuposa zimene Davide anadziwa ponena za dongosolo lathu lakuunikira ndi mbali yathu ya mtambo yomwe iri yowala kwambiri chifukwa cha nyenyezi, mlalang’amba. Iye amadziwanso kuti pali unyinji wosawerengeka wa milalang’amba m’malekezero opanda malire athambo. Kodi mumamva motani; pamene mukulingalira nzeru yaikuru ndi yosayerekezeka ya wopanga? Kodi munganene ndi liwu lenileni: ‘Yehova, “mukupanga zinthu zazikulu zosasanthulika, ndi zodabwiza zosawerengeka”’? Muyenera kutero.​—Yobu 9:10.

Mu zaka zapita zosatchulidwa Yehova anayamba ntchito yake ya chilengedwe, choyamba ndi Mwana wake wobadwa yekha, kenaka zolengedwa zake zauzimu. Ichi chinatsatiridwa ndi dziko lonse la kuthupi. Zonse zinali zabwino ndi za dongosolo. Nchifukwa ninji, ana aungelo a Mulungu mchenicheni anafuula chiyamikiro chawo mwakukweza mawu awo pakukhazikitsidwa kwa dziko lapansi! (Yobu 38:4-7 ) Mwamuna ndi mkazi analengedwa ndipo anaikidwa m’munda wangwiro, koma kenaka chinthu chochititsa mantha chinachitika. Liwu linamveka kuchokera kosawoneka, likumalankhula kupyolera mwa chinjoka, kunamizira Mlengi Wamkulu. Ilo linaimba mlandu kuti Yehova anali kugwiritsira ntchito molakwika ulamuliro wake; linamutcha Mulungu kukhala wabodza. Chotero, mwini wa liwulo anapeza maina oipa amene amamuzindikiritsa iye Mdyerekezi, Chinjoka, ndi Satana. Kodi nchiyani chimene tsopano Wanzeru Zonse adzachita? Kodi nchiyani chimene akanachita? Mbali yatsopano yanzeru ikanafunikira yomwe ikanawombanitsa zokonzedwa zomwe zinali kuwala kale mu ulemerero wa Solomo.​—Genesis 3:1-5.

[Mawu Otsindika pa tsamba 4]

Kuyambira ku timatemba tating’ono kufika ku zisomba zazikulu, nzeru ya umulungu imawoneka mu mkhalidwe wawo ndi kugwira ntchito kwawo

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena