Mulungu Kodi Iye Ali Munthu Weniweni?
”PAYENERA kukhala Mulungu” inalengeza choncho kope ya Daily Express ya August 14, 1981. Pepalalo linali kusimba pa za kutembenuzidwa kwa asayansi otchuka kwambiri awiri kuchikhulupiriro mwa Mulungu Chitsimikiziro chawo chopezedwa posachedwa chinatuluka pambuyo pakupeza masamu osatsimikizirika otsutsana ndi kuwoneka kwa moyo kwa mwadzidzidzi. Komabe, kodi nchiyani chimene okhulupirira atsopano awiri amenewa anatanthauza pamene ananena kuti “Mulungu.” Ikusimba motero DailyExpress: “Mulungu iwo akulingalira, ALI dziko lonse.’
Ngati inu mumakhulupirira mwa Mulungu, kodi nchiyani chimene chiri cholingalira chanu cha iye? Kodi inu mofananamo mumamuwona iye monga chinthu chanzeru chosalongosoleka, mphamvu yosawoneka yopezeka ponseponse, “Chinthu China Chake” chachikulu? Kapena kodi mumamuwona iye monga wolongosoleka, Munthu wanzeru?
Ena amachipeza icho kukhala chovuta kulingalira za Mulungu monga Munthu. Iwo angamve kuti kuchita tero kumamuchepetsa iye kukhala cholengedwa chaumunthu—monga mu chifanizo chachibwana cha munthu wachikulire wovala mkanjo wophimba kumutu ndi mapewa ndi ndevu zazitali zoyera, atakhala pamitambo. Kapena monga mmene Michelangelo anasonyezera Mulungu mu chithunzi chake chotchuka cha Sistine-chapel, wanyonga, munthu wachikulire wamphamvu yemwe amayandama mumpweya.
Zowona, pamene timamva liwu lakuti “munthu,” ife mwachidziwikire tingalingalire za munthu. Webster’s Third New International Dictionary, mwachitsanzo, limatanthauzira “munthu” monga “munthu aliyense payekha.” Koma ilonso limatanthauzira “munthu” monga “chinthu chozindikiritsidwa ndi kumvetsetsa kwa kuzindikira, kulinganiza, ndi maganizo abwino.” Chotero wina molondola angalingalire za Mulungu monga munthu kopanda kumufanizira iye monga munthu.
‘Koma ena angatsutse: ‘Ndikusiyana kotani nanga kumene kumapanga kaya kuti mumawona Mulungu monga mphamvu yosawoneka kapena monga Munthu?’ Chabwino, ngati Mulungu ali mphamvu chabe, “Chinthu china chake,” kodi chimenecho sichimatanthauza kuti moyo wa munthu uli mofananamo wamachitidwe? Munthu chotero angathe kuchepetsedwa kufika ku “icho,” kadzino mu makina aakulu. Koma ngati Mulungu ali munthu wanzeru, kodi chimenecho sichidzapatsa moyo tanthauzo lokulira? Indedi, chidzatsegula njira yakuthekera kwakukhala ndi unansi ndi Mulungu—unansi osati pakati pa “izo” ziwiri koma pakati pa anthu awiri.
Mwachiwonekere, unansi wa munthu ku Munthu ndi Mulungu udzakhala wokhumbirika koposa. Koma pachiyambi, kodi timadziwa bwanji kuti kaya Mulungu ali Munthu kapena ayi? Ndipo, ngati iye ali, ndimotani mmene tingakhalire ndi unansi woterowo? Tiyeni tiwone chimene Baibulo linganene pankhaniyi.