‘Limapitirira Zoyembekezera Zonse’
Mwamuna wa mu Netherlands wolembedwa ntchito monga wofufuzafufuza wa sayansi analemba kuti: “Sikaŵirikaŵiri kuti ndimatenga peni yanga kulongosola chiyamikiro changa kaamba ka zinthu zomwe ndawerenga. Koma chofalitsidwa Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? liridi bukhu lapadera.”
Mwamunayo akulongosola kuti iye tsiku ndi tsiku amakumana ndi ophunzira zaumoyo ndipo kuti “chingatenge chozizwitsa kaamba ka oterowo kukhutiritsidwa nkomwe ponena za chilengedwe. Koma bukhu limeneli kwenikwenidi limapitirira zoyembekezera zonse. Kumangiriridwa kwanzeru kwa mitu yake ndi zisonyezero zake ziri zamakono mwasayansi kotero kuti ukafunikira kukhala wakhungu kuti udzutse zitsutso zirizonse ponena za izo. . . . Chinthu chowonjezera kuposa chiri chonse chimene chimalipanga bukhuli kukhala lolemekezedwa ziri zisonyezero za mabuku mu amene anthanthi otchuka amaloledwa kulankhula . . . Ine kwenikwenidi ndikulingalira kulibweretsa bukhuli ku chidziwitso cha ena a anzanga (akale ndi amtsogolo).”
Tikuganiza kuti inunso mudzamva ponena za bukhu la Creation monga mmene wofufuzafufuza wa sayansi uyu wachitira. Tumizani lero kaamba ka bukhu la zithunzithunzi zokongola la masamba 256 limeneli.
Chonde tumizani, mutalipiliratu positi, bukhu la Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? (mu Chingelezi) Sonyezani mwa kuchonga mabokosi osiyanawo kaya mukufuna laling’ono pa K6. 25 [ ], kapena mukufuna lalikulu pa K12. 50, [ ] ndipo tsekeranimo zopereka zoyenerera.